Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizilalikira Uthenga wa Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu

Tizilalikira Uthenga wa Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu

“Kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”—MAC. 20:24.

NYIMBO: 101, 84

1, 2. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankayamikira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

MTUMWI PAULO ananena zoona pamene anati: “Kukoma mtima kwake kwakukulu kumene [Mulungu] anandisonyeza sikunapite pachabe.” (Werengani 1 Akorinto 15:9, 10.) Iye ankadziwa kuti kunali kosayenera kuti Mulungu amusonyeze chifundo chachikulu chifukwa chakuti poyamba ankazunza Akhristu.

2 Chakumapeto kwa moyo wake analembera Timoteyo kuti: “Ndikuyamika Khristu Yesu Ambuye wathu amene anandipatsa mphamvu poona kuti ndine wokhulupirika, ndipo anandipatsa utumiki.” (1 Tim. 1:12-14) Kodi Paulo ankanena za utumiki uti? Iye anauza akulu a ku Efeso kuti: “Moyo wanga sindikuuona ngati wofunika kapena wamtengo wapatali kwa ine ayi. Chimene ndikungofuna n’chakuti ndimalize kuthamanga mpikisano umenewu, komanso kuti ndimalize utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu basi. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”Mac. 20:24.

3. Kodi Paulo anapatsidwa utumiki wapadera uti? (Onani chithunzi patsamba 26.)

3 Kodi ndi “uthenga wabwino” uti umene Paulo ankalalikira womwe unkasonyeza kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova? Iye anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Munamva kuti ndinaikidwa kukhala woyang’anira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kuti ndikuthandizeni.” (Aef. 3:1, 2) Paulo analamulidwa kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu a mitundu ina kuti nawonso adzakhale m’gulu la olamulira limodzi ndi Khristu mu Ufumu wa Mulungu. (Werengani Aefeso 3:5-8.) Paulo ankachita utumiki wake modzipereka ndipo ndi chitsanzo chabwino kwa tonsefe. Komanso iye anasonyeza kuti kukoma mtima kumene Mulungu anamusonyeza “sikunapite pachabe.”

KODI MUMAYAMIKIRA KUKOMA MTIMA KWAKUKULU KWA MULUNGU?

4, 5. N’chifukwa chiyani tingati “uthenga wabwino wa Ufumu” n’chimodzimodzi ndi uthenga wabwino wa “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu”?

4 M’masiku otsiriza ano anthu a Yehovafe talamulidwa kuti tizilalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu padziko lonse lapansi kumene kuli anthu kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mat. 24:14) Uthenga umene timalalikirawu tingatinso ndi “uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” Tikutero chifukwa choti madalitso onse amene tikuyembekezera kudzapeza Ufumuwu ukamadzalamulira, adzakhalapo chifukwa cha kukoma mtima kumene Yehova watisonyeza kudzera mwa Khristu. (Aef. 1:3) Kodi ifeyo timatsanzira Paulo n’kumalalikira modzipereka posonyeza kuti timayamikira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?—Werengani Aroma 1:14-16.

5 M’nkhani yapita ija taona mmene kukoma mtima kwa Yehova kukutithandizira. Choncho tili ndi udindo wothandiza anthu kuti adziwe mmene Yehova wawasonyezera chikondi komanso zimene angachite kuti apindule ndi zimenezo. Kodi ndi zinthu ziti zokhudza kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova zimene tiyenera kuuza anthu?

TIZILALIKIRA UTHENGA WABWINO WONENA ZA DIPO

6, 7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tikamauza anthu za dipo, tikulalikira uthenga wonena za kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

6 M’dzikoli anthu akachimwa sadandaula chilichonse moti ambiri sadziwa n’komwe kuti akufunika kupulumutsidwa. Koma munthu akamakhala moyo wosaopa Mulungu m’pamenenso amamva mumtima mwake kuti sakusangalala. Ena sadziwanso kuti uchimo n’chiyani, umatikhudza bwanji komanso tingatani kuti tisakhale akapolo ake. Koma akayamba kuphunzira ndi a Mboni m’pamene amamvetsa zonsezi. Anthu amene amamvetsera uthenga wathu amasangalala akadziwa kuti Yehova amatikonda ndipo anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu potumiza Mwana wake kuti adzapereke dipo lotiwombola.—1 Yoh. 4:9, 10.

