Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova—Iye Amene Ali Wolimba Mphamvu

Yehova—Iye Amene Ali Wolimba Mphamvu

Yehova​—Iye Amene Ali Wolimba Mphamvu

“Ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.”​—YESAYA 40:26.

1, 2. (a) Kodi tonsefe timadalira gwero liti la mphamvu yothandiza mwakuthupi? (b) Fotokozani chifukwa chimene Yehova alili Gwero lenileni la mphamvu zonse.

MPHAMVU n’chinthu chimene ambirife sitimachiganizira kwenikweni. Mwachitsanzo, sitiganizira kwambiri za mphamvu ya magetsi imene imatipatsa kuunika ndi kutentha kapena za mmene zida zamagetsi zilizonse zimene tingakhale nazo zimatifeŵetsera ntchito. Pokhapokha magetsi akathima mosayembekezereka m’pamene timazindikira kuti popanda mphamvu yamagetsiyo, mizinda ya anthu itha kuima. M’njira zina, magetsi ambiri amene timadalira amachokera kugwero la mphamvu lodalirika koposa padziko lapansi​—dzuŵa. * Kamphindi kalikonse nyumba yakuthambo yopanga mphamvu imeneyi imamwa mafuta a nyukiliya okwanira matani mamiliyoni asanu, kugwetsera padziko lapansi mphamvu yochirikiza moyo.

2 Kodi mphamvu yonseyi ya dzuŵa imachokera kuti? Kodi ndani anamanga nyumba yakuthambo imeneyi yopanga mphamvu? Ndi Yehova Mulungu. Ponena za iye, Salmo 74:16 limati: “Munakonza kuunika ndi dzuŵa.” Inde, Yehova ndiye Gwero lenileni la mphamvu zonse, monga momwenso ndiye Chitsime cha moyo wamtundu uliwonse. (Salmo 36:9) Sitiyenera kuona mphamvu yake mopepuka. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova akutikumbutsa kuti tiyang’ane ku zinthu zakumwamba, monga dzuŵa ndi nyenyezi, ndi kusinkhasinkha mmene zinakhalirako. “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.”​—Yesaya 40:26; Yeremiya 32:17.

3. Kodi timapindula motani ndi zitsanzo za mphamvu ya Yehova?

3 Popeza kuti Yehova ndi wamphamvu zolimba, tingakhale ndi chidaliro chakuti dzuŵa lidzapitirizabe kutipatsa kuunika ndi kutentha kumene moyo wathu umadalira. Komabe, timadalira mphamvu ya Mulungu kuti tipeze zinthu zinanso zoposa zofunika zathu zakuthupi. Kuomboledwa kwathu ku uchimo ndi imfa, chiyembekezo chathu cham’tsogolo, ndi kukhulupirira kwathu Yehova zonse n’zolukanalukana ndi kusonyeza kwake mphamvu. (Salmo 28:6-9; Yesaya 50:2) Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri zosonyeza umboni wakuti Yehova ali ndi mphamvu yolenga ndi kuwombola, kupulumutsa anthu ake ndi kuwononga adani ake.

Mphamvu ya Mulungu Imaonekera M’chilengedwe

4. (a) Kodi Davide anakhudzidwa motani poyang’ana thambo usiku? (b) Kodi zinthu zakuthambo zimavumbulanji ponena za mphamvu ya Mulungu?

