Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Amayendabe M’choonadi

Amayendabe M’choonadi

Amayendabe M’choonadi

“Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.”​—3 YOHANE 4.

1. Kodi “choonadi cha Uthenga Wabwino” chimanena kwambiri za chiyani?

YEHOVA amayanja anthu okhawo amene amamulambira “mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Iwo amatsatira choonadi ndiponso kukhulupirira ziphunzitso zonse zachikristu zochokera m’Mawu a Mulungu. “Choonadi cha Uthenga Wabwino” chimenechi chimanena kwambiri za Yesu Kristu ndi kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndi kuti adzachita zimenezo kudzera mu Ufumu. (Agalatiya 2:14) Mulungu walola “machitidwe a kusocheretsa” kwa anthu amene amakonda bodza, koma chipulumutso chimadalira kukhulupirira uthenga wabwino ndi kuyenda m’choonadi.​—2 Atesalonika 2:9-12; Aefeso 1:13, 14.

2. Kodi mtumwi Yohane anayamikira kwambiri chiyani, ndipo panali ubale wotani pakati pa iye ndi Gayo?

2 Olengeza Ufumu ndi “othandizana nacho choonadi.” Mofanana ndi mtumwi Yohane ndi mnzake Gayo, iwo amagwiritsitsa choonadi ndi kuyenda mmenemo. Akuganizira za Gayo, Yohane analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 3-8) Ngakhale kuti Yohane wokalambayo sanaphunzitse Gayo choonadi, poona kukalamba kwa mtumwiyo, uchikulire wake wachikristu, ndi chikondi chake chonga cha atate m’pake kuti Yohane anaona mwamuna wocheperapo ameneyu kukhala mmodzi mwa ana ake auzimu.

Choonadi pa Kulambira kwa Akristu

3. Kodi cholinga cha misonkhano ya Akristu oyambirira chinali chiyani ndipo anapindula bwanji?

3 Kuti aphunzire choonadi, Akristu oyambirira anali kusonkhana monga mipingo, ndipo nthaŵi zambiri anali kusonkhanira m’nyumba za anthu. (Aroma 16:3-5) Kuchita zimenezi kunali kuwalimbikitsa ndipo anali kufulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino. (Ahebri 10:24, 25) Pofotokoza za amene anali kudzitcha Akristu amene anadzakhalako nthaŵi ina, Tertullian (amene anakhala ndi moyo kuyambira cha m’ma 155 mpaka kudutsa 220 C.E.) analemba kuti: “Timasonkhana kuti tiŵerenge mabuku a Mulungu . . . Mawu opatulika amenewo amatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu, kukulitsa chiyembekezo chathu, kutsimikiza za chidaliro chathu.”​—Apology, mutu 39.

4. Kodi kuimba kwakhala ndi mbali yotani pamisonkhano yachikristu?

4 Mosakayika, pamisonkhano ya Akristu oyambirira anali kuimbaponso nyimbo. (Aefeso 5:19; Akolose 3:16) Pulofesa Henry Chadwick analemba kuti wotsutsa wina wa m’zaka za m’ma 100, dzina lake Celsus, anapeza kuti nyimbo za anthu odzitcha Akristu zinali “zabwino kwambiri moti anaipidwa ndi mmene zinakhudzira mtima wake.” Chadwick anawonjeza kuti: “Clement wa ku Alexandria anali wolemba za Chikristu woyambirira kufotokoza nyimbo zoyenera Akristu kuimba. Analangiza kuti zisakhale zogwirizana ndi nyimbo za dansi zodzutsa chilakolako cha kugonana.” (The Early Church, masamba 274-5) Mmene Akristu oyambirira anali kuimbira nyimbo akasonkhana, malinga ndi maumboniŵa, Mboni za Yehova nazonso nthaŵi zambiri zimaimba nyimbo zozikidwa m’Baibulo zimene zimakhala ndi mawu amphamvu otamanda Mulungu ndi Ufumu.

5. (a) Kodi anali kulandira bwanji malangizo auzimu m’mipingo yachikristu yoyambirira? (b) Kodi Akristu oona atsatira bwanji mawu a Yesu a pa Mateyu 23:8, 9?

5 M’mipingo ya Akristu oyambirira, oyang’anira anali kuphunzitsa choonadi, ndipo atumiki otumikira anali kuthandiza okhulupirira anzawo m’njira zosiyanasiyana. (Afilipi 1:1) Bungwe lolamulira limene linadalira Mawu a Mulungu ndi mzimu woyera linali kupereka malangizo auzimu. (Machitidwe 15:6, 23-31) Sanali kugwiritsa ntchito mayina aulemu achipembedzo chifukwa Yesu analamula ophunzira ake kuti: “Musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.” (Mateyu 23:8, 9) Pa zinthu zimenezi ndi zinanso zambiri, Akristu oyambirira akufanana ndi Mboni za Yehova.

