Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhondo Idzatha

Nkhondo Idzatha

 Nkhondo Idzatha

‘Tili ndi zaka 12 zokha. Sitingasinthe ndale kapena kuletsa nkhondoyi, koma tikufuna kukhala ndi moyo. Tikuyembekezera mtendere. Kodi udzabwera tili ndi moyo?’ Anatero ana a sitandade faifi.

‘Timafuna kupita kusukulu ndiponso kukaona anzathu ndi abale athu popanda kuchita mantha kuti atigwira. Mwina boma limva madandaulo athu. Tikufuna moyo wabwinopo. Tikufuna mtendere.’ Anatero Alhaji, wazaka 14.

MAWU okhudza mtima ameneŵa akufotokoza chiyembekezo chochokera pansi pamtima cha achinyamata amene avutika kwa zaka zambiri chifukwa cha nkhondo zapachiŵeniŵeni. Zimene akufuna n’kukhala ndi moyo wabwino basi. Koma kukwaniritsa zinthu zimene munthu akulakalaka si chinthu chapafupi. Kodi tingayembekezere kuona dziko lopanda nkhondo?

M’zaka zaposachedwapa, mayiko padziko lonse akhala akuyesayesa kuthetsa nkhondo zina zapachiŵeniŵeni pokakamiza mbali zolimbanazo kuti zisayine mapangano a mtendere. Mayiko ena atumiza asilikali okhazikitsa mtendere kuti akaonetsetse kuti mapanganowo akutsatiridwa. Koma ndi mayiko ochepa amene ali ndi ndalama ndiponso ndi ofunitsitsa kuyang’anira mayiko akutali kumene chidani ndi kukayikirana zimachititsa kuti pangano lililonse limene magulu osagwirizana angapange likhale losalimba. Nthaŵi zambiri, nkhondo imayambanso pakangopita milungu kapena miyezi yochepa atasayina mapangano oti asiye nkhondo. Monga momwe bungwe la Stockholm International Peace Research Institute linanenera, “n’kovuta kukhazikitsa mtendere pamene magulu omenyanawo akufuna ndiponso akhoza kupitiriza kumenyana.”

Komanso, ziwawa zovuta kuthetsa zimene zikuvutitsa mbali zambiri zadziko lapansi zimenezi zimakumbutsa Akristu ulosi wina wa m’Baibulo. Buku la Chivumbulutso limanena za nthaŵi yofunika zedi m’mbiri ya anthu pamene wokwera kavalo wophiphiritsira ‘akudzachotsa mtendere pa dziko.’ (Chivumbulutso 6:4) Nkhondo yosatherapo imene inaloseredwayi ndi mbali imodzi ya chizindikiro chopangidwa ndi zochitika zosiyanasiyana zimene zikusonyeza kuti tsopano tikukhala mu nthaŵi imene yafotokozedwa m’Baibulo monga “masiku otsiriza.” * (2 Timoteo 3:1) Komabe, Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti masiku otsiriza ameneŵa akutipititsa ku mtendere.

Pa Salmo 46:9 Baibulo limafotokoza kuti mtendere weniweni ungabwere ngati nkhondo itatha, osati m’dera limodzi lokha la dzikoli, koma padziko lonse lapansi. Kuwonjezera apo, salmo lomweli limatchula mwachindunji za kuwonongedwa kwa zida zankhondo za m’nthaŵi ya Baibulo monga mauta ndi mikondo. Zida zankhondo zimene zikufala masiku ano ziyeneranso kuwonongedwa kuti anthu adzakhale pamtendere.

Komabe, mfundo ndi yakuti chidani ndi umbombo n’zimene zimachititsa kuti nkhondo zizipitirira, osati zipolopolo ndi mfuti. Chifukwa chachikulu chimene chimayambitsa nkhondo ndicho umbombo, ndipo chidani kaŵirikaŵiri  chimachititsa chiwawa. Kuti malingaliro owononga ameneŵa achoke, anthu afunika kusintha mmene amaganizira. Ayenera kuphunzitsidwa kukhala mwamtendere. N’chifukwa chake mneneri wakale Yesaya ananena molondola kuti nkhondo idzatha nthaŵi yokhayo pamene anthu “sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:4.

Komabe, padakali pano tikukhala m’dziko limene limaphunzitsa akuluakulu ndi ana phindu la nkhondo, osati kufunika kwa mtendere. N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale ana akuphunzitsidwa kupha.

