Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mdyerekezi Alikodi?

Kodi Mdyerekezi Alikodi?

 Kodi Mdyerekezi Alikodi?

KODI mukamaganiza za Mdyerekezi, mumati ndi ndani? Kodi mumaganiza kuti alikodi, ndipo amayesa anthu kuti achite zinthu zoipa? Kodi mumaganiza kuti Mdyerekezi amangoimira khalidwe lililonse loipa? Kodi Mdyerekezi n’ngofunika kumuopa, kapena kodi tingangofunika kumunyalanyaza ngati kuti ndi nkhambakamwa chabe kapena kuti yangokhala nthano basi? Kodi liwu lakuti “mdyerekezi” limaimira mphamvu inayake yosaoneka ya m’chilengedwe koma yowononga? Kapena kodi mawuwo, amangoimira makhalidwe oipa amene anthu ali nawo, monga mmene amanenera akatswiri amakono a zaumulungu?

N’zosadabwitsa kuti anthu amasiyana maganizo pa nkhani yakuti kodi Mdyerekezi ndi ndani kwenikweni. Tangoganizani mmene zingakhalire zovuta kudziwa zoona zenizeni zokhudza winawake amene amatchuka kuti ndi katswiri pankhani yodzibisa. Ndipo zingakhale zovuta kwambiri makamaka ngati munthuyo amayesetsa kudzibisa ngati kuti wavala chinyawu. Baibulo limafotokoza kuti Mdyerekezi ali wotero. Ponena za iyeyu monga Satana, Baibulo limati: ‘Satana adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.’ (2 Akorinto 11:14) Choncho ngakhale kuti ndi woipa, Mdyerekezi amadzionetsa ngati wabwino n’cholinga chakuti akope anthu ena. Ndipo akangowapangitsa kukhulupirira kuti iyeyo kulibe, m’pamene zimagwirizana bwino kwambiri ndi zofuna zake.

Ndiyeno kodi Mdyerekezi, ndi ndani kwenikweni? Kodi anakhalapo liti, ndipo zinatani kuti akhalepo? Kodi ndi motani mmene amasokeretsera anthu masiku ano? Kodi pali chilichonse chimene tingachite ngati chilipo, kuti asatisokeretse? Baibulo lili ndi mbiri yolondola bwino ya Mdyerekezi kuchokera pamene anayambira, ndiponso limapereka mayankho olondola a mafunso omwe ali pamwambawa.

[Chithunzi patsamba 3]

N’zovuta kwambiri kuzindikira munthu amene sakufuna m’pang’onong’ono pomwe kuti ena amuzindikire makamaka ngati wavala chinyawu