Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilengedwe Chodabwitsachi Chimatamanda Yehova

Chilengedwe Chodabwitsachi Chimatamanda Yehova

 Chilengedwe Chodabwitsachi Chimatamanda Yehova

YEHOVA MULUNGU ndi wokwezeka kwambiri kuposa mmene anthu opanda ungwirofe timaganizira. Zinthu zomwe analenga padziko lino lapansi komanso kumwamba zimam’tamanda ndipo zimatipatsa mantha.​—Salmo 19:1-4.

Yehova akamalankhula, timayenera kumumvera popeza ndi Mlengi ndiponso Mfumu ya chilengedwe chonse. Iye akanati azitilankhula anthu wambafe padziko lapansi lino bwenzi zili zodabwitsa kwambiri. Tiyerekeze kuti anakulankhulani, mwina kudzera mwa mngelo. Kunena zoona, mukanamvetsera mwatcheru. Munthu wolungama Yobu ayenera kuti anamvetsera mwachidwi pamene Mulungu analankhula naye zaka 3,500 zapitazo. Kodi tingaphunzire chiyani pa mawu amene Mulungu analankhula kwa Yobu ponena za dziko lapansi ndi zinthu zakumwamba zimene timaona?

Ndani Anaika Maziko a Dziko Lapansi, Ndiponso Ndani Amalamulira Nyanja?

Mulungu anafunsa Yobu za dziko lapansi ndi nyanja m’kavumvulu. (Yobu 38:1-11) Palibe katswiri wolemba mapulani a zomangamanga aliyense amene anaganiza za kukula kwa dziko lapansi ndiyeno n’kuthandiza kulilenga. Poyerekeza dzikoli ndi nyumba, Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Anaika ndani mwala wake wa pangodya?” Palibe munthu aliyense anachita zimenezo. Ana a Mulungu otchedwa angelo anali kuona ndi kusangalala pamene Yehova amalenga dziko lino lapansi.

Nyanja ndi yakhanda poyerekeza ndi Mulungu, amene mophiphiritsa amaiveka zovala. ‘Inakamula ngati kuti ikutuluka m’mimba.’ Mulungu analembera nyanja malire ngati kuti anaika mipikizo ndi zitseko, ndiponso mafunde amayamba ndi kusiya chifukwa chokokedwa ndi mwezi komanso dzuwa.

Buku lotchedwa The World Book Encyclopedia limati: “Mphepo imapangitsa kuti mafunde ambiri a m’nyanja yaikulu akule kuchokera chabe pa mizere yaing’ono imene timaiona pamwamba pa madzi ija n’kufika mpaka pa mafunde otalika kuposa mamita 30. . . . Mphepo ikasiya kuomba, mafunde amapitiriza kuyendabe pamwamba pa nyanja ndipo angathe kuyenda mtunda wautali kuchokera kumene ayambira. Kenako mafundewo amasalala. Ndipo pomaliza pake, mafundewo amaomba gombe n’kupanga thovu.” Choncho, nyanja imamvera lamulo la Mulungu lakuti: “Ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza.”

Ndani Amati Kukhale Mbandakucha?

Kenako Mulungu anafunsa Yobu za kuwala ndi zinthu zina. (Yobu 38:12-18) Palibe munthu yemwe angalamulire kusintha kwa usana ndi usiku. Kuwala kwa m’mawa mophiphiritsa kumagwira malekezero a dziko lapansi n’kukutumula oipa. Anthu oipa amachita ntchito zawo zoipa ‘m’chisisira.’ (Yobu 24:15, 16) Koma mbandakucha umathamangitsa anthu ambiri ochita zoipa.

Kuunika kuli ngati chidindo m’manja mwa Mulungu, chimene chimapangitsa dziko kuti lionetse kukongola kwake. Kuwala kwa dzuwa  kumapangitsa kuti tione mitundu yosiyanasiyana, choncho dziko limakhala ngati lavekedwa zovala zapamwamba. Yobu sanachite nawo chilichonse cha zimenezi ndiponso sanapitepo pansi pa nyanja n’kukawerengera chuma cha m’madzi. Zoona, ngakhale ofufuza za m’madzi mpaka lero amadziwa zochepa chabe ponena za zinthu za moyo zomwe zili m’nyanja zikuluzikulu.

Ndani Ali ndi Nkhokwe za Chipale Chofewa ndi Matalala?

Palibe munthu aliyense amene anayamba waperekezapo kuunika kapena mdima kumalo kwawo kumene zimakhala, ngakhalenso kulowa m’nkhokwe za chipale chofewa ndi matalala, zimene Mulungu akuzisungira ‘tsiku la nsautso ndi lakulimbana nkhondo.’ (Yobu 38:19-23) Pamene Yehova anagwetsera adani ake miyala ya matalala pa Gibeon, ‘amene anafa ndi miyala yamatalala anali ochuluka kuposa amene ana a Israyeli anawapha ndi lupanga.’ (Yoswa 10:11) Yehova akhoza kugwiritsa ntchito miyala ya matalala yosadziwika kukula kwake, kuwononga anthu oipa otsogoleredwa ndi Gogi, kapena kuti Satana.​—Ezekieli 38:18, 22.

