Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mawu Akuti “Mkristu” Akutaya Tanthauzo Lake?

Kodi Mawu Akuti “Mkristu” Akutaya Tanthauzo Lake?

 Kodi Mawu Akuti “Mkristu” Akutaya Tanthauzo Lake?

KODI kukhala Mkristu kumatanthauzanji? Kodi mungayankhe kuti bwanji? Anthu osankhidwa mwachisawawa m’mayiko osiyanasiyana anafunsidwa funso limenelo, ndipo nawa ena mwa mayankho awo:

“Ndiko kutsatira Yesu ndi kukhala monga iye.”

“Kumatanthauza kukhala munthu wabwino ndi kugaŵana zinthu ndi ena.”

“Kumatanthauza kulandira Yesu monga Ambuye ndi Mpulumutsi.”

“Kumatanthauza kupita ku Misa, kupemphera ndi Korona, ndi kulandira Kalistiya Woyera.”

“Sindikhulupirira kuti kupita kutchalitchi kokha n’kumene kungakukhalitse Mkristu.”

Ngakhale mabuku omasulira mawu ali ndi mpambo wautali wa matanthauzo a mawuŵa. Kwenikweni, buku lina lotero lili ndi matanthauzo khumi a mawu akuti “Mkristu,” matanthauzo monga “kukhulupirira mwa Yesu Kristu kapena kukhala m’chipembedzo chake” mpaka “munthu wofatsa kapena wakhalidwe labwino.” M’posadabwitsa kuti ambiri amavutika kulongosola tanthauzo la kukhala Mkristu.

Kufalikira kwa Mzimu Wosafuna Kutsogozedwa

Lerolino, pakati pa anthu odzitcha Akristu​—ngakhale pakati pa anthu a m’tchalitchi chimodzi​—munthu amatha kupeza maganizo ambiri osiyanasiyana pankhani monga kuuziridwa ndi Mulungu kwa Baibulo, nkhani yakuti anthu anachokera ku zinyama, kuloŵerera kwa matchalitchi m’nkhani zandale, ndi kugaŵana chikhulupiriro chako ndi ena. Nkhani zokhudza khalidwe, monga nkhani ya kuchotsa mimba, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha, ndi kukhala muukwati wosalembetsedwa, nthaŵi zambiri zimadzutsa mikangano yadzaoneni. Si china, koma kufalikira kwa mzimu wosafuna kutsogozedwa.

Mwachitsanzo, posachedwapa bungwe la tchalitchi china chachipulotesitanti linavota mochirikiza ufulu wa tchalitchi “wosankha mkulu wina watchalitchi yemwe anali wodziŵika kwambiri ndi kugonana ndi amuna anzake kuti akhale wa m’bungwe lake lolamulira,” inatero magazini ya Christian Century. Akatswiri ena a zaumulungu atchulanso ngakhale malingaliro akuti chikhulupiriro mwa Yesu n’chosafunikira kwenikweni kuti munthu apeze chipulumutso. Iwo amakhulupirira kuti Ayuda, Asilamu, ndi ena “mwina alinso ndi mwayi wofanana [ndi Akristu] woloŵa kumwamba,” inatero nyuzipepala ya The New York Times.

Tangoyerekezani ngati mungathe, kuti munthu wotsatira mfundo zakuti boma liziyendetsa malonda onse akuchirikiza mfundo zolola anthu kudziyendetsera okha malonda kapena munthu wokhulupirira mfundo za demokalase yemwe akuchirikiza ulamuliro wopondereza ena kapena munthu wotetezera malo okhala a anthu amene akuchirikiza kuwononga nkhalango. “Munthu wotero sangakhale wotsatira weniweni wa mfundo zakuti boma liziyendetsa malonda onse kapena wokhulupirira mfundo za demokalase kapena woteteza malo okhala a anthu,” mungatero​—ndipo munganenedi zoona. Komabe, pamene muona kusiyanasiyana kwa malingaliro a anthu odzitcha Akristu, mumaona zikhulupiriro zosagwirizana m’pang’ono pomwe zomwenso zimasemphana ndi zimene Woyambitsa Chikristu, Yesu Kristu, anaphunzitsa. Kodi zimenezo zimasonyezanji ponena za mtundu wawo wa Chikristu?​—1 Akorinto 1:10.

Kusintha ziphunzitso zachikristu mwaphuma kuti zigwirizane ndi malingaliro a anthu a panthaŵiyo kunayamba kale kwambiri, monga momwe tidzaonera. Kodi Mulungu ndi Yesu Kristu amamva bwanji ponena za kusintha kumeneku? Kodi matchalitchi ochirikiza ziphunzitso zosazikidwa mwa Kristu angadzitchedi kuti Akristu? Tidzakambirana mafunso ameneŵa m’nkhani yotsatira.