Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhulupirira Kuti Mdyerekezi Alikodi?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Mdyerekezi Alikodi?

Kodi Mumakhulupirira Kuti Mdyerekezi Alikodi?

MALEMBA amasonyeza kuti Mdyerekezi aliko. Iyeyu sitingathe kumuona pa chifukwa chofanana ndi chimene anthufe timalepherera kuona Mulungu ndi maso. Baibulo limati: “Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 4:24) Mdyerekezi ndi cholengedwa chauzimu. Koma mosiyana ndi Mlengi, Mdyerekezi ali ndi poyambira pake.

Kale Yehova Mulungu asanalenge anthu, anapanga kaye zolengedwa zauzimu zambirimbiri. (Yobu 38:4, 7) M’Baibulo, zolengedwa zimenezi zimatchedwa kuti angelo. (Ahebri 1:13, 14) Angelo onse amene Mulungu analenga anali angwiro ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mdyerekezi kapena wokhala ndi khalidwe lililonse loipa. Nanga kodi Mdyerekezi anabwera bwanji? Liwu lakuti “mdyerekezi” limatanthauza “woneneza,” kutanthauza munthu amene amanena mabodza anjiru onena za anthu ena. “Satana” limatanthauza kuti “Wotsutsa.” Monga mmene munthu amene poyamba anali woona mtima amadzipangira yekha kukhala mbava mwa kuyamba kuba, mmodzi mwa ana a Mulungu angwirowo anayamba kukhala ndi chilakolako choipa ndipo anadzipanga yekha kukhala Satana Mdyerekezi. Baibulo limafotokoza mmene munthu amayambira kukhala woipa podzinyenga yekha motere: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chim’kokera, nichim’nyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.”​—Yakobo 1:14, 15.

Zimenezi ndizo zenizeni zimene zinachitika. Pamene Yehova Mulungu amalenga anthu awiri oyamba, Adamu ndi Hava, n’kuti mngelo amene anadzapandukira Mulunguyu akuona. Ankadziwa kuti Yehova analamula Adamu ndi Hava kuti adzaze dziko lapansi ndi anthu olungama, amene azidzapembedza Mlengi. (Genesis 1:28) Mngeloyu anaona kuti n’zotheka kuti angathe kupeza ulemu ndiponso kutchuka. Mosonkhezeredwa ndi dyera, iye analakalaka chinthu chimene chinali choyenera Mlengi yekha, chomwe ndi kupembedza kochokera kwa anthu. M’malo mokana chilakolako choipacho, mwana wauzimu wa Mulunguyu analola malingaliro oipawo kukula mpaka pamene anabala bodza ndipo kenako mpaka kupanduka. Tamvani zimene anachita.

Mngelo wopandukayu anagwiritsa ntchito njoka kulankhula kwa mkazi woyamba Hava. Njokayo inafunsa Hava kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava atafotokoza zimene Mulungu anawalamula kuchita ndiponso chilango chake ngati atapanda kumvera, njokayo inati: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, [mtengo umene uli m’kati mwa munda] adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:1-5) Apatu nkhani inali yakuti, Mulungu sanauze Adamu ndi Hava chilungamo. Ngati Hava atadya chipatso cha mtengowo, anati akhoza kukhala ngati Mulungu, wokhala ndi mphamvu yodzisankhira chimene chili chabwino ndi choipa. Ili ndilo limene linali bodza loyamba kunenedwa. Kunena bodza limeneli kunam’pangitsa mngelo ameneyu kukhala woneneza. Ndipo iye anakhalanso wotsutsa Mulungu. Chotero Baibulo limafotokoza mdani wa Mulungu ameneyu monga “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.”​—Chivumbulutso 12:9.

Khalani Maso

Bodza limene Mdyerekezi analinena kwa Hava, linagwiradi ntchito monga mmene iye anakonzera. Baibulo limanena kuti: “Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso.” (Genesis 3:6) Hava anakhulupirira Satana ndipo sanamvere Mulungu. Ndipo anathanso kum’sonkhezera Adamu kuti aphwanye lamulo la Mulungu. Choncho Mdyerekezi anapambana pa cholinga chake chakuti mwamuna ndi mkazi oyambirirawo apandukire Mulungu. Kuyambira nthawi imeneyo, Satana wakhala akulamulira anthu pa zochita zawo mwakabisira. Kodi cholinga chake n’chotani? Amafuna kuti anthu asiye kupembedza Mulungu woona ndiyeno n’kuyamba kupembedza iyeyo. (Mateyu 4:8, 9) Choncho, pachifukwa chabwino Malemba amachenjeza kuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire.”​—1 Petro 5:8.