Kuzunzidwa Chifukwa Cholalikira Choonadi

6, 7. Ngakhale kuti Akristu amalalikira uthenga wamtendere, kodi anthu awachitira chiyani?

6 Ngakhale kuti anali kulalikira uthenga wa Ufumu wamtendere, Akristu oyambirira anali kuzunzidwa monganso mmene Yesu anazunzidwira. (Yohane 15:20; 17:14) Wolemba mbiri wina, John L. Von Mosheim anati Akristu oyambirira anali “gulu la anthu osawopseza m’pang’ono pomwe, ndipo analibe maganizo alionse odana ndi boma.” Dr. Mosheim anati chimene “chinaputa Aroma kuti azidana ndi Akristu, ndi kalambiridwe kawo kosavuta, kamene sikanali kufanana ndi miyambo yopatulika ya anthu ena onse.” Anawonjezera kuti: “Iwo sanali kupereka nsembe, analibe akachisi, mafano, alauli, kapena magulu a ansembe. Zimenezi zinawanyozetsa kwa anthu ambiri omwe sanali kudziŵa za iwo, omwenso anaganiza kuti sipangakhale chipembedzo chopanda zinthu zimenezi. Motero, anawaona ngati anthu okana Mulungu; ndipo malinga ndi malamulo a Roma, amene anapezeka ndi mlandu wokana Mulungu anali kuwanena kuti ndi anthu owononga dziko.”

7 Ansembe, amisiri, ndi anthu ena amene anali kudalira mafano kuti apeze zofunika pa moyo wawo anasonkhezera anthu kuti adane ndi Akristuwo, omwe sanali kupembedza mafano. (Machitidwe 19:23-40; 1 Akorinto 10:14) Tertullian analemba kuti: “Iwo amakhulupirira kuti Akristu ndi amene amayambitsa masoka onse ogwera Dziko, masoka onse ogwera anthu. Mtsinje wa Tiber ukafika kumalinga, wa Nile ukapanda kufika kuminda, mitambo ikapanda kugunda, kapena dziko likadirizika, kukakhala njala, kukagwa mliri, onse amafuula kuti: ‘Tengani Akristu muponyere mikango!’” Akristu oona ‘amadzisungira okha kupeŵa mafano,’ mosaganizira kuti kaya pachitika zotani.​—1 Yohane 5:21.

Choonadi pa Miyambo ya Zipembedzo

8. N’chifukwa chiyani anthu amene amayenda m’choonadi sakondwerera Khirisimasi?

8 Anthu amene amayenda m’choonadi amapeŵa miyambo yosagwirizana ndi Malemba chifukwa ‘kuunika sikuyanjana ndi mdima.’ (2 Akorinto 6:14-18) Mwachitsanzo, iwo sakondwerera Khirisimasi, imene imachitika pa December 25. “Palibe amene akudziŵa tsiku lenileni limene Kristu anabadwa,” limatero buku lakuti The World Book Encyclopedia. Buku lakuti The Encyclopedia Americana (la 1956) limati: “Saturnalia, phwando la Aroma limene linali kuchitika chapakati pa December, ndi kumene kunachokera miyambo yambiri yokondwerera Khirisimasi.” Buku la Cyclopædia lolembedwa ndi M’Clintock ndi Strong limati: “Mulungu sindiye amene anakhazikitsa mwambo wa Khirisimasi, ndipo sunayambire mu NT [m’Chipangano Chatsopano].” Ndipo buku lakuti Daily Life in the Time of Jesus limati: “Nkhosa . . . zinali kukhala m’khola nyengo yonse ya dzinja; ndipo ndi mfundo imeneyi yokha munthu angaone kuti deti lodziŵika la Khirisimasi, m’dzinja, silingakhale lolondola, popeza Uthenga Wabwino umati abusa anali ali kuthengo.”​—Luka 2:8-11.

9. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova akale ndi a masiku ano sakondwerera Isitala?

9 Isitala amati n’kukumbukira kuuka kwa Kristu, koma magwero odalirika amati inayambira ku chipembedzo chonyenga. Buku lakuti The Westminster Dictionary of the Bible limati Isitala “poyambirira linali phwando la m’masika lolemekeza mulungu wamkazi wa kuwala ndi wa masika wa Atyutoni amene m’chinenero cha Anglo-Saxon ankamutcha Eastre,” kapena Eostre. Ndipotu buku lakuti Encyclopædia Britannica (la nambala 11) limati: “Mulibe umboni uliwonse m’Chipangano Chatsopano wosonyeza kuti anali kukumbukira phwando la Isitala.” Isitala sunali mwambo wa Akristu oyambirira ndipo anthu a Yehova masiku ano sachita mwambowu.

