Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kabuku Kanga Kapinki

Kabuku Kanga Kapinki

Kabuku Kanga Kapinki

Yosimbidwa ndi Cynthia Newell

MTSIKANA wina wa ku Shreveport, mumzinda wa Louisiana, ku U.S.A, anandipatsa kabuku kapinki kakuti Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo. Panthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 7 ndipo tinali m’basi ya kusukulu kwathu. Iye anandiuza kuti andipatsa kabukuka ndikam’patsa ndalama zokwana masenti 50. Choncho ndinapita naye kwathu ndipo tinawerengera limodzi masenti 50 ndi kum’patsa.

Ndinayamba kukakonda kwambiri kabukuka. Patangopita nthawi yochepa, ndinadwala ndipo anandigoneka m’chipatala. Ndili ku chipatalako anthu a m’banja lathu ankandiwerengera kabukuka ndipo ndinkakakonda kwambiri. Koma nditakula sindinkakawerenga kawirikawiri, chifukwa ndinkaona kuti ndi ka ana. Kabukuka kanandithandiza komabe ndinkafunika kudziwa zinthu zozamirapo. Kenako ndinayamba kupita kumatchalitchi osiyanasiyana mlungu uliwonse kuti ndipeze mayankho a mafunso amene ndimafuna kudziwa okhudza Baibulo. Komabe sindinapeze mayankho ogwira mtima.

Nditafika ku sekondale, ndinayamba kuona kuti nkhani zachipembedzo n’zosafunika kwambiri, ngakhale kuti nthawi zambiri ndinkawerengabe Baibulo. Tsiku lina ndinaona kuti mwana wina sanachite nawo mwambo wolambira mbendera. Nditamufunsa, ananena kuti, “Ineyo ndimalambira Yehova, ndiye ndingalambire bwanji Mulungu ndi mbendera nthawi imodzi?” Ndinaona kuti zinali zomveka. Koma ndinafuna kudziwa kuti, ‘Kodi Yehova ndi ndani?’

Pafunso lililonse limene ndinafunsa, mnzangayo ankandisonyeza yankho lake m’Baibulo. Ndinkadabwa kuti: ‘Anazidziwa bwanji zimenezi? Zaka zathu zinali zofanana, koma iye amalidziwa kwambiri Baibulo.’ Iye anafotokoza kuti: “Ndimaphunzira Baibulo ku Nyumba ya Ufumu.” Anandipempha kuti Lamlungu ndidzapite naye ku Nyumba ya Ufumu ndipo ndinavomera. Ndinali nditapita pafupifupi ku tchalitchi chilichonse kwathuko koma ndinali ndisanapite ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Tsiku limene ndinapita ku Nyumba ya Ufumu, ndinadziwa kuti ndapeza anthu amene amaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo.

Msonkhano utatha, ndinapita pamalo amene amaperekerapo mabuku ndipo ndinapeza kuti pashelefu panali kabuku kapinki ngati kanga kaja. Panali patatha zaka 10 pamene mtsikana uja anandipatsa kabuku kameneko m’basi, choncho sindikanam’kumbukira mtsikana amene anandipatsa kabukuko. Koma tsopano ndinazindikira kuti mtsikanayo anali Nancy, yemwenso anandiitanira ku misonkhano tsiku limenelo.

Kenako ndinayamba kuphunzira Baibulo mlungu uliwonse ndipo ndinadziwa zambiri mofulumira. Ndinali nditaphunzira zambiri kuchokera mu kabuku kanga kapinki kaja choncho zinandithandiza kuti ndizimvetsa msanga pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo. Posapita nthawi ndinadzipereka kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa mu 1985 ndili ndi zaka 18. Panthawiyi n’kuti Nancy atasamukira ku Florida, ndipo sitimalankhulananso.

Patapita zaka zochepa, ndinakwatiwa. M’chaka cha 1991, ine ndi mwamuna wanga, Drew, tinayamba utumiki wa nthawi zonse. Ndipo tinkachita upainiya m’tawuni ina yaing’ono yomwe inali chakum’mawa kwa Texas. Nthawi yonseyi sindinkadziwa kuti Nancy ali kuti. Koma tsiku lina pamene ndinkawerenga Nsanja ya Olonda ya December 1, 1992, ndinadziwa kumene kunali Nancy chifukwa ndinamuona pa chithunzi cha anthu omaliza kumene maphunziro a Gileadi. Iye ndi mwamuna wake Nick Simonelli, anatumizidwa ku Ecuador ku South America.

Mu 2006 ine ndi mwamuna wanga tinadzipereka kuti tikagwire nawo ntchito yomanga nyumba za Mboni za Yehova ku dziko lina. Tinasangalala kwambiri titadziwa kuti poyamba tipita ku Ecuador kumene tikagwire ntchito yokulitsa nthambi ya kumeneko. Titangofika ku nthambi ya ku Ecuador ndinangoona Nancy akubweranso poteropo. Zinangochitika kuti iyenso anabwera ku nthambiko tsiku limenelo. Tinaonananso patatha zaka 32 chindipatsireni kabuku kapinki kaja ndipo tinakumbatirana. Ndimayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha kabuku kameneko komanso chifukwa cha mtsikana amene anandipatsa kabukuko.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 23]

MABUKU AMENE ATHANDIZA ANTHU AMBIRI

Patatha zaka 32 kuchokera pamene buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo linatulutsidwa, buku lina lofanana ndi limeneli lakuti Phunzirani Kwa Mphunzitsi Waluso linatulutsidwa mu 2003. Pakali pano mabuku onse awiriwa omwe amanena zimene Yesu anaphunzitsa, afalitsidwa okwanira 65 miliyoni m’zinenero zoposa 100. Ngati mukufuna buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, pemphani wa Mboni za Yehova aliyense m’dera lanu.

[Zithunzi patsamba 23]

Zithunzi zazing’ono: Nthawi imene tinadziwana tili ana

Cynthia

Nancy

Chithunzi chachikulu: Patapita zaka zambiri, tili ku ofesi ya nthambi ku Ecuador