Miyala ya matalala yaikulu ngati dzira la nkhuku inapha anthu okwana 25 ndi kuvulaza ena okwana 200 m’chigawo cha pakati cha Henan ku China, m’mwezi wa July 2002. Ponena za mvula ya matalala imene inachitika mu 1545, Benvenuto Cellini wosema ziboliboli wa ku Italy analemba kuti: “Tinali pa mtunda wa tsiku limodzi kuchokera ku Lyons dziko la France . . . pamene m’mwamba munayamba kugunda ndi phokoso lalikulu. . . . Atatha mabinguwa m’mwamba munachita phokoso lalikulu kwambiri ndiponso lochititsa mantha mpaka ndinaganiza kuti tsiku lachimaliziro lafika; choncho ndinaimitsa hatchi yanga kwakanthawi, kenako matalala ambirimbiri anayamba kugwa popanda ngakhale dontho la madzi. . . . Kenaka matalalawo anayamba kugwa a ngati mandimu akuluakulu. . . . Ndipo mvula ya mkuntho inagwa kwanthawi ndithu kenako n’kusiya. . . . Tinayamba kuonetsana mabala. Koma titayenda mtunda wa pafupifupi makilomita awiri, tinafika pa malo ena amene matalalawo anawononga kwambiri kuposa mmene anawonongera komwe timachokera, ndipo zinali zosaneneka. Masamba a mitengo anangoti mbwee pansi ponse ndipo mitengoyo inali itathyokathyoka; nyama zakufa zinali ngundanguda; abusa ambiri omwe amaweta nyamazo anali atafanso. Tinaona matalala ochuluka aakulu kwambiri omwe sitikanatha kuwafukatira ndi manja awiri.”​—Autobiography (Book II, 50), Harvard Classics, Voliyumu 31, masamba 352-3.

Kodi chidzachitika n’chiyani Yehova akadzatsegulira adani ake nkhokwe zake za chipale chofewa komanso matalala? Adani akewo sadzapulumuka iye akadzagwiritsa ntchito chipale chofewa kapena matalala.

Ndani Analenga Mvula, Mame, Chisanu, ndi Chipale?

Kenako Yehova anafunsa Yobu za mvula, mame, chisanu, ndi chipale. (Yobu 38:24-30) Mulungu ndiye amapanga mvula, ndipo ngakhale “ku chipululu kosakhala munthu,” kumapindula ndi madalitso ake. Mvula, chipale, ndi chisanu si munthu amene anaziyambitsa.

Nyuzipepala ya Nature Bulletin inati: “Mbali yodabwitsa ndi yofunika kwambiri [ya chipale] ndi yakuti madzi amakhala ngati akufufuma akamaundana. . . . Chipale chimene chimapangika ndi kuyandama padziwe m’nyengo yozizira, chimathandiza kuti zomera ndi nyama (nsomba, ndi zina) zimene  zimakhala m’madzi, zikhalebe ndi moyo pansi pa madzipo. Kukanakhala . . . kuti madzi akaundana safufuma ndiponso kuti amalemera, bwenzi chipale chikumalemera kuposa madzi ndipo bwenzi chikumira. Chipale chambiri bwenzi chikumapangika pamwamba pa madzi mpaka dziwe lonse kuundana ngati mwala. . . . Mitsinje, maiwe, nyanja zazing’ono ndiponso zazikulu bwenzi nthawi zonse zili zouma ngati mwala, makamaka mbali ya dziko yomwe kumazizira kwambiri.”

Tikuyamikira kwambiri chifukwa madzi onse m’nyanja ndi maiwe sazizira kwambiri n’kufika pouma ngati mwala. Ndiponso timayamikira chilengedwe cha Yehova, chifukwa mvula ndi mame zimapangitsa zomera za padziko lapansi kuti zikhale ndi moyo.

Ndani Anakhazikitsa Malamulo a Kuthambo?

Kenako Mulungu anafunsa Yobu za kuthambo. (Yobu 38:31-33) Nsangwe nthawi zambiri zimadziwika ndi dzina lakuti Pleiades, limene ndi gulu la nyenyezi zikuluzikulu zokwana zisanu ndi ziwiri ndi nyenyezi zinanso zing’onozing’ono zomwe pamatenga zaka 380 kuti kuwala kwa dzuwa kukafike pa nyenyezi zimenezi. Palibe munthu amene angathe “kumanga gulu la Nsangwe” pamodzi. Palibe munthu amene ‘angamasule zomangira za Akamwiniatsatana,’ lomwe amati ndi gulu la nyenyezi limene limatchedwa kuti Orion. Ngakhale sitikudziwa masiku ano kuti magulu ena a nyenyezi amene Mulungu anatchula ndi ati, chodziwika n’chakuti munthu sangathe kuzilamulira ndi kuzitsogolera. Anthu sangathe kusintha “malemba a kuthambo,” omwe ndi malamulo amene amayendetsa chilengedwe chonse.

