Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 13

Muzigwiritsa Ntchito Chilengedwe Pophunzitsa Ana Anu Zokhudza Yehova

Muzigwiritsa Ntchito Chilengedwe Pophunzitsa Ana Anu Zokhudza Yehova

“Kodi ndani amene analenga zinthu zimenezo?”​—YES. 40:26.

NYIMBO NA. 11 Chilengedwe Chimatamanda Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi makolo amafunitsitsa kuchitira chiyani ana awo?

 MAKOLO, timadziwa kuti mumafuna kuphunzitsa ana anu kuti adziwe komanso kuyamba kukonda Yehova. Komatu Mulungu ndi wosaoneka. Ndiye kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azimuona kuti iye ndi weniweni komanso akhale naye pa ubwenzi?​—Yak. 4:8.

2. Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo zokhudza makhalidwe a Yehova?

2 Njira yofunika kwambiri yothandizira ana anu kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova ndi kuphunzira nawo Baibulo. (2 Tim. 3:14-17) Koma Baibulo limatchulanso njira ina imene angaphunzirire zokhudza Yehova. M’buku la Miyambo, zikuoneka kuti bambo akukumbutsa mwana wake wamwamuna kuti asasiye kuganizira makhalidwe a Yehova omwe amasonyezedwa m’chilengedwe. (Miy. 3:19-21) Tiona mmene makolo angagwiritse ntchito chilengedwe pothandiza ana awo kuphunzira makhalidwe a Yehova.

KODI MUNGAGWIRITSE NTCHITO BWANJI CHILENGEDWE POPHUNZITSA ANA ANU?

3. Kodi makolo ayenera kuthandiza ana awo kuchita chiyani?

3 Baibulo limati “chilengedwere dziko kupita m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.” (Aroma 1:20) Makolo, n’zosachita kufunsa kuti mumasangalala kupita koyenda ndi ana anu. Muzigwiritsa ntchito mpata umenewu powathandiza kuona kugwirizana pakati pa “zimene [Yehova] anapanga” ndi makhalidwe ake ochititsa chidwi. Pa nkhaniyi, tiyeni tione zimene makolo angaphunzire pa chitsanzo cha Yesu.

4. Kodi Yesu anagwiritsira ntchito bwanji chilengedwe pophunzitsa ophunzira ake? (Luka 12:24, 27-30)

4 Taonani mmene Yesu anagwiritsira ntchito chilengedwe pophunzitsa. Pa nthawi ina iye anauza ophunzira ake kuti aonetsetse makwangwala komanso maluwa. (Werengani Luka 12:24, 27-30.) Yesu akanatha kutchula nyama kapena zomera zilizonse koma anasankha kutchula mbalame ndi maluwa, zinthu zimene ophunzira akewo ankazidziwa bwino. N’kutheka kuti ophunzirawo ankaona makwangwala akamauluka komanso maluwa akamaphuka. Yerekezerani kuti mukuona Yesu akuloza zinthu zimenezi pamene akulankhula. Ndiye kodi anatani atatchula zitsanzozi? Iye anaphunzitsa ophunzirawo mfundo yofunika kwambiri yokhudza kukoma mtima komanso kuwolowa manja kwa Atate wawo wakumwamba. Yehova adzaonetsetsa kuti atumiki ake okhulupirika ali ndi chakudya komanso zovala monga mmene amasamalirira makwangwala ndi maluwa.

5. Kodi ndi zinthu ngati ziti m’chilengedwe zomwe makolo angagwiritse ntchito pophunzitsa ana awo zokhudza Yehova?

5 Makolo, kodi mungatsanzire bwanji mmene Yesu ankaphunzitsira? Mungauze mwana wanu zokhudza chinthu chinachake chomwe mumakonda m’chilengedwe, monga nyama kapena chomera. Mukamachita zimenezo, muzionetsetsa kuti mukumuuza mmene chinthucho chimatithandizira kudziwa zokhudza Yehova. Kenako mungamufunse kuti akuuzeni nyama kapena chomera chomwe amachikonda. N’kutheka kuti angamvetsere mwatcheru ngati mukufotokoza zokhudza makhalidwe a Yehova pogwiritsa ntchito chinthu chinachake m’chilengedwe, chomwe iyeyo amachikonda.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha amayi ake a Christopher?