4 Mtumwi Paulo analongosola kuti ‘mphamvu yosatha [ya Mlengi wathu] ingaonekere bwino lomwe m’zinthu zimene analenga.’ (Aroma 1:20) Zaka mazana angapo mawu ameneŵa asanalembedwe, wamasalmo Davide, amene pokhala mbusa wa ziŵeto ayenera kuti nthaŵi zambiri ankayang’ana kumwamba usiku, anazindikira ulemerero wa thambo ndi mphamvu ya Wolipanga wake. Iye analemba kuti: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?” (Salmo 8:3, 4) Ngakhale kuti sanali kudziŵa zambiri ponena za zinthu zakumwamba zimenezo, Davide anaona kuti sanali kanthu podziyerekeza ndi Mlengi wa thambo lathu lalikululi. Lerolino, akatswiri a zakuthambo akudziŵa zinthu zambirimbiri ponena za ukulu wa thambo ndi mphamvu imene imalichirikiza. Mwachitsanzo, amatiuza kuti pakamphindi kalikonse dzuŵa lathu limatulutsa mphamvu yofanana ndi kuphulika kwa bomba lokhala ndi wonga wotchedwa TNT wokwanira mamegatoni 100,000 miliyoni. * Kachigawo kochepa kokha ka mphamvu imeneyi ndiko kamafika padziko lapansi, komabe n’kokwanira kuchirikiza zamoyo zonse padziko lathuli. Ngakhale zili motero, dzuŵa lathuli sindiyo nyenyezi ya mphamvu koposa kumwambaku. Nyenyezi zina, pakamphindi kamodzi kokha, zimatulutsa mphamvu imene dzuŵa limatulutsa patsiku lonse lathunthu. Chotero tangolingalirani za mphamvu imene Mlengi wa zinthu zakumwamba zimenezi ali nayo! Elihu analondoladi ponena motsindika kuti: “Kunena za Wamphamvuyonse, sitingam’santhule; ndiye wamphamvu yoposa.”​—Yobu 37:23.

5. Kodi tikupeza umboni wotani wa mphamvu za Yehova m’ntchito zake?

5 Ngati ‘tifunafuna ntchito za Mulungu’ monga anachitira Davide, tidzaona umboni wa mphamvu yake kulikonse. Tidzauona m’mphepo yokuntha ndi mafunde, m’mabingu ndi ziphaliŵali, m’mitsinje yamphamvu ndi mapiri okongola. (Salmo 111:2; Yobu 26:12-14) Komanso, monga momwe Yehova anakumbutsira Yobu, nyama zimasonyeza umboni wa mphamvu Yake. Pakati pa nyama zimenezi pali mvuwu. Yehova anauza Yobu kuti: “Mphamvu yake ili m’chuuno mwake . . . Ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu.” (Yobu 40:15-18) Mphamvu yoopsa ya njati inkadziŵikanso bwino lomwe m’nthaŵi za Baibulo, ndipo Davide anapemphera kuti apulumutsidwe ‘m’kamwa mwa mkango ndi pa nyanga za njati.’​—Salmo 22:21; Yobu 39:9-11.

6. Kodi ng’ombe imaphiphiritsa chiyani m’Malemba, ndipo n’chifukwa chiyani? (Onani mawu a m’munsi.)

6 Chifukwa cha mphamvu yake, njati, kapena ng’ombe, imagwiritsidwa ntchito m’Baibulo pophiphiritsa mphamvu ya Yehova. * Masomphenya a mtumwi Yohane a mpando wachifumu wa Yehova amasonyeza zamoyo zinayi, ndipo chimodzi mwa zamoyozo chinali ndi nkhope ngati yang’ombe. (Chivumbulutso 4:6, 7) Umboni ukusonyeza kuti umodzi mwa mikhalidwe yaikulu ya Yehova yosonyezedwa ndi akerubi ameneŵa ndiwo mphamvu. Inayo ndiyo chikondi, nzeru, ndi chilungamo. Popeza kuti mphamvu ndi mbali yaikulu chonchi ya umunthu wa Mulungu, kudziŵa bwino ponena za mphamvu yake ndi mmene amaigwiritsira ntchito kudzatiyandikizitsa kwa iye ndi kutithandiza kutsanzira chitsanzo chake mwa kugwiritsa ntchito bwino mphamvu iliyonse imene tingakhale nayo.​—Aefeso 5:1.

