Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kulenga

Kulenga

Kodi Mulungu analenga dzikoli kwa masiku 6 enieni monga mmene anthu ena amanenera?

“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”Genesis 1:1.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu analenga zinthu zonse, kuphatikizapo dziko lapansili, kale kwambiri. Nthawi yeniyeni imene chilengedwechi chinakhalapo siidziwika chifukwa lemba la Genesis 1:1 limangonena kuti “pa chiyambi.” Asayansi a masiku ano nawonso amanena kuti chilengedwechi chili ndi chiyambi ndipo chinakhalapo zaka pafupifupi 14 biliyoni zapitazo.

Baibulo limanenanso za “masiku” 6 amene Mulungu analenga zinthu. Komabe silinena kuti masiku amenewa anali masiku a maola 24. (Genesis 1:31) Nthawi zina Baibulo likamanena za “tsiku,” limatanthauza nthawi zotalika mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, limatchula nthawi yonse imene Mulungu analenga zinthu zonse kuti ‘tsiku.’ (Genesis 2:4) N’zodziwikiratu kuti “masiku” amene Mulungu analenga zinthu amenewa anali a zaka masauzande ambiri.—Salimo 90:4.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Mfundo yakuti Mulungu analenga chilengedwe chonse kwa masiku 6 enieni ingakupangitseni kukayikira zimene Baibulo limanena. Koma mfundo zimene zili m’Baibulo zokhudza chilengedwe ndi “nzeru zopindulitsa” zomwe zingakuthandizeni.—Miyambo 3:21.

 Kodi Mulungu analenga zamoyo pongozisintha kuchokera ku zinthu zina?

“Mulungu anati: ‘Dziko lapansi likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake.’”Genesis 1:24.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu sanalenge zamoyo m’njira yakuti zizitha kusintha n’kukhala zinthu zina. M’malomwake iye analenga “mitundu” ya zomera komanso nyama zomwe zimaberekana “monga mwa mtundu wake.” (Genesis 1:11, 21, 24) Zimenezi zakhala zikupitirira ngakhale masiku ano, zomwe zapangitsa kuti m’dzikoli mukhalebe “mitundu” ya zinthu zimene Mulungu analenga poyamba.—Salimo 89:11.

Baibulo silinena kuti pambuyo pokwatitsa nyama zosiyana mitundu, kapena potengera malo amene nyama zikukhala, mtundu wa nyama ungatulutse mitundu yochuluka bwanji. Ngakhale anthu ena amaganiza kuti izi ndi umboni wakuti zamoyo zimasintha kuchokera ku zamoyo zina, njira imeneyi sipangitsa kuti mtundu wa chinthu usinthe. Mwachitsanzo, njirayi singapangitse kuti ng’ombe isinthe kukhala mbuzi. Akatswiri ofufuza zinthu amagwirizana ndi mfundo yoti zomera komanso nyama, zangosintha pang’ono zedi ngakhale kuti padutsa nthawi yaitali kwambiri kuchokera pamene zinalengedwa.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA

Kudziwa kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mitundu ya zinthu n’zolondola, kungatithandize kukhulupiriranso kuti zimene limanena pa nkhani ya mbiri yakale komanso maulosi osiyanasiyana ndi zolondolanso.

Kodi Mulungu anatenga kuti zinthu zimene anagwiritsa ntchito polenga zinthu?

“Manja anga anatambasula kumwamba.”—Yesaya 45:12.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire. (Yobu 37:23) Mfundo imeneyi ndi yofunika kwambiri chifukwa asayansi anatulukira kuti mphamvu zikhoza kusinthidwa n’kukhala chinthu chinachake. Baibulo limanena kuti Mulungu anagwiritsa ntchito “mphamvu zake zoopsa” popanga chilengedwechi. (Yesaya 40:26) Mulungu amagwiritsanso ntchito mphamvu zakezi kusamalira zinthu zimene analenga, chifukwatu ponena za dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, Baibulo limanena kuti “[Mulungu] amazichititsa kukhalapobe kwamuyaya, ngakhalenso mpaka kalekale.”—Salimo 148:3-6.

CHIFUKWA CHAKE KUDZIWA ZIMENEZI N’KOFUNIKA”

Wasayansi wina, dzina lake Allan Sandage, ananena kuti: “Asayansi sangakwanitse kuyankha mafunso ovuta kwambiri okhudza chilengedwe.Zimene asayansi ena apeza zokhudza chilengedwe n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Koma Baibulo limayankhanso mafunso ovuta amene asayansi sangayankhe monga lakuti, kodi Mulungu analengeranji dziko lapansi komanso anthu? *

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.