Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kutentha Mtembo N’kulakwa?

Kodi Kutentha Mtembo N’kulakwa?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Kutentha Mtembo N’kulakwa?

Anthu ena amaona kuti kutentha mtembo n’kulakwa chifukwa kumakhala kunyoza munthu wakufayo. Iwo amaona kuti ‘anthu amene amalambira Mulungu sayenera kuchita zimenezi chifukwa n’zachikunja.’ Koma ena amakhulupirira kuti kutentha mtembo sikulakwa chifukwa ndi njira yabwino yotayira munthu wakufa. Kodi inuyo mukuona bwanji?

NTHAWI za m’Baibulo munthu akafa ankamuika kumanda. Mwachitsanzo, Abulahamu anaika mtembo wa mkazi wake, Sara, m’phanga. Yesu atafa anaikidwanso m’phanga losemedwa m’mwala. (Genesis 23:9; Mateyo 27:60) Kodi Baibulo limanena kuti njira yabwino yotayira mtembo ndi kukaika kumanda basi? Kodi limasonyeza kuti atumiki akale a Mulungu ankaona kuti kutentha mtembo n’kulakwa?

Kodi Mitembo Imene Inkatenthedwa Inali ya Anthu Ochimwa?

Kungowerenga mothamanga nkhani zina za m’Baibulo mungaone ngati anthu amene mitembo yawo inkatenthedwa anali ochimwa. Mwachitsanzo, Chilamulo cha Mose chinanena kuti ngati mwana wamkazi wa wansembe ali hule, ayenera kuphedwa ndi ‘kutenthedwa ndi moto.’ (Levitiko 20:10; 21:9) Komanso Akani ndi banja lake atachita tchimo limene linachititsa kuti Aisiraeli agonje ku Ai, Aisiraeli anzawo anawaponya miyala ndipo kenako ‘anawatentha ndi moto.’ (Yoswa 7:25) Akatswiri ena a zamaphunziro amakhulupirira kuti chilango chimenechi chinkaperekedwa kwa anthu amene imfa yawo inali yochititsa manyazi ndipo ankawatentha n’cholinga choti asaikidwe m’manda.

Komanso Mfumu Yosiya inatsegula manda a ansembe a Baala ndi kutentha mafupa awo pamaguwa awo kuti ku Yuda kusapezekenso munthu wolambira mafano. (2 Mbiri 34:4, 5) Kodi zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti anthu onse amene mitembo yawo inkatenthedwa anali ochimwa? Ayi, chifukwa pali nkhani ina ya m’Baibulo imene imasonyeza kuti zimenezi si zoona.

Afilisti atagonjetsa mfumu Sauli ya Isiraeli pankhondo, anapachika mtembo wake ndi mitembo ya ana ake atatu pakhoma la mzinda wa Betisani. Koma Aisiraeli a mu mzinda wa ku Jabezi Gileadi atamva za chipongwe chimenechi, anapita kukachotsa mitemboyo ndipo anaitentha kenako anaika m’manda mafupa awo. (1 Samueli 31:2, 8-13) Kungowerenga nkhaniyi munthu ungaone ngati zimenezi ndi umboni wakuti anthu amene amatenthedwa, amakhala ochimwa. Ndipotu Sauli analidi wochimwa chifukwa ankafuna kupha Davide, wodzozedwa wa Yehova, ndipo anafa atachimwira Mulungu.

Onani kuti Sauli anafa limodzi ndi mwana wake, Yonatani, amenenso thupi lake linatenthedwa. Koma Yonatani sanali munthu woipa. Iye anali mnzake wapamtima wa Davide. Aisiraeli ankadziwa kuti Yonatani ‘ankagwirizana ndi Mulungu.’ (1 Samueli 14:45) Davide atamva zimene anthu a ku Jabezi Gileadi anachita, anawathokoza kwambiri kuti: “Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Sauli.” Choncho Davide sanakwiye ndi kutenthedwa kwa mitembo ya Sauli ndi Yonatani.—2 Samueli 2:4-6.

Adzaukitsidwabe

Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu adzaukitsa anthu ambiri amene anafa. (Mlaliki 9:5, 10; Yohane 5:28, 29) Polosera za nthawi imene akufa adzauka, buku la Chivumbulutso limati: “Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo, nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo.” (Chivumbulutso 20:13) Kaya mtembo unaikidwa m’manda, kutenthedwa, kumira m’nyanja, kudyedwa ndi nyama zolusa kapena kuphulitsidwa ndi bomba, Mulungu Wamphamvuyonse adzakwaniritsa zimene lembali likunena.

Baibulo silipereka lamulo la mmene tiyenera kutayira mtembo. Ndipo Yehova saletsa kutentha mtembo. Komabe munthu wakufa sayenera kuikidwa mwachipongwe.

Anthu ayenera kusankha njira yoikira mtembo mogwirizana ndi dera limene amakhala. Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo ayenera kuyesetsa kuti asakhumudwitse anthu a m’dera lawo. Komabe n’zosayenera kuchita miyambo imene imalimbikitsa ziphunzitso za chipembedzo chonyenga monga chakuti munthu ali ndi mzimu umene suufa akamwalira. Dziwani kuti munthu payekha kapena apabanja pake ndi amene ali ndi udindo wosankha mmene adzatayire mtembo wake akadzafa.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi ndi munthu wokhulupirika uti amene Baibulo limanena kuti mtembo wake unatenthedwa?—1 Samueli 31:2, 12.

▪ Kodi Davide anachita chiyani ndi anthu amene anatentha ndi kuika m’manda mtembo wa Sauli?—2 Samueli 2:4-6.

▪ Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti munthu amene mtembo wake unatenthedwa atha kuukitsidwa?—Chivumbulutso 20:13.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Baibulo silipereka lamulo lililonse la mmene tingamatayire mitembo