NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) April 2016

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira May 30 mpaka June 26, 2016.

Kodi Utumiki Wanu Uli Ngati Mame?

Kodi tingatani kuti utumiki wathu uzikhala ngati mame, omwe amagwa pang’onopang’ono, amasangalatsa komanso amathandiza kuti zomera zisafe?

Yehova Amadalitsa Anthu Okhulupirika

Kodi Akhristu angaphunzire chiyani pa nkhani ya m’Baibulo ya Yefita ndi mwana wake wamkazi?

Luso Loona Zinthu M’maganizo Mwathu

Lingakubweretsereni mavuto kapena kukuthandizani kukhala munthu wabwino.

“Mulole Kuti Kupirira Kumalize Kugwira Ntchito Yake”

Tikakumana ndi mavuto n’kukhalabe okhulupirika timasonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira. Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zingakuthandizeni kupirira?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusonkhana?

Tikamasonkhana timalimbikitsidwa, timalimbikitsa ena komanso Yehova amasangalala.

MBIRI YA MOYO WANGA

Masisitere Anasintha N’kukhala Alongo

N’chiyani chinawapangitsa kuchoka pamalo a masisitere kenako n’kusiya chipembedzo chawo chachikatolika?

Musakhale Mbali ya Dzikoli

Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kukonzekera mavuto okhudza kulowerera ndale.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi odzozedwa amalandira bwanji chikole nanga amadindidwa bwanji chidindo?