“Yehova wa Makamu Wamphamvu”

7. Kodi tingakhale otsimikizira motani kuti zabwino zidzapambana zoipa?

7 M’Malemba, Yehova amatchedwa kuti “Mulungu Wamphamvuyonse,” dzina limene limatikumbutsa kuti sitiyenera konse kuona mphamvu yake mopepuka kapena kukayikira zoti angafafanize adani ake. (Genesis 17:1; Eksodo 6:3) Dongosolo la Satana la zinthu lingaoneke ngati kuti n’lokhazikika kwambiri, koma m’maso mwa Yehova “amitundu akunga dontho la m’mtsuko, naŵerengedwa ngati fumbi losalala la m’muyeso.” (Yesaya 40:15) Chifukwa cha mphamvu ya Mulungu imeneyi, sitingakayikire kuti zabwino zidzapambana zoipa. Panthaŵi imene kuipa kuli paliponse, tingapeze chitonthozo podziŵa kuti “Yehova wa makamu wamphamvu wa Israyeli” adzachotsapo zoipa kosatha.​—Yesaya 1:24; Salmo 37:9, 10.

8. Kodi Yehova ali ndi magulu ankhondo akumwamba ati, ndipo tili ndi chisonyezero chotani cha mphamvu zawo?

8 Mawu akuti “Yehova wa makamu,” amene amapezeka nthaŵi 285 m’Baibulo, n’chikumbutso chinanso cha mphamvu ya Mulungu. “Makamu” amene akutanthauzidwa pano ndiwo zolengedwa zauzimu zimene Yehova amazigwiritsa ntchito. (Salmo 103:20, 21; 148:2) Usiku umodzi wokha, mngelo mmodzi yekha mwa angelowo anapha asilikali a ku Asuri okwanira 185,000 amene ankafuna kuukira Yerusalemu. (2 Mafumu 19:35) Ngati tikuzindikira mphamvu ya makamu ankhondo akumwamba a Yehova, sitidzaopsezedwa wambawamba ndi otsutsa. Mneneri Elisa sanachite mantha pamene anazingidwa ndi gulu lonse lankhondo lomwe linkam’funafuna, chifukwa chakuti, mosiyana ndi mnyamata wake, iye ankaona ndi maso achikhulupiriro chikhamu chachikulu koposa cha ankhondo akumwamba omwe anali kumbali yake.​—2 Mafumu 6:15-17.

9. N’chifukwa chiyani, monga Yesu, tiyenera kudalira chitetezo cha Mulungu?

9 Yesu nayenso anali kudziŵa kuti angelo akanatha kum’chirikiza pamene anayang’anizana ndi khamu la anthu okhala ndi malupanga ndi zibonga m’munda wa Getsemane. Atauza Petro kuti abweze lupanga lake m’chimake, Yesu anamuuza kuti, zitakhala kuti n’zofunika, Iye atha kupempha Atate wake kuti am’tumizire “mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri.” (Mateyu 26:47, 52, 53) Ngati timazindikiranso zomwezo ponena za makamu a angelo amene Mulungu ali nawo, tidzadaliranso chichirikizo cha Mulungu ndi mtima wonse. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?”​—Aroma 8:31.

10. Kodi Yehova amasonyeza mphamvu yake m’malo mwa ndani?

10 Chotero tili ndi zifukwa zabwino zodalira chitetezo cha Yehova. Nthaŵi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu yake kuti achite zabwino komanso mogwirizana ndi mikhalidwe yake inanso​—chilungamo, nzeru, ndi chikondi. (Yobu 37:23; Yeremiya 10:12) Pamene nthaŵi zambiri anthu amphamvu amapondereza osauka ndi apansi kuti apeze phindu mwanjira yadyera, Yehova ‘amautsa wosauka kum’chotsa kufumbi,’ ndipo iye ‘ndi wamphamvu ya kupulumutsa.’ (Salmo 113:5-7; Yesaya 63:1) Monga momwenso Mariya anaonera, amayi wodzichepetsa ndi wosadzikudzayo wa Yesu “Wamphamvuyo,” amasonyeza mphamvu yake mopanda dyera m’malo mwa amene amamuopa, kutsitsa odzitama ndi kukweza aumphaŵi.​—Luka 1:46-53.