Anaphunzira Kupha

Ali ndi zaka 14, Alhaji anakhala msilikali amene anapuma pantchito. Anali ndi zaka khumi zokha pamene magulu ankhondo oukira boma anamugwira ndi kum’phunzitsa kumenya nkhondo ndi mfuti ya AK-47. Atakakamizidwa kukhala msilikali, ankaba zakudya moopseza ndi mfuti ndiponso kutentha nyumba. Ankaphanso ndi kudula anthu ziwalo. Masiku ano, Alhaji amavutika kuti aiŵale zinthu zimene zinachitika pankhondoyo ndiponso kuti akhale munthu wamba osati msilikali. Abraham, amene anakhala msilikali ali mwana, nayenso anaphunzira kupha ndipo sankafuna kubweza mfuti yake. Iye anati: “Ngati atandiuza kuti ndizipita popanda mfuti yanga, sindikudziŵa zimene ndikachite, ndiponso mmene ndikapezere chakudya.”

Ana oposa 300,000, anyamata ndi atsikana amene ndi asilikali, akumenyabe nkhondo ndipo akufa pankhondo zapachiŵeniŵeni zosatha zimene zikuvutitsabe dziko lathu lapansili. Mtsogoleri wina wa gulu loukira boma anafotokoza kuti: “Amamvera zimene auzidwa; saganizira zobwerera kwa mkazi wawo kapena banja lawo; ndipo sachita mantha.” Komatu, ana ameneŵa amafuna ndipo amayenera kukhala ndi moyo wabwino.

M’mayiko otukuka, nkhani yoopsa ya ana amene ndi asilikali ingakhale yovuta kuimvetsa. Ngakhale zili choncho, ana ambiri m’mayiko otukuka akuphunzira kumenya nkhondo m’nyumba zawo zomwe. Motani?

Tiyeni tione chitsanzo cha José, wakum’mwera cha kum’maŵa kwa dziko la Spain. Anali ndi zaka zosakwana 20 ndipo ankakonda kuchita maseŵera omenyana monga judo ndi karate. Iye ankakonda kwambiri lupanga lalitali lachijapani limene bambo ake anam’gulira ngati mphatso pa Khirisimasi. Ndipo ankakonda maseŵera apavidiyo, makamaka achiwawa. Pa April 1, 2000, anatsanziradi chiwawa chimene munthu amene ankamukonda pa maseŵera a vidiyo ankachita. Pachiwawa choopsa chimene anachita, anapha bambo ake, mayi ake, ndi mchemwali wake ndi lupanga limene bambo ake anam’patsa lija. Pofotokoza kwa apolisi, iye anati: “Ndinkafuna kukhala ndekha m’dzikoli; sindinkafuna kuti makolo anga azindifunafuna.”

Polankhulapo za mmene zosangulutsa zachiwawa zikukhudzira anthu, mlembi ndiponso mkulu wa asilikali, Dave Grossman, anati: “Anthu tsopano tafika pouma mitima moti kupwetekana ndi kuvutitsana zili ngati maseŵera osangalatsa: anthu tikusangalala tikamadziyerekezera ngati kuti tikuchita nawo nkhanzazo mmalo moipidwa nazo. Tikuphunzira kupha, ndiponso tikuphunzira kukonda kuphako.”

Alhaji ndi José anaphunzira kupha. Palibe aliyense wa aŵiriwa amene anafuna kukhala wakupha, koma kuphunzitsidwa mwanjira zosiyana kunasokoneza kaganizidwe kawo. Maphunziro oterowo, kaya akhale kwa ana kapena akuluakulu, amachititsa chiwawa ndi nkhondo.

Kuphunzira Mtendere M’malo mwa Nkhondo

Mtendere wokhalitsa sungakhazikitsidwe pamene anthu akuphunzira kupha. Zaka mazana ambiri zapitazo, mneneri Yesaya analemba kuti: ‘Ukanamvera malamulo [a Mulungu] mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje.’ (Yesaya 48:17, 18) Anthu akadziŵa Mawu a Mulungu molondola ndiponso akaphunzira kukonda malamulo a Mulungu, amanyansidwa ndi chiwawa ndi nkhondo. Ngakhale panopo, makolo angaonetsetse kuti maseŵera amene ana awo amaseŵera sakulimbikitsa chiwawa. Anthu akuluakulu nawonso angaphunzire kuthetsa chidani ndi umbombo. Nthaŵi ndi nthaŵi Mboni za Yehova zapeza kuti Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu zosintha khalidwe la anthu.​—Ahebri 4:12.

