Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu

Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu

 Mgonero wa Ambuye uli ndi Tanthauzo Lalikulu kwa Inu

KODI Mgonero wa Ambuye uli ndi tanthauzo limene lidzakhale lofunika mpaka kalekale kwa inu? Kuti tiyankhe funso limeneli, choyamba tiyeni tione tanthauzo limene Mgonero umenewu unali nalo kwa Yesu Kristu mwiniwakeyo.

Usiku pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu anasonkhana pamodzi ndi atumwi ake 12 m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu kuti achite phwando la Paskha. Atamaliza kudya chakudya cha Paskha, Yudasi mthirakuŵiriyo anatuluka m’chipindamo kupita kokamupereka Yesu. (Yohane 13:21, 26-30) Ali ndi atumwi 11 otsalaŵo, Yesu anakhazikitsa “Mgonero wa Ambuye.” (1 Akorinto 11:20) Mgonero umenewu umatchedwanso Chikumbutso, chifukwa Yesu analamula otsatira ake kuti: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.” Mwambo umenewu ndi wokhawo umene Akristu analamulidwa kuti aziukumbukira.​—1 Akorinto 11:24.

M’madera ambiri, anthu amamanga zipilala kapena amaika tsiku lapadera loti azikumbukira, kapena kukondwerera munthu kapena chinthu chapadera. Mogwirizana ndi zimenezi, Yesu anakhazikitsa mwambo wa chakudya cha chikumbutso choti chikakumbutse ophunzira ake kuti asaiŵale zinthu zofunika kwambiri zimene zinachitika tsiku limenelo. Kwa zaka zambiri kuyambira pamenepo, mwambo wa chakudya umenewu unali kudzakumbutsa anthu oonerera za tanthauzo lalikulu la zimene Yesu anachita usiku umenewo, makamaka tanthauzo la zizindikiro zimene anazigwiritsa ntchito. Kodi Yesu anagwiritsa ntchito zizindikiro zanji, ndipo kodi zili ndi tanthauzo lotani? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena, zimene zinachitika usiku umene uja mu 33 C.E.

Zizindikiro Zopatulika

“Adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi [chitanthauza, NW] thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.”​Luka 22:19.

Pamene Yesu anatenga mkatewo nanena kuti “ichi chitanthauza thupi langa,” amasonyeza kuti mkate wopanda chotupitsawo unali kuimira, kapena unali chizindikiro, cha thupi lake lanyama lopanda uchimo, limene analipereka kuti “[li]khale moyo wa dziko lapansi.” (Yohane 6:51) Ngakhale kuti mabaibulo ena amanena kuti “ichi ndi [Chigiriki, es·tinʹ] thupi langa,” buku lolembedwa ndi Thayer lotchedwa Greek-English Lexicon of the New Testament limati verebu  limeneli nthaŵi zambiri limatanthauza ‘kutanthauza kapena kuimira.’ Pa Chigiriki, munthu akamva liwu limeneli amaganiza za kuimira, kapena kuyerekezera.​—Mateyu 26:26, NW.

N’chimodzimodzinso ndi chikho cha vinyo chija. Yesu anati: “Chikho ichi ndi [chitanthauza, NW] pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.”​Luka 22:20.

Mu nkhani imene analemba Mateyu, Yesu ananena za chikhocho kuti, “ichi ndicho [chitanthauza, NW] mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.” (Mateyu 26:28) Yesu anali kugwiritsa ntchito vinyo amene anali m’chikhoyo monga choimira, kapena chizindikiro, cha mwazi wake. Mwazi wake ndi umene unadzakhala maziko a “pangano latsopano” la ophunzira ake odzozedwa ndi mzimu, amene adzalamulire ngati mafumu ndi ansembe limodzi naye kumwamba.​—Yeremiya 31:31-33; Yohane 14:2, 3; 2 Akorinto 5:5; Chivumbulutso 1:5, 6; 5:9, 10; 20:4, 6.

Vinyo amene anali m’chikho muja amatikumbutsanso kuti mwazi wokhetsedwa wa Yesu ndi umene udzakhale maziko othandiza “kuchotsa machimo,” n’kupangitsa anthu a m’panganolo kuti aitanidwe kumwamba ngati olamulira limodzi ndi Kristu. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu oitanidwa kumwamba, amene alipo ochepa chabe, ndi okhawo amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso.​—Luka 12:32; Aefeso 1:13, 14; Ahebri 9:22; 1 Petro 1:3, 4.

Nanga bwanji za otsatira onse a Yesu amene sali nawo m’pangano latsopano? Ameneŵa ndi “nkhosa zina” za Ambuye, amene sakuyembekezera kukalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba, koma kudzasangalala ndi moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. (Yohane 10:16; Luka 23:43; Chivumbulutso 21:3, 4) Pokhala “khamu lalikulu” la Akristu okhulupirika amene “amtumikira [Mulungu] usana ndi usiku,” amasangalala kukhala ongoonerera chabe pa Mgonero wa Ambuye posonyeza kuyamikira kwawo. Mwa mawu awo ndi ntchito zawo iwo amakhala akunena kuti: “Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”​—Chivumbulutso 7:9, 10, 14, 15.

