Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonyeza Kuti Timayamikira?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonyeza Kuti Timayamikira?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonyeza Kuti Timayamikira?

“Wokondedwa Raquel,

Zikomo kwambiri pondilimbikitsa. N’kutheka kuti iweyo sukudziwa, koma ndikufuna ndikuuze kuti khalidwe lako komanso zimene umanena zimandilimbikitsa kwambiri.”​—Analemba motero Jennifer.

KODI nthawi inayake munayamba mwalandirapo kalata yokuthokozani? Ngati munalandirapo kalata yotere n’zosakayikitsa kuti munamva bwino kwambiri. Palibe amene safuna kuona kuti ndi wofunika ndiponso kuti anthu amayamikira zimene amachita.​—Mateyo 25:19-23.

Nthawi zambiri mawu oyamikira amathandiza kuti woyamikira ndi woyamikiridwayo ayambe kugwirizana kwambiri. Komanso munthu akasonyeza kuti akuyamikira ndiye kuti akutsanzira Yesu Khristu, amene nthawi zonse ankaona zabwino zimene anthu ankachita.​—Maliko 14:3-9; Luka 21:1-4.

N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri ayamba kusiya kusonyeza mtima woyamikira, kaya mwamawu kapena polemba kalata. Baibulo linachenjeza kuti “m’masiku otsiriza” anthu adzakhala “osayamika.” (2 Timoteyo 3:1, 2) Tikapanda kusamala, tingathe kutengera mtima wosayamika umene anthu ambiri ali nawo masiku ano.

Kodi ndi zinthu zotani zimene makolo angachite kuti aphunzitse ana awo kukhala anthu oyamikira? Kodi ndani amene tiyenera kuwayamikira? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kuyamikira ngakhale kuti anthu ena satero?

M’banja

Makolo amayesetsa kupezera ana awo zinthu zofunikira pa moyo wawo. Koma nthawi zina makolowo angaone kuti ana awo sayamikira zimenezi. Kodi vutoli angalithetse bwanji? Pali zinthu zitatu zofunikira.

(1) Perekani chitsanzo. Pankhani imeneyi, monganso pankhani zambiri zokhudza kuphunzitsa ana, chitsanzo chanu n’chothandiza kwambiri. Pofotokoza za mayi wakhama wa ku Isiraeli, Baibulo limati: “Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala.” Kodi anawo amaphunzira kuti mtima woyamikirawo? Mbali yomalizira ya vesili ingatithandize kupeza yankho chifukwa imati: “Mwamuna wake nam’tama.” (Miyambo 31:28) Choncho makolo amene amayamikirana, amathandiza ana awo kuona kuti kuyamikira ena n’kwabwino chifukwa woyamikiridwayo amasangalala ndiponso zimathandiza kuti anthu m’banja azigwirizana. Amadziwanso kuti kuyamikira ndi umboni wakuti munthu woyamikirayo ndi wozindikira.

Bambo wina dzina lake Stephen, yemwe anali ndi ana aakazi awiri, anati: “Ndimayesetsa kupereka chitsanzo kwa ana anga mwa kuyamikira mkazi wanga akaphika chakudya.” Kodi zotsatira zake n’zotani? Stephen anapitiriza kuti: “Anawa atengera chitsanzo changa ndipo amaona kufunika koyamikira ena.” Ngati muli pabanja kodi mumayesetsa kuyamikira mwamuna kapena mkazi wanu pa ntchito zapakhomo? Ambiritu sayamikira. Nanga kodi mumayamikira ana anu pa zinthu zimene achita ngakhale kuti ndi udindo wawo kuchita zimenezo?

(2) Aphunzitseni. Mtima woyamikira uli ngati maluwa. Kuti maluwa akule amafunika kuwasamalira bwino. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale ndi mtima woyamikira? Mfumu yanzeru Solomo inatchulapo chinthu chimodzi chofunika kwambiri, ponena kuti: “Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe.”​—Miyambo 15:28.

Ngati ndinu kholo, kodi mumaphunzitsa ana anu kuti akalandira mphatso inayake aziganizira kuti munthu amene wawapatsa mphatsoyo anavutikira kuti aipeze ndiponso kuti ndi wowolowa manja? Maganizo amenewa ali ngati nthaka yabwino imene imathandiza mwanayo kukulitsa mtima woyamikira. Maria ndi mayi wa ana atatu ndipo anati: “Pamafunika nthawi ndithu kuti ufatse ndi ana ako n’kuwafotokozera zinthu zokhudza mphatso imene alandira. M’pofunika kuti azidziwa kuti munthu amene wapereka mphatsoyo amawaganizira ndipo wapereka mphatsoyo pofuna kusonyeza kuti amawakonda. Ndipo ndikuona kuti kuchita zimenezi n’kothandiza kwambiri.” Pambuyo pokambirana, anawo amadziwa mmene angathokozere ndiponso chifukwa chake ayenera kuthokoza.

Makolo anzeru amathandiza ana awo kuti asamakhale ndi mtima womaona kuti mwana amayenera kumapatsidwa zinthu. * Ngakhale kuti mfundo ya pa Miyambo 29:21 (Malembo Oyera) imanena za anthu antchito, ingathandizenso ana. Lembalo limati: “Ngati munthu wina achitira kapolo wake ufulu wopitirira kuyambira ubwana wake, iyeyu adzadziyesa pambuyo pake ngati mwana wake.”

Kodi ana ang’ono angathandizidwe motani kuti azisonyeza kuyamikira? Linda ali ndi ana atatu ndipo anati: “Ine ndi mwamuna wanga timalimbikitsa ana athu kuti ajambule chithunzi kapena kulemba dzina lawo pa kalata yothokoza imene tikufuna kutumizira munthu wina.” N’zoona kuti zolemba zawo zingakhale zosaoneka bwino koma amatengapo phunziro lofunika kwambiri.

(3) Musatope kuwaphunzitsa. Tonsefe tinabadwa ndi mtima wodzikonda ndipo mtima umenewu umachititsa kuti tikhale osayamika. (Genesis 8:21; Mateyo 15:19) Koma Baibulo limalimbikitsa atumiki a Mulungu kuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.”​—Aefeso 4:23, 24.

Makolo ozindikira amadziwa kuti kuphunzitsa ana “kuvala umunthu watsopano” si chinthu chapafupi. Stephen amene tam’tchula poyamba uja anati: “Tinkaona kuti ana athu akutenga nthawi yaitali kwambiri kuti aphunzire kunena kuti zikomo ndipo ankafunika kuwakumbutsa pafupipafupi.” Komabe, Stephen ndiponso mkazi wake sanatope kuphunzitsa ana awo. Iye anapitiriza kuti: “Ana athu anaphunzira chifukwa chakuti sitinatope kuwaphunzitsa. Panopa timasangalala kuona akuyamikira ena.”

Kuyamikira Anzathu

Nthawi zina sitinena kuti zikomo chifukwa cha kuiwala osati chifukwa cha kusayamika. Komabe n’chifukwa chiyani sitiyenera kungothokoza chamumtima basi? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tione zimene anachita anthu ena odwala khate m’nthawi ya Yesu.

Yesu akupita ku Yerusalemu anakumana ndi anthu 10 odwala khate. Pofotokoza nkhaniyi Baibulo limati: “Pamenepo anafuula mokweza ndi kunena kuti: ‘Yesu, Mlangizi, tichitireni chifundo!’ Atawaona anati kwa iwo: ‘Pitani mukadzionetse kwa ansembe.’ Ndiyeno pamene anali kupita anayeretsedwa. Mmodzi wa iwo ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, akutamanda Mulungu mokweza mawu. Atafika anadzigwetsa pansi naweramira nkhope yake pa mapazi a Yesu, namuyamika; komatu iyeyu anali Msamariya.”​—Luka 17:11-16.

Kodi Yesu anangonyalanyaza kusayamikira kwa enawo? Nkhaniyo imapitiriza kuti: “Poyankha Yesu anati ‘Amene ayeretsedwa si khumi kodi? Nanga ena asanu ndi anayi ali kuti? Kodi sanapezeke wina aliyense wobwerera kudzalemekeza Mulungu koma munthu wa mtundu wina yekhayu?’”​—Luka 17:17, 18.

Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu 9 enawo anali oipa. Chifukwatu poyambirira anthuwa anasonyeza kuti amakhulupirira Yesu ndipo anamvera malangizo amene iye anawapatsa. Kenako anapita ku Yerusalemu kukaonekera kwa ansembe. Komabe, ngakhale kuti mumtima mwawo anayamikira kukoma mtima kumene Yesu anawachitira, iwo sanachite zinthu zosonyeza kuti akuyamikira. Izi zinakhumudwitsa Khristu. Ndiyeno kodi ifeyo timatani? Kodi munthu wina akatichitira zinthu zabwino timanena mwamsanga kuti zikomo kapena kuchita zinthu zina zosonyeza kuyamikira?

Baibulo limanena kuti chikondi “sichichita zosayenera, sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:5) Motero kuyamikira mochokera pansi pamtima kumasonyeza kuti tili ndi khalidwe labwino komanso kuti ndife achikondi. Nkhani ya anthu odwala khate aja ikutiphunzitsa kuti ngati tikufuna kusangalatsa Khristu, tifunika kukonda ndiponso kuyamikira anthu onse mosasamala kanthu za kumene achokera, mtundu wawo kapena chipembedzo chawo.

Motero dzifunseni kuti: ‘Ndi liti pamene ndinayamikira anthu oyandikana nawo, anzanga a kuntchito, kusukulu, ogwira ntchito kuchipatala, ogulitsa mu sitolo kapena munthu wina aliyense amene anandichitira zabwino?’ Mwina mungayese kukhala ndi pepala loti muzilembapo nthawi zimene mwayamikira munthu wina pakutha pa tsiku limodzi kapena awiri. Pepala limenelo lidzakuthandizani kuti musinthe n’kumayamikira kwambiri anthu.

Yehova Mulungu ndi amene tiyenera kumuyamikira kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Iye ndi amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro.” (Yakobe 1:17) Kodi ndi liti pamene munapemphera kwa Yehova posonyeza kuti mukuyamikira kuchokera pansi pa mtima zinthu zabwino zimene anakuchitirani?​—1 Atesalonika 5:17, 18.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonyeza Kuyamikira Ngakhale Kuti Ena Satero?

Anthu ena sayamika tikawachitira zabwino. Ndiyeno, n’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza kuyamikira ngakhale kuti ena sayamika? Taonani chifukwa chimodzi.

Tikamachitira zabwino anthu osayamika timatsanzira Yehova Mulungu yemwe ndi Mlengi wathu wachifundo. Iye sasiya kuchitira anthu zinthu zabwino ngakhale kuti ambiri sayamikira chikondi chake. (Aroma 5:8; 1 Yohane 4:9, 10) Iye “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” Tikamayesetsa kusonyeza kuyamikira ngakhale kuti tili m’dziko la anthu osayamika, tidzasonyeza kuti ndifedi ‘ana a Atate [wathu] wa kumwamba.’​—Mateyo 5:45.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Makolo ambiri amawerengera ana awo ndi kukambirana nawo buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mutu 18 ndi wakuti: “Kodi Umakumbukira Kunena Kuti Zikomo?

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Khalani ndi pepala loti muzilembapo nthawi zimene mwayamikira munthu wina pakutha pa tsiku limodzi kapena awiri

[Chithunzi patsamba 15]

Ngakhale ana aang’ono angaphunzitsidwe kuyamikira

[Chithunzi patsamba 15]

Perekani chitsanzo kwa ana anu pankhani yosonyeza kuyamikira