Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Luso Loona Zinthu M’maganizo Mwathu

Luso Loona Zinthu M’maganizo Mwathu

UBONGO wa munthu umangolemera pafupifupi kilogalamu imodzi ndi hafu koma zimene umachita n’zodabwitsa kwambiri. Anthufe tikadziwa zambiri zokhudza ubongo, timayamba kumvetsa mfundo yakuti ntchito za Yehova “ndi zodabwitsa.” (Sal. 139:14) Mwachitsanzo, ubongo umatithandiza kuona zinthu m’maganizo mwathu.

Nthawi zambiri anthufe tikamva zinthu kapena nkhani timatha kuziona m’maganizo mwathu ndipo zina zimakhala zosangalatsa. Mwachitsanzo, kodi munawerengapo kapena kuuzidwa za malo ena amene simunapiteko? Muyenera kuti munkatha kuona malowo m’maganizo mwanu. Tonsefe timatha kuyerekezera m’maganizo mwathu zinthu zimene sitinazimvepo, sitinazionepo, sitinazilawepo, sitinazigwirepo komanso sitinamvepo fungo lake.

Baibulo limanena kuti anthufe tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Gen. 1:26, 27) Izi zikusonyeza kuti nayenso Yehova amatha kuona zinthu m’maganizo mwake. Popeza iye ndi amene anatipatsa luso limeneli, ayenera kuti amafuna tiziligwiritsa ntchito kuti timvetse zolinga zake. (Mlal. 3:11) Komabe tiyenera kupewa kugwiritsa ntchito mosayenera luso limeneli n’kumayesetsa kuligwiritsa ntchito bwino. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

TIZIPEWA KUGWIRITSA NTCHITO LUSOLI MOSAYENERA

(1) Tisamaganizire zinthu zolakwika kapena pa nthawi yosayenera.

Kuganizira zinthu zina si kolakwika ngati kukuchitika pa nthawi yoyenera. Tikutero chifukwa choti lemba la Mlaliki 3:1 limati chinthu “chilichonse chili ndi nthawi yake.” Koma zikhoza kutheka kuyamba kuganizira zinthu zina pa nthawi yolakwika. Mwachitsanzo, kodi ndi nzeru kuti maganizo athu aziyendayenda tikakhala pamisonkhano ndiponso tikamaphunzira patokha? Komanso nthawi zina tikhoza kuyamba kuganizira zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, Yesu anapereka chenjezo pa nkhani yoganizira zinthu zolakwika monga zachiwerewere. (Mat. 5:28). Ndipo munthu amene amakonda kuganizira zachiwerewere akhoza kuchitadi. Choncho tisalole kuti zimene timaganiza zitilepheretse kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.

(2) Tisamaganize kuti chuma chingatiteteze.

Chuma chimathandiza koma tikhoza kukhumudwa tikamaganiza kuti chumacho chingatiteteze komanso kutipangitsa kukhala osangalala. Paja Solomo analemba kuti: “Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma ndizo mzinda wake wolimba, ndipo m’maganizo mwake zili ngati mpanda woteteza.” (Miy. 18:11) Taganizirani zimene zinachitika ku Manila m’dziko la Philippines mu September 2009. Madzi anasefukira ndipo anawononga zinthu zambiri. Kodi anthu olemera anatetezedwa ndi chuma chawo? Ayi ndithu. Munthu wina amene chuma chake chambiri chinawonongeka anati: “Madzi osefukira anachititsa kuti olemera ndi osauka afanane chifukwa onse ankavutika.” Choncho si zoona kuti chuma chingatiteteze.

(3) Tisamadere nkhawa zinthu zimene mwina sizingachitike n’komwe.

Yesu ananena kuti tisamade nkhawa kwambiri za tsiku lotsatira. (Mat. 6:34) Munthu akamangoganizira zinthu zoipa zimene mwina sizingachitike amakhala wankhawa nthawi zonse. Anthufe tikhoza kufooka chifukwa chodera nkhawa zinthu zimene sizinachitike ndipo mwina sizidzachitika n’komwe. Malemba amasonyeza kuti munthu akhoza kutaya mtima kapenanso kudwala chifukwa cha nkhawa zoterezi. (Miy. 12:25) Choncho ndi nzeru kumvera malangizo a Yesu akuti tisamadere nkhawa kwambiri za mawa.

TIZIGWIRITSA NTCHITO LUSOLI MOYENERA

(1) Tizioneratu m’maganizo mwathu zinthu zoipa n’kuzipewa.

Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziganizira zotsatira za zinthu zoipa. (Miy. 22:3) Tikamatero tikhoza kuoneratu mavuto amene angabwere tikasankha kuchita zinthu zinazake. Mwachitsanzo, ngati mwaitanidwa kuti mukacheze kwinakwake, mungagwiritse ntchito luso loona zinthu m’maganizo mwanu n’kudziwa ngati n’koyenera kupita kapena ayi. Mungaganizire anthu amene aitanidwa, kuchuluka kwa anthuwo komanso malo ndi nthawi yake. Ndiyeno dzifunseni kuti: Kodi kumeneko kukachitika zotani? Kodi zikakhala zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo? Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kudziwiratu zimene zikachitike ku phwandolo. Tikamagwiritsa ntchito mwanzeru luso loona zinthu m’maganizo mwathu, tikhoza kupewa zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.

(2) Tiziganizira zimene tingachite tikakumana ndi mavuto.

Luso lotha kuona zinthu m’maganizo lingatithandizenso kuthana ndi mavuto. Tiyerekeze kuti mwasemphana maganizo ndi munthu wina mumpingo. Kodi mungatani kuti muyambenso kugwirizana naye? Pali zinthu zingapo zimene muyenera kuziganizira. Kodi munthuyo amalankhula bwanji? Kodi nthawi yabwino yolankhula naye ingakhale iti? Mungaganizirenso mawu amene mukanene komanso mmene mukawanenere. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kupeza njira yabwino yokambirana naye. (Miy. 15:28) Izi zingathandize kuti mumpingo mukhale mtendere.

(3) Tiziganizira kwambiri zimene taphunzira m’Baibulo.

Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse n’kofunika kwambiri. Koma kungowerenga si kokwanira. Tiziyesetsa kumvetsa zimene tikuphunzirazo komanso kuona mmene tingazigwiritsire ntchito pa moyo wathu. Tikamachita khama kuphunzira Baibulo timamvetsa bwino mmene Yehova amachitira zinthu. Ndiyeno luso lotha kuona zinthu m’maganizo mwathu lingatithandize kumvetsa bwino zimene tikuphunzira. Tiyerekeze kuti mukuwerenga buku lakuti, Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo. Nkhani za m’bukuli zimatithandiza kuona m’maganizo mwathu anthu otchulidwa m’Baibulo komanso zimene zinawachitikira. Timatha kuona malo amene zinthuzo zinachitikira komanso kumva phokoso ndi fungo lomwe linalipo. Timathanso kuzindikira mmene anthuwo ankamvera. Izi zimathandiza chifukwa timaphunzira zambiri m’nkhaniyo komanso imatilimbikitsa ngakhale zitakhala kuti tinkaidziwa kale.

(4) Tiziyesetsa kukhala achifundo.

Munthu wachifundo amayesetsa kumva mumtima mwake mmene munthu wina akumvera. Yehova ndi Yesu ali ndi khalidweli ndipo tiyenera kuwatsanzira. (Eks. 3:7; Sal. 72:13) Ndiye kodi tingawatsanzire bwanji? Apanso tingathe kugwiritsa ntchito luso loona zinthu m’maganizo mwathu. Tikhoza kukhala kuti sitinakumanepo ndi mavuto amene m’bale kapena mlongo wina akukumana nawo. Komabe tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndikanakhala ine ndikanamva bwanji? Nanga ndikanafuna kuti ena andichitire chiyani?’ Tikadzifunsa mafunsowa tikhoza kumvetsa mmene munthuyo akumvera. Zimenezi zingatithandize kuti tizichitira chifundo Akhristu anzathu komanso anthu amene timakumana nawo mu utumiki.

(5) Tiziganizira mmene zinthu zidzakhalire m’dziko latsopano.

Pali malemba ambiri amene amanena za mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso. (Yes. 35:5-7; 65:21-25; Chiv. 21:3, 4) M’mabuku athu muli zithunzi zotithandiza kuona zinthu zimenezi m’maganizo mwathu. Izi zimatithandiza kudziwa kuti tidzasangalala kwambiri malonjezowa akadzakwaniritsidwa. Yehova amadziwa bwino za luso loona zinthu m’maganizo popeza iye ndi amene anatipatsa lusoli. Kugwiritsa ntchito luso limeneli n’kumaganizira zimene iye watilonjeza, kungatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri kuti malonjezowo adzakwaniritsidwadi. Kungatithandizenso kuti tikhalebe okhulupirika komanso kuti tizipirira tikakumana ndi mavuto.

Tiziyamikira Yehova potipatsa luso lotha kuona zinthu m’maganizo mwathu. Luso limeneli lingatithandize kuti tizimutumikira mokhulupirika. Choncho tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira lusoli poligwiritsa ntchito moyenera.