Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Dzipulumutseni Nokha ndi Iwo Akumva Inu’

‘Dzipulumutseni Nokha ndi Iwo Akumva Inu’

‘Dzipulumutseni Nokha ndi Iwo Akumva Inu’

“Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. . . . Pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”​—1 TIMOTEO 4:16.

1, 2. Kodi chimasonkhezera Akristu oona kupitirizabe ntchito yawo yopulumutsa moyo n’chiyani?

M’MUDZI wina wakutali kumpoto kwa Thailand, mwamuna wina ndi mkazi wake omwe ndi Mboni za Yehova anayesa chinenero chimene anali atachiphunzira kumene polankhula ndi anthu afuko la kumapiri. Kuti akhoze kugaŵana uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi anthu a m’mudzimo, posachedwapa banjali laphunzira chinenero cha Chilahu.

2 “N’kovuta kulongosola chimwemwe ndi chikhutiro zomwe tili nazo, pogwira ntchito pakati pa anthu ochititsa chidwi ngati aŵa,” anafotokoza motero mwanunayo. “Ndithudi, tikudzimva kuti tikukhudzidwa pa kukwaniritsidwa kwa Chivumbulutso 14:6, 7, kulalika uthenga wabwino ‘kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe.’ Kuli madera oŵerengeka komwe uthenga wabwino sunafikebe, ndipo ili mwachionekere ndi limodzi la madera ameneŵa. Maphunziro a Baibulo omwe tili nawo n’ngochuluka pafupifupi kuposa amene tingathe kukwanitsa.” N’chachidziŵikire kuti aŵiriŵa n’ngofunitsitsa osati kungodzipulumutsa iwo okha koma kupulumutsanso awo akumva iwo. Monga Akristu, kodi tonsefe sitingakonde kuchita mofananamo?

“Udzipenyerere Wekha”

3. Kuti tipulumutse ena, kodi tiyenera kuchitanji choyamba?

3 Mtumwi Paulo anapereka uphungu kwa Timoteo wakuti, “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho,” ndipotu uphungu umenewu ukugwiranso ntchito lerolino kwa Akristu onse. (1 Timoteo 4:16) Indedi, kuti tithandize ena kupeza chipulumutso, n’kofunika kudzipenyerera tokha choyamba. Kodi tingachite zimenezi motani? Choyamba, tikhale atcheru ku nthaŵi yomwe tikukhala ino. Yesu anapereka chizindikiro cha zochitika zosiyanasiyana kotero kuti otsatira ake adzadziŵe kuyandikira kwa “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Komabe, Yesu ananenanso kuti sitingadziŵe nthaŵi yeniyeni pamene mapetowo adzafika. (Mateyu 24:3, 36) Kodi tiyenera kuchitanji pamenepa?

4. (a) Kodi nthaŵi yotsala ya dongosolo lino tiyenera kuiona motani? (b) Kodi tiyenera kupeŵa malingaliro ati?

4 Aliyense wa ife angafunse kuti, ‘Kodi ineyo ndikugwiritsa ntchito nthaŵi iliyonse yotsala ya dongosolo lino kudzipulumutsa ndekha ndi awo akumva ine? Kapena ndikuganiza kuti, “Popeza sitikudziŵa nthaŵi yeniyeni pamene mapetowo adzafika, ndiyeno sindiyenera kuda nazo nkhaŵa”?’ Malingaliro omalizaŵa n’ngoopsa. Akutsutsana kotheratu ndi chilimbikitso cha Yesu chakuti: “Khalani inunso okonzekeratu; chifukwa m’nthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:44) Ndithudi ino si nthaŵi yoleka kutumikira Yehova mwachangu kapena yoyang’ana kudziko kaamba ka chitetezo kapena chikhutiro.​—Luka 21:34-36.

5. Kodi mboni za Yehova zomwe zinakhalako Chikristu chisanayambe zinasonyeza zitsanzo zotani?

5 Njira inanso yomwe tingasonyezere kuti tikudzipenyerera tokha ndiyo mwa kupirira mokhulupirika monga Akristu. Atumiki a Mulungu kalelo anapirira mosalekeza, mosasamala kanthu kuti anali kuyembekezera kulanditsidwa nthaŵi yomweyo kapena ayi. Atatsiriza kutchula zitsanzo za mboni zomwe zinalipo Chikristu chisanakhaleko monga Abele, Enoke, Nowa, Abrahamu, ndi Sara Paulo anati: ‘Iwo onse sanalandira malonjezano, komatu anawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.’ Iwo sanakodwe m’msampha wa zilakolako zilizonse zofunitsa moyo wofeŵerapo, ngakhale kuloŵerera m’mikhalidwe yonyansa yowazinga, koma anayembekezera mwachidwi ‘kulandira [“kukwaniritsidwa kwa,” NW] malonjezano.’​—Ahebri 11:13; 12:1.