Mulungu anakhazikitsa malamulo amene amayendetsa zinthu za kuthambo, zimene zimalamulira nyengo, mafunde, mphepo, ndi kuthandiza kuti moyo weniweniwo utheke padziko lino lapansi. Taganizirani za dzuwa. Ponena za ilo, Encyclopedia Americana (ya 1996) imati: “Dzuwa limapangitsa dziko kuti litenthe ndiponso kuwala. Zinthu ziwiri zimenezi, zimathandiza kuti zomera zizikula, kuti madzi azikwera kumwamba monga nthunzi kuchoka m’nyanya zazikulu ndi m’nyanja zina, zimathandizanso kupanga mphepo, ndiponso kuchita zinthu zina zambiri zofunika kuti zamoyo zikhalepo padziko lapansi.” Buku lomwelo limanenanso kuti: “Kuti munthu azindikire za kukula kwa mphamvu ya dzuwa, ayenera kungoganiza za  mphamvu zimene zimakhala m’mphepo, m’madamu, m’mitsinje ndiponso mphamvu zonse zopezeka mu zinthu za chilengedwe zimene zimayaka monga nkhuni, malasha, ndi mafuta, kuti zimachokera ku mphamvu ya dzuwa, imene imasungidwa ndi pulaneti laling’ono kwambiri lotchedwa [dziko], ndipo pulaneti limeneli linatalikirana ndi dzuwa mtunda wa makilomita okwana 150 miliyoni.”

Ndani Analonga Nzeru M’mitambo?

Yehova anauzanso Yobu kuti aganizire za mitambo. (Yobu 38:34-38) Munthu sangathe kulamulira mtambo kuti uonekere ndi kutulutsa madzi ake. Komabe anthu amadalira kwambiri dongosolo la kayendedwe ka madzi limene Mlengi analikhazikitsa.

Kodi dongosolo la kayendedwe madzilo ndi lotani? Buku lina limati: “Dongosolo la kayendedwe ka madzi lili ndi mbali zinayi: choyamba madzi amasungika, ndipo amachita nthunzi, kenako amagwa monga mvula, ndiyeno amayenda. Madzi amasungika kwa nthawi yochepa m’nyanja zikuluzikulu, nyanja zing’onozing’ono, m’mitsinje, m’mapiri amene amapangika ndi madzi oundana komanso madzi oundana amene amatsetsereka kuchoka m’mapiri. Madzi amakwera kumwamba monga nthunzi kuchokera padziko lapansi, ndiyeno amazizira n’kupanga mitambo, kenako amagwanso monga mvula kapena chipale chofewa, ndipo m’kupita kwa nthawi amayenda kupita ku nyanja kapena amakweranso kupita m’mlengalenga. Pafupifupi madzi onse amene ali pa dziko lapansi amatsata dongosolo limeneli kambirimbiri.”​—Microsoft Encarta Reference Library 2005.

Mitambo yokhathamira ndi mvula ili ngati mitsuko ya kumwamba. Yehova akaitsanula, mvula yambiri imagwa mpaka fumbi limakandika ndi kuundana kupanga zibuma. Mulungu angathe kuvumbitsa mvula kapena kuigwira kuti isavumbe.​—Yakobo 5:17, 18.

Mvula ikamagwa kumachitanso mphenzi, koma munthu sangalamule mphenzi kuti ichite zimene iye akufuna. Mphenzi zimakhala ngati zikupereka lipoti kwa Mulungu mwa kunena kuti: “Tili pano!” Compton’s Encyclopedia imati: “Mphenzi zimasintha kwambiri mpweya m’mlengalenga. Popeza mphenzi imatentha kwambiri ikamadutsa mu mpweya, kutentha kumeneko kumapangitsa mpweya wa naitirojeni ndi okosijeni kuphatikizana pamodzi n’kupanga naitireti ndi zinthu zina. Ndipo zinthu zimenezi zimagwera limodzi ndi mvula padziko lapansi. Mwanjira imeneyi m’mlengalenga mumapitirizabe kubwezeretsa zinthu zofunikira m’nthaka, kuti ithe kumeretsa mbewu.” Anthu sadziwa zinthu zambiri zokhudza mphenzi mpaka pano, koma Mulungu adziwa zonse.

Chilengedwe Chodabwitsachi Chimatamanda Mulungu

Zoona, chilengedwe chodabwitsachi chimalemekeza Mlengi wa zinthu zonse. (Chivumbulutso 4:11) Yobu ayenera kuti anachita chidwi ndi mawu a Yehova onena za dziko lapansi ndi zinthu za kumwamba.

Sikuti ndi zinthu takambirana zokhazi zokhudza chilengedwe chodabwitsachi zimene Mulungu anafunsa Yobu n’kumufotokozera ayi. Ngakhale ndi tero, zimene taonazi zimatilimbikitsa kunena kuti: “Taonani, Mulungu, ndiye wamkulu, ndipo sitim’dziwa.”​—Yobu 36:26.

[Mawu a Chithunzi patsamba 14]

Snowflake: snowcrystals.net

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

Pleiades: NASA, ESA and AURA/​Caltech; fish: U.S. Fish & Wildlife Service, Washington, D.C./​William W. Hartley