Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Italy

Dziko la Italy

MBALI ina ya dziko la Italy ndi yamapiri ndipo mbali ina ndi m’mbali mwa nyanja. Kum’mwera kwa dzikoli kumatentha, pamene kumpoto kwake ndi kozizira kwambiri. Mapiri ambiri a m’dzikoli ndi oti akhoza kuphulika n’kutulutsa ziphalaphala zapansi panthaka komabe ochepa okha, monga phiri la Stromboli ndi la Etna, ndi amene nthawi zambiri amaphulika.

Dziko la Italy ndi limodzi mwa mayiko amene kuli anthu ambiri ku Ulaya. M’dzikoli mumapezeka anthu monga Aluya, Agiriki, Afoinike ndi enanso.

M’dzikoli muli zinthu zakale zambiri zochititsa chidwi. M’mizinda ndi m’matauni ambiri mumapezekabe zomangamanga zakale za Agiriki ndi Aroma. Zinthu monga zithunzi, zipilala za mabo komanso akasupe a madzi, ndi zina mwa zimene zimakumbutsa anthu a m’dzikoli za akatswiri ena monga Bernini, Michelangelo ndi Raphael.

Anthu okaona malo m’dzikoli amakonda kukwera mabwato akakhala mumzinda wa Venice

Anthu a m’dzikoli amakonda chakudya chosiyanasiyana ndipo chikhalidwe chilichonse chimadziwika ndi kaphikidwe kawo ka chakudya. Anthu ambiri amakonda chakudya chotchedwa pasta ndipo nthawi zambiri amadyera nyama kapena nsomba, ndi masamba. Mafuta a maolivi amagwiritsidwanso ntchito kwambiri chifukwa amapangidwa m’dziko lomweli. Anthu enanso a m’dzikoli amakonda chakudya chotchedwa pizza komanso risotto.

Anthu ambiri a ku Italy amakonda chakudya chotchedwa Pasta

 Anthu a ku Italy ndi okonda kuchereza alendo, ansangala komanso okonda kucheza. Anthu a m’dzikoli amakonda kuuza anthu ena nkhani zawo moti si zachilendo kuona anthu akucheza m’malo opezeka anthu ambiri kapena kukambirana nkhani uku akuyenda.

Anthu ambiri a ku Italy amati ndi Akatolika, koma ndi ochepa okha amene amapita kutchalitchi. Anthu ambiri asiya kutsatira zimene tchalitchichi chimaphunzitsa komanso asiya kutsatira mfundo zimene tchalitchichi chakhala chikuyendera kwa zaka zambiri monga zokhudza kuchotsa mimba komanso kuthetsa ukwati.

A Mboni za Yehova akuchuluka ku Italy. A Mboniwa amadziwika ndi kuphunzitsa anthu Baibulo komanso kuti amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. M’dzikoli muli mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 3,000, ndipo yambiri ya mipingo imeneyi imalalikira anthu amene amalankhula zinenero zina kuwonjezera pa Chitaliyana. Pa zaka 10 zapitazi, chiwerengero cha anthu ochokera m’mayiko ena kupita ku Italy chawonjezeka kwambiri ndipo izi zikusonyezeratu kuti pakufunikadi kuti anthuwa aziphunzitsidwa Baibulo m’zinenero zawo.

KODI MUKUDZIWA?

Ngakhale kuti mzinda wa Vatican uli ku Rome, kuyambira mu 1929 umaonedwa ngati dziko la palokha ndipo anthu a ku Italy amaona kuti anthu a mumzinda umenewu si a m’dziko lawo.

Dera la mapiri a Dolomites, lomwe lili kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Italy