Taganizirani chitsanzo cha Hortêncio. Anali wachinyamata pamene anakakamizidwa kuti akakhale msilikali mosemphana ndi zimene ankafuna. Iye anafotokoza kuti maphunziro a  usilikali anakonzedwa kuti “atilimbikitse mtima wokonda kupha anthu ena ndiponso kuti tisakhale ndi mantha aliwonse pakupha.” Anamenya nawo nkhondo ina yapachiŵeniŵeni mu Africa muno imene inatenga nthaŵi yaitali. Iye anavomereza kuti: “Nkhondoyo inasintha khalidwe langa. Ngakhale masiku ano ndimakumbukirabe chilichonse chimene ndinachita. Ndimamva chisoni chifukwa cha zimene ndinakakamizidwa kuchita.”

Msilikali mnzake atam’fotokozera Hortêncio za Baibulo, zinamugwira mtima. Lonjezo la Mulungu pa Salmo 46:9 lakuti adzathetsa mitundu yonse yankhondo linam’fika pamtima. Pamene amaphunzira kwambiri Baibulo, sankafunanso kumenya nkhondo. Pasanapite nthaŵi yaitali, iyeyo ndi anzake ena aŵiri anawachotsa usilikali, ndipo anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova Mulungu. Hortêncio anafotokoza kuti: “Choonadi cha m’Baibulo chinandithandiza kukonda adani anga. Ndinazindikira kuti pamene ndimamenya nawo nkhondo, kwenikweni ndimachimwira Yehova, chifukwa Mulungu amati sitiyenera kupha anthu anzathu. Kuti ndisonyeze chikondi chimenechi, ndinafunika kusintha kaganizidwe kanga ndiponso kusaona anthu ngati adani anga.”

Zinthu zimene zinachitikadi zimenezi zikusonyeza kuti kuphunzira Baibulo kumalimbikitsa mtendere. Zimenezi n’zosadabwitsa. Mneneri Yesaya anafotokoza kuti pali kugwirizana kwenikweni pakati pa maphunziro a Mulungu ndi mtendere. Analosera kuti: ‘Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.’ (Yesaya 54:13) Mneneri yemweyu anaoneratu nthaŵi pamene anthu a mitundu yonse anali kudzakhamukira ku kulambira koyera kwa Yehova Mulungu kuti akaphunzire njira zake. Kodi padzakhala zotsatira zotani? ‘Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.’​—Yesaya 2:2-4.

Mogwirizana ndi ulosi umenewu, Mboni za Yehova zikugwira ntchito yophunzitsa padziko lonse imene yathandiza kale anthu mamiliyoni ambiri kuthetsa chidani chimene chimayambitsa nkhondo.

Umboni Wotsimikizira kuti Padziko Lonse Padzakhala Mtendere

Kupatula pa kuphunzitsa anthu, Mulungu wakhazikitsa boma, kapena kuti “ufumu,” umene ungathe kubweretsa mtendere padziko lonse lapansi. Mochititsa chidwi, Baibulo limafotokoza Wolamulira wosankhidwa ndi Mulungu, Yesu Kristu, monga “Kalonga wa Mtendere.” Limatitsimikiziranso kuti “za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”​—Yesaya 9:6, 7.

Kodi tili ndi umboni wotani wotsimikizira kuti ulamuliro wa Kristu udzakwanitsa bwinobwino kuthetsa nkhondo ya mtundu wina uliwonse? Mneneri Yesaya anawonjezera kuti: “Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” (Yesaya 9:7) Mulungu akufuna kubweretsa mtendere wosatha, ndiponso ali ndi njira zosungitsira mtendere umenewu. Yesu amakhulupirira kwambiri lonjezo limeneli. N’chifukwa chake anaphunzitsa otsatira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu kuti udze ndiponso chifuno cha Mulungu kuti chichitike padziko lapansi. (Mateyu 6:9, 10) Pemphero lochokera pansi pa mtima limeneli likadzayankhidwa, nkhondo sizidzawononganso dziko lapansi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mupende umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza, onani mutu 11 wa buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 7]

Kuphunzira Baibulo kumalimbikitsa mtendere weniweni