6. Kodi kaonedwe ka chipulumutso ka Akristu a m’zaka za zana loyamba kanakhudza motani moyo wawo?

6 Akristu a m’zaka za zana loyamba nawonso ankadziona ngati “alendo” m’dziko lino. (1 Petro 2:11) Ngakhale pambuyo pa kupulumutsidwa pa chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E., Akristu oonawo sanaleke kulalikira kapena kubwerera ku njira yamoyo wakudziko. Iwo anadziŵa kuti okhulupirika anali kuyembekezera chipulumutso chachikulu. Kwenikweni, kalelo cha m’ma 98 C.E., mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”​—1 Yohane 2:17, 28.

7. Kodi Mboni za Yehova zasonyeza motani kupirira m’nthaŵi yamakono ino?

7 M’nthaŵi zamakono zino a Mboni za Yehova apitirizabe kugwira ntchito yachikristu, ngakhale kuti azunzidwa mwankhalwe. Kodi kupirira kwawoko n’kosapindula? Ndithudi ayi, chifukwatu Yesu akutitsimikizira kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka,” kaya chimalizirocho chikhale mapeto a dongosolo lino lakale kapena mapeto a moyo wa munthu panopa. Pachiukiriro, Yehova adzaukitsa atumiki ake onse okhulupirika omwe anamwalira ndi kuwapatsa mphoto.​—Mateyu 24:13; Ahebri 6:10.

8. Kodi tingasonyeze motani kuti timayamikira kupirira kwa Akristu akale?

8 Ndiponso ndife okondwa kuti Akristu okhulupirika akalewo sanali kudera nkhaŵa za chipulumutso chawo chokha. Ndithudi ifeyo amene taphunzira za Ufumu wa Mulungu kupyolera m’khama lawo tikuthokoza kwambiri kuti anapirira pogwira ntchito imene Yesu anawapatsa. Iye anawauza kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Malinga ngati mwayi uli wotseguka kwa ife, tingasonyeze kuyamikira kwathu mwa kulalikira ena amene chikhalirecho sanamvepo uthenga wabwino. Komabe, kulalikira ndi sitepe loyamba chabe pa kupanga ophunzira.

‘Dzipenyerereni ndi Chiphunzitsocho’

9. Kodi kaonedwe kabwino ka gawo kangatithandize motani kuyambitsa maphunziro a Baibulo?

9 Ntchito yathu sikulalikira kokha komanso kuphunzitsa. Yesu anatipatsa ntchito yophunzitsa anthu kutsatira zinthu zonse zimene analamulira. N’zoona kuti m’madera ena, ndi anthu ochepa kwambiri omwe amaoneka ngati akufuna kuphunzira za Yehova. Komabe kumangoganizira zoipa zokhazokha za gawolo kungafoole khama lathu lofuna kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Yvette, yemwe akuchita upainiya m’gawo linalake lomwe ena amati n’losabala zipatso, anaona kuti alendo odzacheza kugawolo, amene analibe malingaliro alionse osasangalala ndi gawolo anali kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. Atakhala ndi kaonedwe kabwino, Yvette nayenso anapeza anthu ofunitsitsa kuphunzira Baibulo.

10. Kodi cholinga chathu chachikulu monga aphunzitsi a Baibulo n’chiyani?

10 Akristu ena angaope kuphunzira Baibulo ndi osonyeza chidwi chifukwa chakuti amadzimva kuti sangathe kuchititsa phunziro. N’zoona kuti maluso athu n’ngosiyanasiyana. Komabe sitifunikira maluso adzaoneni kuti tikhale aphunzitsi a Mawu a Mulungu. Uthenga woyera wa m’Baibulo n’ngwamphamvu kwabasi, ndipo Yesu ananena kuti onga nkhosa akamva mawu a Mbusa weniweni amawazindikira. Chotero, ife ntchito yathu ndiyo kungopereka uthenga wa Mbusa Wabwino, Yesu, momveka bwino monga momwe tingathere.​—Yohane 10:4,14.

