Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tiziyamikira Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu

Tiziyamikira Kukoma Mtima Kwakukulu kwa Mulungu

“Tonsefe tinalandira . . . kukoma mtima kwakukulu kosefukira.”—YOH. 1:16.

NYIMBO: 95, 13

1, 2. (a) Fotokozani fanizo la Yesu la munthu wolima munda wa mpesa. (b) Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu?

TSIKU lina m’mawa, munthu wolima mpesa anapita pamsika kukafufuza aganyu. Atapeza anthu anagwirizana nawo zoti akalime komanso mtengo wake. Munthuyo ankafunabe aganyu ena choncho anapitanso kumsika kuja maulendo angapo ndipo ankatenga anthu ena n’kupita nawo kumundako. Pofika madzulo, anapereka malipiro ofanana kwa anthu onse kaya anawapeza m’mawa, masana kapena madzulo. Anthu amene anayamba ntchito m’mawa aja ataona zimenezi anayamba kudandaula. Ndiyeno mwinimundayo anawafunsa kuti, ‘Kodi malipiro amene ndakupatsani si amene tinagwirizana? Kodi n’kosaloleka kuchita zimene ndikufuna ndi zinthu zanga? Kapena mukuchita nsanje chifukwa chakuti ndine wabwino?’—Mat. 20:1-15.

2 Nkhaniyi ikutikumbutsa za “kukoma mtima kwakukulu” kwa Yehova. [1] (Werengani 2 Akorinto 6:1.) Anthu amene anangogwira ntchito ola limodzi aja, sankayenera kulandira malipiro a tsiku lonse. Koma mwinimundayo anawasonyeza kukoma  mtima kwapadera. M’Mabaibulo ambiri mawu oti kukoma mtima kwakukulu anawamasulira kuti “chisomo.” Katswiri wina analemba kuti: “Mawu amenewa amatanthauza kupereka mphatso kwa munthu amene sakuyenera kuilandira kapena kukomera mtima munthu amene sakuyenera kumukomera mtima.”

MPHATSO YAMTENGO WAPATALI IMENE YEHOVA ANATIPATSA

3, 4. Kodi Yehova anatisonyeza bwanji kukoma mtima kwakukulu ndipo anachita bwanji zimenezi?

3 Baibulo limanena kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndi “mphatso yaulere.” (Aef. 3:7) Anthufe tikanakhala kuti timatha kuchita bwinobwino zonse zimene Mulungu amafuna, bwenzi kuli koyeneradi kuti azitisonyeza kukoma mtima kwakukulu. Koma vuto ndi loti nthawi zina timalakwitsa. Mfumu Solomo analemba kuti: “Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.” (Mlal. 7:20) Nayenso mtumwi Paulo anati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” Ananenanso kuti: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” (Aroma 3:23; 6:23a) Choncho tonsefe timayenera kufa basi.

4 Koma Yehova amatikonda kwambiri ndipo anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu. Anatumiza “Mwana wake wobadwa yekha” kuti adzatifere ndipo iyi ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. (Yoh. 3:16) Mtumwi Paulo analemba kuti Yesu anavekedwa “ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anazunzika mpaka imfa. Zimenezi zinamuchitikira kuti mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Aheb. 2:9) Choncho “mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23b.

5, 6. Kodi chimachitika n’chiyani tikamalamuliridwa ndi (a) uchimo? (b) kukoma mtima kwakukulu?

5 Kodi uchimo ndi imfa zinayamba bwanji? Baibulo limati: “Chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo [Adamu] imfa inalamulira monga mfumu.” (Aroma 5:12, 14, 17) Uchimowu ukulamulira ana onse a Adamu ndipo umachititsa kuti tizifa. Komabe tingathe kusankha kuti uchimo usamatilamulire. Tikamakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu timayamba kulamuliridwa ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Baibulo limati: “Pamene uchimo unawonjezeka, kukoma mtima kwakukulu kunasefukiranso. Chifukwa chiyani? Kuti mmene uchimo unalamulira monga mfumu pamodzi ndi imfa, momwemonso kukoma mtima kwakukulu kulamulire monga mfumu kudzera m’chilungamo. Zimenezi zichitike kuti moyo wosatha ubwere kudzera mwa Yesu Khristu.”—Aroma 5:20, 21.

6 Ngakhale kuti ndife ochimwa, sitiyenera kulola kuti uchimo uzitilamulira. Koma tikachimwa mwangozi tizipempha Yehova kuti atikhululukire. Paulo anachenjeza Akhristu kuti: “Uchimo usakhale mbuye kwa inu, chifukwa simuli pansi pa chilamulo koma pansi pa kukoma mtima kwakukulu.” (Aroma 6:14) Kodi chimachitika n’chiyani tikamalamuliridwa ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu? Paulo ananena kuti ‘kukoma mtima kwake kwakukulu kwatiphunzitsa kukana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko, koma kukhala amaganizo abwino, achilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’nthawi ino.’—Tito 2:11, 12.

