Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi n’chifukwa chiyani manambala a mavesi m’buku la Masalmo amasiyana m’mabaibulo osiyanasiyana?

Baibulo lathunthu loyamba kukhala ndi machaputala ndi mavesi linali Baibulo la Chifalansa lomwe linafalitsidwa ndi Robert Estienne mu 1553. Komabe, zikuoneka kuti buku la Masalmo analigaŵa kale zimenezi zisanachitike, chifukwa chakuti linapangidwa ndi masalmo osiyanasiyana, kapena nyimbo, zolembedwa ndi anthu angapo.

Zikuoneka kuti poyamba Yehova anauza Davide kuti asonkhanitse pamodzi masalmo kuti aziwagwiritsa ntchito pa mapemphero a anthu onse. (1 Mbiri 15:16-24) Zikuonekanso kuti Ezara, wansembe ndiponso “mlembi waluntha” ndi amene anakonza buku lonse la Masalmo kuti likhale mmene lilili lerolino. (Ezara 7:6) Choncho, buku la Masalmo linapangidwa ndi masalmo osiyanasiyana oikidwa pamodzi.

Paulo, polankhula ndi anthu amene anali m’sunagoge ku Antiokeya (Pisidiya) pa ulendo wake woyamba waumishonale, anatchula mawu amene ali m’buku la Masalmo oti: “Monganso mulembedwa m’Salmo lachiŵiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.” (Machitidwe 13:33) Mpaka pano, mawu ameneŵa akupezekabe m’Baibulo pa salmo lachiŵiri vesi 7. Komabe, pali kusiyana pa kalembedwe ka manambala m’masalmo ambiri m’mabaibulo osiyanasiyana. Izi zili choncho chifukwa chakuti mabaibulo ena anawamasulira kuchokera ku malemba a Chihebri olembedwa ndi Amasorete, pamene ena anawamasulira kuchokera ku Baibulo la Septuagint la Chigiriki. Baibulo limeneli analimasulira kuchokera ku Chihebri ndipo anamaliza kulimasulira m’zaka 200 zoyambirira za m’ma B.C.E. Mwachitsanzo, Baibulo la Vulgate la Chilatini, limene mabaibulo ambiri a Chikatolika analigwiritsa ntchito pomasulira, linagwiritsa ntchito kagaŵidwe ka manambala kopezeka mu Baibulo la Septuagint, pamene Baibulo la New World Translation ndi ena anatsatira kagaŵidwe ka Chihebri.

Kodi kusiyana kwake kwenikweni n’kotani? Baibulo la Chihebri lili ndi masalmo okwana 150. Koma Baibulo la Septuagint limaphatikiza Salmo 9 ndi 10 kukhala limodzi, ndiponso Salmo 114 ndi 115 kukhalanso limodzi. Kuwonjezera apo, linagaŵa Salmo 116 kukhala masalmo aŵiri, chimodzimodzinso ndi Salmo 147. Ngakhale kuti nambala ya masalmo onse pamodzi ndi yofanana, kuyambira Salmo 10 mpaka Salmo 146 mu Baibulo la Septuagint manambala ake ndi otsika ndi salmo limodzi, kusiyana ndi Baibulo la Chihebri. Choncho Salmo lodziŵika kwambiri la nambala 23 linakhala Salmo la nambala 22 m’Baibulo la Douay Version, chifukwa linatsatira kagaŵidwe ka manambala ka Vulgate ya Chilatini, imenenso inatengera ku Septuagint.

Pomaliza, manambala ena a mavesi a m’buku la masalmo angasiyanenso malinga ndi Baibulo lake. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Mabaibulo ena anatengera “kalembedwe ka Chiyuda kotenga timawu tapamwamba ngati vesi,” linatero buku la Cyclopedia lolembedwa ndi McClintock ndi Strong, koma ena sanatengere kalembedwe kameneka. Ndiponso, ngati kamutu kapena mawu apamwamba ndi atali, nthaŵi zambiri amawagaŵa kuti akhale mavesi aŵiri, ndipo manambala a mavesi m’buku la masalmo amawonjezekanso.