10. Kodi Yesu anayambitsa mwambo wotani, ndipo ndani amene akhala akuchita mwambowu moyenera?

10 Yesu sanalamule otsatira ake kuti azikumbukira kubadwa kwake kapena kuuka kwake, koma anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake ya nsembe. (Aroma 5:8) Inde, umenewu ndi mwambo wokhawo umene analamula ophunzira ake kuti azikumbukira. (Luka 22:19, 20) Mboni za Yehova zikupitiriza kukumbukira mwambo umenewu womwe umachitika kamodzi pachaka ndipo umatchedwanso Mgonero wa Ambuye.​—1 Akorinto 11:20-26.

Kulalikira Choonadi pa Dziko Lonse

11, 12. Kodi oyenda m’choonadi amatani nthaŵi zonse kuti athandize ntchito yawo yolalikira?

11 Amene amadziŵa choonadi amaona kuti ndi mwayi kugwiritsa ntchito nthaŵi yawo, mphamvu zawo, ndi zinthu zina pa ntchito yolalikira uthenga wabwino. (Marko 13:10) Ntchito yolalikira ya Akristu oyambirira inali kuthandizika ndi zopereka zaufulu. (2 Akorinto 8:12; 9:7) Tertullian analemba kuti: “Ngakhale pamakhala bokosi loponyamo kangachepe, zimenezi si ndalama zolipira kuti munthu aloŵe, ngati kuti chipembedzo ndi malonda. Munthu aliyense amabweretsa khobiri lochepa kamodzi pamwezi​—kapena nthaŵi iliyonse imene akufuna, ndiponso kokha ngati wafuna kutero komanso ngati angathe; popeza palibe amene amachita kumuumiriza; n’chopereka chaufulu.”​—Apology, mutu 39.

12 Ntchito yolalikira Ufumu padziko lonse ya Mboni za Yehova imathandizikanso ndi zopereka zaufulu. Kuphatikiza pa Mboni, anthu achidwi oyamikira amaona kuti ndi mwayi kuthandiza ntchito imeneyi ndi zopereka zaufulu. Apanso, Akristu oyambirira akufanana ndi Mboni za Yehova.

Choonadi pa Makhalidwe a Munthu

13. Pankhani ya makhalidwe awo, kodi ndi langizo la Petro liti limene Mboni za Yehova zimamvera?

13 Monga anthu oyenda m’choonadi, Akristu oyambirira anali kumvera langizo la mtumwi Petro lakuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.” (1 Petro 2:12) Mboni za Yehova zimatsatira mawu ameneŵa ndi mtima wonse.

14. Kodi Akristu amaona bwanji zosangalatsa zoipa?

14 Ngakhale pamene mpatuko unali utaloŵerera, Akristu mwa dzina lokha anali kupeŵa makhalidwe oipa. W. D. Killen, pulofesa wa mbiri ya tchalitchi, analemba kuti: “M’zaka za m’ma 100 ndi 200, nyumba ya zisudzo m’tauni yaikulu iliyonse inali kukopa anthu ambiri; ndipo popeza kuti ochita zisudzowo nthaŵi zambiri anali anthu a makhalidwe otayirira, zisudzo zawozo nthaŵi zonse cholinga chake chinali kukhutiritsa zilakolako zoipa za anthu panthaŵiyo. . . . Akristu oona onse anali kuipidwa ndi malo a zisudzowo. . . . Iwo ananyansidwa ndi zolaula za kumeneko; ndipo kupembedza milungu yachikunja yachimuna ndi yachikazi kumeneko kunali kulakwira zimene iwo anakhulupirira m’chipembedzo chawo.” (The Ancient Church, masamba 318-19) Otsatira enieni a Yesu masiku ano amapeŵanso zosangalatsa zonyansa ndiponso zowononga makhalidwe.​—Aefeso 5:3-5.

Choonadi pa “Maulamuliro Aakulu”

15, 16. Kodi “maulamuliro aakulu” ndani, nanga anthu oyenda m’choonadi awaona bwanji maulamuliro ameneŵa?