11. Kodi mungathandize motani wophunzira Baibulo wanu mogwira mtima?

11 Kodi mungapereke bwanji uthenga wa Yesu mogwira mtima kwambiri? Choyamba, dziŵani bwino lomwe zomwe Baibulo limanena pa nkhani yomwe mudzakambirana. Muyenera kuimvetsa bwino nkhaniyo choyamba musanayambe kuphunzitsa ena. Komanso, sonyezani ulemu ndi ubwenzi nthaŵi zonse pamene mukuphunzira. Ophunzira, kuphatikizamo ana aang’ono kwambiri, amaphunzira bwino zedi ngati ali omasuka ndiponso ngati mphunzitsi wawoyo akuwasonyeza ulemu ndi chifundo.​—Miyambo 16:21.

12. Kodi mungatsimikizire motani kuti wophunzira wanu akumvetsa zomwe mukum’phunzitsa?

12 Monga mphunzitsi, simufunikira kungotchula chabe mfundo zomwe wophunzirayo angaziloŵeze pamtima. M’thandizeni kumvetsa zomwe akuphunzirazo. Maphunziro a wophunzirayo, zomwe zam’chitikira m’moyo, komanso zomwe akudziŵa ponena za Baibulo zidzakhudza kumvetsetsa kwake zomwe inu mukunena. Choncho mungadzifunse kuti, ‘Kodi akuzindikira kufunika kwa malemba otchulidwa m’nkhani yophunziridwayo?’ Mungam’chititse kulankhula momasuka pom’patsa mafunso omwe sangayankhe mwachidule kungoti inde kapena ayi koma amene angayankhe mwa kufotokoza. (Luka 9:18-20) Komabe, ophunzira ena amazengereza kufunsa mphunzitsi. Chifukwa cha chimenecho, iwo angapitirize kuphunzirako asanamvetse mokwanira zomwe akuphunzirazo. M’limbikitseni wophunzirayo kufunsa mafunso ndi kuti azinena ngati sakumvetsa bwino mfundo inayake.​—Marko 4:10; 9:32, 33.

13. Kodi wophunzira mungam’thandize motani kuti akhale mphunzitsi?

13 Cholinga chofunika kwambiri chochititsira phunziro la Baibulo ndicho kuthandiza wophunzira kuti nayenso akhale mphunzitsi. (Agalatiya 6:6) Kuti zimenezo zitheke, pendani phunziro lanulo mwa kum’pempha wophunzira wanu kuti akufotokozereni mwachidule mfundo inayake, monga momwe angachitire pofotokozera winawake yemwe akumva nkhaniyo kwa nthaŵi yoyamba. Pambuyo pake, pamene adzayeneretsedwa kutenga nawo mbali muutumiki, mungam’pemphe kudzayenda nanu m’munda. Iye mwachionekere adzakhala womasuka kutumikira nanu limodzi, ndipo zokumana nazo zidzam’thandiza kukulitsa chidaliro chake kufikira ataona kuti angakhoze kupita yekha muutumiki.

Thandizani Wophunzira Kukhala Bwenzi la Yehova

14. Monga mphunzitsi, kodi cholinga chanu chachikulu n’chotani, ndipo n’chiyani chomwe chidzathandizira kuti muchikwaniritse?

14 Cholinga chachikulu cha mphunzitsi aliyense wachikristu ndicho kuthandiza wophunzira kupanga ubwenzi ndi Yehova. Mudzakwaniritsa zimenezi osati mwa mawu anu okha komanso mwa zitsanzo zanu. Kuphunzitsa posonyeza chitsanzo kumakhudza kwambiri mitima ya ophunzira. Ndithudi zochita zingasonkhezere kwambiri kuposa mawu okha, makamaka pamene mukukhomereza mikhalidwe yabwino ndi kusonkhezera changu mwa wophunzira. Ngati aona kuti mawu anu ndi zochita zanu zikuchokera pa unasi wabwino ndi Yehova, nayenso angasonkhezereke kwambiri kukulitsa unansi woterowo.

15. (a) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti wophunzira wanu akulitse malingaliro oyenera a kutumikira Yehova? (b) Mungathandize motani wophunzira wanu kupitirizabe kupita patsogolo mwauzimu?

15 Mukufuna kuti wophunzirayo atumikire Yehova osati kokha chifukwa chakuti sakufuna kudzawonongedwa pa Armagedo koma chifukwa chakuti amam’konda. Mwa kum’thandiza kukulitsa malingaliro abwino choterowo, mudzakhala mukumanga ndi zomangira zosagwira moto zomwe zidzapirira mayesero a chikhulupiriro chake. (1 Akorinto 3:10-15) Malingaliro olakwa, monga kufunitsitsa monyanyira kuti atsanzire inuyo kapena munthu wina aliyense, sikudzam’patsa konse nyonga kuti apirire zisonkhezero zosakhala zachikristu kapena kumulimbikitsa kuchita chomwe chili chabwino. Kumbukirani, simudzakhala mphunzitsi wake mpaka kalekale. Pamene mwayi mudakali nawo, mungam’limbikitse kuyandikira kwambiri kwa Yehova mwa kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku ndi kuwalingalira. Mwa njira imeneyi adzapitiriza kutsata “chitsanzo cha mawu a moyo” kuchokera m’Baibulo ndi zofalitsa zofotokoza Baibulo patsogolo pake inuyo mutatsiriza kuphunzira naye.​—2 Timoteo 1:13.