MULUNGU AMATISONYEZA KUKOMA MTIMA KWAKUKULU “M’NJIRA ZOSIYANASIYANA”

7, 8. Kodi mawu oti Yehova amatisonyeza kukoma mtima m’njira zosiyanasiyana amatanthauza chiyani? (Onani chithunzi patsamba 21.)

7 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Molingana  ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana monga oyang’anira abwino amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene wakusonyeza m’njira zosiyanasiyana.” (1 Pet. 4:10) Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Ponena kuti Yehova watisonyeza kukoma mtima m’njira zosiyanasiyana, ankatanthauza kuti Yehova akhoza kutithandiza kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo. (1 Pet. 1:6) Nthawi zonse iye amatisonyeza kukoma mtima mogwirizana ndi vuto limene takumana nalolo.

8 N’zoonadi kuti Yehova amatisonyeza kukoma mtima m’njira zosiyanasiyana. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Pakuti tonsefe tinalandira zinthu kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo. Tinalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira.” (Yoh. 1:16) Yehova akatisonyeza kukoma mtima m’njira zosiyanasiyana, timapeza madalitso ambiri. Tiyeni tsopano tikambirane ena mwa madalitsowa.

9. Kodi kukoma mtima kwakukulu kwa Yehova kumatithandiza bwanji, nanga tingasonyeze bwanji kuyamikira?

9 Timakhululukidwa machimo. Yehova amatikhululukira machimo athu chifukwa cha kukoma mtima kwake. Koma chofunika n’kulapa komanso kuyesetsa kulimbana ndi mtima wofuna kuchita machimo. (Werengani 1 Yohane 1:8, 9.) Popeza Mulungu amatisonyeza chifundo chonchi, tiyenera kumuyamikira komanso kumulemekeza. Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Iye [Yehova] anatilanditsa ku ulamuliro wa mdima, n’kutisamutsira mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo, kutanthauza kuti machimo athu anakhululukidwa.” (Akol. 1:13, 14) Tikakhululukidwa machimo timapezanso madalitso ambirimbiri.

10. Kodi ndi madalitso ati amene timapeza chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu?

10 Timakhala pa ubwenzi ndi Yehova. Uchimo umachititsa kuti munthu aliyense azibadwa ali mdani wa Mulungu. Paulo anasonyeza zimenezi polemba kuti: “Pamene tinali adani, tinayanjanitsidwa kwa Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake.” (Aroma 5:10) Tikayanjanitsidwa ndi Mulungu timakhala naye pa mtendere. Paulo anasonyezanso kuti izi zimatheka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Yehovayo. Ponena za iyeyo ndi odzozedwa anzake, analemba kuti: “Chotero, popeza tsopano tayesedwa olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro, tiyeni tikhale pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Mwa ameneyunso, ndiponso chifukwa cha chikhulupiriro, takhala ndi ufulu wolowa m’kukoma mtima kwakukulu, mmene tilimo tsopano.” (Aroma 5:1, 2) Kunena zoona awatu ndi madalitso osaneneka.

Mulungu watisonyezera kukoma mtima m’njira zotsatirazi: Amatithandiza kuti timve uthenga wabwino (Onani ndime 11)

11. Kodi odzozedwa amathandiza bwanji a “nkhosa zina” kukhala olungama?

11 Yehova amationa kuti ndife olungama. Mwachibadwa anthufe ndife osalungama. Koma mneneri Danieli ananeneratu kuti m’masiku otsiriza ‘anthu ozindikira [odzozedwa amene ali padzikoli] adzathandiza anthu ambiri kukhala olungama.’ (Werengani Danieli 12:3.) Ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa yathandiza a “nkhosa zina” ambirimbiri kukhala olungama pamaso pa Yehova. (Yoh. 10:16) Zonsezi zikuchitika chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Paulo ananena kuti: “Kuyesedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu, kuli ngati mphatso yaulere.”—Aroma 3:23, 24.

Amatilola kuti tizipemphera kwa iye (Onani ndime 12)

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti pemphero ndi njira ina imene Yehova watisonyezera kukoma mtima?

12 Timapemphera kwa Mulungu momasuka. Yehova watisonyezanso kukoma mtima  kwakukulu potilola kuti tizipemphera kwa iye. Paja Paulo ananena kuti mpando wachifumu wa Yehova ndi “mpando wachifumu wa kukoma mtima kwakukulu” ndipo anati tiyenera kuyandikira mpandowo “ndi ufulu wa kulankhula.” (Aheb. 4:16a) Kuti zimenezi zitheke, Yehova watipatsa Mwana wake ndipo “kudzera mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula ndiponso njira yofikira Mulungu popanda kukayikira pokhala ndi chikhulupiriro mwa Yesuyo.” (Aef. 3:12) Apa tinganenedi kuti Yehova watisonyeza kukoma mtima kwakukulu.

