Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”

“Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”

“Liwu Lawo Linatulukira ku Dziko Lonse Lapansi”

“Phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.”​—MATEYU 28:19.

1, 2. (a) Kodi Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito yotani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anakwanitsa kuchita zambiri?

ATATSALA pang’ono kukwera kumwamba, Yesu anapatsa ophunzira ake ntchito. Anawauza kuti: “Phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:19) Imeneyo inalidi ntchito yaikulu kwambiri.

2 Tangoganizani. Pa Pentekoste wa mu 33 C.E., mzimu woyera unatsanulidwa pa ophunzira pafupifupi 120, ndipo anayamba kukwaniritsa ntchito imeneyo mwa kuuza ena kuti Yesu anali Mesiya, amene anakhala akumuyembekezera kwa nthaŵi yaitali, ndipo akanatha kupeza chipulumutso kudzera mwa iye. (Machitidwe 2:1-36) Kodi kagulu kakang’ono kameneko kakanatha bwanji kufikira “anthu a mitundu yonse”? Zimenezo zinali zosatheka ndi anthu, koma “zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.” (Mateyu 19:26) Akristu oyambirirawo anali kuthandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova, ndipo anali ndi mtima wachangu. (Zekariya 4:6; 2 Timoteo 4:2) Choncho, patangotha zaka makumi ochepa chabe, mtumwi Paulo anatha kunena kuti uthenga wabwino unali kulengezedwa kwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.”​—Akolose 1:23.

3. Kodi n’chiyani chinaphimba “tirigu,” amene ndi Akristu oona, kuti asaoneke?

3 M’kati mwa zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, kulambira koona kunapitiriza kufalikira. Komabe, Yesu ananeneratu kuti idzafika nthaŵi imene Satana adzafesa “namsongole” ndipo “tirigu,” amene ali Akristu oona, adzaphimbidwa kwa zaka mazana ambiri mpaka pa nthaŵi yakututa. Atamwalira atumwi, zimenezo zinachitikadi.​—Mateyu 13:24-39.

Kuwonjezeka Kofulumira Masiku Ano

4, 5. Kuyambira mu 1919, kodi Akristu odzozedwa anayamba kugwira ntchito yanji, ndipo kodi n’chifukwa chiyani ntchito imeneyo inali yovuta kwambiri kuikwanitsa?

4 Mu 1919, inali nthaŵi yoti tirigu, kapena kuti Akristu oona, alekanitsidwe ndi namsongole. Akristu odzozedwa ankadziŵa kuti ntchito yaikulu imene Yesu analamula inali ikadalipobe. Ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti anali kukhala mu “masiku otsiriza” ndipo ankadziŵa za ulosi wa Yesu wakuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (2 Timoteo 3:1; Mateyu 24:14) Inde, ankadziŵa kuti panali ntchito yaikulu yoti ichitike.

5 Komabe, mofanana ndi ophunzira mu 33 C.E., Akristu odzozedwa amenewo anali ndi chintchito chachikulu. Analipo zikwi zochepa zokha ndipo anali m’mayiko ochepa chabe. Kodi akanatha bwanji kulalikira uthenga wabwino “padziko lonse lapansi”? Kumbukirani kuti chiŵerengero cha anthu padziko lapansi chinawonjezeka kuchoka pa anthu mwina 300 miliyoni mu nthaŵi ya a Kaisara kufika pafupifupi anthu 2 biliyoni nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha. Ndipo m’zaka zonse za m’ma 1900 chiŵerengerocho chinali kudzapitirira kuwonjezeka mofulumira.

6. Kodi ntchito yofalitsa uthenga wabwino inali itafika pati pofika zaka za m’ma 1930?

6 Komabe, atumiki odzozedwa a Yehova, mofanana ndi abale awo a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, anayamba kugwira ntchito imene anafunika kuchitayi mokhulupirira Yehova ndi mtima wonse, ndipo mzimu wake unali nawo. Pofika cha m’ma 1935, ofalitsa pafupifupi 56,000 anali atalengeza choonadi cha m’Baibulo m’mayiko okwana 115. Ntchito yambiri inali itachitika, komabe panali ntchito yaikulu kwambiri yofunikabe kuchita.

