Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhulupirira Ena N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akhale Wosangalala

Kukhulupirira Ena N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akhale Wosangalala

 Kukhulupirira Ena N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akhale Wosangalala

MATENDA a m’mimba odzera m’chakudya amasoŵetsa mtendere. Munthu amene amadwala matenda ameneŵa mobwerezabwereza amafunika kusamala kwambiri zimene amadya. Koma kungosiyiratu kudya pofuna kupeŵa matendaŵa sikungakhale kwanzeru. Kuchita zimenezo kungayambitse mavuto ambiri kuposa amene angathetsedwe. Popanda chakudya palibe amene angathe kukhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali.

N’chimodzimodzinso ndi kukhulupirira anthu ena. Kukhumudwitsidwa ndi munthu amene tinali kumukhulupirira n’kopweteka. Kukhumudwitsidwa mobwerezabwereza ndi anthu amene tinali kuwakhulupirira kungatichititse kuganizira mosamala za anthu amene timasankha kucheza nawo. Komabe, kusiyiratu kucheza ndi anthu pofuna kupeŵa kukhumudwitsidwa si njira yothetsera vutolo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kusakhulupirira anthu ena kungatichititse kukhala osasangalala. Kuti tikhale osangalala pa moyo wathu, timafunikira mabwenzi oti tiziwakhulupirira ndipo nawonso azitikhulupirira.

Buku lina la Jugend 2002 linati: “Kukhulupirira ena n’chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri kuti tikhale bwino ndi anthu ena.” Nyuzipepala ya Neue Zürcher Zeitung inati: “Aliyense amalakalaka kukhala ndi munthu woti azimukhulupirira. Kukhulupirira ena kumathandiza kuti moyo ukhale wabwino kwambiri” moti “n’kofunika kwambiri kuti munthu apitirize kukhala ndi moyo.” Nyuzipepalayo inapitiriza kuti, kunena zoona, popanda kukhulupirira ena, “munthu sangathe kulimbana ndi mavuto pa moyo wake.”

Popeza timafunika kukhulupirira munthu wina, kodi ndani amene tingamukhulupirire popanda vuto lakuti angatikhumudwitse?

Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse

Baibulo limatiuza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” (Miyambo 3:5) Inde, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa mobwerezabwereza kukhulupirira Mlengi wathu, Yehova Mulungu.

N’chifukwa chiyani tingakhulupirire Mulungu? Chifukwa choyamba n’chakuti Yehova Mulungu ndi woyera. Mneneri Yesaya analemba kuti: “Woyera, Woyera, Woyera, Yehova.” (Yesaya 6:3) Kodi mfundo yakuti Yehova ndi woyera ikukuchititsani kusakopeka naye? Kunena zoona, mfundo imeneyi iyenera kukuchititsani  kukopeka naye chifukwa kuyera kwa Yehova kumatanthauza kuti iye sachita zoipa zilizonse, ndipo ndi wodalirika kwambiri. Sangachite chinyengo kapena kulakwitsa ndipo sangatigwiritse fuwa lamoto tikamukhulupirira.

Ndiponso, tingakhulupirire Mulungu chifukwa chakuti angathe kuthandiza anthu amene amamutumikira ndipo iye amafuna kuchita zimenezo. Mwachitsanzo, mphamvu zake zopanda malire zimamuthandiza kuchita zinthu. Chilungamo ndi nzeru zake zangwiro zimatsogolera mmene amachitira zinthu. Ndipo chikondi chake chosayerekezeka chimamulimbikitsa kuti achite zinthuzo. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Chikondi cha Mulungu chimakhudza chilichonse chimene amachita. Kuyera kwa Yehova ndi makhalidwe ake ena abwino kwambiri amamuchititsa kukhala Atate wabwino kwambiri, amene tingamukhulupirire ndi mtima wonse. Palibe chilichonse, ndiponso palibe wina aliyense amene angakhale wokhulupirika kuposa Yehova.

Khulupirirani Yehova Kuti Mukhale Wosangalala

Chifukwa china chomveka chokhulupirira Yehova n’chakuti amatidziŵa bwino kwambiri kuposa mmene wina aliyense amatidziŵira. Amadziŵa kuti munthu aliyense amafuna kukhala ndi ubwenzi wotetezeka, wokhalitsa, ndiponso wokhulupirika ndi Mlengi. Anthu amene ali ndi ubwenzi woterowo amaona kuti ndi otetezeka kwambiri. Mfumu Davide inati: “Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika.” (Salmo 40:4) Anthu ambirimbiri masiku ano amavomereza ndi mtima wonse maganizo a Davide ameneŵa.