15 Ngakhale kuti Akristu oyambirira anali ndi makhalidwe abwino, mafumu ambiri a Roma anali kuwaganizira molakwika. Wolemba mbiri wina, E. G. Hardy, anati mafumuwo anaona Akristu kukhala “anthu otengeka onyansa.” Makalata amene Kazembe Pliny Wamng’ono wa ku Bituniya anali kulemberana ndi Mfumu Trajan akusonyeza kuti olamulira ambiri sanali kudziŵa kuti Chikristu chinali chotani kwenikweni. Kodi Akristu amaliona bwanji Boma?

16 Mofanana ndi otsatira a Yesu oyambirira, Mboni za Yehova zimagonjera “maulamuliro aakulu” a boma. (Aroma 13:1-7) Koma ngati zimene anthu akufuna zikusemphana ndi chifuniro cha Mulungu, iwo amatsatira mfundo yakuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Buku lakuti After Jesus​—The Triumph of Christianity limati: “Ngakhale kuti Akristu sanali kulambira mfumu, iwo sanali anthu oyambitsa chisokonezo, ndipo chipembedzo chawo, ngakhale kuti chinali chosiyana ndipo nthaŵi zina akunja ananyansidwa nacho, sichinali choti n’kuukira ufumuwo.”

17. (a) Kodi Akristu oyambirira anali kumbali ya boma liti? (b) Kodi otsatira Kristu oona agwiritsa ntchito bwanji mawu a pa Yesaya 2:4 m’miyoyo yawo?

17 Akristu oyambirira anali kumbali ya Ufumu wa Mulungu, monganso mmene makolo akale Abrahamu, Isake, ndi Yakobo anakhulupirira lonjezo la ‘mudzi womangidwa ndi Mulungu.’ (Ahebri 11:8-10) Mofanana ndi Mbuye wawo, ophunzira a Yesu ‘sanali a dziko lapansi.’ (Yohane 17:14-16) Ndipo pankhani za nkhondo ndi mikangano, iwo analondola mtendere mwa ‘kusula malupanga awo kukhala zolimira.’ (Yesaya 2:4) Poona kufanana kochititsa chidwi, mphunzitsi wina wa payunivesite, Geoffrey F. Nuttall, yemwe amaphunzitsa mbiri ya chipembedzo, anati: “Mmene Akristu oyambirira ankaonera nkhondo zikufanana kwambiri ndi mmene zimachitira Mboni za Yehova ngakhale kuti zimenezi zimativuta kuvomereza.”

18. N’chifukwa chiyani boma lililonse lilibe chifukwa choopera Mboni za Yehova?

18 Monga anthu osaloŵerera m’nkhani zandale koma ogonjera “maulamuliro aakulu,” Akristu oyambirira sanali oti angaukire maulamuliro andale amene analipo. N’chimodzimodzinso ndi Mboni za Yehova. Mkonzi wa nkhani wa ku North America analemba kuti: “Munthu wa maganizo osamva za ena ndi wosakhulupirira ena ndiye angaganize kuti Mboni za Yehova zingaukire boma lililonse. Izo siziukira boma ndipo zimakonda kwambiri mtendere monga momwe gulu la chipembedzo liyenera kukhalira.” Olamulira amene akudziŵa bwinobwino Mboni za Yehova saziopa.

19. Pankhani ya misonkho, kodi tinganene chiyani za Akristu oyambirira ndi Mboni za Yehova?

19 Njira ina imene Akristu oyambirira anasonyezera kulemekeza “maulamuliro aakulu” inali kukhoma misonkho. Polembera Mfumu ya Roma Antoninus Pius (138-161 C.E.), Justin Martyr anati Akristu anali kukhoma misonkho “mosaumira kuposa anthu ena onse.” (First Apology, mutu 17) Ndipo Tertullian anauza olamulira a Roma kuti anthu awo okhometsa misonkho anali ndi “mangawa oyamikira Akristu” chifukwa cha kukhoma kwawo misonkho mokhulupirika. (Apology, mutu 42) Akristu anapindula ndi Pax Romana, kapena kuti Mtendere wa Aroma, nthaŵi imene kunali bata ndi mtendere, misewu yabwino, ndi maulendo apanyanja otetezekapo. Pozindikira udindo wawo kwa anthu onse, iwo anamvera mawu a Yesu akuti: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) Anthu a Yehova masiku ano amatsatira langizo limeneli ndipo anthu awayamikira chifukwa cha kuona mtima kwawo, monga pankhani yokhoma misonkho.​—Ahebri 13:18.

Choonadi Chimagwirizanitsa Anthu

20, 21. Pankhani ya ubale wamtendere, kodi zinali motani pakati pa Akristu oyambirira ndipo zili motani kwa atumiki a Yehova masiku ano?