Yehova Asonyeza Mphamvu Yake kwa Atumiki Ake

11. Kodi Aisrayeli anaona umboni wotani wosonyeza mphamvu za Mulungu m’chaka cha 1513 B.C.E.?

11 Nthaŵi zambiri, Yehova anasonyeza nyonga yake kwa atumiki ake. Imodzi mwa nthaŵi zimenezi inali pa Phiri la Sinai mu 1513 B.C.E. M’chaka chimenecho Aisrayeli anali ataona kale umboni wochititsa chidwi wa mphamvu za Mulungu. Miliri khumi yowononga inavumbula dzanja lamphamvu la Yehova ndi kupanda pake kwa milungu ya Aigupto. Pasanapitenso nthaŵi yaitali, kudutsa Nyanja Yofiira mozizwitsa ndi kuwonongedwa kwa gulu lankhondo la Farao kunaperekanso umboni wina wa nyonga za Mulungu. Miyezi itatu pambuyo pake, m’munsi mwa Phiri la Sinai, Yehova anauza Aisrayeli kuti akhale “chuma [chake] chapadera koposa mitundu yonse ya anthu.” Ndiyeno Aisrayeliwo analonjeza kuti: “Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita.” (Eksodo 19:5, 8) Ndiyeno, Yehova anawasonyeza chitsanzo chosaiŵalika cha mphamvu yake. Pakati pa mabingu ndi ziphaliŵali ndi kulira kwa lipenga kogonthetsa m’khutu, Phiri la Sinai linafuka utsi ndipo linagwedezeka. Anthu, omwe anaima cha apo, anagwidwa ndi mantha. Koma Mose anawauza kuti chochitika chimenechi chiyenera kuwaphunzitsa mantha aumulungu, mantha amene adzawasonkhezera kumvera Mulungu wawo yekhayo wamphamvuyonse ndi woona, Yehova.​—Eksodo 19:16-19; 20:18-20.

12, 13. Ndi zochitika zotani zimene zinapangitsa Eliya kusiya ntchito yake, koma kodi Yehova anam’limbitsa motani?

12 Zaka mazana ambiri pambuyo pake, m’nthaŵi ya Eliya, Phiri la Sinai linaonanso chisonyezero china cha mphamvu za Mulungu. Mneneriyo anali ataona kale zochita za mphamvu ya Mulungu. Kwa zaka zitatu ndi theka, Mulungu ‘anatseka kumwamba’ chifukwa cha mpatuko wa mtundu wa Israyeli. (2 Mbiri 7:13) M’nthaŵi ya chilala yotsatirayo, makungubwi anadyetsa Eliya kumtsinje wa Keriti, ndiyeno kenako ufa ndi mafuta zochepazo za mkazi wamasiye zinawonjezedwa mozizwitsa kuti Eliyayo apeze nawo chakudya. Yehova anam’patsanso mphamvu Eliya kuti aukitse mwana wamwamuna wa mkazi wamasiyeyo. Pomalizira pake, pamayeso ochititsa nthumanzi ofuna kusonyeza kuti Mulungu weniweni ndani pa Phiri la Karimeli, moto unatuluka kumwamba ndi kupsereza nsembe ya Eliya. (1 Mafumu 17:4-24; 18:36-40) Koma ngakhale zinatero, mwamsanga pambuyo pake, Eliya anagwidwa ndi mantha ndipo analefuka pamene Yezebeli anamuwopseza kuti adzamupha. (1 Mafumu 19:1-4) Anathaŵa m’dzikolo, ndi kumaganiza kuti ntchito yake monga mneneri yatha tsopano. Kuti am’tsimikizire ndi kum’limbitsa, Yehova mokoma mtima anam’sonyeza chitsanzo cha mphamvu yaumulungu.