Taonani zitsanzo izi. Doris anakhalapo ku Dominican Republic, Germany, Greece, ndi ku United States. Iye anati: “Ndimasangalala kwambiri kukhulupirira Yehova. Amadziŵa mmene angandisamalire pondipatsa zinthu zimene ndimafunikira, kundisamala mwauzimu, ndiponso kundikonda. Ndi bwenzi labwino kwambiri kuposa lina lililonse limene munthu angakhale nalo.” Wolfgang, mlangizi wa zamalamulo, anafotokoza kuti: “N’zosangalatsa kwambiri kukhulupirira winawake amene amakufunira zabwino zokhazokha, amene angathe kuchita, ndiponso amene adzachite zinthu zabwino kwambiri kwa munthuwe.” Ham, amene anabadwira ku Asia koma tsopano akukhala ku Ulaya, anati: “Ndimakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu pa china chilichonse, ndipo salakwitsa, motero ndimasangalala kumudalira.”

Komabe, aliyense amafunika kukhulupiriranso anthu ena osati Mlengi wathu yekha. Motero, Yehova, monga bwenzi lanzeru ndiponso lodziŵa zambiri, amatipatsa malangizo otithandiza kuona kuti ndi anthu ati amene tiyenera kuwakhulupirira. Mwa kuŵerenga Baibulo mosamala, tingaone malangizo ake pankhani imeneyi.

Anthu Amene Tingawakhulupirire

Wamasalmo analemba kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Mawu ouziridwa ameneŵa akutithandiza kuona kuti anthu ambiri si oyenera kuwakhulupirira. Ngakhale anthu amene amalemekezedwa kwambiri ngati “zinduna” za m’dzikoli, monga akatswiri pankhani zinazake kapena pantchito zinazake, sikuti popeza ndi akatswiri ndiye kuti basi tiyenera kuwakhulupirira. Malangizo awo nthaŵi zambiri amakhala olakwika, ndipo kukhulupirira “zinduna” zoterozo kungatikhumudwitse pasanapite nthaŵi yaitali.

 Inde, zimenezi siziyenera kutichititsa kusakhulupirira aliyense. Komabe, mwachionekere tifunika kusankha kuti ndi anthu ati amene tingawakhulupirire. Kodi ndi muyezo uti umene tingagwiritse ntchito posankha anthu amene tingawakhulupirire? Chitsanzo cha mtundu wakale wa Israyeli chingatithandize. Nthaŵi imene panafunika kusankha anthu oti akhale ndi maudindo aakulu mu Israyeli, Mose analangizidwa kuti ‘asankhe mwa anthu ake onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, odana nalo phindu la chinyengo.’ (Eksodo 18:21) Tingaphunzirepo chiyani pamenepa?

Amuna ameneŵa anali atasonyeza makhalidwe ena ake auzimu asanaikidwe kukhala pa maudindo amene anthu anafunika kuwakhulupirira. Anali atasonyeza kale umboni wakuti anali kuopa Mulungu, anali kulemekeza kwambiri Mlengi ndipo anali kuopa kusamusangalatsa. Aliyense anatha kuona kuti amuna ameneŵa anachita zonse zimene akanatha polimbikitsa miyezo ya Mulungu. Anali kudana ndi phindu lonyenga, zimene zinasonyeza kuti anali otsatira kwambiri makhalidwe abwino, zomwe zikanawathandiza kupeŵa kugwiritsa ntchito udindo wawowo molakwika. Sakanawagwiritsa fuwa la moto anthu amene anali kuwakhulupirira n’cholinga choti ziwakomere iwowo kapena achibale ndi mabwenzi awo.

Kodi sikungakhale kwanzeru kugwiritsa ntchito muyezo umenewu masiku ano posankha anthu amene tingawakhulupirire? Kodi tikudziŵapo anthu amene makhalidwe awo amasonyeza kuti amaopa Mulungu? Kodi amafunitsitsa kutsatira miyezo ya makhalidwe abwino ya Mulungu? Kodi ndi otsimikiza kupeŵa kuchita zinthu zolakwika? Kodi ndi oona mtima moti sangagwiritse ntchito mpata umene aupeza kuchita zinthu zoti ziwakomere iwowo basi kapena kuti apeze zimene akufuna? Inde, amuna ndi akazi amene amasonyeza makhalidwe ameneŵa ndi oyenera kuwakhulupirira.

Musataye Mtima Chifukwa Chokhumudwitsidwa mwa Apa ndi Apo

Posankha anthu amene tingawakhulupirire, tiyenera kuleza mtima, popeza kuti kukhulupirira munthu kumatenga nthaŵi. Ndibwino kuyamba kumukhulupirira munthuyo pang’onopang’ono. Motani? Tingaone kaye khalidwe la munthuyo kwa nthaŵi ndithu, kuona mmene amachitira pa nkhani zina. Kodi munthuyo ndi wokhulupirika pa zinthu zazing’ono? Mwachitsanzo, kodi akabwereka zinthu amabweza monga mmene analonjezera ndiponso kodi amasunga nthaŵi akapangana ndi wina kuti aonane panthaŵi inayake? Ngati amatero, mwina tingaganize zomukhulupirira pa zinthu zokulirapo. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu.” (Luka 16:10) Kusankha anthu oti tingawakhulupirire ndiponso kuleza mtima kungatithandize kupeŵa kukhumudwitsidwa kwambiri.

