Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amadalitsa Anthu Odzimana

Yehova Amadalitsa Anthu Odzimana

“Thandizo Langa Lidzera kwa Yehova”

Yehova Amadalitsa Anthu Odzimana

MUNTHU wina ku Cameroon akupalasa njinga m’kati mwa nkhalango yowirira mothinana. Akuyenda kwa maola ambiri m’misewu yodzaza madzi komanso kudutsa m’matope. Munthuyu akukumana ndi zinthu zoopsa n’cholinga chofuna kukalimbikitsa anthu ena. Ku Zimbabwe ena amayenda makilomita okwana 15 kudutsa mitsinje yosefukira, atasenza zovala ndi nsapato zawo pamutu kuti zisanyowe, n’cholinga chofuna kukaphunzitsa kagulu kakutali ka anthu. Kwina kwake, mzimayi wina amadzuka folo koloko m’mawa kuti akaphunzitse nesi yemwe amapeza mpata wa ola limodzi lokha m’mawa pa tsiku.

Kodi anthu onsewa akufanana pati? Amenewa ndi atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova, amene amagwira ntchito yophunzitsa choonadi cha Baibulo. Atumiki a nthawi zonse amaphatikizapo apainiya okhazikika, apainiya apadera, amishonale, oyang’anira oyendayenda, komanso zikwizikwi za antchito odzipereka m’nyumba za Beteli padziko lonse. Ndipo kudzimana ndilo khalidwe lawo. *

Kutumikira pa Chifukwa Chabwino

Mboni za Yehova zimamvera mawu olimbikitsa omwe mtumwi Paulo ananena kwa Timoteo akuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Komabe, kodi n’chifukwa chiyani Mboni zambirimbiri zimatumikira monga atumiki a nthawi zonse?

Atumiki a nthawi zonse amenewa akawafunsa chimene chimawapangitsa kudzipereka ndi mtima wonse pantchito ya Yehova imeneyi, m’mayankho awo amaphatikizamo kukonda Mulungu komanso anthu anzawo. (Mateyu 22:37-39) Zimenezi n’zofunika kwambiri, chifukwa kudzipereka kwawo kungakhale kopanda ntchito ngati iwo alibe chikondi.​—1 Akorinto 13:1-3.

Utumiki Wofuna Kudzimana

Akristu onse odzipereka alabadira pempho la Yesu lakuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.” (Mateyu 16:24) Kudzikana tokha kumatanthauza kuvomera mwaufulu kukhala akapolo a Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndiponso kutsogozedwa ndi iwo. Zimenezi n’zimene zachititsa anthu ambiri kugwira ntchito modzimana mu utumiki wa nthawi zonse.

Mboni zambiri zimayesetsa kufutukula utumiki wawo wa kwa Yehova. Taganizani za Júlia wa zaka 56 yemwe ndi mpainiya wokhazikika, wa ku São Paulo m’dziko la Brazil. Iye anati: “Mbale wina wachitchaina anandiimbira telefoni n’kundifunsa ngati ndikufuna kuphunzira Chitchaina. Koma chifukwa cha msinkhu wanga, sindinaganizirepo zophunzira chinenero chatsopano. Patapita masiku, ndinavomera kuchita ntchito yovutayo. Tsopano, ndimagwiritsa ntchito Malemba polalikira mu Chitchaina.”

Ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Peru inapereka lipoti lakuti: “M’zaka zaposachedwapa, apainiya okhazikika ambirimbiri asamukira kumagawo osagawiridwa posonyeza kulimba mtima ndi kudzimana. Apainiyawa amapita kumizinda yakutali komwe kulibe zinthu zamakono, komanso kumene mwayi wantchito uli wochepa. Abale ndi alongo amenewa ndi okonzeka kuchita zomwe angathe kuti apitirizebe utumiki wawo. Komabe chosangalatsa kwambiri n’chakuti, ntchito imene iwo amachita muutumiki, imabweretsa madalitso m’madera ambiri. Oyang’anira oyendayenda akuti, magulu atsopano apangidwa chifukwa cha thandizo la apainiya okhazikika ndi odzimana amenewa.”

Akristu ena aika moyo wawo pangozi ndi cholinga chofuna kuthandiza Akristu anzawo. (Aroma 16:3, 4) M’dera lina la ku Africa kumene kunali nkhondo, woyang’anira dera wa kumeneko anati: “Tisanafike pa malo omaliza ochitira chipikisheni m’malire mwa dera lomwe kumakhala zigawenga ndi dera lomwe lili m’manja mwa boma, ine ndi mkazi wanga tinazingidwa ndi atsogoleri azigawenga anayi ndi alonda awo, omwe ankafuna kutidziwa. Ataona zitupa zathu, anadziwa kuti tikuchokera ku dera lomwe linali m’manja mwa boma, choncho anachita mantha. Anandiimba mlandu waukazitape. Kenako, anaganiza zondiponya m’dzenje. Pamene ndinalongosola kuti ndife ndani, anatilola kuti tizipita.” Mipingo inayamikira kwambiri kuona banja lodzimana limeneli litakwanitsa kukawayendera!

Ngakhale kuti pali zovuta zambiri zimene amakumana nazo, gulu la atumiki a nthawi zonse limeneli likuwonjezeka padziko lonse lapansi. (Yesaya 6:8) Antchito akhama amenewa amasangalala ndi mwayi wawo wapadera umenewu wotumikira Yehova. Ndi mzimu wodzimana ngati umenewu, mamiliyoni ambiri tsopano akutamanda Yehova. Ndipo Yehova akuwadalitsa kwambiri. (Miyambo 10:22) Pokhala ndi chidaliro kuti adzapitirizabe kupeza madalitso ndi chithandizo, anthu ogwira ntchito mwakhama amenewa ali ndi maganizo ngati a wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”​—Salmo 121:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, pa mwezi wa November ndi December.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu”​—SALMO 110:3

[Bokosi patsamba 8]

YEHOVA AMAKONDA ATUMIKI AKE ODZIPEREKA

“Khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.”​—1 Akorinto 15:58.

“Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.”​—Ahebri 6:10.