7 Ponena za Mwana wa Mulunguyu, Paulo analemba kuti: “Kudzera mwa iyeyu [Yesu], tinamasulidwa ndi dipo la magazi ake, inde, takhululukidwa machimo athu, malinga ndi chuma cha kukoma mtima kwake [kwa Mulungu] kwakukulu.” (Aef. 1:7) Nsembe ya dipo imasonyeza kuti Yehova amatikonda kwambiri ndiponso kukoma mtima kwake ndi kwakukulu kwabasi. N’zosangalatsa kudziwa kuti tikakhulupirira nsembeyi, machimo athu amakhululukidwa ndipo sitidziimba mlandu. (Aheb. 9:14) Umenewutu ndi uthenga wabwino wofunika kuuza anthu ena.

TIZITHANDIZA ANTHU KUKHALA PA UBWENZI NDI MULUNGU

8. N’chifukwa chiyani anthufe timafunika kugwirizananso ndi Mulungu?

8 Tiyenera kuuza anthu kuti ali ndi mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Mlengi wathu. Anthu amene sanayambe kukhulupirira nsembe ya Yesu amakhala adani a Mulungu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) N’zosangalatsa kuti nsembe ya Khristu imatithandiza kuti tigwirizanenso ndi Mulungu. Paja Paulo ananena kuti: “Inu amene kale munali otalikirana naye ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa, tsopano wagwirizana nanunso pogwiritsa ntchito thupi lanyama la mwanayo kudzera mu imfa yake.”—Akol. 1:21, 22.

9, 10. Kodi Khristu wapereka udindo wotani kwa abale ake odzozedwa? (b) Kodi a “nkhosa zina” amathandiza bwanji odzozedwa?

9 Paulo ananena kuti Khristu anapatsa odzozedwa “utumiki wokhazikitsanso mtendere.” Pofotokoza utumikiwu, iye anati: “Zinthu zonse n’zochokera kwa Mulungu, amene anatigwirizanitsa ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, ndipo anatipatsa utumiki wokhazikitsanso mtendere. Utumiki wake ndi woti tilengeze kuti Mulungu anali kugwirizanitsa dziko ndi iyeyo kudzera mwa Khristu, moti sanawawerengere anthuwo machimo awo, ndipo watipatsa ifeyo ntchito yolengeza uthenga umenewu wokhazikitsanso mtendere. Chotero ndife akazembe m’malo mwa Khristu, ngati kuti Mulungu akuchonderera anthu kudzera mwa ife. Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti: ‘Gwirizananinso ndi Mulungu.’”—2 Akor. 5:18-20.

10 A “nkhosa zina” amaona kuti ndi mwayi waukulu kuchita utumikiwu limodzi ndi odzozedwa. (Yoh. 10:16) Iwo ali ngati nthumwi za Khristu ndipo amagwira kwambiri ntchito yophunzitsa anthu n’kumawathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Zimene amachitazi n’zofunika kwambiri pa ntchito yochitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.

TIZIUZA ANTHU UTHENGA WOTI MULUNGU AMAMVA MAPEMPHERO

11, 12. Kodi uthenga wakuti Yehova amamva mapemphero ungathandize bwanji anthu?

11 Anthu ambiri amangopemphera chifukwa amaona kuti akapemphera mtima wawo umakhala m’malo. Koma sakhulupirira kuti Mulungu amamva mapemphero awo. Anthu oterewa tiyenera kuwathandiza kudziwa kuti Yehova ndi “Wakumva pemphero.” Davide analemba kuti: “Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu. Zolakwa zanga zandikulira. Inu mudzatikhululukira machimo athu.”—Sal. 65:2, 3.

12 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati mutapempha chilichonse m’dzina langa, ine ndidzachichita.” (Yoh. 14:14) Mawu akuti “chilichonse” akunena za chilichonse chogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. Yohane anati: “Timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yoh. 5:14) Tiyenera kuphunzitsa anthu kuti adziwe kuti pemphero silimangothandiza kuti maganizo a munthu akhale m’malo. Koma lingatithandize kuti tiyandikire “mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu” wa Yehova. (Aheb. 4:16) Tikawaphunzitsa kuti azipemphera kwa Yehova, moyenera komanso azipempha zinthu zoyenera, tingawathandize kuti akhale naye pa ubwenzi ndiponso azilimbikitsidwa pa nthawi ya mavuto.—Sal. 4:1; 145:18.

M’DZIKO LATSOPANO MULUNGU ADZATISONYEZANSO KUKOMA MTIMA KWAKUKULU

13, 14. (a) Kodi Akhristu odzozedwa adzakhala ndi mwayi wotani? (b) Kodi odzozedwa adzagwira ntchito yofunika iti yokhudza anthu?