13 Eliya ali chibisalire m’phanga, anaona chitsanzo cha zitatu mwa mphamvu zimene Yehova amagwiritsa ntchito: mphepo yamphamvu, chivomezi, ndipo pomalizira pake moto. Komabe, pamene Yehova anayankhula ndi Eliya, anam’yankhula ndi “mawu ofeŵa ndiponso am’munsi.” Anam’patsa ntchito yowonjezereka yoti akaichite namuuza kuti m’dzikomo munali mudakali olambira Yehova okhulupirika 7,000. (1 Mafumu 19:9-18, NW) Ngati, monga Eliya, tilefuka poona kuti utumiki wathu sukubala zipatso, tingapemphe Yehova kuti atigaŵire “ukulu woposa wamphamvu”​—mphamvu imene ingatilimbitse kuti tipitirizebe kulalikira uthenga wabwino mosaleka.​—2 Akorinto 4:7.

Mphamvu za Yehova Zimatitsimikizira Kuti Adzakwaniritsa Malonjezo Ake

14. Kodi dzina lake la Yehova limavumbula chiyani, ndipo mphamvu zake zikugwirizana motani ndi dzina lake?

14 Mphamvu za Yehova n’zogwirizananso kwambiri ndi dzina lake ndi kuchita chifuniro chake. Dzina lapaderalo lakuti Yehova, limene limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhalako,” limavumbula mfundo yakuti iye amadzipangitsa kukhala Wokwaniritsa malonjezo. Palibe chinthu kapena munthu amene angatsekereze Mulungu kuti asakwaniritse zifuno zake, mosasamala kanthu kuti anthu ongokayikira zilizonse akuzikayikira motani zifuno zakezo. Monga momwe Yesu anauzira atumwi ake panthaŵi inayake, “zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.”​—Mateyu 19:26.

15. Kodi Abrahamu ndi Sara anakumbutsidwa motani kuti palibe chimene chingam’lake Yehova?

15 Mwachitsanzo, panthaŵi inayake Yehova analonjeza Abrahamu ndi Sara kuti mbadwa zawo adzazipanga kukhala mtundu waukulu. Komabe, iwo anakhalabe opanda mwana kwa zaka zambiri. Onse aŵiri anali okalamba kwambiri pamene Yehova anawauza kuti lonjezolo linali pafupi kukwaniritsidwa ndipo Sara anaseka. Poyankha, mngelo anati: “Kodi chilipo chinthu chom’laka Yehova?” (Genesis 12:1-3; 17:4-8; 18:10-14) Patapita zaka mazana anayi, Mose atasonkhanitsa mbadwa za Abrahamuzo, zomwe tsopano zinali mtundu waukulu, m’Zigwa za Moabu, iye anawakumbutsa kuti Mulungu anali atakwaniritsa lonjezo lake. Mose anati: “Popeza [Yehova] anakonda makolo anu, anasankha mbewu zawo zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, m’Aigupto; kupitikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukuloŵetsani ndi kukupatsani dziko lawo likhale choloŵa chanu, monga lerolino.”​—Deuteronomo 4:37, 38.

16. N’chifukwa chiyani Asaduki analoŵa m’cholakwa cha kukana chiukiriro?

16 Patapita zaka mazana ambiri, Yesu anadzudzula Asaduki, amene sanali kukhulupirira chiukiriro. N’chifukwa chiyani iwo anakana kukhulupirira lonjezo la Mulungu lakuti adzaukitsa akufa? Yesu anawauza kuti: “[Simu]dziŵa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.” (Mateyu 22:29) Malemba amatitsimikizira kuti ‘onse ali m’manda adzamva mawu a Mwana wa munthu, nadzatulukira.’ (Yohane 5:27-29) Ngati tikudziŵa zimene Baibulo limanena pankhani ya chiukiriro, kudalira kwathu mphamvu ya Mulungu kudzatitsimikizira kuti akufa adzaukitsidwa. Mulungu ‘adzameza imfa ku nthaŵi yonse; chifukwa Yehova wanena.’​—Yesaya 25:8.