Amatithandiza tikavutika (Onani ndime 13)

13. Kodi Yehova amatithandiza bwanji “pa nthawi imene tikufunika thandizo”?

13 Amatithandiza tikavutika. Paulo ananena kuti tiyenera kupemphera momasuka kwa Yehova kuti “atichitire chifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:16b) Pa nthawi iliyonse imene tapanikizika ndi mavuto tingathe kupemphera kwa Yehova kuti atichitire chifundo n’kutithandiza. Mwa chisomo chake amatiyankha ndipo nthawi zambiri amagwiritsira ntchito Akhristu anzathu. Izi zimatithandiza kuti “tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”—Aheb. 13:6.

14. Kodi Yehova amatithandizanso bwanji?

14 Amatilimbikitsa. Yehova amatilimbikitsanso tikakhala ndi nkhawa. (Sal. 51:17) M’kalata imene Paulo analembera Atesalonika amene ankazunzidwa, ananena kuti: “Ambuye wathu Yesu Khristu mwiniyo, ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ndipo amatilimbikitsa m’njira yosalephera ndiponso anatipatsa chiyembekezo chabwino, mwa kukoma mtima kwakukulu, alimbikitse mitima yanu ndi kukulimbikitsani.” (2 Ates. 2:16, 17) Timayamikira kwambiri kuti Yehova ndi wokoma mtima ndipo amatilimbikitsa mwachikondi.

15. Tchulani chiyembekezo chimene tili nacho chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.

15 Amatipatsa chiyembekezo cha moyo  wosatha. Anthu ochimwafe tinalibe chiyembekezo chilichonse. (Werengani Salimo 49:7, 8.) Koma Yehova watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri. Paja Yesu analonjeza otsatira ake kuti: “Chifuniro cha Atate wanga ndi chakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupirira mwa iye akhale nawo moyo wosatha.” (Yoh. 6:40) Kunena zoona, chiyembekezo chimenechi ndi mphatso yamtengo wapatali imene timaipeza chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. Paulo ankadziwa bwino mfundo imeneyi ndipo anati: “Mulungu waonetsa kukoma mtima kwake kwakukulu kumene kumabweretsa chipulumutso kwa anthu, kaya akhale a mtundu wotani.”—Tito 2:11.

TISAGWIRITSE NTCHITO MOLAKWIKA KUKOMA MTIMA KWA MULUNGU

16. Perekani umboni wosonyeza kuti Akhristu ena ankagwiritsa ntchito molakwika kukoma mtima kwa Mulungu.

16 Taona kuti timapeza madalitso ambiri chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu. Koma sitiyenera kugwiritsa ntchito molakwika kukoma mtima kumeneku. Kalelo panali Akhristu ena amene ankafuna kutenga “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa chochitira khalidwe lotayirira.” (Yuda 4) Iwo ankaganiza kuti akhoza kumachimwa dala kenako n’kupempha Yehova kuti awakhululukire. Chomvetsa chisoni n’chakuti ankakopa Akhristu ena kuti azichitanso zomwezo. Masiku anonso, aliyense wochita zimenezi amanyoza “mzimu wa Mulungu, yemwe amasonyeza kukoma mtima kwakukulu.”—Aheb. 10:29.

17. Kodi Petulo anapereka malangizo amphamvu ati?

17 Masiku ano, Akhristu enanso asocheretsedwa ndi Satana n’kumaganiza kuti akhoza kumangochimwa ndipo Yehova aziwakhululukira. N’zoona kuti Yehova amatikhululukira tikalapa koma amafunanso kuti tizichita khama polimbana ndi mtima wofuna kuchimwa. Paja anauzira Petulo kulemba kuti: “Inu okondedwa, popeza mukudziwiratu zimenezi, chenjerani kuti musasochere pokopeka ndi zolakwa za anthu ophwanya malamulowo, kuopera kuti mungalephere kukhala olimba ndipo mungagwe. Ndithu musatero ayi, koma pitirizani kulandira kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.”—2 Pet. 3:17, 18.

ZIMENE TIYENERA KUCHITA

18. Popeza Yehova watisonyeza kukoma mtima kwakukulu, kodi tiyenera kuchita chiyani?

18 Popeza Yehova amatisonyeza kukoma mtima kwakukulu tiyenera kumulemekeza komanso kuthandiza anzathu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Paulo ananena kuti: “Tili ndi mphatso zosiyanasiyana mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu kumene tinapatsidwa. . . . Ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni tichitebe utumikiwo. Amene akuphunzitsa, aziphunzitsa ndithu. Wochenjeza, aike mtima wake pa kuchenjeza. . . . Ndipo wosonyeza chifundo, achite zimenezo mokondwa.” (Aroma 12:6-8) Yehova watisonyezadi kukoma mtima. Choncho tiyenera kugwira ntchito yolalikira, kulimbikitsa Akhristu anzathu komanso kukhululukira aliyense amene watilakwira.

19. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Tiyeni tonse tiziyamikira Mulungu chifukwa cha chikondi chake. Tiziyesetsanso “kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (Mac. 20:24) M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene tingachitire zimenezi.

^ [1] (ndime 2) Onani mawu akuti, “Kukoma mtima kwakukulu” pakamutu kakuti “Matanthauzo a Mawu Ena” patsamba 1969 m’Baibulo la Dziko Latsopano.