Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani Elisa anapempha “magawo aŵiri” a mzimu wa Eliya?

Eliya atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake monga mneneri mu Israyeli, mneneri wamng’ono Elisa anamupempha kuti: “Mundipatse magawo aŵiri a mzimu wanu ukhale pa ine.” (2 Mafumu 2:9) Zikuoneka kuti mwauzimu, Elisa ankapempha magawo aŵiri monga amene ankapatsidwa kwa mwana wamwamuna woyamba kubadwa. (Deuteronomo 21:17) Kuonanso mwachidule nkhani imeneyi kutithandiza kumvetsetsa zimenezi ndiponso kupeza maphunziro pa zimene zinachitikazo.

Mogwirizana ndi malangizo a Yehova, mneneri Eliya anadzoza Elisa kuti akhale womuloŵa mmalo. (1 Mafumu 19:19-21) Kwa zaka pafupifupi zisanu ndi chimodzi, Elisa anali mtumiki wa Eliya wokhulupirika ndipo anali wotsimikiza kum’tumikira mpaka mapeto. Anatumikirabe mphunzitsi wakeyo, mpaka pa tsiku lomaliza la Eliya monga mneneri mu Israyeli. Ngakhale kuti Eliya anapempha Elisa kuti asamutsatire, mneneri wamng’onoyo ananena katatu kuti: “Sindikusiyani.” (2 Mafumu 2:2, 4, 6; 3:11) Kunena zoona, Elisa anaona mneneri wachikulireyo monga atate wake wauzimu.​—2 Mafumu 2:12.

Komabe, Eliya anali ndi ana auzimu ena osati Elisa yekha. Eliya ndi Elisa ankagwirizananso ndi gulu la amuna amene ankadziŵika kuti “ana a aneneri.” (2 Mafumu 2:3) Nkhani imene ili m’buku Lachiŵiri la Mafumu imasonyeza kuti “ana” ameneŵa analinso ogwirizana kwambiri ndi atate wawo wauzimu, Eliya. (2 Mafumu 2:3, 5, 7, 15-17) Komabe, chifukwa chakuti Elisa anali wodzozedwa kuti alowe mmalo mwa Eliya, anali wamkulu mwauzimu pa ana auzimu a Eliya ndipo anali ngati woyamba kubadwa. Mu Israyeli wakale, mwana wamwamuna woyamba kubadwa ankalandira zigawo ziŵiri za cholowa cha atate wake, pamene ana ena onse ankalandira chigawo chimodzi. N’chifukwa chake Elisa anapempha zigawo ziŵiri za cholowa chauzimu cha Eliya.

N’chifukwa chiyani Elisa anapempha magawo aŵiri pa nthaŵi imeneyi? Chifukwa chakuti ankayembekezera kutenga udindo waukulu, wolowa mmalo Eliya monga mneneri mu Israyeli. Elisa anadziŵa kuti ankafunikira mphamvu zauzimu zoposa zimene anali nazo, mphamvu zimene akanam’patsa ndi Yehova yekha, kuti akwaniritse udindo wochititsa mantha umenewo. Anafunika kukhala wopanda mantha monga mmene Eliya analili. (2 Mafumu 1:3, 4, 15, 16) Motero, n’chifukwa chake anapempha magawo aŵiri a mzimu wa Eliya. Anapempha mzimu wolimba mtima ndiponso ‘wochitira changu Yehova,’ makhalidwe ofunika amene mzimu wa Mulungu umapereka. (1 Mafumu 19:10, 14) Kodi Eliya anamuyankha bwanji?

Eliya anadziŵa kuti Elisa anali atapempha chinthu chimene iye sakanatha kum’patsa koma Mulungu yekha ndi amene akanam’patsa. Modzichepetsa Eliya anayankha kuti: “Wapempha chinthu chapatali, koma ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe.” (2 Mafumu 2:10) Ndipo Yehova analoladi Elisa kuti aone Eliya akukwera kumwamba m’kamvulumvulu. (2 Mafumu 2:11, 12) Pempho la Elisa linayankhidwa. Yehova anam’patsa mzimu umene ankafuna kuti ayambe kugwira ntchito yake yatsopano ndiponso kuti alimbane ndi mayesero amene anali kubwera.

Masiku ano, Akristu odzozedwa (amene nthaŵi zina amatchedwa a gulu la Elisa) ndi atumiki ena onse a Mulungu akhoza kulimbikitsidwa kwambiri ndi nkhani ya m’Baibulo imeneyi. Nthaŵi zina, tingaone ngati kuti sitingakwanitse kuchita utumiki watsopano, kapena mwina tingayambe kutaya chikhulupiriro kuti tipitirize ntchito yathu yolalikira Ufumu tikamakumana kaŵirikaŵiri ndi anthu osowa chidwi kapena otsutsa m’gawo lathu. Koma ngati tipempha Yehova ndi mtima wonse kuti atithandize, adzatipatsa mzimu woyera kuti tilimbane ndi ziyeso ndiponso kusintha kwa zochitika. (Luka 11:13; 2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Ndipo monga momwe Yehova analimbitsira Elisa chifukwa cha udindo waukulu umene anali nawo, adzathandizanso tonsefe, achinyamata ndi achikulire, kuti tikwaniritse utumiki wathu.​—2 Timoteo 4:5.