GALAMUKANI! January 2014 | Webusaiti Yothandiza Kwambiri

Kodi mukufuna kumvetsa bwino Baibulo kapena kupeza mfundo zothandiza banja lanu? Kodi ndinu wachinyamata ndipo mukufuna kupeza malangizo othandiza? Pa webusaiti yathu yovomerezeka pali nkhani zothandiza aliyense.

NKHANI YAPACHIKUTO

Webusaiti Yothandiza Kwambiri

Idziweni bwino webusaiti yathu ndipo mudzaona kuti pali mfundo za m’Baibulo zambiri zimene zingathandize inuyo komanso banja lanu.

Zochitika Padzikoli

Muli nkhani monga: Ufulu wa ana m’mayiko a kum’mwera kwa chipululu cha Sahara, kuvutitsidwa komanso kuopsezedwa pa Intaneti ku Italy, achinyamata ambiri safuna kukwezedwa pa ntchito ku Japan.

KUCHEZA NDI ANTHU

Katswiri Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Kucholowana kwa selo kunathandiza wasayansi wina wa ku Japan, dzina lake Feng-Ling Yang, kusintha mmene ankaganizira pa nkhani yoti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Chifukwa chiyani?

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?

Munthu akhoza kuyamba kuchita zoipa chifukwa chotengera zochita za anzake. Zimene muyenera kudziwa zokhudza kutengera zochita za anzanu komanso zimene mungachite pothetsa vutoli.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Kulenga

Baibulo limafotokoza za masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu. Kodi masiku amenewa anali a maola 24?

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Italy

Dziko la Italy limadziwika ndi zinthu zakale, madera osiyanasiyana komanso kuli anthu okonda kucheza. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zambiri za dzikoli komanso zokhudza Mboni za Yehova za kumeneko.

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kangaude Wam’nyumba Amachita Zogometsa Kwambiri

Kangaude wam’nyumba amatulutsa ulusi umene umakhala womata kwambiri komanso wosamata kwambiri. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene zimenezi zimachitikira komanso chifukwa chake.