Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mphunzitsi Anasintha Maganizo Ake

Mphunzitsi Anasintha Maganizo Ake

Mphunzitsi Anasintha Maganizo Ake

▪ Zaka zingapo zapitazo, mphunzitsi wina mu mzinda wa Batumi m’dziko la Georgia anauza ophunzira ake kuti atchule Malamulo Khumi a m’Baibulo. Mphunzitsiyo anadabwa kwambiri kuti wophunzira wina wa m’kalasi mwake, dzina lake Anna, anatchula bwinobwino malamulo onse. Anayankhanso molondola mafunso ena a m’Baibulo. Mphunzitsiyo modabwa anafunsa Anna kuti afotokoze zimene zimamuchititsa kuti azidziwa zinthu zambiri. Anna atayankha kuti amaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mphunzitsiyo anamudula mawu n’kumuuza kuti iye amaona kuti Mboni za Yehova ndi anthu amakani.

Nthawi inanso, mphunzitsiyo anauza ophunzirawo kuti alembe nkhani ya anthu a m’dziko la Georgia ndi mavuto amene amakumana nawo. Kumapeto kwa nkhani yake, Anna analemba kuti: “Anthu sangathe kusintha zinthu kuti ziyambe kuyenda bwino m’dzikoli chifukwa lemba la Yeremiya 10:23 limati: ‘Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.’ Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto onse.”

Tsiku lotsatira, mphunzitsiyo anayamikira Anna m’kalasimo chifukwa cha nkhani yake. Iye anati: “Nkhani ya Anna yandisangalatsa kwambiri chifukwa wailemba m’mawu akeake. M’nkhaniyi wafotokozamo chimene chingachititse kuti dzikoli lisinthe.” Mphunzitsiyo anamuyamikiranso Anna chifukwa cha khalidwe lake ndipo anamuthokoza pamaso pa anzake a m’kalasi kuti ali ndi khalidwe labwino ndiponso amavala modzilemekeza.

Mboni za Yehova zitafika pakhomo pake, mphunzitsiyo anawauza kuti poyamba ankaona kuti Mboni za Yehova ndi zamakani koma anasintha maganizo ake chifukwa cha khalidwe la wophunzira wake wina, dzina lake Anna. Mu 2007, mphunzitsiyu anapezeka pa mwambo wa Mboni za Yehova wokumbukira imfa ya Yesu Khristu ndipo anamvetsera mwachidwi mwambo wonse.

Mwambowu utatha, mphunzitsi wa Anna ananena kuti anasirira kwambiri ndi mmene Mboni za Yehova zimadziwira Baibulo. Panopa, akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Sitikukayikira kuti inunso, monga mmene anachitira mphunzitsiyu, mumafuna kudziwa zimene anthu ena amakhulupirira komanso zimene zimawachititsa kukhala ndi khalidwe linalake. Mungachite bwino kupempha wa Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere.

[Chithunzi patsamba 21]

Anna akulemba nkhani yake