7. (a) Kodi Akristu odzozedwa anakhala ndi ntchito yatsopano yotani? (b) Kodi ntchito yotuta yafika pati tsopano mothandizidwa ndi a “nkhosa zina”?

7 Kenaka, kumvetsetsa bwino amene anali a “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9 kunawonjezera ntchito ina komanso kunasonyeza kuti Akristu akhama amenewo adzakhala ndi owathandiza. A “nkhosa zina” osadziŵika chiŵerengero chawo, okhulupirira okhala ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi, anayenera kusonkhanitsidwa ‘kuchokera mu mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ (Yohane 10:16) Ameneŵa anali ‘kudzatumikira Yehova usana ndi usiku.’ (Chivumbulutso 7:15) Zimenezi zikutanthauza kuti anali kudzathandiza pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. (Yesaya 61:5) Chifukwa cha zimenezi, Akristu odzozedwa anasangalala kwambiri kuona chiŵerengero cha ofalitsa chikukwera kufika zikwi makumi ambiri, kenaka kufika mamiliyoni. M’chaka cha 2003, chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa okwana 6,429,351 anachita nawo ntchito yolalikira, ndipo ambiri a iwo ndi a khamu lalikulu. * Akristu odzozedwa amayamikira thandizo limeneli, ndipo a nkhosa zina amayamikira kukhala ndi mwayi wothandiza abale awo odzozedwa.​—Mateyu 25:34-40.

8. Kodi Mboni za Yehova zinachita chiyani pamene zinali kuzunzidwa kwambiri panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse?

8 Pamene gulu la tirigu linadzadziŵikanso, Satana analimbana nalo koopsa. (Chivumbulutso 12:17) Kodi iye anachita chiyani pamene khamu lalikulu linayamba kuoneka? Anachita chiwawa chachikulu! Kodi tingakayikire zoti iye ndi amene anachititsa kuti kulambira koona padziko lonse kuukiridwe panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse? Ku mbali zonse ziŵiri zimene zinkalimbana pa nkhondoyo, Akristu anavutika kwambiri. Abale ndi alongo ambiri okondedwa anavutika ndi mayeso aakulu, ndipo ena mwa iwo anafera chikhulupiriro chawo. Komabe, iwo anasonyeza kuti anali ndi malingaliro ofanana ndi a wamasalmo amene analemba kuti: “Mwa Mulungu ndidzalemekeza mawu ake; ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji.” (Salmo 56:4; Mateyu 10:28) Akristu odzozedwa ndi nkhosa zina, atalimbikitsidwa ndi mzimu wa Yehova, anakhulupirika molimba pamodzi. (2 Akorinto 4:7) Zotsatirapo zake zinali zoti “mawu a Mulungu anakula.” (Machitidwe 6:7) Mu 1939, pamene nkhondo inayamba, Akristu okhulupirika okwana 72,475 anachitira lipoti kuti anali kuchita nawo ntchito yolalikira. Komabe, lipoti la mu 1945, chaka chimene nkhondo inatha, linasonyeza kuti Mboni zachangu zokwana 156,299, osaŵerengera ena amene sanachitire lipoti, zinali kufalitsa uthenga wabwino. Satana anagonjadi!

9. Kodi ndi masukulu atsopano ati amene anakhazikitsidwa panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse?

9 Mwachionekere, chipwirikiti cha nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse sichinachititse atumiki a Yehova kukayika zoti ntchito yolalikira idzakwaniritsidwa. M’malomwake, mu 1943, pamene nkhondoyo inali pakaindeinde, masukulu aŵiri atsopano anakhazikitsidwa. Imodzi mwa masukulu ameneŵa, imene tsopano imatchedwa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, inali yoti izichitika m’mipingo yonse kuti iphunzitse Mboni iliyonse kulalikira ndi kupanga ophunzira. Inayo, Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, inali yophunzitsa amishonale kuti akapititse patsogolo ntchito yolalikira m’mayiko ena. Inde, pamene nkhondo imatha, Akristu oona anali okonzeka kuchita ntchito yowonjezereka.

