Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akazi Achikristu Okhulupirika Ndi Olambira Mulungu Ofunika Kwambiri

Akazi Achikristu Okhulupirika Ndi Olambira Mulungu Ofunika Kwambiri

 Akazi Achikristu Okhulupirika Ndi Olambira Mulungu Ofunika Kwambiri

“Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.”​—MIYAMBO 31:30.

1. Kodi mmene Yehova amaonera kukongola zimasiyana bwanji ndi mmene dziko limaonera?

DZIKOLI limaona kuti maonekedwe ndi ofunika kwambiri, makamaka kwa akazi. Koma Yehova amaona kuti umunthu wamkati ndiye wofunika kwambiri, umene ukhoza kupitirirabe kukongola kwambiri pamene munthu akupita ku uchikulire. N’chifukwa chake Baibulo limalimbikitsa akazi kuti: “Kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golidi, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.”​—1 Petro 3:3, 4.

2, 3. Kodi akazi anathandiza bwanji kuti uthenga wabwino ulalikidwe kwambiri m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, ndipo kodi zimenezi zinanenedweratu motani?

2 Akazi ambiri amene anatchulidwa m’Baibulo anasonyeza mtima wosiririka woterowo. M’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, ena mwa akazi ameneŵa anali ndi mwayi wapadera wotumikira Yesu ndi atumwi ake. (Luka 8:1-3) Kenaka, akazi achikristu anadzakhala alaliki achangu. Ena anathandiza kwambiri amuna achikristu amene anali kutsogolera, kuphatikizapo mtumwi Paulo; ndipo ena anachereza alendo mwa njira yochititsa chidwi kwambiri, mpaka kulola kuti nyumba zawo azichitiramo misonkhano yampingo.

3 Malemba ananeneratu zoti Yehova adzagwiritsa ntchito akazi kuti agwire ntchito yaikulu pokwaniritsa zolinga zake. Mwachitsanzo, lemba la Yoweli 2:28, 29 linaneneratu kuti amuna ndi akazi, ana ndi akuluakulu, adzalandira mzimu woyera ndipo adzagwira nawo ntchito yofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu. Ulosi umenewo unayamba kukwaniritsidwa pa Pentekoste wa mu 33 C.E. (Machitidwe 2:1-4, 16-18) Akazi ena odzozedwa ndi mzimu anapatsidwa mphatso zodabwitsa, monga mphatso yakunenera. (Machitidwe 21:8, 9) Chifukwa cha changu chawo potumikira, gulu lalikulu la asilikali auzimu la alongo okhulupirika limeneli linathandiza kuti Chikristu chifalikire mwamsanga m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Moti pofika cha m’ma  60 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali ‘utalalikidwa kwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’​—Akolose 1:23.

Anawayamikira Chifukwa cha Kulimba Mtima, Changu, ndi Kuchereza Alendo Kwawo

4. Kodi ndi zifukwa zabwino ziti zimene zinam’pangitsa Paulo kuyamikira akazi angapo mu mpingo wachikristu wa m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino?

4 Mtumwi Paulo anali m’modzi mwa anthu amene anayamikira mwapadera utumiki wa akazi enaake, monga mmene oyang’anira achikristu masiku ano amayamikirira utumiki wa akazi achangu. Ena mwa akazi amene Paulo anachita kuwatchula mayina awo anali “Trufena, ndi Trufosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye,” ndi “Persida, wokondedwayo amene anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye.” (Aroma 16:12) Paulo analembanso kuti Euodiya ndi Suntuke, ‘anakangalika naye pamodzi mu Uthenga Wabwino.’ (Afilipi 4:2, 3) Priska, pamodzi ndi mwamuna wake, Akula, nawonso anatumikira limodzi ndi Paulo. Priska ndi Akula mpaka “anapereka khosi lawo” chifukwa cha Paulo, zimene zinam’pangitsa Pauloyo kulemba kuti: “Ndiwayamika, siine ndekha, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu.”​—Aroma 16:3, 4; Machitidwe 18:2.