Tizichita Kangati?

“Chitani ichi chikumbukiro changa.”​Luka 22:19.

Kodi tiyenera kuchita kangati Chikumbutso kuti tizikumbukira imfa ya Yesu? Yesu sanatiuze mwachindunji. Komabe, iye anakhazikitsa Mgonero wa Ambuye pa Nisani 14, usiku umene ankakondwerera Paskha. Aisrayeli ankachita Paskhayu kamodzi pachaka, choncho n’zachidziŵikire kuti Yesu anafuna kuti Chikumbutso chizichitikanso chimodzimodzi. Aisrayeli ankakumbukira kuwomboledwa kwawo kuchoka ku ukapolo ku Igupto kamodzi pa chaka, pamene Akristu amakumbukira kuwomboledwa kwawo kuchoka ku ukapolo wa uchimo ndi imfa kamodzi pa chaka.​—Eksodo 12:11, 17; Aroma 5:20, 21.

Nkhani yomakumbukira chinachake chofunikira kwambiri kamodzi pa chaka siyachilendo. Mwachitsanzo, ganizirani mmene anthu okwatirana amakondwerera tsiku limene anakwatirana, kapena mmene dziko limakumbukirira chinthu china chofunika kwambiri chimene chinachitika m’mbiri yake. Kukumbukirako nthaŵi zambiri kumachitika kamodzi pa chaka pa tsiku limene chinthucho chinachitika. Chochititsa chidwi n’chakuti, kwa zaka mazana ambiri pambuyo pa imfa ya Yesu, Akristu ambiri ankatchedwa Akwatodesimani, kutanthauza kuti “a pa fotini,” chifukwa ankakumbukira imfa ya Yesu kamodzi pa chaka, pa Nisani 14.

 Mwambo Wosavuta Koma Wofunika Kwambiri

Mtumwi Paulo anafotokoza kuti kusunga Mgonero wa Ambuye kudzawathandiza ophunzira a Yesu “[ku]lalikira imfa ya Ambuye.” (1 Akorinto 11:26) Choncho, chikumbutso chimenechi chinali choti chidzasonyeze mbali yofunika kwambiri ya chifuniro cha Mulungu imene Yesu anachita mwa imfa yake.

Mwa kukhala wokhulupirika mpaka imfa, Yesu Kristu anasonyeza kuti Yehova Mulungu ndi Mlengi wanzeru ndi wachikondi, komanso ndi Mfumu yaikulu yolungama. Mosiyana ndi zimene ananena Satana, komanso zimene anachita Adamu, Yesu anasonyeza kuti n’zotheka munthu kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu, ngakhale pamene akuvutika kwambiri.​—Yobu 2:4, 5.

Mgonero wa Ambuye umatithandizanso kuti tizikumbukira komanso kuyamikira chikondi ndi kudzimana kwa Yesu. Ngakhale kuti Yesu anazunzidwa kwambiri, iye anamverabe Atate ake m’zonse. N’chifukwa chake anatha kupereka moyo wake waumunthu wangwiro kuti afafanize ngongole yaikulu ya tchimo la Adamu. Monga mmene Yesu mwiniwakeyo anafotokozera, anabwera “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Choncho, onse amene amakhulupirira Yesu angakhululukidwe machimo awo n’kulandira moyo wosatha, monga mmene Yehova anafunira kuti anthu akhalire kuyambira pachiyambi pomwe.​—Aroma 5:6, 8, 12, 18, 19; 6:23; 1 Timoteo 2:5, 6. *

Zimenezi zimasonyezanso kuchuluka kwa ubwino ndi chifundo cha Yehova, zimene zinam’pangitsa kuti akonze njira yoti anthu apulumukire. Baibulo limati: “Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.”​—1 Yohane 4:9, 10.

Zoonadi, Chikumbutso ndi mwambo wofunika kuusunga wochititsa chidwi kwambiri! Ndi mwambo wosavuta woti ungathe kuchitika m’malo osiyanasiyana pa dziko lonse lapansi, koma uli ndi tanthauzo lofunika ndipo wakhalabe chikumbutso chokwanira kwa nthaŵi yaitali.

Tanthauzo Lake kwa Inu

Siinali nkhani yamaseŵera kwa Ambuye Yesu Kristu ndi Atate ake, Yehova kuti Yesu afe popereka moyo wake nsembe. Chifukwa anali munthu wangwiro, Yesu sanabadwe kuti adzafe ngati  mmene tinabadwira ifemu. (Aroma 5:12; Ahebri 7:26) Akanatha kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Palibe amene akanatha kutenga moyo wake, ngakhale mochita kulanda, ngati iye sakanalola. Iye anati: “Palibe wina andichotsera [moyo wanga], koma ndiutaya ine ndekha.”​—Yohane 10:18.