16. Mungaphunzitse motani wophunzira kupemphera kuchokera mumtima?

16 Mungathandizenso wophunzira kuyandikira kwambiri kwa Yehova mwa kum’phunzitsa kupemphera kuchokera pansi pa mtima. Kodi mungachite motani zimenezo? Mwinamwake mungam’sonyeze pemphero la chitsanzo la Yesu, ngakhalenso mapemphero ambirimbiri ogwira mtima olembedwa m’Baibulo, monga a m’masalmo. (Salmo 17, 86, 143; Mateyu 6:9, 10) Kuwonjezera pamenepo, pamene wophunzira wanu akumvani mukupemphera potsegula ndi potseka phunziro lanu, adzazindikira malingaliro anu pa Yehova. Choncho nthaŵi zonse sonyezani kuona mtima ndi kumasuka pamene mupemphera, ndiponso kukula kwanu mwauzimu ndi mwa malingaliro.

Kugwira Ntchito Yopulumutsa Ana Anu

17. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti asachoke m’njira ya ku chipulumutso?

17 N’chachidziŵikire kuti a m’banja lathu ali m’gulu la anthu ambirimbiri omwe tikufuna kuwapulumutsa. Ana ochuluka zedi a makolo achikristu n’ngokhulupirika ndi “olimba m’chikhulupiriro.” Komabe n’kutheka kuti ena choonadi sichinazike mizu m’mitima yawo. (1 Petro 5:9; Aefeso 3:17; Akolose 2:7) Ochuluka mwa achinyamata ameneŵa amaleka kutsata njira yachikristu pamene ayandikira kapena kufika pa uchikulire. Ngati ndinu kholo, kodi mungachitenji kuti zimenezo zisadzakuchitikireni? Choyamba, mungayese mwakhama kupanga banja lanu kukhala malo abwino. Moyo wabwino wabanja umayala maziko a kaonedwe kabwino ka ulamuliro, kuzindikira makhalidwe abwino, ndi ubwenzi wosangalatsa. (Ahebri 12:9) Chifukwa cha chimenecho, mgwirizano wamphamvu m’banja ungakhale malo abwino pomwe ubwenzi wa mwana ndi Yehova ungakulire. (Salmo 22:10) Mabanja olimba amachita zinthu mogwirizana monga gulu limodzi​—ngakhale kuli kwakuti makolo angafunikire kugwiritsa ntchito nthaŵi yomwe akanatha kuigwiritsa ntchito pa zinthu zina zofunika. Mwa njira imeneyi mungapereke chitsanzo chabwino chomwe chingaphunzitse ana anu kusankha moyenerera zofunika kuchita m’moyo. Makolo, chomwe ana anu akufuna kwambiri kuchokera kwa inu, si chuma ayi, koma inuyo​—nthaŵi yanu, mphamvu zanu, ndi chikondi chanu. Kodi mukupatsa ana anu zinthu zimenezi?

18. Kodi makolo ayenera kuthandiza ana awo kuyankha mafunso amtundu wanji?

18 Makolo achikristu sayenera kungoganizira kuti mwachibadwa ana awo nawonso adzakhala Akristu. Daniel, mkulu komanso tate wa ana asanu, anati: “Makolo ayenera kuthandiza ana awo nthaŵi zonse kuchotsa zikayiko zomwe anawo mosapeŵeka amazitenga kusukulu ndi m’malo ena. Ayenera kuthandiza ana awo moleza mtima kupeza mayankho a mafunso ngati aŵa: ‘Kodi tikukhaladi m’nthaŵi ya chimaliziro? Kodi palidi chipembedzo chimodzi chokha choona? Kodi n’chifukwa chiyani winawake yemwe amaoneka ngati mnzathu wabwino wa kusukulu sali bwenzi labwino? Kodi nthaŵi zonse n’kulakwa kugonana musanakwatirane?’” Makolo, yembekezerani kuti Yehova adzadalitsa kuyesayesa kwanu, popeza kuti nayenso amadera nkhaŵa kwambiri ana anuwo.