5, 6. Kodi Priska anapereka chitsanzo chabwino kwa alongo masiku ano m’njira zotani?

5 Kodi n’chiyani chinapangitsa Priska kukhala wachangu ndi wolimba mtima? Tingapeze yankho mu nkhani imene ili pa Machitidwe 18:24-26, pamene timaŵerenga kuti Priska limodzi ndi mwamuna wake anathandiza Apolo, munthu wodziŵa kulankhula, kuti adziŵe bwinobwino choonadi chimene chinali chitavumbulidwa panthaŵiyo. Choncho, zikuoneka kuti Priska anali kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu ndi ziphunzitso za atumwi. Chifukwa cha zimenezi, anakhala ndi makhalidwe abwino kwambiri amene anam’pangitsa kukhala wofunika kwambiri kwa Mulungu ndi kwa mwamuna wake ndiponso anali wofunika mumpingo woyambirira. Alongo achikristu akhama masiku ano nawonso ndi ofunika chimodzimodzi. Alongo ameneŵa amaphunzira Baibulo mwakhama ndiponso amadya chakudya chauzimu chimene Yehova amapereka kudzera mwa “mdindo wokhulupirika.”​—Luka 12:42.

6 Akula ndi Priska anali anthu odziŵa kuchereza alendo kwambiri. Paulo anakhala kunyumba kwawo pamene anali kugwira nawo limodzi ntchito yopanga mahema ku Korinto. (Machitidwe 18:1-3) Pamene banjali linasamukira ku Efeso, ndipo kenaka ku Roma, linapitirizabe kuchereza alendo mwachikristu, ndipo mpaka linalola kuti nyumba yawo azichitiramo misonkhano yampingo. (Machitidwe 18:18, 19; 1 Akorinto 16:8, 19) N’chimodzimodzinso ndi Numfa ndiponso Mariya, amayi ake a Yohane Marko. Nawonso analola kuti nyumba zawo azichitiramo misonkhano yampingo.​—Machitidwe 12:12; Akolose 4:15.

Ndi Ofunika Kwambiri Masiku Ano

7, 8. Kodi akazi achikristu ambiri masiku ano ali ndi mbiri yabwino yotani ya utumiki wopatulika, ndipo kodi angakhale otsimikiza za chiyani?

7 Monga mmene zinalili m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, akazi achikristu okhulupirika masiku ano nawonso amachita zambiri pa kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Mulungu, makamaka pa ntchito yolalikira. Ndipo alongo ameneŵa ali ndi mbiri yabwino kwabasi! Taganizirani chitsanzo cha a Gwen, amene anatumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zopitirira 50 mpaka pamene anamwalira m’chaka cha 2002. “Changu cha a Gwen polalikira chinali chodziŵika kwa aliyense mu mzinda wathu,” anatero amuna awo. “Iwo anali kuona munthu aliyense ngati woti akhoza kupindula ndi chikondi ndi malonjezo a Yehova. Kukhulupirika kwawo kwa Mulungu, ku gulu lake, ndi ku banja lathu, kuphatikizapo kutilimbikitsa kwawo kwachikondi pa nthaŵi zovuta, kunali thandizo lalikulu kwa ine ndi ana athu pa nthaŵi yonse imene takhala mosangalala limodzi pa moyo wathu. Tikuwasoŵa kwambiri.” A Gwen ndi amuna awo anakhala pa banja kwa zaka 61.

8 Akazi achikristu ambirimbiri, osakwatiwa ndi okwatiwa, amatumikira monga apainiya ndi amishonale, ndipo amakhutira ndi zinthu zochepa zokha zofunika pamoyo pamene akufalitsa uthenga wa Ufumu m’magawo osiyanasiyana, kuyambira m’mizinda yapikitipikiti mpaka kumadera otalikirana ndi ena. (Machitidwe 1:8) Ena alolera kusakhala ndi nyumba kapena ana kuti atumikire Yehova mokwanira. Palinso alongo amene amathandiza mokhulupirika amuna awo amene akutumikira monga oyang’anira oyendayenda, ndipo  alongo ambiri akutumikira m’mabanja a Beteli padziko lonse lapansi. Mosakayikira, akazi odzimana ameneŵa ali m’gulu la “zofunika za amitundu onse” zimene zadzaza nyumba ya Yehova ndi ulemerero.​—Hagai 2:7.