10. Kodi changu cha anthu a Yehova chinaoneka bwanji m’chaka cha 2003?

10 Ndipo masukulu ameneŵa athandiza kwambiri! Chifukwa chophunzitsidwa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, onse, achinyamata ndi achikulire, makolo ndi ana, ngakhale anthu odwala chifukwa cha ukalamba, akwaniritsa ndipo akupitiriza kukwaniritsa nawo ntchito yaikulu ya Yesu. (Salmo 148:12, 13; Yoweli 2:28, 29) M’chaka cha 2003, pa avareji mwezi uliwonse anthu 825,185 anasonyeza changu chawo mwa kuchita nawo utumiki waupainiya kwa nthaŵi yochepa kapena nthaŵi zonse. M’chaka chimenechi, Mboni za Yehova zinathera maola 1,234,796,477 zikuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu. Ndithudi, Yehova ndi wosangalala ndi changu cha anthu ake!

M’mayiko Akunja

11, 12. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza ntchito yabwino ya amishonale?

11 M’zaka zapitazi, anthu omaliza maphunziro a Gileadi, ndipo chaposachedwapa anthu omaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki, agwira ntchito yabwino kwambiri. Mwachitsanzo, ku Brazil kunali ofalitsa osakwana 400 pamene amishonale oyamba anafikako mu 1945. Amishonale ameneŵa, ndiponso amishonale ena amene anafika pambuyo pawo, limodzi ndi abale achangu a ku Brazil komweko agwira ntchito mwakhama, ndipo Yehova wadalitsa kwambiri khama lawolo. N’zosangalatsa kwambiri kwa aliyense amene akukumbukira masiku oyambirira amenewo kuona kuti dziko la Brazil linachitira lipoti chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 607,362 mu 2003!

12 Taganizirani za dziko la Japan. Nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse isanayambe, ku Japan kunali ofalitsa pafupifupi 100. Panthaŵi ya nkhondoyo, chizunzo choopsa chinachepetsa chiŵerengero chawo, ndipo pamene nkhondoyo imatha, kunali kutatsala Mboni zochepa chabe zimene zinali ndi moyo mwauzimu ndiponso moyo weniweni. (Miyambo 14:32) Anthu ochepa chabe okhulupirika amenewo analidi osangalala mu 1949 pamene analandira amishonale 13 oyamba amene anaphunzitsidwa ku sukulu ya Gileadi, ndipo amishonalewo sanachedwe kuyamba kukonda abale awo achijapani ofunitsitsa kumvetsera ndi ochereza alendowo. Zaka 50 pambuyo pake, m’chaka cha 2003, dziko la Japan linachitira lipoti chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa okwana 217,508. Yehova wadalitsadi kwambiri anthu ake m’dziko limenelo. Pali malipoti ofanana ndi amenewo ochokera m’mayiko ena ambiri. Anthu amene akwanitsa kulalikira m’magawo akunja athandizadi kwambiri pofalitsa uthenga wabwino, ndipo chifukwa cha zimenezi, m’chaka cha 2003, uthenga wabwinowu unamveka m’mayiko, zilumba, ndi magawo okwana 235 padziko lonse lapansi. Zoonadi, khamu lalikulu likuchokera ‘m’mitundu yonse.’

‘Ochokera mwa Mafuko, Anthu, ndi Manenedwe Onse’

13, 14. Kodi Yehova anasonyeza bwanji ubwino wolalikira uthenga wabwino ‘m’manenedwe onse’?

13 Chozizwitsa choyamba chimene chinachitika ophunzira atadzozedwa ndi mzimu woyera pa Pentekoste wa mu 33 C.E. chinali choti, ophunzirawo analankhula m’malilime kwa khamu limene linasonkhana pamenepo. Anthu onse amene anawamvawo mwina ankalankhula chinenero chimene anthu ambiri ankalankhula padziko lonse, mwina Chigiriki. Popeza anali “amuna opembedza,” mwachidziŵikire ankathanso kumva nkhani za m’Chihebri zimene zimakambidwa pakachisi. Koma anamvetseradi mwachidwi pamene anamva uthenga wabwino m’chinenero chawo chobadwira.​—Machitidwe 2:5, 7-12.

