KUCHEZA NDI | FENG-LING YANG
Katswiri Wasayansi Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake
Mayi Feng-Ling Yang ndi mkulu woyang’anira za kafukufuku pa sukulu ina mumzinda wa Taipei, ku Taiwan. Zimene anafufuzapo zakhala zikulembedwa m’magazini onena za sayansi. Poyamba ankakhulupirira kuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma kenako anasintha zimene ankakhulupirira. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za ntchito yake.
Tiuzeni za mbiri yanu.
Makolo anga anali osauka kwambiri ndipo mayi anga sankadziwa n’komwe kuwerenga. Tinkaweta nkhumba komanso kulima masamba kudera lina mumzinda wa Taipei, komwe kunkakonda kusefukira madzi. Makolo anga anandiphunzitsa kuti ndizilimbikira ntchito komanso kuthandiza ena.
Kodi banja lanu linali la chipembedzo chanji?
Chipembedzo chathu chinali Chitao. Tinkadziwa kuti kumwamba kuli Mulungu, ndipo tinkapereka nsembe kwa Mulunguyo ngakhale kuti sitinkamudziwa. Ndinkadabwa kuti: ‘N’chifukwa chiyani anthu amavutika? Nanga n’chifukwa chiyani anthu ali odzikonda?’ Ndinawerengapo mabuku onena za Chitao, Chibuda, mbiri ya mayiko a ku Asia komanso onena za mbiri ya mayiko a azungu. Ndinayesanso kupita ku matchalitchi osiyanasiyana koma sindinapeze mayankho a mafunso amenewa.
N’chifukwa chiyani munasankha kukhala katswiri wasayansi?
Ndinkakonda kwambiri masamu ndipo ndinkachita chidwi kwambiri kuona kuti zinthu zosiyanasiyana zimayenda motsatira malamulo. Chilichonse m’chilengedwechi, kuyambira zinthu zikuluzikulu mpaka tinthu ting’onozing’ono kwambiri, zimatsatira malamulo enaake. Choncho ndinkafunitsitsa kumvetsa bwino zokhudza malamulo amenewa.
N’chiyani chinakupangitsani kuti muzikhulupirira kuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?
Zimenezi ndi zimene ndinkaphunzitsidwa basi. Kuyambira ndili kupulayimale mpaka kukafika ku yunivesite sindinaphunzitsidwepo kuti zinthu zinachita kulengedwa. Komanso, popeza ndinkachita kafukufuku wokhudza zinthu zamoyo, ndinkayenera kukhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.
Popeza ndinkachita kafukufuku wokhudza zinthu zamoyo, ndinkayenera kukhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina
N’chiyani chinakupangitsani kuyamba kuwerenga Baibulo?
M’chaka cha 1996, ndinapita ku Germany kukapitiriza maphunziro anga. Chaka chotsatira ndinakumana ndi mayi wina, dzina lake Simone. Mayiyu anali wa Mboni za Yehova, ndipo anandiuza kuti akhoza kuyankha mafunso anga pogwiritsa ntchito Baibulo. Atandiuza kuti Baibulo limafotokoza chifukwa chimene Mulungu analengera anthufe, ndinachita chidwi kwambiri. Ndinayamba kumadzuka 4:30 m’mawa n’kumawerenga Baibulo kwa ola lathunthu. Kenako ndinkapita kukayenda, kukaganizira zimene ndawerengazo. Chaka chotsatira, ndinali nditawerenga Baibulo lonse. Ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti maulosi a m’Baibulo ndi olondola kwambiri. Patapita nthawi ndinakhulupirira ndi mtima wonse kuti Baibulo ndi buku lochokera kwa Mulungu.
Mutawerenga Baibulo, kodi munkaonabe kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?
Chakumapeto kwa chaka cha 1990 pamene ndinkaganizira kwambiri za nkhaniyi, asayansi ena anali atayamba kupeza kuti zinthu zimene zimapangitsa kuti chinthu chikhale chamoyo ndi zovuta kuzimvetsa kuposa mmene ankaganizira poyamba. N’zoona kuti asayansi anali atatulukira kale kuti zinthu zimene zimapanga maselo zimakhala zocholowana kwambiri. Koma pa nthawiyi anapeza kuti zinthu zimene zimapanga maselozi, zinapangidwa mwadongosolo kwambiri ndipo zimagwira ntchito mogometsa zedi. Zinthu zimene zimapanga maselo zimakhala zosiyanasiyana ndipo muselo iliyonse zimakhalapo zoposa 50. Ngakhale selo losavuta limakhala ndi zinthu zimenezi, zomwe zimagwira ntchito zosiyanasiyana.
Kodi kudziwa zimenezi kunakuthandizani bwanji?
Nditadziwa zinthu zonsezi, ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi n’chiyani chinachititsa kuti zinthu zimene zimapanga maselo zizigwira ntchito yake mwadongosolo chonchi?’ Pa nthawi yomweyinso, akatswiri asayansi ambiri anayamba kukhala ndi mafunso ngati omwewa akaganiza mmene selo limapangidwira. Pulofesa wina wa ku America analemba buku, ndipo m’bukuli anafotokoza kuti zinthu zimene zimapanga maselo ndi zovuta kuzimvetsa moti sizingatheke kuti zimenezi zingochitika zokha. Ndinagwirizana ndi maganizo akewa ndipo ndinkaona kuti payenera kukhala winawake amene analenga zamoyo..
Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi n’chiyani chinachititsa kuti zinthu zimene zimapanga maselo zizigwira ntchito yake mwadongosolo chonchi?’
N’chiyani chinakupangitsani kuti mukhale wa Mboni za Yehova?
Ndinachita chidwi kuona kuti Simone, ngakhale kuti anali wodwaladwala, ankayenda makilomita 56 mlungu uliwonse kubwera kunyumba kwathu kudzandiphunzitsa Baibulo. Komanso ndinaphunzira kuti pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi ku Germany, a Mboni anaikidwa m’ndende chifukwa chosalowerera ndale. Ndinachita chidwi kwambiri chifukwa cha kulimba mtima kwawo. A Mboni amakonda kwambiri Mulungu ndipo inenso ndinkafuna kukhala ngati iwowo.
Kodi kukhulupirira kuti kuli Mulungu kwakuthandizani bwanji?
Anzanga akuntchito amanena kuti panopa ndine munthu wosangalala kuposa kale. Poyamba ndinkadziona kuti ndine wosafunika chifukwa choti ndinachokera kubanja losauka. Choncho sindinkauza aliyense za komwe ndinachokera komanso zokhudza makolo anga. Koma ndaphunzira kuchokera m’Baibulo kuti Mulungu alibe nazo kanthu zoti munthu ndi wolemera kapena wosauka. Ndipotu Yesu anabadwira kubanja lomwe linali losauka ngati lathu. Panopa ndimawakonda kwambiri makolo anga ndipo sindichita manyazi kuuza anzanga zokhudza makolo angawo.