9, 10. Kodi anthu ena m’mabanja ayamikira bwanji chitsanzo chabwino cha akazi ndi amayi achikristu?

9 Komabe, akazi achikristu ambiri ali ndi udindo wosamalira banja lawo. Ngakhale zili choncho, iwo amaika zinthu zokhudzana ndi Ufumu patsogolo. (Mateyu 6:33) Mpainiya wina wosakwatiwa analemba kuti: “Mayi anga ndi amene anapangitsa kwambiri kuti ndikhale mpainiya wokhazikika chifukwa cha chikhulupiriro chawo cholimba ndi chitsanzo chawo chabwino. Ndipo anali mmodzi mwa anthu odalirika kwambiri amene ndinali kuchita nawo upainiya.” Mwamuna wina ananena mawu otsatiraŵa onena za mkazi wake, mayi wa ana aakazi asanu amene panopa ndi akuluakulu: “M’nyumba mwathu nthaŵi zonse munkakhala moyera ndipo zinthu zinkakhala zoikidwa mwadongosolo. Bonnie anaonetsetsa kuti m’nyumba mwathu musamakhale zinthu zambirimbiri n’cholinga choti banja lathu lizithera nthaŵi yambiri pa zinthu zauzimu. Chifukwa chakuti anali kugwiritsa ntchito ndalama mosamala, zinatheka kuti ine ndizigwira ntchito yaganyu kwa zaka 32, zimene zinandithandiza kuti ndizikhala ndi nthaŵi yambiri yokhala ndi banja langa komanso yochita zinthu zauzimu. Mkazi wanga anaphunzitsanso ana athu kufunika kogwira ntchito molimbika. Zonse zimene ndinganene n’zomuyamikira basi.” Pakadali pano, mwamuna ndi mkazi ameneyu akutumikira ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova.

10 Mwamuna wina analemba mawu otsatiraŵa onena za mkazi wake, mayi wa ana amene panopa ndi akuluakulu: “Makhalidwe amene ndimasirira kwambiri mwa a Susan ndi kukonda kwawo kwambiri Mulungu ndi anthu, komanso kumvetsetsa kwawo zinthu, kumvera ena chisoni, ndi kuona mtima. Nthaŵi zonse akhala akutsatira mfundo yoti Yehova tiyenera kum’patsa zinthu zabwino kwambiri zimene tingathe, ndipo amagwiritsa ntchito mfundo imeneyi pa moyo wawo monga mtumiki wa Mulungu komanso monga mayi.” Chifukwa cha thandizo la mkazi wake, mwamuna ameneyu watha kulandira maudindo auzimu angapo, monga kutumikira ngati mkulu, mpainiya, woyang’anira dera wogwirizira, ndi kukhala nawo m’Komiti Yolankhulana ndi Chipatala. Akazi oterowo ndi ofunikadi kwambiri kwa amuna awo, Akristu anzawo, ndipo koposa zonse, kwa Yehova!​—Miyambo 31:28, 30.

Akazi Ofunika Kwambiri Omwe Alibe Mwamuna

11. (a) Kodi Yehova wasonyeza bwanji kuti amadera nkhaŵa akazi okhulupirika, makamaka akazi amasiye? (b) Akazi amasiye achikristu ndi alongo ena okhulupirika amene alibe mwamuna angakhale otsimikiza za chiyani?

11 Nthaŵi zambiri Yehova anasonyeza kuti anali kudera nkhaŵa akazi amasiye. (Deuteronomo 27:19; Salmo 68:5; Yesaya 10:1, 2) Mpaka pano sanasinthe. Iye amaderabe nkhaŵa osati akazi amasiye okha komanso amayi olera okha ana ndi akazi amene alibe mwamuna chifukwa chochita kusankha okha kapena amene sanapeze mwamuna wachikristu woyenera woti akwatirane naye. (Malaki 3:6; Yakobo 1:27) Ngati ndinu mmodzi mwa akazi amene akutumikira Yehova mokhulupirika opanda kuthandizidwa ndi mwamuna wachikristu, mungakhale otsimikiza kuti ndinu wofunika kwambiri kwa Mulungu.

12. (a) Kodi alongo ena achikristu amasonyeza bwanji kukhulupirika kwawo kwa Yehova? (b) Kodi ena mwa alongo athu akulimbana ndi mavuto otani?

12 Taganizirani mwachitsanzo alongo athu achikristu amene sanakwatiwe chifukwa chomvera mokhulupirika langizo loti ayenera kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; Miyambo 3:1) Mawu a Mulungu akuwatsimikizira kuti:  ‘Kwa munthu wokhulupirika, [Yehova] adzakhala wokhulupirika.’ (2 Samueli 22:26, NW) Komabe, kwa ambiri a iwo, kukhala wosakwatiwa ndi chinthu chovuta. Mlongo wina anati: “Ndinatsimikiza kuti ndidzakwatiwa mwa Ambuye, koma nthaŵi zambiri ndakhetsa misozi poona anzanga ambiri akukwatiwa ndi amuna achikristu abwino kwambiri pamene ine ndikadali ndekha.” Mlongo wina anati: “Ndatumikira Yehova kwa zaka 25. Ndine wotsimikiza kukhala wokhulupirika kwa iye, koma nthaŵi zambiri sindisangalala chifukwa cha kusungulumwa.” Iye akupitiriza kuti: “Alongo ngati ineyo amafunika kuwalimbikitsa.” Kodi tingathandize bwanji alongo okhulupirika oterowo?

13. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha anthu amene ankapita kukaona mwana wamkazi wa Yefita? (b) Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere kuti timadera nkhaŵa alongo osakwatiwa mu mpingo wathu?

13 Njira imodzi timaipeza m’chitsanzo chakale. Pamene mwana wamkazi wa Yefita analola kutaya mwayi wake wokhala ndi mwamuna, anthu anazindikira kuti anali kudzimana kwambiri. Kodi anachita chiyani kuti amulimbikitse? ‘Ana aakazi a Israyeli anamuka chaka ndi chaka kum’lirira [“kum’yamikira,” NW] mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anayi pachaka.’ (Oweruza 11:30-40) Nafenso tiyenera kuyamikira kuchokera pansi pamtima alongo osakwatiwa amene amamvera lamulo la Mulungu mokhulupirika. * Kodi njira ina imene tingasonyezere kuti timawadera nkhaŵa ndi iti? M’mapemphero athu tiyenera kupempha Yehova kuti azilimbikitsa alongo okondedwa okhulupirika ameneŵa kuti apitirizebe kumutumikira mokhulupirika. Amafunika kuwalimbikitsa powakumbutsa kuti Yehova ndi mpingo wonse wachikristu umawakonda kwambiri ndi kuwaona kuti ndi ofunika kwambiri.​—Salmo 37:28.

Zimene Zimathandiza Makolo Olera Okha Ana Kuti Zinthu Ziwayendere Bwino

14, 15. (a) Kodi n’chifukwa chiyani akazi achikristu olera okha ana ayenera kupempha Yehova kuti awathandize? (b) Kodi makolo olera okha ana angachite bwanji zinthu mogwirizana ndi mapemphero awo?