Komabe, Yesu analolela kupereka moyo wake waumunthu wangwiro ngati nsembe kuti “mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdyerekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m’moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo.” (Ahebri 2:14, 15) Chikondi komanso kudzimana kwa Yesu kumaonekanso tikayang’ana njira imene iye analola kuti afere. Iye ankadziŵa bwinobwino mmene adzazunzikire ndi kufera.​—Mateyu 17:22; 20:17-19.

Chikumbutso chimatikumbutsanso za njira yaikulu kuposa zonse imene Atate wathu wakumwamba Yehova anasonyezera chikondi chake. Zinalidi zopweteka kwambiri kwa iye, amene ali “wodzala chikondi, ndi wachifundo” kuti amve ndi kuona “kulira kwakukulu ndi misozi” ya Yesu m’munda wa Getsemane, komanso kuti aone Yesu akukwapulidwa ngati nyama, kupachikidwa mwankhanza, ndi kufa imfa yofa pang’onopang’ono yopweteka kwambiri. (Yakobo 5:11; Ahebri 5:7; Yohane 3:16; 1 Yohane 4:7, 8) Kungoganizira chabe za zimenezi, ngakhale panopo, zaka mazana ambiri pambuyo pake, kumawamvetsabe chisoni anthu ambiri.

Tikaganizira kuti Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu analolela kuti zinthu zopweteka ngati zimenezi ziwachitikire chifukwa cha ife anthu ochimwa, timasoŵa chonena. (Aroma 3:23) Tsiku lililonse pa moyo wathu timalimbana ndi mavuto obwera chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro kwathu. Komabe, chifukwa timakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu, tingapemphe Mulungu kuti atikhululukire. (1 Yohane 2:1, 2) Zimenezi zimatithandiza kukhala omasuka naye Mulungu komanso kukhala ndi chikumbumtima choyera. (Ahebri 4:14-16; 9:13, 14) Kuphatikiza apo, tingayembekezere kudzakhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi la paradaiso. (Yohane 17:3; Chivumbulutso 21:3, 4) Madalitso ameneŵa, ndi enanso ambiri, alipo chifukwa chakuti Yesu anadzipereka nsembe, chimene chili chinthu chachikulu kwambiri koposa zonse chosonyeza kuti Yesu ndi wodzimana.

Kuyamikira Mgonero wa Ambuye

Mosakaikira, Mgonero wa Ambuye ulidi njira yabwino kwambiri imene timaonera “chisomo choposa cha Mulungu.” Ndipo zimene Yehova Mulungu anachita potipatsa dipo la nsembe, limene linatheka chifukwa cha chikondi komanso kudzimana kwa Yesu, ndithudi ndi “mphatso yake yake yosatheka kuneneka.” (2 Akorinto 9:14, 15) Kodi ubwino umene Mulungu anasonyezawu, kudzera mwa Yesu Kristu, sukukhudza mtima wanu n’kukupangitsani kukhala oyamikira kwambiri kuchokera pansi pamtima?

Tikukhulupirira kuti inu ndinu oyamikira ndithu. Choncho, tikukuitanani kuti mukasonkhane pamodzi ndi Mboni za Yehova pochita Chikumbutso cha imfa ya Yesu, ndipo tidzakulandirani ndi manja aŵiri. Chaka chino Chikumbutso chidzachitika Lachitatu pa 16 April, dzuŵa litaloŵa. Mboni za Yehova kumene mumakhalako zidzakondwa kukuuzani nthaŵi ndi malo enieni kumene kukachitikire mwambo wofunika kwambiri umenewu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Kuti mumve tsatanetsatane wa nkhani ya dipo, chonde onani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 6]

KODI TITI “ICHI NDI THUPI LANGA” KAPENA “ICHI CHITANTHAUZA THUPI LANGA?”

Pamene Yesu ananena kuti “Ine ndine khomo” komanso, “Ine ndine mpesa weniweni,” palibe amene anaganiza kuti Yesu anali khomo lenileni kapena mpesa weniweni. (Yohane 10:7; 15:1) Momwemonso, pamene Baibulo limanena kuti Yesu anati: “Chikho ichi ndi pangano latsopano,” sitiganiza kuti chikhocho n’chimene chili pangano latsopanolo. N’chimodzimodzinso pamene ananena kuti mkate ‘unali’ thupi lake, m’posachita kufunsa kuti mkatewo umatanthauza, kapena umaimira, thupi lake. N’chifukwa chake Baibulo la Charles B. Williams limati: “Ichi chikuimira thupi langa.”​—Luka 22:19, 20.

[Chithunzi patsamba 5]

Mkate wopanda chotupitsa ndiponso vinyo ndi zizindikiro zoyenera za thupi la Yesu lopanda uchimo ndi mwazi wake wokhetsedwa

[Chithunzi patsamba 7]

Chikumbutso chimatikumbutsa za chikondi chachikulu kwambiri chimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anasonyeza