20 Popeza anali kuyenda m’choonadi, Akristu oyambirira anali ogwirizana pamodzi mu ubale wamtendere, monganso mmene Mboni za Yehova zilili masiku ano. (Machitidwe 10:34, 35) Kalata imene anaisindikiza mu The Moscow Times inati: “[Mboni za Yehova] n’zodziŵika monga anthu abwino, okoma mtima, ndiponso anthu ofatsa omwe savuta kugwirizana nawo, savutitsa anthu ena ndipo nthaŵi zonse amayesetsa kukhala mwamtendere ndi anzawo . . . M’gulu lawo mulibe anthu akatangale, zidakwa kapena okonda mankhwala osokoneza bongo, ndipo chifukwa chake n’chapafupi: Amayesetsa kutsatira zikhulupiriro zawo za m’Baibulo pa chilichonse chimene akuchita kapena kunena. Ngati anthu onse padziko lapansi akanayesetsa kutsatira zimene Baibulo limanena monga mmene zimachitira Mboni za Yehova, dziko lathu lankhanzali likanasinthiratu.”

21 Buku lakuti Encyclopedia of Early Christianity limati: “M’tchalitchi choyambirira anali kudziona monga anthu amodzi atsopano ndipo magulu omwe kale anali kudana, Ayuda ndi Akunja, tsopano ankakhalira limodzi mwamtendere.” Mboni za Yehova nazonso ndi abale a padziko lonse okonda mtendere​—inde, gulu la anthu a dziko latsopano. (Aefeso 2:11-18; 1 Petro 5:9; 2 Petro 3:13) Mkulu woyang’anira za chitetezo pabwalo la Pretoria Show Grounds ku South Africa ataona mmene Mboni za mafuko onse zinasonkhanira kumeneko mwamtendere pamsonkhano wawo, anati: “Aliyense anali waulemu ndipo ndi waulemu, anthu amalankhulana bwino, khalidwe limene asonyeza masiku angapo apitaŵa​—likungosonyeza mtima umene anthu a m’gulu lanu ali nawo, ndiponso kuti onse amagwirizana monga banja limodzi lachimwemwe.”

Madalitso Chifukwa Chophunzitsa Choonadi

22. N’chiyani chakhala chikuchitika chifukwa chakuti Akristu akhala akuonetsa choonadi?

22 Mwa makhalidwe awo ndi ntchito yawo yolalikira, Paulo ndi Akristu ena anali ‘kuonetsa choonadi.’ (2 Akorinto 4:2) Kodi simukuvomereza kuti Mboni za Yehova zikuchitanso chimodzimodzi ndipo zikuphunzitsa mitundu yonse choonadi? Anthu padziko lonse lapansi akutsatira kulambira koona ndipo akukhamukira ku ‘phiri la nyumba ya Yehova’ ndiponso akuwonjezeka nthaŵi zonse. (Yesaya 2:2, 3) Chaka chilichonse, anthu zikwizikwi akubatizidwa posonyeza kudzipatulira kwawo kwa Mulungu, zimene zikuchititsa kuti mipingo yatsopano yambiri ipangike.

23. Kodi mumawaona bwanji anthu amene akuphunzitsa mitundu yonse choonadi?

23 Ngakhale kuti anthu a Yehova amachokera kosiyanasiyana, ndi ogwirizana pa kulambira koona. Chikondi chimene amasonyeza chimawadziŵikitsa kuti ndi ophunzira a Yesu. (Yohane 13:35) Kodi mukuona kuti ‘Mulungu ali ndithu mwa iwo’? (1 Akorinto 14:25) Kodi muli kumbali ya anthu amene akuphunzitsa mitundu yonse choonadi? Ngati ndi choncho, yamikiranibe choonadi ndipo khalani ndi mwayi woyenda m’choonadicho mpaka kalekale.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Pankhani ya kalambiridwe, kodi Akristu oyambirira akufanana bwanji ndi Mboni za Yehova?

• Kodi mwambo wokha wa chipembedzo umene oyenda m’choonadi amakumbukira ndi uti?

• Kodi “maulamuliro aakulu” ndani, ndipo Akristu amawaona bwanji?

• Kodi choonadi chimawagwirizanitsa bwanji anthu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Misonkhano yachikristu nthaŵi zonse yakhala ikuthandiza amene akuyenda m’choonadi

[Zithunzi patsamba 23]

Yesu analamula otsatira ake kuchita Chikumbutso cha imfa yake ya nsembe

[Chithunzi patsamba 24]

Mofanana ndi Akristu oyambirira, Mboni za Yehova zimalemekeza “maulamuliro aakulu”