Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyimbo Zomwe Zimakondweretsa Mulungu

Nyimbo Zomwe Zimakondweretsa Mulungu

 Nyimbo Zomwe Zimakondweretsa Mulungu

Nyimbo akuti ndizo “luso lakale kwambiri komanso lachibadwa kwambiri mwa maluso onse osangalatsa.” Mofanana ndi chiyankhulo, kuimba ndiko mphatso yapadera kwambiri imene imasiyanitsa anthu ndi nyama. Nyimbo zimaloŵa mumtima. Zimatha kumveka bwino m’makutu ndi kukhala m’maganizo mwathu. Chachikulu kwambiri, nyimbo zingakondweretse Mulungu.

MONGA momwe Baibulo limasonyezera, Aisrayeli anali anthu okonda kuimba. Nyimbo zinali “luso lotchuka m’nthaŵi zakale za m’Baibulo,” limatero buku la Unger’s Bible Dictionary. Monga mbali ya moyo watsiku ndi tsiku, nyimbo za mawu komanso zoimbidwa ndi zoimbira zokhazokha zinali kuimbidwa pakulambira kwawo. Koma nthaŵi zambiri anali kuimba ndi mawu.

Mfumu Davide anasankha anthu ena pakati pa Alevi “a udindo wa nyimbo” pa chihema chokumanako, kachisi womangidwa ndi Solomo, mwana wake, asanapatulidwe. (1 Mbiri 6:31, 32) Pamene likasa la chipangano, losonyeza kuti Yehova ali pamalopo, linafika m’Yerusalemu, Davide analinganiza Alevi ena kuti ‘ayamike, nalemekeze Yehova.’ Nyimbo zawo zamawu ankaziimba “ndi zisakasa ndi azeze . . . ndi nsanje zomvekatu . . . ndi malipenga.” Amuna ameneŵa anali “otchulidwa mayina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake n’chosatha.”​—1 Mbiri 16:4-6, 41; 25:1.

Mawuwo akuti “chifundo [cha Yehova] n’chosatha” amapezeka nthaŵi zambirimbiri m’Masalmo, buku la m’Baibulo lomwe limadziŵika kwambiri pankhani za nyimbo. Mwachitsanzo, mbali yachiŵiri ya vesi lililonse la mavesi 26 a m’Salmo 136 ili ndi mawu ameneŵa. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Kufupika kwa mawuwo ndiponso kusapita kwake m’mbali kumawapangitsa kukhala osavuta kuwatchula. Aliyense amene anawamva, sanawaiwale.”

Mawu aang’ono oyambirira m’machaputala a masalmo amasonyeza kuti anagwiritsa  ntchito ziŵiya zoimbira zosiyanasiyana. Salmo 150 limatchula za lipenga, zeze, lingaka, chitoliro, ndi nsanje kuwonjezera pa zoimbira za zingwe. Komabe, kwenikweni likulimbikitsa kuimba ndi mawu. Vesi 6 likulimbikitsa kuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Haleluya [“Tamandani Ya, anthu inu,” NW].”

Popeza kuti nyimbo zimasonyeza mmene tikumvera mumtima mwathu, m’nthaŵi za m’Baibulo madandaulo ankapangitsa anthuwo kuimba nyimbo zodandaula kapena zoimba mawu amodzimodzi mobwerezabwereza. Komabe, kaimbidwe kameneka sikanali kofala pakati pa Aisrayeli. “M’nyimbo zodandaula kapena zachisoni zokha ndi mmene ankakonda kuimba mawu mobwerezabwereza ndi tchuni chimodzimodzi m’malo moimba nyimbo za tchuni chokoma kapena kuyankhula mwaluso ndi motsindika,” limatero buku lamaumboni a Baibulo la Insight on the Scriptures. *

Yesu ndi atumwi ake okhulupirika anaimbira Yehova zitamando usiku woti iye aphedwa maŵa, mosakayikira anali kuimba mawu a m’Masalmo a Hallel. (Masalmo 113-118) Zimenezi ziyenera kuti zinawalimbitsadi mtima ophunzira a Yesu kuti ayang’anizane ndi imfa ya Ambuye wawo! Komanso, ayenera kuti anakhalanso otsimikiza kwambiri mumtima kukhalabe atumiki okhulupirika a Mfumu Yaikulu m’chilengedwe chonse, Yehova, pamene anaimba mawuwo kasanu konse akuti “pakuti chifundo chake n’chosatha.”​—Salmo 118:1-4, 29.

