Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mlomo Wochititsa Chidwi wa Nyama ya M’madzi

Mlomo Wochititsa Chidwi wa Nyama ya M’madzi

Panagona Luso!

Mlomo Wochititsa Chidwi wa Nyama ya M’madzi

▪ Asayansi amachita chidwi kwambiri ndi mlomo wa nyama ya m’madzi yotchedwa squid. Iwo amadzifunsa kuti: ‘Zingatheke bwanji kuti mlomo wolimba wa nyamayi ulumikizane ndi thupi lake lopanda mafupa? Kodi kulumikizana kwa fupa ndi mnofu kumeneku sikungavulaze nyamayi?’

Taganizirani izi: Mlomo wa nyamayi ndi wolimba kwambiri ngati fupa, koma mbali imene walumikizana ndi thupi ndi yofewa ndipo umalimba pang’onopang’ono mpaka kukafika kumapeto kwake, komwe ndi kolimba kwambiri. Zimenezi zimathandiza kuti nyamayi izigwiritsa ntchito mlomo wake popanda kumva kuwawa.

Pulofesa wa payunivesite ya California, dzina lake Frank Zok, ananena kuti, kuphunzira za mlomo wa nyamayi “kungathandize kwambiri kuti anthu opanga zinthu apeze njira yolumikizira zinthu zolimba ndi zofewa.” Nzeru imeneyi ingathandize popanga miyendo kapena manja apulasitiki. Katswiri wina wa payunivesite yomweyi, dzina lake Ali Miserez, akuona kuti n’zotheka “kupanga miyendo ndi manja apulasitiki potsanzira kapangidwe ka mlomo wa nyamayi kuti mbali yolumikizana ndi thupi izikhala yofewa ndipo mbali inayo izikhala yolimba kwambiri. Zimenezi zingathandize kuti munthu amene amuika miyendo kapena manja apulasitikiwa asamamve kupweteka.”

Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika kuti nyamayi ikhale ndi mlomo wochititsa chidwi chonchi kapena unachita kupangidwa?

[Mawu a Chithunzi patsamba 9]

© Bob Cranston/​SeaPics.com

© Richard Herrmann/​SeaPics.com