Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Madalitso Oposa Chuma

Madalitso Oposa Chuma

Madalitso Oposa Chuma

JON ankagwira ntchito yapamwamba ku United States. Ankayenda m’mayiko ambiri ndipo ankapeza ndalama zambiri ngakhale kuti anali wachinyamata. Iye ndi mkazi wake anali ndi nyumba yabwino ndipo ankasangalala moti anthu ambiri ankawasirira.

Taganiziraninso chitsanzo cha munthu wina dzina lake Kostas. * Pa anthu 5,000 omwe anafunsira ntchito ku banki ina yotchuka kwambiri ku Ulaya, anthu 80 okha ndi omwe analembedwa ntchito ndipo Kostas anali nawo m’gulu limenelo. Patangodutsa miyezi yochepa, anakwezedwa pantchito kangapo ndipo kenako anasankhidwa kukhala mkulu woyang’anira banki. Koma kenako anasiya ntchitoyo n’kukayambitsa kampani yake. Panthawi imene ankasiya ntchitoyo, ndalama zimene ankapeza pachaka zinali zambiri kuposa ndalama zimene anthu ambiri amapeza pamoyo wawo wonse. Iye ankaona kuti wadalitsidwa.

Komatu anthu onse tawatchulawa amakhulupirira kuti pali madalitso ena oposa chuma. Mwachitsanzo, masiku ano Jon amagwira ntchito yongodzipereka yophunzitsa Baibulo ndi kuthandiza anthu kuti adziwe Mulungu. Iye anati: “Ineyo ndaona kuti chuma sichingapangitse munthu kukhala wosangalala ndipo munthu ukamachifunafuna kwambiri sukhala ndi nthawi yochita zinthu zina zofunikira. Koma munthu akamatsatira mfundo za m’Baibulo amapeza madalitso ambiri, amakhala ndi banja losangalala, mtendere wa mumtima ndiponso chikumbumtima chabwino.”

Kostas anaonanso kuti zimenezi n’zoona. Iye anati: “Mulungu safuna kuti tizidzikundikira chuma chambiri. Ndikuona kuti ngati Mulungu watipatsa zinthu zoposa zimene tingafunikire pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, iye amafuna kuti tizigwiritse ntchito mogwirizana ndi chifuniro chake.” Posachedwapa, Kostas ndi banja lake anayamba kuphunzira chinenero china n’cholinga chakuti aziphunzitsa anthu Baibulo. Iye anati: “Taphunzira kuti ‘kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.’”—Machitidwe 20:35.

Indedi, Jon ndi Kostas aphunzira kuti madalitso auzimu ndi ofunika kwambiri kuposa chuma. Pulofesa wina wa ku yunivesite ya Havard, dzina lake Daniel Gilbert, ananena kuti akatswiri a matenda a maganizo “atha zaka zambiri akufufuza za kugwirizana kwa chuma ndi chisangalalo, ndipo apeza kuti chuma chimapangitsa munthu kukhala wosangalala ngati munthuyo akutha kupeza zinthu zofunika kwambiri pamoyo wake.” Koma iye ananenanso kuti: “Munthu akapeza chuma choposa pamenepa, chumacho sichimuchititsa kukhala wosangalala.”

Anazindikira Mochedwa

Munthu wina ananena kuti: “Munthu akachoka mu umphawi n’kuyamba kupeza zinthu zofunika kwambiri pamoyo wake, ndalama zina zowonjezera pamenepa zimene angapeze sizimuchititsa kukhala wosangalala.” Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, mtolankhani wina anazindikira mfundo yofunika kwambiri imeneyi, pomwe ankafunsa mafunso mkulu wina wolemera kwambiri, yemwe anali mmodzi mwa anthu oyambirira kukhala ndi kampani yopanga zitsulo ku United States, dzina lake Andrew Carnegie. Mkuluyu anauza mtolankhaniyu kuti: “Anthu asamandisirire, chuma changa chilibe phindu. Panopa ndili ndi zaka 60, ndipo ndili ndi vuto lakuti chakudya sichigayika bwino m’thupi mwanga. Zikanakhala zotheka, ndikanatha kupereka chuma changa chonse kuti ndikhalenso mnyamata wathanzi labwino.”

Kenako mtolankhaniyo anati: “A Carnegie anandiuza motsitsa mawu komanso mokhudza mtima kuti, ‘Ndingasangalale kutaya chilichonse chimene ndili nacho kuti ndikhalenso mnyamata.’” Mkulu winanso wolemera kwambiri amene anali ndi kampani yoyenga mafuta, dzina lake Paul Getty, ananena kuti: “Ndalama sizichititsa munthu kukhala wosangalala koma mwina zimam’pangitsa kukhala wosasangalala.”

Pamenepa tingamvetse zimene wolemba Baibulo wina ananena kuti: “Musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.”—Miyambo 30:8, 9.

Mfumu yakale ya Isiraeli, Solomo, inati: “Ndinakula chikulire kupambana onse anali m’Yerusalemu ndisanabadwe ine.” Koma ananenanso kuti: “Zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima.” Solomo anatinso: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Mlaliki 2:9-11; 5:12, 13; Miyambo 10:22.

Njira Yopezera Madalitso

Kuti tikhale ndi moyo wosangalala, tiyenera kukwaniritsa zosowa zathu zauzimu. Tikamaika Mulungu patsogolo, moyo wathu umakhala waphindu ndi wosangalatsa.

N’zosangalatsa kuti nthawi ina m’tsogolomu tidzaleka kuganiza za ndalama. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu adzawononga anthu opondereza anzawo ndi okonda kwambiri ndalama. (1 Yohane 2:15-17) Kenako boma la Mulungu lidzayamba kulamulira dziko lapansi mwachilungamo. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso monga mmene zinalili nthawi imene Mulungu analenga anthu awiri oyambirira. Panthawiyo tidzadalitsidwa kwambiri chifukwa anthu padziko lonse lapansi azidzakhala mosangalala, mwamtendere ndiponso mwachikondi.—Yesaya 2:2-4; 2 Petulo 3:13; 1 Yohane 4:8-11.

Moyo panthawiyo udzakhala wosangalatsa kwambiri chifukwa tidzakhala paubwenzi wabwino ndi Mulungu komanso tidzakhala ndi zinthu zonse zimene timafunikira pamoyo wathu. Panthawiyi Mulungu adzakwaniritsa cholinga chake chakuti anthu akhale ndi moyo wosatha m’paradaiso. Baibulo limatitsimikizira kuti tidzakhala ndi chakudya chokwanira, malo ogona abwino, ndiponso ntchito yosangalatsa. Ndipo umphawi sudzakhalakonso.—Salmo 72:16; Yesaya 65:21-23; Mika 4:4.

Aliyense amene amakhulupirira Yehova, Mulungu amene analemba Baibulo, sadzagwiritsidwa mwala. (Aroma 10:11-13) Choncho, ndi nzeru kwambiri pakali pano kufunafuna madalitso oposa chuma amenewa.—1 Timothy 6:6-10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Dzinali talisintha.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Tikamaika Mulungu patsogolo, timakhala ndi moyo wosangalala

[Chithunzi patsamba 8]

Kugwiritsa ntchito bwino ndalama, kungatithandize kukhala ndi moyo wosangalala