14 Akazi achikristu amene akulera okha ana amakumana ndi mavuto ambiri. Komabe, angapemphe Yehova kuti awathandize kulera ana awo motsatira mfundo za m’Baibulo. N’zoona kuti ngati ndinu kholo lolera lokha ana simungakwanitse kuchita zinthu zonse zimene mayi ndi bambo amafunika kuchita. Komabe, Yehova adzakuthandizani kukwanitsa kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene mumafunika kuchita ngati mumupempha mwachikhulupiriro. Mwachitsanzo: Yerekezerani kuti muli ndi thumba lolemera la chimanga chimene mukufuna kupita nacho ku chigayo. Ndiyeno munthu wina wakuuzani kuti angakubwerekeni njinga yake kuti munyamulirepo chimangacho popita kuchigayoko. Kodi mutakhala kuti mumatha kupalasa bwinobwino mungakane kugwiritsa ntchito njingayo, n’kunena kuti musenza thumba lolemeralo nokha mpaka kukafika kuchigayoko? Ayi simungatero. Mofanana ndi zimenezo, musamanyamule katundu wolemera wa m’maganizo nokha pamene mungathe kupempha Yehova kuti akuthandizeni. Ndipotu, iye akukuuzani kuti muzimupempha. Lemba la Salmo 68:19 limati: ‘Wolemekezeka Ambuye,  tsiku ndi tsiku atisenzera katundu.’ Lemba la 1 Petro 5:7 likukupemphaninso kuti mutaye nkhaŵa zanu zonse pa Yehova ‘pakuti Iye asamalira inu.’ Choncho mavuto ndi nkhaŵa zikakuchulukirani, dzipepuzeni mwa kuziponya kwa Atate anu akumwamba, ndipo muzichita zimenezi “kosaleka.”​—1 Atesalonika 5:17; Salmo 18:6; 55:22.

15 Mwachitsanzo, ngati ndinu mayi, mwachidziŵikire mumadera nkhaŵa kuti ana anu angatengere makhalidwe oipa a anzawo ku sukulu, kapena ziyeso za chikhulupiriro chawo zimene angakumane nazo. (1 Akorinto 15:33) Zimenezi ndi nkhaŵa zomveka ndithu. Koma ndi zinthunso zoti mungazitchule m’pemphero. Ndipo, bwanji osapempherera zinthu zimenezi limodzi ndi ana anu asanapite kusukulu, mwina mukatha kukambirana lemba la tsiku? Mapemphero ochokera pansi pamtima otchula mavuto amene mukukumana nawo angakhudze kwambiri ana anu. Koposa zonse, Yehova adzakudalitsani ngati mumayesetsa moleza mtima kukhomereza Mawu ake mumtima mwa ana anu. (Deuteronomo 6:6, 7; Miyambo 22:6) Kumbukirani kuti “maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo.”​—1 Petro 3:12; Afilipi 4:6, 7.

16, 17. (a) Kodi mwana wina wamwamuna ananena chiyani za chikondi chimene mayi ake anasonyeza? (b) Kodi kukonda zinthu zauzimu kwa mayiyo kunakhudza bwanji ana awo?

16 Taganizirani chitsanzo cha Olivia, mayi wa ana asanu ndi mmodzi. Mwamuna wake wosakhulupirira anawasiya patangopita kanthaŵi kochepa mwana wawo womaliza atabadwa, koma Olivia anatenga ndi mtima wonse udindo wophunzitsa ana ake motsatira njira za Mulungu. Mwana wake wamwamuna, dzina lake Darren, amene tsopano ali ndi zaka 31 ndipo ndi mkulu wachikristu komanso mpainiya, anali ndi zaka pafupifupi 5 panthaŵiyo. Kuonjezera pa nkhaŵa zimene Olivia anali nazo, Darren anayamba kudwala matenda aakulu amene mpaka pano amavutika nawobe. Poganizira za ubwana wake, Darren analemba kuti: “Ndimakumbukirabe ndili pa bedi langa kuchipatala ndikudikira Mayi kuti abwere. Ankakhala pambali panga n’kundiŵerengera Baibulo tsiku lililonse. Ndiyeno ankayimba nyimbo ya Ufumu yakuti ‘Tikuyamikani, Yehova.’ * Mpaka lero, imeneyo ndi nyimbo ya Ufumu imene ndimaikonda koposa zonse.”