Akristu oyambirira a ku Efeso ndi ku Kolose anaimba “masalmo ndi mayamiko” (m’mawu ena, nyimbo zotamanda Mulungu). Anawonjezaponso “nyimbo zauzimu” zomwe anaimba m’mitima mwawo. (Aefeso 5:19; Akolose 3:16) Mwa nyimbo ndi kuyankhula, iwo anagwiritsanso ntchito moyenerera pakamwa pawo popereka chitamando. Kodi si Yesu uja anati “mkamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima”?​—Mateyu 12:34.

Nyimbo Zomwe Sizikondweretsa Mulungu

Si nyimbo zonse zotchulidwa m’Baibulo zomwe zinakondweretsa Mulungu. Tiyeni titenge zomwe zinachitika pa Phiri la Sinai, pamene Mose anali kulandira Chilamulo, kuphatikizapo Malamulo Khumi. Pamene Mose anali kutsika m’phirimo, kodi anamva phokoso lotani? “Sindilo la kufuula kwa olakika,” osatinso “la kufuula kwa opasuka,” koma “la othirirana mang’ombe.” Nyimbo zimenezi zinali zogwirizana ndi kulambira fano, chinthu chimene chinam’nyansa Mulungu moti anthu pafupifupi 3,000 mwa oimbawo anaphedwa.​—Eksodo 32:18, 25-28.

Ngakhale kuti anthu amatha kupeka, kuimba, ndi kusangalala ndi mitundu yosiyanasiyana ya nyimbo, sizitanthauza kuti nyimbo zonsezo zimakondweretsa Mulungu. Chifukwa chiyani? Paulo, mtumwi wachikristu, anafotokoza kuti: “Onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Miyambo yachikunja yokhudzana ndi mphamvu za kubala, chiphunzitso chakuti moyo wa munthu siufa, ndi kutamanda Mariya monga “amayi wa Mulungu” ndizo nkhani zomwe kaŵirikaŵiri zimaimbidwa m’nyimbo. Komabe, zikhulupiriro ndi zochitika zimenezi sizilemekeza Mulungu wa choonadi, chifukwa chakuti zikusemphana ndi zimene zavumbulidwa m’Mawu ake ouziridwa, Baibulo.​—Deuteronomo 18:10-12; Ezekieli 18:4; Luka 1:35, 38.

Kusankha Bwino Nyimbo

Nyimbo zomwe zilipo n’zosaŵerengeka. Zikuto za mbale za nyimbo zimakonzedwa kuti zikope makasitomala kugula nyimbo zamitundu yonse. Koma ngati wolambira Mulungu akufuna kum’kondweretsa, iye adzakhala wosamala ndipo adzasankha mwanzeru ndi kupeŵa nyimbo za mawu kapena za ziŵiya zokhazokha zoimbidwa chifukwa cha zikhulupiriro zonyenga zachipembedzo kapena zokhudzana ndi chiwerewere ndi kulambira ziŵanda.

Albert, amene anatumikirapo monga mmishonale wachikristu mu Afirika, akuvomereza kuti analibe mpata weniweni woimba piyano kunoko. Komabe, ankamvetsera mobwerezabwereza nyimbo za pa mbale zochepa zimene anabwera nazo. Koma tsopano atabwerera kudziko lakwawo, Albert amachezera mipingo yachikristu monga woyang’anira woyendayenda. Alibe nthaŵi yochuluka yomvetsera nyimbo. “Ndimakonda kwambiri nyimbo za Beethoven,” iye akutero. “Pazaka zonsezi, ndapeza nyimbo zake zamitundumitundu.” Kumvetsera nyimbo zimenezi kumam’sangalatsa kwabasi. Zoonadi, munthu aliyense ali ndi nyimbo zake zimene amakonda, koma monga Akristu timakumbukira uphungu wa Paulo wakuti: “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena,  chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:31.