17. Kodi ndi patsiku liti la m’tsogolo pamene kukhulupirira Yehova kudzakhala kofunika m’njira yapadera?

17 Patsogolopa, nthaŵi idzafika pamene aliyense wa ife adzafunikira kukhulupirira mphamvu yopulumutsa ya Mulungu m’njira yapadera. Satana Mdyerekezi adzaukira anthu a Mulungu, amene adzaoneke ngati osatetezeka. (Ezekieli 38:14-16) Kenako Mulungu adzasonyeza mphamvu yake yaikulu m’malo mwathu, ndipo aliyense adzayenera kudziŵa kuti iye ndi Yehova. (Ezekieli 38:21-23) Inoyi ndiyotu nthaŵi yokulitsa chikhulupiriro ndi chidaliro chathu mwa Mulungu wamphamvu yonse kuti tisadzagwedezeke panthaŵi yovuta ngati imeneyo.

18. (a) Kodi timapeza mapindu otani posinkhasinkha za mphamvu ya Yehova? (b) Ndi funso liti limene lidzayankhidwa m’nkhani yotsatira?

18 Mosakayikira, pali zifukwa zambiri zosinkhasinkhira ponena za mphamvu ya Yehova. Pamene tikuganizira za zochita zake, modzichepetsa timasonkhezereka kutamanda Mlengi wathu Wamkulu ndi kum’thokoza kuti amagwiritsa ntchito mphamvu yake m’njira yanzeru ndi yachikondi imeneyo. Sitidzaopa kanthu ngati timakhulupirira Yehova wa makamu. Chikhulupiriro chathu pa malonjezo ake sichidzakhala chogwedera. Komano, kumbukirani kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu. Chotero, ifeyonso tili ndi mphamvu, ngakhale kuti zili ndi malire ake. Kodi tingatsanzire motani Mlengi wathu mwa njira yomwe timasonyezera mphamvu yathu? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Ambiri amakhulupirira kuti mafuta okumba pansi osiyanasiyana kuphatikizapo malasha, amene ali magwero aakulu a mphamvu m’nyumba zopangira magetsi, amapeza mphamvu yawo kudzuŵa.

^ ndime 4 Mosiyana ndi zimenezo, bomba la nyukiliya lamphamvu koposa limene linayesedwapo linali ndi mphamvu ya wonga wa TNT wokwanira mamegatoni 57.

^ ndime 6 Njati yotchulidwa m’Baibuloyo iyenera kuti inali nyama yotchedwa aurochs (Chilatini urus). Zaka zikwi ziŵiri kalelo, nyama zimenezi zinkapezeka ku Gaul (kumene tsopano ndi ku France), ndipo Julius Caesar analemba mafotokozedwe a nyamazi akuti: “Nyama za urus zimenezi sizisiyana ndi njovu ukulu wake, koma khalidwe lake, maonekedwe, ndi thupi lake, ndi ng’ombe zenizeni. N’zamphamvu zedi, komanso zaliŵiro labasi: zikaona munthu kapena nyama ina zimangofuna zitapha basi.”

Kodi Mungayankhe Mafunsoŵa?

Kodi chilengedwe chimasonyeza motani umboni wa mphamvu za Yehova?

Kodi ndi makamu ati amene Yehova angawagwiritse ntchito pothandiza anthu ake?

Ndi pazochitika zina ziti pamene Yehova anasonyeza mphamvu yake?

Kodi tili ndi chitsimikizo chotani chakuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

“Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo”

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chinajambulidwa ndi Malin, © IAC/​RGO 1991

[Zithunzi patsamba 13]

Kusinkhasinkha pa zochitika zosonyeza mphamvu ya Yehova kumalimbikitsa kukhulupirira malonjezo ake