17 Chifukwa chakuti Olivia anali kukhulupirira ndi kukonda Yehova, zinamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino pa ntchito yolera yekha ana. (Miyambo 3:5, 6) Maganizo abwino amene anali nawo anaonekera pa zolinga zimene ankafuna kuti ana ake akhale nazo. Darren anati: “Mayi nthaŵi zonse anali kutilimbikitsa kuti tizikhala n’cholinga chodzachita utumiki wa nthaŵi zonse. Chifukwa cha zimenezi, azichemwali anga anayi mwa asanu ndi ineyo tonse tinaloŵa utumiki wa nthaŵi zonse. Koma Mayi sankalankhula modzitukumula za zimenezi kwa ena. Ndimayesetsa kwambiri kutsatira makhalidwe awo abwino.” N’zoona kuti si ana onse amene amatumikira Mulungu akakula monga mmene anachitira ana a Olivia. Koma ngati  mayi akuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, angakhale wotsimikiza kuti Yehova adzamutsogolera ndi kumuthandiza mwachikondi.​—Salmo 32:8.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Yehova watichitira potipatsa mpingo wachikristu?

18 Mulungu amapereka thandizo makamaka kudzera ku mpingo wachikristu, kumene kumakhala ndondomeko yolandirira chakudya chauzimu, ubale wachikristu, ndi amuna achikulire mwauzimu amene ndi “mphatso mwa amuna.” (Aefeso 4:8, NW) Akulu okhulupirika amagwira ntchito mwakhama kuti alimbikitse onse mu mpingo, ndipo amasamala makamaka zosoŵa za “ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo.” (Yakobo 1:27) Choncho, gwirizanani kwambiri ndi anthu a Mulungu, ndipo musamadzipatule.​—Miyambo 18:1; Aroma 14:7.

Ubwino wa Kugonjera

19. Kodi n’chifukwa chiyani kugonjera sikutanthauza kuti mkazi ndi wopereŵera, ndipo ndi chitsanzo chiti m’Baibulo chimene chikugwirizana ndi mfundo imeneyi?

19 Yehova analenga mkazi kuti athandize mwamuna. (Genesis 2:18) Choncho mkazi akamagonjera mwamuna wake sizitanthauza kuti mkaziyo ndi wopereŵera m’njira ili yonse. M’malomwake, kugonjera kumapatsa mkazi ulemu, ndipo kumalola mkaziyo kugwiritsa ntchito mphatso ndi luso lake losiyanasiyana mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Miyambo chaputala 31 amafotokoza ntchito zambiri zosiyanasiyana zimene mkazi waluso anali kugwira mu Israyeli wakale. Anathandiza osoŵa, kudzala minda ya mpesa, ndi kugula malo. Inde, ‘mtima wa mwamuna wake unam’khulupirira, sanasoŵe phindu.’​—Mavesi 11, 16, 20.

20. (a) Kodi mkazi wachikristu ayenera kuona motani mphatso kapena luso limene Mulungu anam’patsa? (b) Kodi Estere anasonyeza makhalidwe abwino otani, ndipo chifukwa cha zimenezi, kodi Yehova anamugwiritsira ntchito motani?