14 Masiku anonso, zinenero zambiri zikugwiritsidwa ntchito polalikira. Zinanenedweratu kuti khamu lalikulu lidzachokera osati chabe m’mitundu yonse, komanso mu “mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Mogwirizana ndi zimenezi, Yehova ananeneratu kudzera mwa Zekariya kuti: ‘Amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’ (Zekariya 8:23) Ngakhale kuti Mboni za Yehova pakadali pano zilibe mphatso yolankhula m’malilime, zimadziŵa ubwino wophunzitsa anthu m’chinenero chawo.

15, 16. Kodi amishonale ndi ena adzipereka bwanji kugwira ntchito yovuta yolalikira m’zinenero za kumayiko ena?

15 N’zoona kuti masiku ano kuli zinenero zingapo zimene zimagwiritsidwa ntchito m’mayiko ambiri, monga Chingelezi, Chifalansa, ndi Chispanya. Komabe, anthu amene achoka kwawo n’kupita ku mayiko ena amayesera kuphunzira zinenero zakumeneko kuti uthenga wabwino ufikire anthu “ofuna moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48, NW) Zimenezo zingakhale zovuta. Pamene abale a kudziko la ku South Pacific la Tuvalu anafunikira mabuku m’chinenero chawo, m’modzi mwa amishonale kumeneko anayambapo kugwira ntchito imeneyo. Chifukwa chakuti kunalibe buku lotanthauzira mawu, anayamba kulemba ndandanda ya mawu a Chituvalu. Patapita nthaŵi, buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi * linafalitsidwa m’chinenero cha Chituvalu. Pamene amishonale anafika ku Curaçao, kunalibe mabuku ofotokoza Baibulo, ndipo kunalibe buku lotanthauzira mawu m’chinenero chakumeneko, Chipapiamento. Panalinso kusiyana maganizo kwakukulu pa mmene chinenerocho chiyenera kulembedwera. Komabe, patatha zaka ziŵiri chifikireni amishonale oyambawo, thirakiti loyamba lachikristu lofotokoza Baibulo linafalitsidwa m’chinenero chimenecho. Masiku ano, Chipapiamento ndi chimodzi mwa zinenero 133 zimene Nsanja ya Olonda imafalitsidwamo panthaŵi imodzimodzi ndi Chingelezi.

16 Ku Namibia, amishonale oyambirira sanathe kupeza Mboni yobadwira ku Namibia komweko kuti iwathandize kumasulira mawu. Kuwonjezera apo, chinenero chimodzi chakumeneko chotchedwa Chinama, chinalibe mawu amene timawagwiritsa ntchito kwambiri m’mabuku athu, monga “ungwiro.” M’mishonale wina anati: “Kuti ndimasulire mawu, nthaŵi zambiri ndinagwiritsa ntchito aphunzitsi a sukulu amene anali kuphunzira Baibulo. Chifukwa chakuti choonadi samachidziŵa bwino, ndinayenera kukhala nawo pansi n’kuonetsetsa kuti chiganizo chilichonse chinali cholondola.” Ngakhale zinali choncho, thirakiti lakuti Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere pamapeto pake analimasulira m’zinenero zinayi za ku Namibia. Masiku ano, Nsanja ya Olonda imafalitsidwa nthaŵi zonse m’chinenero cha Chikwanyama ndi Chindonga.

17, 18. Kodi ndi ntchito yovuta iti imene ikuchitika ku Mexico ndi ku mayiko ena?

17 Ku Mexico, chinenero chimene amachigwiritsa ntchito kwambiri ndi Chispanya. Komabe, Aspanya asanabwere, kunali zinenero zambiri zimene ankalankhula kumeneko, ndipo zina mwa izo amazilankhulabe. Choncho, mabuku a Mboni za Yehova tsopano amatulutsidwa m’zinenero zisanu ndi ziŵiri za ku Mexico, ndiponso m’chinenero chamanja cha ku Mexico. Chofalitsa choyamba kumatuluka nthaŵi ndi nthaŵi m’chinenero cha Amwenye Achimereka chinali Utumiki wa Ufumu wa m’chinenero cha Chimaya. Inde, anthu zikwi zingapo a Chimaya, Chiaziteki, ndi mitundu ina ndi ena mwa ofalitsa Ufumu okwana 572,530 amene ali ku Mexico.