6 Kodi makolo amayenera kuthera nthawi yambiri akufufuza za nyama kapena chomera chinachake asanakambirane ndi mwana wawo mmene chinthucho chimatithandizira kudziwa zokhudza Yehova? Osati kwenikweni. Yesu sanafotokoze zambiri zokhudza mmene makwangwala amadyera kapenanso mmene maselo a maluwa alili. N’zoona kuti nthawi zina mwana wanu angamasangalale kukambirana mozamirapo zokhudza chilengedwe. Koma nthawi zina zimakhala zokwanira kufunsa funso losavuta kapena kukambirana mwachidule zimene mwaona. M’bale wina dzina lake Christopher amakumbukirabe zomwe zinkachitika ali wamng’ono ndipo anati: “Mayi anga ankatha kungolankhula mfundo zochepa pofuna kutithandiza kuti tiziyamikira zinthu zam’chilengedwe zomwe tinkaona. Mwachitsanzo, tikakhala pafupi ndi mapiri ankatha kunena kuti, ‘Taonani phiri lalikulu ndi lokongolali. Yehova ndi wodabwitsa eti!’ Kapenanso tikakhala pafupi ndi nyanja ankatha kunena kuti, ‘Taonani mafunde amphamvuwa. Koma ndiye Mulungu ndi wamphamvutu!’” Christopher anati: “Mawu achidule koma okuthandiza kuganizawa ankatikhudza kwambiri.”

7. Kodi mungaphunzitse bwanji ana kuti aziganizira zinthu zachilengedwe?

7 Ana anu akamakula muziwaphunzitsa kuti aziganizira zokhudza chilengedwe n’kumaona mmene chikuwathandizira kudziwa makhalidwe a Yehova. Mungawafotokozere chinthu chimodzi chomwe Mulungu analenga n’kuwafunsa kuti, “Kodi chinthu chimenechi chikukuphunzitsani chiyani zokhudza makhalidwe a Yehova?” Mungadabwe kwambiri kumva zinthu zomwe angakufotokozereni.​—Mat. 21:16.

KODI NDI LITI POMWE TINGAGWIRITSE NTCHITO CHILENGEDWE POPHUNZITSA ANA ATHU?

8. Kodi makolo a Chiisiraeli ankakhala ndi mipata yotani poyenda “pamsewu”?

8 Makolo a Chiisiraeli ankalimbikitsidwa kuti aziphunzitsa ana awo malamulo a Yehova poyenda “pamsewu.” (Deut. 11:19) M’madera a kumidzi ku Isiraeli kunali misewu imene anthu ankayendamo. Anthu akamayenda ankatha kuona nyama zosiyanasiyana, mbalame komanso maluwa. Mabanja a Chiisiraeli akamayenda m’misewuyi, makolo ankakhala ndi mipata yambiri yothandiza ana awo kuti azichita chidwi ndi chilengedwe cha Yehova. Mosakayikira, inunso makolo muli ndi mipata ngati imeneyi yophunzitsa ana anu pogwiritsa ntchito chilengedwe. Tiyeni tione mmene makolo ena achitira zimenezi.

9. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Punitha ndi Katya?

9 Mayi wina dzina lake Punitha, yemwe amakhala mumzinda waukulu ku India, ananena kuti: “Tikamapita kukaona achibale kumudzi, timaona kuti umenewu ndi mwayi woti tiphunzitse ana athu zokhudza chilengedwe chochititsa chidwi cha Yehova. Ndimaona kuti ana anga amamvetsa bwino zokhudza chilengedwe akakhala kutali ndi mzinda chifukwa sikukhala anthu komanso magalimoto ambiri m’misewu.” Makolo, dziwani kuti ana anu sangadzaiwale nthawi imene munachita nawo zinthu muli ku malo enaake okongola. Mlongo wina wa ku Moldova dzina lake Katya ananena kuti: “Zinthu zosangalatsa zimene ndimakumbukira kwambiri ndi zomwe ndinkachita ndi makolo anga ndili wamng’ono tikapita kumudzi. Ndimawayamikira kwambiri chifukwa chondiphunzitsa kuyambira ndili wamng’ono kuti ndiziima kaye n’kuona zimene Yehova analenga komanso zimene zinthuzo zikundiphunzitsa zokhudza iye.”