Apatu Baibulo limamufotokoza bwino kwambiri Mdyerekezi monga mzimu, mngelo amene anakhala woipa ndiponso woopsa. Mbali yoyamba ndiponso yofunika kwambiri kuti tikhale maso ndiyo kudziwa kuti Mdyerekezi alikodi. Koma kukhala maso kumaphatikizapo zinthu zambiri. M’pofunikanso kuti tisakhale mbuli ponena za “machenjera” ake ndiponso njira zake zimene amasokeretsera nazo anthu. (2 Akorinto 2:11) Kodi njira zimene amasokeretsa nazo anthu ndi ziti? Ndipo kodi tingatani kuti tilimbane naye?

Mdyerekezi Amapezerapo Mwayi pa Chibadwa cha Anthu

Satana wakhala akuwadziwa bwino kwambiri anthu kuchokera pamene munthu analengedwa. Amadziwa bwino mmene munthu anapangidwira, zimene amafuna, zimene amakonda, ndiponso zimene amalakalaka. Satana amadziwa bwino kwambiri kuti munthu analengedwa kuti azikonda zinthu zauzimu, ndipo Mdyerekeziyu mochenjera amagwiritsa ntchito kukonda zinthu zauzimu kumeneko m’njira yolakwika. Motani? Mwa kuphunzitsa anthu ziphunzitso zabodza za zipembedzo. (Yohane 8:44) Ziphunzitso zambiri zimene zipembedzo zimaphunzitsa ponena za Mulungu zimatsutsana ndipo n’zosokoneza. Kodi mukuganiza kuti zimakwaniritsa zofuna za ndani? Ziphunzitso zotsutsana sizingakhale zoona zonse ayi. Kodi si zotheka pamenepa kuti ziphunzitso zambiri za zipembedzo n’zokonzedwa ndi Satana ndiponso kuti akuzigwiritsa ntchito kusokeretsera nazo anthu? Ndipotu Baibulo limanena za iye kuti ndi “mulungu wa nthawi ino ya pansi pano,” amene wachititsa khungu mitima ya anthu.​—2 Akorinto 4:4.

Choonadi cha Mulungu chimateteza ku mabodza a zipembedzo. Baibulo limayerekezera choonadi cha Mawu a Mulungu ndi lamba wachikopa amene msilikali wa m’nthawi yakale ankavala kuteteza chiuno chake. (Aefeso 6:14) Ngati mutaphunzira choonadi cha Baibulo ndi kuchisunga, monga ngati kuti mwachivala ngati lamba wachikopa, Mawu a Mulungu adzakutetezani kuti musasokeretsedwe ndi mabodza a zipembedzo ndiponso zolakwa zake.

Chibadwa cha munthu chokonda zinthu zauzimu cham’pangitsa kufufuza zinthu zosadziwika. Zimenezi zapangitsa kuti munthu alowe mu msampha wina wa bodza la Satana. Pogwiritsa ntchito molakwa chidwi chimene anthu ali nacho chofuna kudziwa zinthu zachilendo ndiponso zodabwitsa, Satana wagwiritsa ntchito zamizimu pofuna kuti azilamulira anthu ambiri. Monga mmene mlenje amagwiritsira ntchito nyambo kunyengerera nyama kuti igwidwe, Satana wabweretsa zinthu monga kulosera za m’tsogolo, kukhulupirira nyenyezi, kugoneka tulo, ufiti, kupenda zikhatho ndiponso zamatsenga n’cholinga chofuna kukopa ndiponso kukola anthu padziko lonse.​—Levitiko 19:31; Salmo 119:110.

Kodi mungadziteteze bwanji kuti musagwidwe mu msampha wokhulupirira mizimu? Lemba la Deuteronomo 18:10-12 limati: “Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.”

Malangizo a m’Malemba ndi osapita m’mbali. Amati: Musachite chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. Nanga bwanji ngati mwakhala mukuchita zinthu zina zokhudzana ndi zamizimu ndipo tsopano mukufuna kusiya? Mungathe kutsatira chitsanzo cha Akristu akale a mu mzinda wa Aefeso. Baibulo limati atangolandira “mawu a Ambuye,” “ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo, nawatentha pamaso pa onse.” Mabukuwotu anali a ndalama zambiri zedi. Anali a ndalama za siliva zokwanira 50,000. (Machitidwe 19:19, 20) Koma Akristu a ku Aefeso sanazengereze kuwawononga.