18 Posachedwapa, anthu mamiliyoni ambiri athaŵira ku mayiko ena monga othaŵa kwawo, kapena asamukira kumeneko pankhani zachuma. Chifukwa cha zimenezi, mayiko ambiri tsopano ali ndi magawo aakulu ndithu a anthu olankhula chinenero chakunja. Mboni za Yehova zadzipereka kugwira ntchito yovuta yolalikira anthu a zinenero zakunja ameneŵa. Mwachitsanzo, ku Italy kuli mipingo ndi magulu m’zinenero 22 kuphatikiza pa Chitaliyana. Pofuna kuthandiza abale kuti azilalikira kwa anthu amene amalankhula zinenero zina, posachedwapa anakonza makalasi ophunzitsa zinenero 16, kuphatikizapo chinenero chamanja cha ku Italy. M’mayiko ena ambiri, Mboni za Yehova zayesetsa chimodzimodzi pofuna kulalikira anthu ambiri amene asamukira kumeneko kuchokera ku mayiko ena. Indedi, ndi chithandizo cha Yehova, khamu lalikulu likuchokeradi m’zinenero zambirimbiri.

“Ku Dziko Lonse Lapansi”

19, 20. Kodi ndi mawu ati a Paulo amene akukwaniritsidwa mochititsa chidwi masiku ano? Fotokozani.

19 M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, mtumwi Paulo analemba kuti: “Sanamva iwo kodi! Indetu, liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi maneno awo ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.” (Aroma 10:18) Zimenezo zinachitikadi m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino ndipo tangoganizirani mmene zawonjezekera masiku ano. Anthu mamiliyoni ambiri, mwina kuposa panthaŵi ina iliyonse m’mbiri, akunena kuti: “Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kum’lemekeza kwake kudzakhala m’kamwa mwanga kosalekeza.”​—Salmo 34:1.

20 Kuwonjezera apo, ntchitoyi sikubwerera m’mbuyo. Chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chikukwera. Nthaŵi imene timathera mu ntchito yolalikira ikuwonjezeka. Tikuchita maulendo obwereza mamiliyoni ambiri ndi maphunziro a Baibulo mazana ambiri. Ndipo pali anthu ambiri amene akuchitabe chidwi. Chaka chatha, tinali ndi chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha anthu amene anabwera kudzachita nawo Chikumbutso cha imfa ya Yesu okwana 16,097,622. Mwachionekere, pakadali ntchito yambiri yoti ichitike. Tiyeni tipitirize kutsanzira kukhulupirika kolimba kwa abale athu amene apirira chizunzo choopsa. Ndipo tiyeni tisonyeze changu chofanana ndi cha abale athu onse amene kuyambira 1919 adzipereka kotheratu kutumikira Yehova. Tiyeni tonse tisonyeze kuti tikugwirizana ndi nyimbo ya wamasalmo yoti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya.”​—Salmo 150:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani lipoti lapachaka pa masamba 18 mpaka 21 m’magazini ino.

^ ndime 15 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi abale anayamba kugwira ntchito yotani mu 1919, ndipo n’chifukwa chiyani inali yovuta?

• Kodi ndani amene anasonkhanitsidwa kudzathandiza pa ntchito yolalikira?

• Kodi amishonale ndi ena amene akutumikira m’mayiko akunja agwira ntchito yotani?

• Kodi pali umboni wotani umene mungatchule wosonyeza kuti Yehova akudalitsa ntchito ya anthu ake masiku ano?

[Mafunso]

[Tchati patsamba 18-21]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2003 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Zithunzi pamasamba 14, 15]

Chipwirikiti cha nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse sichinachititse Akristu kukayika zoti uthenga wabwino udzalalikidwa

[Mawu a Chithunzi]

Kuphulika kwa bomba: Chithunzi cha U.S. Navy; zina: Chithunzi cha U.S. Coast Guard

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Khamu lalikulu linali kudzachokera ku mafuko ndi manenedwe onse