19. N’chifukwa chiyani kuli kwabwino kwambiri kuti makolo aphunzire nawo okha ana awo?

19 Makolo ena angaganize kuti sangathe kuphunzira ndi ana awo. Komabe, simuyenera kulingalira choncho, chifukwatu palibe wina aliyense amene angalangize ana anuwo bwino lomwe kuposa inuyo. (Aefeso 6:4) Kuphunzira ndi ana anuwo kudzakuthandizani kudziŵa mwachindunji zomwe zili m’mitima ndi m’malingaliro awo. Kodi zomwe akunenazo n’zochokera pansi pa mtima kapena ndi chiphamaso chabe? Kodi akukhulupiriradi zomwe akuphunzirazo? Kodi Yehova ndi weniweni kwa iwo? Mungapeze mayankho a mafunso ameneŵa ndi enanso ofunika kwambiri pokhapokha ngati inuyo mumaphunzira nawo nokha ana anuwo.​—2 Timoteo 1:5.

20. Kodi makolo angachititse motani phunziro la banja kukhala losangalatsa ndi lopindulitsa?

20 Kodi mungachitenji kuti pamene mwayamba phunziro lanu la banja musaphonye ndondomeko yanu? Joseph, mkulu ndi tate wa mnyamata ndi msungwana, anati: “Mofanana ndi maphunziro ena onse a Baibulo, phunziro la banja liyenera kukhala losangalatsa, lomwe aliyense aziliyembekezera mwachidwi. Kuti tithe kuchita zimenezo m’banja lathu, sitiyang’ana kuchuluka kapena kuchepa kwa nthaŵi yomwe tilinayo. Tingathe kuchita phunziro lathu kwa ola limodzi, koma ngati nthaŵi zina tili ndi mphindi khumi zokha, timathabe kuphunzira. Chinthu chimodzi chimene chimapanga phunziro lathu kukhala chochitika chosangalatsa mlungu uliwonse kwa ana athu n’chakuti timapanga seŵero lachidule kuchokera mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. * Chidwi chochuluka ndi kumvetsa bwino zomwe kuchita zimenezi kumadzetsa ndizo zofunika kwambiri kuposa kuchuluka kwa ndime zomwe taphunzira.”

21. Kodi ndi liti pamene makolo angalangize ana awo?

21 Inde, kuphunzitsa ana anu sikudalira panthaŵi ya phunziro yokha ayi. (Deuteronomo 6:5-7) Mboni ya ku Thailand yomwe taitchula m’ndime zoyambirira zija inati: “Ndikukumbukira bwino lomwe pamene atate ankanditenga kupita nane ku ulaliki. Aliyense panjinga yake, tinkapita kumadera akumidzi a m’gawo la mpingo wathu. Ndithudi, chinali chitsanzo chabwino cha makolo athu ndi kutiphunzitsa kwawo m’mikhalidwe yonse zomwe zinatithandiza kuganiza zoloŵa muutumiki wanthaŵi zonse. Ndipo maphunzirowo akundithandiza kwambiri. Ndikupitirizabe kugwira ntchito kumadera akumidzi!”

22. Kodi pamene ‘mudzipenyerera nokha ndi chiphunzitsocho’ zotsatira zake zidzakhala zotani?

22 Tsiku linalake posachedwapa, panthaŵi yake yoyenera, Yesu adzadza kudzapereka chiweruzo cha Mulungu pa dongosolo lino. Chochitika chachikulu chimenecho pambuyo pake chidzangokhala mbiri chabe, koma atumiki okhulupirika a Yehova adzapitirizabe kum’tumikira ali ndi chiyembekezo cha chipulumutso chosatha. Kodi mukufuna kudzakhala m’gululo limodzi ndi ana anu ndi ophunzira Baibulo anu? Ngati ndi choncho kumbukirani: “Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.”​—1 Timoteo 4:16.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi malingaliro athu ayenera kukhala otani, pamene kuli kwakuti sitikudziŵa nthaŵi yeniyeni ya chiweruzo cha Mulungu?

• Kodi ‘tingapenyerere chiphunzitso chathu’ m’njira ziti?

• Kodi mungathandize motani wophunzira kuti akhale bwenzi la Yehova?

• N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti makolo azikhala ndi nthaŵi yokwanira yophunzitsa ana awo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Kuphunzira kumapita patsogolo pamene zonse zichitidwa mwaulemu ndi mwaubwenzi

[Chithunzi patsamba 18]

Kupanga seŵero lachidule la nkhani za m’Baibulo, monga kuweruza akazi aŵiri adama kwa Solomo, kumachititsa phunziro la banja kukhala losangalatsa