Satana Amapezerapo Mwayi pa Zofooka za Anthu

Mngelo wangwiro anakhala Satana Mdyerekezi chifukwa chakuti analola kukhala ndi mtima wodzikweza. Ndiponso anadzutsa mtima wonyada mwa Hava wofuna kukhala ngati Mulungu. Masiku ano, Satana amalamulira anthu ambiri mwa kuwalimbikitsa kukhala ndi mtima wonyada. Mwachitsanzo, ena amaganiza kuti mtundu wawo, fuko lawo kapena dziko lawo n’zoposa za ena. Komatu zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. (Machitidwe 10:34, 35) Baibulo limafotokoza momveka bwino kwambiri kuti: “[Mulungu mwa munthu] mmodzi anapanga mitundu yonse ya anthu.”​—Machitidwe 17:26.

Chitetezo champhamvu chokanizira mtima wonyada umene Satana amalimbikitsa ndicho kudzichepetsa. Baibulo limatilangiza kuti ‘tisadziyese [tokha] koposa kumene tiyenera kudziyesa.’ (Aroma 12:3) Ndiponso limati: “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.” (Yakobo 4:6) Njira yothandiza kwambiri yokanizira zoyesayesa za Satana ndiyo kukhala odzichepetsa pa moyo wathu ndiponso kukhala ndi makhalidwe ena amene Mulungu amawavomereza.

Mdyerekezi amapezeraponso mpata pa mtima wa anthu wolakalaka kuchita zoipa. Yehova Mulungu anakonza zoti anthu azisangalala ndi moyo. Munthu akamakhutiritsa zikhumbo zake mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, munthuyo amapeza chimwemwe chenicheni. Koma Satana amayesa anthu kuti akhutiritse zikhumbo zawo m’njira zoipa. (1 Akorinto 6:9, 10) Ndi bwino kwambiri kuika mtima wathu pa zinthu zomwe zili zoyera ndiponso zabwino. (Afilipi 4:8) Zimenezi zidzakuthandizani kuti muzitha kudziletsa mwamphamvu pa zimene mumaganiza ndiponso zimene mumachita.

Pitirizani Kum’kaniza Mdyerekezi

Kodi mungakwanitse kum’kaniza Mdyerekezi? Inde, mukhoza kukwanitsa. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani inu.” (Yakobo 4:7) Koma ngakhale mum’kanize Satana, sikuti adzangosiyiratu nthawi yomweyo osakuvutitsaninso pamene mukuphunzira choonadi cha Mulungu. Mdyerekezi adzakuyesaninso “nthawi ina.” (Luka 4:13) Koma musachite naye mantha Mdyerekezi. Ngati mupitirizabe kum’kaniza, ndiye kuti adzalephera kukulekanitsani ndi Mulungu woona.

Komabe, kukaniza Mdyerekezi kumafuna kum’dziwa bwino kuti iyeyo ndi ndani ndiponso mmene amasokeretsera anthu, kuphatikizapo kudziwa njira zodzitetezera zimene mungatsatire kuti mupewe machenjera ake. Koma pali njira imodzi yokha yodalirika imene mungadziwire zimenezi yomwe ndi Mawu a Mulungu, Baibulo. Ndiye limbikirani chosankha chanu chofuna kuphunzira Malemba owuziridwa, ndipo gwiritsani ntchito zimene mukuphunzirazo pa moyo wanu. Mboni za Yehova za m’dera lakwanuko zikufuna kukuthandizani mwa kuphunzira nanu kwaulere panthawi iliyonse imene ingakhale yabwino kwa inuyo. Chonde musazengereze kuwauza kuti aziphunzira nanu kapena kulembera amene amafalitsa magazini ino.

Pamene mwayamba kuphunzira Baibulo, muyenera kudziwa kuti Satana akhoza kugwiritsa ntchito chitsutso kapena chizunzo kuti musiye kuphunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Ena mwa achibale anu kapena mabwenzi anu angakwiye nanu chifukwa chakuti mukuphunzira Baibulo. Zimenezi zingachitike chifukwa chakuti iwowo sakudziwa kuti m’Baibulo muli mfundo zabwino kwambiri za choonadi. Ena akhoza kumakusekani. Koma kodi kulolera kuti zimenezi zikulepheretseni, kungasangalatsedi Mulungu? Satana amafuna kukufooketsani n’cholinga chakuti musiye kuphunzira za Mulungu woona. Kodi n’kumuloleranji Satana kupambana? Palibetu chimene iye anakupatsani. (Mateyu 10:34-39) Koma Yehova anakupatsani moyo umene muli nawowo. Ndiyetu limbikirani kum’kaniza Mdyerekezi ndi ‘kukondweretsa mtima wa Yehova.’​—Miyambo 27:11.

[Chithunzi patsamba 6]

Amene anakhala Akristu anatentha mabuku awo a zamizimu

[Chithunzi patsamba 7]

Limbikirani kuphunzira Baibulo