13 Yehova adzasonyezanso anthu kukoma mtima kwake kwakukulu m’dziko latsopano. Paulo anatchula za mwayi umene a 144,000, amene asankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba, ali nawo. Iye anati: “Mulungu, amene ndi wachifundo chochuluka, mwachikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, anatikhalitsa amoyo pamodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa m’machimo, (pakuti inu mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu) ndipo anatikweza pamodzi, ndi kutikhazika pamodzi m’malo akumwamba mogwirizana ndi Khristu Yesu. Anachita zimenezi kuti mu nthawi zimene zikubwera padzasonyezedwe chuma chopambana cha kukoma mtima kwake kwakukulu kumene anatisonyeza mogwirizana ndi Khristu Yesu.”​—Aef. 2:4-7.

14 Pali madalitso ambiri amene Yehova wasungira odzozedwa kumwamba akadzakhala m’mipando yachifumu n’kumalamulira limodzi ndi Khristu. (Luka 22:28-30; Afil. 3:20, 21; 1 Yoh. 3:2) Yehova ‘adzawasonyeza chuma chopambana cha kukoma mtima kwake kwakukulu.’ Odzozedwawa adzakhala “Yerusalemu Watsopano” kapena kuti mkazi wophiphiritsa wa Khristu. (Chiv. 3:12; 17:14; 21:2, 9, 10) Iwo limodzi ndi Yesu adzagwira ntchito ‘yochiritsa mitundu ya anthu,’ kutanthauza kuti adzawathandiza kuti amasuke ku uchimo ndi imfa n’kukhala angwiro.—Werengani Chivumbulutso 22:1, 2, 17.

15, 16. Kodi Yehova adzawasonyeza bwanji a “nkhosa zina” kukoma mtima kwake m’dziko latsopano?

15 Lemba la Aefeso 2:7 limati Mulungu adzasonyeza kukoma mtima kwakukulu “mu nthawi zimene zikubwera.” Choncho aliyense amene adzakhale padziko lapansi pa nthawiyo ‘adzasonyezedwa kukoma mtima kwakukulu’ kwa Yehova. (Luka 18:29, 30) Njira ina imene Yehova adzachitire zimenezi ndi kuukitsa anthu amene ali “m’Manda.” (Yobu 14:13-15; Yoh. 5:28, 29) Anthu okhulupirika amene anamwalira Khristu asanatifere adzaukitsidwa n’kuyambanso kutumikira Yehova. Nawonso a “nkhosa zina” amene amamwalira ali okhulupirika m’masiku otsiriza ano, adzaukitsidwa.

16 Anthu ambirimbiri amene anamwalira asanadziwe Mulungu nawonso adzaukitsidwa. Yohane analemba kuti: “Ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo. Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense wa iwo anaweruzidwa malinga ndi ntchito zake.” (Chiv. 20:12, 13) Anthuwa adzapatsidwa mwayi wosankha kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Kuti athe kuchita zimenezi, adzaphunzitsidwa za Yehova komanso zimene angachite kuti azitsatira mfundo zake zolungama. Komanso adzafunika kutsatira malangizo a ‘m’mipukutu’ amene adzafotokoze zimene Yehova adzafune kuti tizichita m’dziko latsopanolo. Malangizo amenewo adzasonyezanso kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.

PITIRIZANI KULALIKIRA UTHENGA WABWINO

17. Nthawi zonse tikamalalikira, tizikumbukira chiyani?

17 Popeza mapeto ali pafupi kwambiri, cholinga chathu chachikulu ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Maliko 13:10) Paja takambirana kuti uthenga wabwinowu umasonyeza kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Nthawi zonse tikamalalikira tizikumbukira zimenezi. Tizikumbukiranso kuti cholinga chathu ndi kulemekeza Yehova. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuuza anthu kuti zabwino zonse zimene zidzachitike m’dziko latsopano zidzatheka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.

Muzilalikira mwakhama monga “oyang’anira abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.”​—1 Pet. 4:10 (Onani ndime 17-19)

18, 19. Kodi timauza bwanji anthu za kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova?

18 Tikamalalikira tizifotokozera anthu kuti mu Ufumu wa Khristu anthu adzapindula kwambiri ndi nsembe ya dipo ndipo kenako adzakhala angwiro. Baibulo limati: “Chilengedwecho chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Zonsezi zidzatheka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.

19 Tilinso ndi mwayi waukulu wouza anthu lonjezo losangalatsa lopezeka m’buku la Chivumbulutso. Baibulo limasonyeza kuti, “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Ndiyeno Yehova wokhala pampando wachifumu anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” Iye ananenanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.” (Chiv. 21:4, 5) Tikamachita khama kuuza anthu uthenga wabwino umenewu, timakhala kuti tikuwauza za kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova.