GALAMUKANI! Na. 5 2016 | Kodi Nkhani Yonena za Yesu Ndi Yongopeka?

Pali umboni wotani m’mabuku a mbiri yakale?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Nkhani Yonena za Yesu Ndi Yongopeka?

Kodi akatswiri a mbiri yakale amanena zotani pa nkhani ya Yesu Khristu?

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani za ku North ndi South America

Anthu a ku North ndi South America amavutika ndi nkhawa komanso m’derali mumachitika zachiwawa. Kodi mfundo za m’Baibulo zingathandize anthuwa?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kuphunzitsa Mwana Wanu Nkhani Zokhudza Kugonana

Masiku ano ana akumaona ndiponso kumva zinthu zokhudza kugonana ali aang’ono kwambiri. Kodi muyenera kudziwa zotani? Kodi mungachite chiyani kuti muziteteza ana anu?

Chinthu Chodabwitsa

Kaboni ndi wofunika kwambiri kuti moyo upangike. Kodi kaboni n’chiyani ndipo n’chifukwa chiyani ndi wofunika kwambiri?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kuyamikira

Kukhala ndi mtima woyamikira ndi kothandiza kwambiri. Kodi kungakuthandizeni bwanji ndipo mungatani kuti mukhale ndi mtima woyamikira?

TIONE ZAKALE

Aristotle

Matchalitchi anayamba kuphunzitsa zimene Aristotle ankakhulupirira.

“Mfundozi Zindithandiza Kwambiri”

Anthu monga aphunzitsi ndiponso alangizi ayamba kugwiritsa ntchito mavidiyo a pawebusaiti ya jw.org.

Zina zimene zili pawebusaiti

Uzithokoza

Kodi mungayamikire bwanji anthu amene akuchitirani zabwino?