Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi ndi nthaŵi ziti pamene mkazi wachikristu ayenera kuvala chophimba kumutu pa zifukwa zauzimu?

“Mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake,” analemba motero mtumwi Paulo. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha mfundo yaumulungu ya umutu imene imati: “Mutu wa mkazi ndiye mwamuna.” Kupemphera kapena kulalikira mu mpingo wachikristu ndi udindo wa mwamuna. Motero, mkazi wachikristu akamagwira ntchito zokhudza kulambira zofunika kuchitidwa ndi mwamuna wake kapena mwamuna wina wobatizidwa, iye adzafunika kuvala chophimba kumutu.​—1 Akorinto 11:3-10.

Nthaŵi inanso imene mkazi wachikristu angafunike kuvala chophimba kumutu ndi pa zochitika zina za m’banja lake. Mwachitsanzo, banjalo likakhala pamodzi kuti lichite phunziro la Baibulo kapena kudya, mwamuna ndi amene ayenera kutsogolera mkazi ndi ana ake powaphunzitsa ndi kuwaimira m’pemphero kwa Mulungu. Koma ngati mwamunayo ndi wosakhulupirira, udindo umenewu ungakhale wa mkazi wakeyo. Choncho, popemphera mokweza m’malo mwake ndiponso m’malo mwa ena kapena pophunzitsa ana ake Baibulo mwamuna wake ali pomwepo, mkazi wachikristu ayenera kuvala chophimba kumutu. Ngati mwamuna wake palibe, mkaziyo safunika kuvala chophimba kumutu, popeza iyenso ali ndi udindo umene Mulungu anam’patsa wophunzitsa ana ake.​—Miyambo 1:8; 6:20.

 Nanga bwanji ngati mwana wina wamwamuna m’banjamo ndi mtumiki wa Yehova Mulungu wodzipatulira ndiponso wobatizidwa? Popeza mwanayo ali mumpingo wachikristu, ayenera kulandira malangizo kwa amuna anzake a mumpingomo. (1 Timoteo 2:12) Ngati bambo ake ali okhulupirira, iye ayenera kuphunzitsidwa ndi bambowo. Komabe, ngati bambowo palibe, mayi avale chophimba kumutu ngati akuphunzitsa Baibulo mwana wamwamuna wobatizidwayo pamodzi ndi ana ena. Zili kwa mayiyo kusankha ngati mwana wamwamuna wobatizidwayo angapereke pemphero pa phunzirolo kapena pa nthaŵi ya chakudya. Mwina angaone kuti mwanayo sanafikebe poyenerera kuwaperekera pemphero ndipo mayiyo angaganize zopereka pempherolo yekha. Ngati wasankha kupereka pemphero nthaŵi ngati imeneyi, ayenera kuvala chophimba kumutu.

Pamene akuchita nawo ntchito zina za mpingo, akazi achikristu angafunikire kuvala chophimba kumutu. Mwachitsanzo, pamsonkhano wa utumiki wa kumunda m’kati mwa mlungu, mwina pangakhale alongo achikristu okha basi, popanda mwamuna wobatizidwa. Pangakhalenso nthaŵi zina pamene palibe mwamuna aliyense wobatizidwa pamsonkhano wa mpingo. Ngati pamsonkhano wokonzedwa ndi mpingo kapena msonkhano wa utumiki wa kumunda mlongo adzafunika kuchita ntchito zimene mbale amachita, mlongoyo ayenera kuvala chophimba kumutu.

Kodi akazi achikristu ayenera kuvala chophimba kumutu akamamasulira nkhani za Baibulo m’chinenero china kapena chinenero cha manja kapena poŵerenga pagulu ndime za m’buku lothandiza kuphunzira Baibulo limene likugwiritsidwa ntchito pamsonkhano wa mpingo? Ayi. Alongo akamachita zimenezi satsogolera kapena kuphunzitsa. Mofananamo, alongo amene akuchita zitsanzo, kusimba zokumana nazo, kapena kukamba nkhani m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase safunikira kuvala chophimba kumutu.

Ngakhale kuti amuna obatizidwa ndi amene ayenera kuphunzitsa mumpingo, amuna ndi akazi omwe ali ndi udindo wolalikira ndi kuphunzitsa kunja kwa mpingo. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Choncho, ngati mkazi wachikristu akulankhula kwa akunja za Mawu a Mulungu Mboni ya Yehova yachimuna ili pomwepo, sangafunikire kuvala chophimba kumutu.

Komabe, zimenezi sizili choncho ngati akuchititsa phunziro la Baibulo la nthaŵi zonse panyumba ya munthu ndipo pali mwamuna wodzipatulira wobatizidwa. Kumeneku n’kuphunzitsa kumene amakhala atakonzeratu ndipo wochititsa phunziroyo amatsogolera ndithu. Pa zochitika ngati zimenezi, phunzirolo limakhala mbali yowonjezera ya maphunziro a mpingo. Ngati Mboni yachikazi yobatizidwa ikuchititsa phunziro loterolo Mboni yachimuna yobatizidwa ilipo, iyenera kuvala chophimba kumutu. Komabe, mbale wodzipatulirayo ayenera kupereka pemphero. Mlongo sangapemphere mbale wodzipatulira ali pomwepo pokhapokha patakhala zifukwa zina zapadera, mwachitsanzo, ngati mbaleyo ali ndi vuto loti sangathe kutulutsa mawu.

Nthaŵi zina mlongo wachikristu angatsagane ndi mwamuna wofalitsa Ufumu wosabatizidwa ku phunziro la Baibulo. Ngati mlongoyo akufuna, angapemphe mwamunayo kuchititsa phunzirolo. Koma popeza sakuyenerera kuimira mlongo wobatizidwayo m’pemphero kwa Yehova, zingakhale bwino kuti mlongoyo apemphere pa phunzirolo. Ngati akuchititsa phunzirolo ndiponso akupemphera, mlongoyo afunika kuphimba mutu wake. Ngakhale kuti mwamuna wofalitsayo sanabatizidwe, anthu akunja amamuona kuti ali mumpingowo chifukwa cha ntchito yake yolalikira.

“Mkazi ayenera kukhala nawo ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo,” analemba motero mtumwi Paulo. Inde, alongo achikristu ali ndi mwayi wapadera wokhala zitsanzo zabwino kwa angelo miyandamiyanda amene amagonjerabe Yehova mokhulupirika. Ndiyetu n’koyenera kuti akazi oopa Mulungu azikumbukira kuvala chophimba kumutu pakafunika kutero!

[Zithunzi patsamba 26]

Chophimba kumutu chimasonyeza kulemekeza umutu