20 Mkazi wofatsa, woopa Mulungu salakalaka kukhala wapamwamba kapena kuchita mpikisano ndi mwamuna wake. (Miyambo 16:18) Safuna kudzisangalatsa yekha pofunafuna zinthu za m’dziko koma amagwiritsa ntchito mphatso zimene Mulungu anam’patsa makamaka potumikira ena, monga a m’banja mwake, Akristu anzake, okhala nawo pafupi, ndipo koposa onse, Yehova. (Agalatiya 6:10; Tito 2:3-5) Taganizirani chitsanzo cha m’Baibulo cha Mfumukazi Estere. Ngakhale anali wokongola, iye anali wofatsa ndi womvera. (Estere 2:13, 15) Atakwatiwa, anasonyeza ulemu waukulu kwa mwamuna wake, Mfumu Ahaswero, mosiyana ndi mkazi wakale wa mfumuyo, Vasiti. (Estere 1:10-12; 2:16, 17) Ndiponso, Estere anamvera maganizo a Moredekai, mwana wamwamuna wa bambo ake aakulu, yemwe anali wamkulu kwa iye, ngakhale pamene anakhala mfumukazi. Koma sanali wofooka! Molimba mtima anaulula kuipa kwa Hamani, mwamuna waudindo waukulu komanso wankhanza amene anachita chiwembu chofuna kupulula mtundu wa Ayuda. Yehova anamugwiritsira ntchito Estere mwamphamvu kuti ateteze anthu ake.​—Estere 3:8–4:17; 7:1-10; 9:13.

21. Kodi mkazi wachikristu angakhale bwanji wofunika kwambiri kwa Yehova kuposa kale?

21 Mwachionekere, kuyambira kale mpaka masiku ano, akazi oopa Mulungu asonyeza kudzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova ndiponso pa kulambira kwake. Choncho, akazi oopa Mulungu ndi ofunika kwambiri kwa Yehova. Alongo achikristu, lolani kuti Yehova mwa mzimu wake akuumbeni pang’onopang’ono mpaka mudzakhale “chotengera” chosiririka kwambiri, “chokonzera ntchito yonse yabwino.” (2 Timoteo 2:21; Aroma 12:2) Ponena za olambira ofunika kwambiri oterowo, Mawu a Mulungu amati: “Mum’patse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zim’tame kubwalo.” (Miyambo 31:31) Zimenezi zichitiketu choncho kwa inu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Kuti mudziŵe mmene mungawalimbikitsire, onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 2002, masamba 26 mpaka 28.

^ ndime 16 Nyimbo 212 m’buku lakuti Imbirani Yehova Zitamando, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi akazi ena achikristu m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anasonyeza bwanji kuti anali ofunika kwa Yehova?

• Kodi alongo ambiri mu nthaŵi yathu ino achita chiyani kuti akhale ofunika kwa Mulungu?

• Kodi Yehova amathandiza bwanji amayi olera okha ana ndi alongo ena amene alibe mwamuna?

• Kodi mkazi angasonyeze bwanji kuti amalemekezadi umutu?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 17]

ZITSANZO ZOFUNIKA KUZIGANIZIRA

Kodi mukufuna kuona zitsanzo zina zoonjezera za akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo? Ngati mukufuna, chonde ŵerengani malemba amene taika m’munsiŵa. Pamene mukusinkhasinkha za anthu osiyanasiyana amene tawandandalikawo, yesetsani kupeza mfundo zimene mungagwiritse ntchito mokulirapo m’moyo wanu.​—Aroma 15:4.

Sara: Genesis 12:1, 5; 13:18a; 21:9-12; 1 Petro 3:5, 6.

Akazi achiisrayeli ooloŵa manja: Eksodo 35:5, 22, 25, 26; 36:3-7; Luka 21:1-4.

Debora: Oweruza 4:1–5:31.

Rute: Rute 1:4, 5, 16, 17; 2:2, 3, 11-13; 4:15.

Mkazi wa ku Sunemu: 2 Mafumu 4:8-37.

Mkazi wa ku Kanani: Mateyu 15:22-28.

Marita ndi Mariya: Marko 14:3-9; Luka 10:38-42; Yohane 11:17-29; 12:1-8.

Tabita: Machitidwe 9:36-41.

Ana aakazi anayi a Filipo: Machitidwe 21:9.

Febe: Aroma 16:1, 2.

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi mumayamikira alongo osakwatiwa amene amamvera lamulo la Mulungu mokhulupirika?

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi ndi zinthu ziti zimene mungatchule m’pemphero ana anu asanapite ku sukulu?