Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ndi Mtima Woyamikira

Khalani ndi Mtima Woyamikira

Mfundo Yachitatu

Khalani ndi Mtima Woyamikira

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: “Muziyamika pa chilichonse.”​—1 Atesalonika 5:18.

N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMENEZI ZIMAKHALA ZOVUTA? M’dzikoli, tikukhala ndi anthu odzikuza ndiponso osayamika, choncho nafenso tikhoza kuyamba kutengera makhalidwe amenewa. (2 Timoteyo 3:1, 2) Kuonjezera pamenepa, tingakakamizike kudziunjikira zochita zambirimbiri ngakhale kuti ndife otanganidwa kale ndi zinthu zina. Zimenezi zingachititse kuti tizipanikizika kwambiri ndi mavuto ndiponso kutanganidwa ndi kufunafuna zinthu zongotisangalatsa. Zimenezi zingatilepheretse kuyamikira pa zimene tili nazo kale kapenanso kuthokoza pa zinthu zabwino zimene ena atichitira.

ZIMENE MUNGACHITE: Muzipeza nthawi yoganizira zinthu zabwino zimene muli nazo panopa. N’kutheka kuti mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana, koma taganizirani zimene zinachitikira Mfumu Davide. Nthawi zingapo iye anakumana ndi mavuto ndiponso mayesero aakulu. Komabe iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse, ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.” (Salimo 143:3-5) Ngakhale kuti Davide anakumana ndi mayesero, iye sanasiye kukhala ndi mtima woyamikira ndipo ankakhutitsidwa ndi zimene anali nazo.

Ganizirani zinthu zimene anthu ena akuchitirani ndipo athokozeni. Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Mariya yemwe anali mnzake anamuthira mafuta onunkhira ndiponso amtengo wapatali, pamutu komanso m’miyendo mwake. Koma ena ataona zimenezi anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani akuwononga chonchi mafuta onunkhirawa?” * Anthu otsutsa amenewa ankaona kuti zikanakhala bwino mafuta amenewo akanagulitsidwa, ndalama zake n’kupatsa osauka. Koma Yesu anawayankha kuti: “Mulekeni. N’chifukwa chiyani mukum’vutitsa mayiyu?” Kenako Yesu anawonjezera kuti: “Mayiyu wachita zimene angathe.” (Maliko 14:3-8; Yohane 12:3) Pamenepa, Yesu anaganizira zimene Mariya anachita, osati zimene sanachite.

Anthu ena amadzazindikira kuti anthu a m’banja mwawo kapena anzawo anali ofunika kwambiri anthuwo akachoka kapena akamwalira. Komanso zinthu zina zikatha kapena kutayika, ndi pamene anthu ena amadzazindikira kuti zinali zofunika. Kuti zimenezi zisakuchitikireni, muyenera kumayamikira pa zabwino zimene muli nazo. Ndipo mungachite bwino kuganizira kapena kulemba zinthu zimene mumayamikira kwambiri.

Popeza kuti “mphatso iliyonse yabwino” imachokera kwa Mulungu, tingachite bwino kumuthokoza m’pemphero. (Yakobo 1:17) Kuchita zimenezi nthawi zonse kungatithandize kukhala ndi mtima woyamikira ndiponso kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo.​—Afilipi 4:6, 7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 M’nthawi ya Yesu, kuthira mlendo mafuta pamutu kunkasonyeza kuti mlendoyo walandiridwa. Pamene kuthira mafuta mapazi ake kunkasonyeza kuti wothirayo ndi wodzichepetsa.

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi mumayamikira anthu ena akakuchitirani zabwino?