Nyimbo ndi Kudzipatulira

Kwa Susie, chinthu choyamba kuchikonda kwambiri chinali nyimbo. “Ndinayamba kuimba piyano ndili ndi zaka 6, limba ndili ndi zaka 10, ndipo pomalizira pake zeze ndili ndi zaka 12,” akufotokoza motero. Pambuyo pake Susie anakaphunziranso kuimba zeze ku Royal College of Music mu London, England. Kumeneko anaphunzira kwa zaka zinayi ndi katswiri winawake wotchuka wachisipanya woimba zeze kenako chaka chinanso ku Paris Conservatoire, kumene anapata digiri yaulemu paluso loimba komanso madipuloma paluso loimba zeze ndi kuphunzitsa kuimba piyano.

Susie anayamba kugwirizana ndi mpingo wa Mboni za Yehova ku London. Kumeneko iye anapeza kuti Mboni zimasamalana kwambiri ndiponso zimakondana. M’kupita kwa nthaŵi, chikondi chake pa Yehova chinakula, ndipo changu chake chofuna kum’tumikira chinam’pangitsa kuti afunefune njira zom’tumikirira. Zimenezi zinam’pangitsa kuti adzipatulire ndi kubatizidwa. “Kukhala ndi ntchito yoimba nyimbo ndiko moyo wodzipatulira, choncho moyo wodzipatulira sunali wachilendo kwa ine,” akutero Susie. Nthaŵi yake yoimbira magulu a anthu inayamba kuchepa pamene anayamba kuchita nawo utumiki wachikristu wolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu pomvera malangizo a Yesu.​—Mateyu 24:14; Marko 13:10.

Tsopano pamene amathera nthaŵi yochepa yoimba, kodi amamva bwanji? “Nthaŵi zina sindimva bwino kuti ndilibe nthaŵi yochuluka yopititsa patsogolo maluso anga,” akuvomereza motero, “koma ndimaimbabe ziŵiya zanga ndipo ndimasangalala. Nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Yehova. Ndimasangalala nazo kwambiri tsopano pamene ndatsogoza utumiki wake m’moyo wanga.”​—Mateyu 6:33.

Nyimbo Zomwe Zimatamanda Mulungu

Albert ndi Susie kuphatikizaponso Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni asanu ndi imodzi amatamanda Yehova Mulungu m’nyimbo nthaŵi zonse. Pamisonkhano yachikristu yochitikira pa Nyumba za Ufumu m’mayiko 234, iwo amayamba ndi kumaliza misonkhano yawo, ngati n’kotheka, mwa kuimba nyimbo kwa Yehova. Nyimbo zokoma, zoimbidwa m’matchuni osiyanasiyana, zili ndi mawu ozikidwa m’Malemba otamanda Yehova Mulungu.

Onse osonkhana amakweza mawu awo poimba mochokera mumtima kuti Yehova ndi Mulungu wosamala (Nyimbo 44). Amaimba nyimbo yotamanda Yehova (Nyimbo 190). Nyimbo zawo zimasonyeza zinthu zosangalatsa ndi maudindo a ubale wachikristu, moyo wachikristu, ndi mikhalidwe yachikristu. Zimene zimawonjezeranso kukoma kwake ndizo kusiyanasiyana kwa maimbidwe kumene Mboni za ku Asia, Australia, Ulaya, ndi ku North ndi South America zinagwiritsa ntchito popeka nyimbozo. *

“M’yimbireni Yehova nyimbo yatsopano; m’yimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. M’yimbireni Yehova, lemekezani dzina lake,” amatero mawu oyambirira a nyimbo yaikulu yoimbira mfumu yomwe inalembedwa m’tsiku la wamasalmo. “Lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwiza zake mwa mitundu yonse ya anthu.” (Salmo 96:1-3) Ndi zimene Mboni za Yehova zikuchita kwanuko, ndipo zikukuitanani kuti muimbe nazo zitamandozi. Ndinu aufulu kufika ku Nyumba zawo za Ufumu, kumene mungaphunzire mmene mungatamandire Yehova ndi nyimbo zomwe zimam’kondweretsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

^ ndime 22 Nyimbo zimenezi zili m’buku la Imbirani Yehova Zitamando, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 28]

Kuimbira Yehova zitamando