Koma bwanji ngati munthu wina watikhumudwitsa? Anthu amene amaphunzira Baibulo angakumbukire kuti usiku umene Yesu Kristu anagwidwa, anakhumudwitsidwa kwambiri ndi atumwi ake. Yudasi Isikariote ndi amene anam’pereka kwa adani, ndipo atumwi enawo anathawa chifukwa cha mantha. Petro anakana Yesu katatu. Koma Yesu anazindikira kuti Yudasi yekha ndi amene anachita zinthu mwadala. Kukhumudwitsidwa panthaŵi yovuta kwambiri imeneyo sikunalepheretse Yesu kuwatsimikizira atumwi ake 11 otsalawo kuti amawakhulupirira ndipo anatero patangopita milungu yochepa. (Mateyu 26:45-47, 56, 69-75; 28:16-20) Mofananamo, ngati taona kuti munthu amene tinali kum’khulupirira watikhumudwitsa, tingachite bwino kuona ngati zimene wachitazo zikusonyeza kuti ndi wosakhulupirika kapena anangosonyeza kufooka panthaŵi imeneyo.

Kodi Ndine Wokhulupirika?

Munthu amene waganiza zosankha anthu amene angawakhulupirire asangoyang’ana mbali imodzi, m’malo mwake ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndine wokhulupirika? Kodi ndi miyezo yoyenera iti ya kukhulupirika imene ndifunika kukhala nayo ndiponso imene ndingafune kuiona mwa ena?’

Mosakayika, munthu amene ali wokhulupirika amalankhula zoona nthaŵi zonse. (Aefeso 4:25) Sasinthasintha zonena zake kuti zigwirizane ndi anthu amene akulankhula nawo n’cholinga choti zimukomere. Ndipo munthu wokhulupirika akalonjeza, amachita zonse zimene angathe kuti akwaniritse lonjezo lake. (Mateyu 5:37) Munthu wina akamuululira zakukhosi, munthu wokhulupirika amasunga chinsinsi ndipo sanena miseche kwa ena. Munthu wodalirika amakhulupirika kwa munthu amene wakwatirana naye. Saonera zinthu zolaula, saganizira zinthu zoipa zokhudza kugonana, ndipo sakopa akazi kapena amuna ena. (Mateyu 5:27, 28) Munthu amene tingamukhulupirire amalimbikira ntchito kuti apeze zinthu zimene amafunikira pa moyo wake ndiponso zimene banja lake limafunikira,  ndipo saganizira zopeza ndalama mosavuta powadyera masuku pamutu anthu ena. (1 Timoteo 5:8) Kuganizira miyezo yoyenera ndiponso ya m’Malemba imeneyi kudzatithandiza kuzindikira anthu amene tingawakhulupirire. Ndiponso, nthaŵi zonse kutsatira miyezo ya makhalidwe abwino yofananayi kudzathandiza aliyense wa ife kuti anthu ena azitikhulupirira.

Zingakhale zosangalatsa kwambiri kukhala m’dziko limene anthu onse adzakhala okhulupirika ndipo zoti anthu amakhumudwitsidwa ndi amene anali kuwakhulupirira zidzakhala mbiri yakale. Kodi kumeneku n’kungoganizira zinthu zosatheka? Sizili choncho kwa anthu amene saona mopepuka malonjezo a m’Baibulo, chifukwa Mawu a Mulungu amalonjeza kuti “dziko latsopano” lokongola kwambiri lidzafika limene simudzakhala chinyengo, bodza, ndi kudyerana masuku pamutu. Simudzakhalanso chisoni, matenda, ngakhale imfa. (2 Petro 3:13; Salmo 37:11, 29; Chivumbulutso 21:3-5) Kodi sichingakhale chinthu chanzeru kumva zambiri zokhudza chiyembekezo chimenechi? Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuuzani zambiri pankhani imeneyi ndiponso pankhani zina zofunika kwambiri.

[Chithunzi patsamba 4]

Kusakhulupirira anthu ena kungatichititse kuti tikhale osasangalala

[Chithunzi patsamba 5]

Yehova ndi woyenera kumukhulupirira kuposa wina aliyense

[Zithunzi patsamba 7]

Tonsefe timafunikira mabwenzi oti tiziwakhulupirira ndipo nawonso azitikhulupirira