Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuyamikira

Kuyamikira

Tonsefe tiyenera kukhala ndi mtima woyamikira chifukwa pali maumboni ambiri osonyeza kuti kuyamikira kumathandiza munthu kuti azikhala wosangalala komanso wathanzi.

Kodi kuyamikira kungakuthandizeni bwanji?

ZIMENE MADOKOTALA AMANENA

Nkhani ya m’magazini ina inati: “Kuyamikira kumathandiza munthu kukhala wosangalala. Zili choncho chifukwa chakuti kumathandiza munthu kuganizira zinthu zolimbikitsa, kukumbukira zinthu zabwino zimene zamuchitikira, kukhala wathanzi, kupirira mavuto ndiponso kugwirizana ndi anthu ena.”—Harvard Mental Health Letter.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizikhala ndi mtima woyamikira. Mtumwi Paulo anali chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndipo analemba kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” Iye ‘ankayamikadi Mulungu mosalekeza’ chifukwa choti anthu ankamvetsera mwachidwi uthenga wake wabwino. (Akolose 3:15; 1 Atesalonika 2:13) Koma sikuti munthu amangokhala wosangalala chifukwa choti nthawi zina amanena kuti ‘zikomo’ koma chifukwa chokhala ndi mtima woyamikira. Mtima umenewu ungatithandize kupewa makhalidwe amene angachititse kuti tisamasangalale komanso kuti anthu asamatikonde monga kudzimva, nsanje, ndiponso kusunga chakukhosi.

Mlengi wathu ndi chitsanzo chabwino kwambiri poyamikira ena. Iye amayamikira anthufe ngakhale kuti ndife osanunkha kanthu poyerekezera ndi iyeyo. Lemba la Aheberi 6:10 limanena kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” Zimenezi zikusonyeza kuti iye amaona kuti kusayamikira ena n’kupanda chilungamo.

“Muzikhala okondwera nthawi zonse. Muziyamika pa chilichonse.”1 Atesalonika 5:16, 18.

Kodi kuyamikira kumathandiza bwanji kuti tizigwirizana ndi ena?

ZIMENE ZIMACHITIKA

Tikamayamikira mochokera pansi pa mtima mphatso, mawu olimbikitsa kapena zabwino zimene munthu watichitira, timathandiza munthuyo kuti azimva kuti ndi wofunika. Nawonso anthu amene sitikuwadziwa amasangalala tikawathokoza chifukwa chotichitira zinthu zabwino, ngakhale zinthu zing’onozing’ono.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Yesu Khristu ananena kuti: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulira m’matumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira.” (Luka 6:38) Mtsikana wina dzina lake Rose ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye amakhala pachilumba cha Vanuatu kum’mwera kwa nyanja ya Pacific ndipo ali ndi vuto losamva.

Rose ankapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova koma sankapindula kwenikweni chifukwa iyeyo komanso anthu amumpingowo sankadziwa chinenero chamanja. Koma kenako banja lina limene linkadziwa chinenero chamanja linabwera mumpingowo. Iwo ataona kuti Rose ali ndi vuto losamva anakonza zoti ayambe kuphunzitsa anthu chinenero chamanja. Rose anayamikira kwambiri ndipo anati: “Ndikusangalala kuti ndili anzanga ambiri amene amandikonda.” Banja limene linathandiza Rose limasangalala kwambiri kuona kuti iye akuyamikira zimene linamuchitira ndiponso kuti panopa amatha kuyankha pamisonkhano. Rose amayamikiranso zimene anthu ena anachita pophunzira chinenero chamanja n’cholinga choti azitha kulankhula naye.—Machitidwe 20:35.

“Amene akupereka nsembe yoyamikira kwa [Mulungu] ndi amene [amamulemekeza].”Salimo 50:23.

N’chiyani chingatithandize kukhala oyamikira?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuganizira kwambiri zimene ena atichitira kumathandiza kuti tizikhala oyamikira. Davide anauza Mulungu m’pemphero kuti: “Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse, ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.” (Salimo 143:5) Lembali likusonyeza kuti Davide ankaganizira kwambiri za Mulungu komanso zomwe zinkamuchitikira. Kuganizira zochita za Mulungu nthawi zonse kunamuthandiza kuti akhale ndi mtima woyamikira.—Salimo 71:5, 17.

Baibulo limatipatsa malangizo othandiza kwambiri akuti: ‘Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.’ (Afilipi 4:8) Mawu akuti “pitirizani kuganizira” akusonyeza kuti nthawi zonse tiyenera kumaganizira zinthu zimene zatichitikira pa moyo wathu ndipo zimenezi zingatithandize kukhala ndi mtima woyamikira.

“Zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zinthu zakuya.”Salimo 49:3.