Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tichitire Onse Chokoma”

“Tichitire Onse Chokoma”

 “Idzani Kuno kwa Ine . . . Ndipo Ine Ndidzakupumulitsani Inu”

“Tichitire Onse Chokoma”

NTCHITO yolalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiyo inali chinthu choyamba pamoyo wa Yesu. (Marko 1:14; Luka 8:1) Popeza otsatira a Kristu amafuna kutengera chitsanzo chake, amaona ntchito yophunzitsa uthenga wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Mulungu kukhala chinthu choyamba pamoyo wawo. (Luka 6:40) Mboni za Yehova zimasangalala kwambiri kuona mmene uthenga wa Ufumu ukudzetsera mpumulo wokhalitsa kwa anthu amene amaulandira monga unachitira panthaŵi yomwe Yesu anali padziko lapansi.​—Mateyu 11:28-30.

Yesu anachita ntchito zina zabwino monga kuchiritsa odwala ndiponso kudyetsa anjala kuwonjezera pa ntchito yophunzitsa Mawu a Mulungu. (Mateyu 14:14-21) N’chimodzimodzinso Mboni za Yehova. Izo zimaphunzitsa Baibulo komanso zimagwira ntchito zina zomwe zimathandiza anthu osoŵa. Ndipotu Malemba amakonzekeretsa Akristu ‘kuchita ntchito iliyonse yabwino’ ndiponso kuwalimbikitsa ‘kuchitira onse chokoma.’​—2 Timoteo 3:16, 17; Agalatiya 6:10.

“Abale Athu Anali Komweko”

Mu September 1999, ku Taiwan kunachitika chivomezi choopsa. Patangopita miyezi yoŵerengeka, mvula yamkuntho ndiponso zigumukire zinawononga kwambiri ku Venezuela kuposa tsoka lachilengedwe lina lililonse m’mbiri ya dzikolo. Posachedwapa, madzi osefukira anawononga kwambiri ku Mozambique. Pa zochitika zitatu zonsezi, Mboni za Yehova zinafika ndi thandizo kumalo angoziwo mofulumira. Zinapereka zakudya, madzi, mankhwala, zovala, matenti, ndiponso ziŵiya zophikira kwa anthu okhudzidwa ndi masokawo. Anthu odzipereka odziŵa zachipatala anakhazikitsa malo ongoyembekezera othandizirako anthu ovulala. Ndipo odziŵa ntchito yomanga anadzipereka kumanga nyumba zatsopano za anthu omwe nyumba zawo zinawonongeka.

Ovutikawo anakhudzidwa mtima kwambiri ndi thandizo lapanthaŵi yake lomwe analandira. “Pamene tinasoŵeratu chochita, abale athu anatithandiza,” anatero Malyori yemwe nyumba yake inawonongeka  ndi chigumukire ku Venezuela. Amene anadzipereka kumangira nyumba yatsopano mlongoyu ndi banja lake, anati: “Tikusoŵa mawu omuthokozera Yehova chifukwa cha zonse zomwe watichitira.” Ndipo anthu amene nyumba zawo zinapita ndi madzi osefukira ku Mozambique atalandira makiyi a nyumba zatsopano zomwe anawamangira, nthaŵi yomweyo onse anayamba kuimba nyimbo ya Ufumu yakuti “Yehova Ndiye Pothaŵirapo Pathu.” *

Kuthandiza anthu osoŵa kunalimbikitsanso kwambiri anthu amene anadzipereka kugwira ntchitoyi. Marcelo yemwe anali nesi pamsasa wina ku Mozambique anati: “Ndinali wokondwa kuthandiza abale ovutika kwambiriwo.” Huang yemwe anadzipereka kuti athandize ku Taiwan anati: “Unali mwayi wapadera kwambiri kugwira nawo ntchito yopereka zakudya komanso matenti kwa abale osoŵa. Zinali zolimbitsa chikhulupiriro kwambiri.”

Ntchito Yodzifunira Imene Imapindulitsadi

Ntchito yodzifunirayi yapereka mpumulo wauzimu kwa akaidi zikwizikwi padziko lonse. Motani? M’zaka zaposachedwapa, Mboni za Yehova zagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo kwa anthu oposa 30,000 amene ali m’ndende pafupifupi 4,000 ku United States kokha. Komanso, ngati n’kotheka, Mboni zimapita kundendeko kukaphunzira Baibulo ndi akaidi ndiponso kukachititsa misonkhano yachikristu. Kodi akaidiwo apindula?

Akaidi ena amene akuphunzira Baibulo amayamba kuuza akaidi anzawo ziphunzitso zopatsa mpumulo za m’Mawu a Mulungu. Mapeto ake, m’ndende zambiri padziko lonse muli magulu a akaidi omwe akulambira Yehova. M’chaka cha 2001, mkaidi wina kundende ya ku Oregon, U.S.A. anati: “Kagulu kathu kakuchita bwino kwambiri. Tili ndi ofalitsa Ufumu 7 ndipo akuchititsa maphunziro a Baibulo 38. Anthu opitirira 25 amabwera pa nkhani ya onse ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Pa Chikumbutso [cha imfa ya Kristu] tinalipo anthu 39. Anthu ena atatu adzabatizidwa posachedwa!”

Phindu ndi Ubwino Wake

Akuluakulu a ndende aona kuti ntchito yodzifunirayi ikuthandizadi. Chomwe akuluakuluŵa akuchita nacho chidwi kwambiri ndi phindu lokhalitsa la ntchito yodzifunirayi. Lipoti lina linati: “Kwa zaka khumi chiyambireni ntchitoyi, akaidi onse amene anatulutsidwa atabatizidwa m’ndende kukhala Mboni za Yehova palibe ndi mmodzi yemwe amene wabwereranso kundende kusiyana ndi akaidi ambiri a zipembedzo zina omwe abwereranso kundende.” Wansembe wina pandende ya ku Idaho analembera kalata ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova atachita chidwi kwambiri ndi zotsatira za ntchito yawo. M’kalatayo anati: “Gulu lanu landigwira mtima kwambiri ngakhale kuti sindigwirizana nazo zikhulupiriro zanu.”

Kuthandiza anthu amene ali m’ndende kumasangalatsanso amene akugwira ntchitoyi. Wina wochita ntchito imeneyi atamaliza kuchititsa msonkhano ndi gulu la akaidi amene anaimba nyimbo ya Ufumu kwanthaŵi yawo yoyamba, analemba kuti: “Zinali zolimbikitsa kwambiri kuona amuna 28 akuimbira pamodzi kutamanda Yehova. Ndipo anaimba mokweza! Unalitu mwayi wapadera kukhala nawo limodzi pamenepo.” Winanso amene amachita ntchitoyi kundende ya ku Arizona anati: “Ndi mwayi waukulutu zedi kugwira nawo ntchito yapaderayi.”

A Mboni padziko lonse amene amachita ntchito imeneyi akugwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Iwo amatsimikizanso kuti kutsatira langizo la m’Baibulo lakuti chitirani onse chokoma kumapatsadi mpumulo.​—Miyambo 11:25.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani nyimbo 85 m’buku lakuti Imbirani Yehova Zitamando, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 8]

Venezuela

[Chithunzi patsamba 8]

Taiwan

[Chithunzi patsamba 8]

Mozambique