Ngakhale mumzinda, mungapeze zinthu zachilengedwe zomwe mungagwiritse ntchito pophunzitsa ana anu zokhudza Yehova (Onani ndime 10)

10. Kodi makolo angatani ngati n’zovuta kuti apite kutali ndi mzinda? (Onani bokosi lakuti “ Zimene Zingathandize Makolo.”)

10 Bwanji ngati n’zosatheka kuti mupite dera la kumudzi? Amol, yemwenso amakhala ku India ananena kuti: “Kumene ndimakhala, makolo amafunika kugwira ntchito nthawi yaitali komanso angafunike kuwononga ndalama zambiri kuti apite dera la kumudzi. Komabe kupita ku paki yaing’ono kapena kukhala pamalo ochezera padenga kungawathandize kuti aone chilengedwe komanso kukambirana ndi ana awo zokhudza makhalidwe a Yehova.” Ngati mutafufuza mosamala, inunso mukhoza kupeza zinthu zachilengedwe kufupi ndi kumene mumakhala zomwe mungaonetse ana anu. (Sal. 104:24) Mungathe kupeza zinthu ngati mbalame, tizilombo, zomera ndi zina. Karina wa ku Germany ananena kuti: “Mayi anga amakonda maluwa. Choncho ndili wamng’ono, nthawi zonse ndikamayenda nawo ankakonda kundionetsa maluwa okongola.” Makolo, mungagwiritsenso ntchito mabuku ndi mavidiyo ambiri a gulu lathu okhudza chilengedwe pophunzitsa ana anu. Choncho kaya zinthu zili bwanji, mungathandize ana anu kuti azichita chidwi ndi zimene Mulungu anapanga. Tsopano tiyeni tikambirane ena mwa makhalidwe a Yehova omwe mungaphunzitse ana anu.

“MAKHALIDWE [A YEHOVA] OSAONEKA NDI MASO AKUONEKERA BWINO”

11. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuzindikira chikondi cha Yehova?

11 Kuti muthandize ana anu kuzindikira chikondi cha Yehova, mungawafotokozere mmene nyama zambiri zimasamalirira ana awo mwachikondi. (Mat. 23:37) Mungawauzenso zinthu zosiyanasiyana zochititsa chidwi zomwe timasangalala nazo m’chilengedwe. Karina yemwe tamutchula kale uja anati: “Tikamayenda ndi amayi anga, ankandilimbikitsa kuti ndiziima kaye n’kuganizira mmene duwa lililonse lilili losiyana ndi linzake komanso mmene kukongola kwake kukusonyezera chikondi cha Yehova. Panopa papita zaka zambiri, koma ndimachitabe chidwi ndi maluwa osiyanasiyana, mmene anapangidwira komanso mitundu yawo. Maluwawo amandikumbutsabe kuti Yehova amatikonda kwambiri anthufe.”

Mungafotokozere ana anu mmene thupi lathu linalengedwera mochititsa chidwi powaphunzitsa zokhudza nzeru za Mulungu (Onani ndime 12)

12. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuzindikira nzeru za Mulungu? (Salimo 139:14) (Onaninso chithunzi.)

12 Muzithandiza ana anu kuzindikira nzeru ya Mulungu. Yehova ndi wanzeru kwambiri kuposa anthufe. (Aroma 11:33) Mwachitsanzo, mungawafotokozere mmene madzi amapangira mitambo komanso mmene mitamboyo imayendera mosavuta. (Yobu 38:36, 37) Mungawafotokozerenso mmene thupi lathu linapangidwira mochititsa chidwi. (Werengani Salimo 139:14.) Taganizirani mmene bambo wina dzina lake Vladimir anachitira zimenezi. Iye anati: “Tsiku lina mwana wathu anagwa panjinga n’kuvulala. Patapita masiku ochepa balalo linapola. Ine ndi mkazi wanga tinamufotokozera kuti Yehova analenga thupi lathu m’njira yoti lizitha kudzichiritsa lokha. Kenako tinamufotokozera kuti zoterezi sizimachitika ndi zinthu zomwe anthu anapanga. Mwachitsanzo, galimoto siimadzikonza yokha ikachita ngozi. Zimenezi zinathandiza mwana wathuyo kumvetsa kuti Yehova ndi wanzeru.”

13. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuzindikira mphamvu za Mulungu? (Yesaya 40:26)

13 Yehova amatipempha kuti tikweze maso athu kumwamba n’kuganizira mmene mphamvu zake zochititsa chidwi zimathandizira kuti nyenyezi zikhale m’malo ake. (Werengani Yesaya 40:26.) Mungalimbikitse ana anu kuti aziyang’ana kumwamba n’kuganizira zimene akuona. Mlongo wina wa ku Taiwan amakumbukirabe zomwe zinachitika ali mwana, ndipo anati: “Ine ndi amayi anga tinapita kukaona malo ndipo usiku, popanda kusokonezedwa ndi magetsi a mumzinda, tinayang’ana kumwamba. Pa nthawiyi n’kuti ndikuda nkhawa kuti mwina sindipitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika chifukwa anzanga ankandikakamiza kuti ndizichita zoipa. Amayi anandilimbikitsa kuti ndiganizire mphamvu zimene Yehova anagwiritsa ntchito polenga nyenyezi zonsezo, komanso kukumbukira kuti iye angagwiritse ntchito mphamvuzo pondithandiza kuti ndilimbane ndi mayesero alionse. Zinthu zachilengedwe zomwe ndinaona pa ulendo umenewu zinandilimbikitsa kuti ndimudziwe bwino Yehova, ndipo ndinatsimikiza mtima kuti ndipitiriza kumutumikira.”

14. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachimwemwe?

14 Chilengedwe cha Yehova chimasonyeza kuti iye ndi wachimwemwe komanso wanthabwala. Asayansi anapeza kuti nyama zambiri, kuphatikizapo mbalame ndi nsomba, zimasewera. (Yobu 40:20) Kodi nthawi ina ana anu anasekapo ataona nyama inayake ikusewera? N’kutheka kuti iwo anaona mphaka akusewera kapena tiana ta galu tikumenyana. Nthawi ina ana anu akadzaseka poona nyama inayake ikuchita zoseketsa mudzawakumbutse kuti timatumikira Mulungu wachimwemwe.​—1 Tim. 1:11.

MUZISANGALALA NDI CHILENGEDWE CHA YEHOVA MONGA BANJA

Ana anu amakhala omasuka kufotokoza mmene akumvera mukamasangalala ndi zachilengedwe muli nawo limodzi (Onani ndime 15)

15. Kodi n’chiyani chingathandize makolo kuti adziwe zimene ana awo akuganiza? (Miyambo 20:5) (Onaninso chithunzi.)

15 Nthawi zina makolo angamavutike kuti akambirane ndi ana awo mavuto amene anawo amakumana nawo. Ngati umu ndi mmene zilili ndi inu, muyenera kuyesetsa kuti mudziwe maganizo a ana anu. (Werengani Miyambo 20:5.) Makolo ena amaona kuti zimakhala zosavuta kuchita zimenezi akamaona zinthu zachilengedwe limodzi ndi ana awo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti pa nthawiyi sipakhala zinthu zambiri zomwe zingawasokoneze. Bambo wina wa ku Taiwan dzina lake Masahiko anatchulanso chifukwa china. Iye anati: “Tikapita koyenda ndi ana athu, kaya kukakwera mapiri kapena kuyenda mphepete mwa nyanja, nthawi zambiri maganizo awo amakhala okhazikika. Choncho zimakhala zosavuta kudziwa zimene akuganiza.” Katya yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Ndikaweruka kusukulu, amayi ankanditengera ku paki inayake yokongola. Kumalo abata amenewo, sizinkandivuta kuwafotokozera zimene zandichitikira kusukulu komanso zimene zikundidetsa nkhawa.”

16. Kodi mabanja angagwiritse ntchito bwanji chilengedwe kuti apeze mipata yopuma komanso kusangalala?

16 Kuona zimene Yehova analenga kungathandizenso mabanja kupeza nthawi yopuma komanso yosangalala, zomwe zingachititse kuti onse m’banja azigwirizana kwambiri. Baibulo limanena kuti pali “nthawi yoseka” komanso “nthawi yodumphadumpha mosangalala.” (Mlal. 3:1, 4) Yehova anapanga malo ambiri okongola omwe tingakasangalaleko. Mabanja ambiri amakonda kupita kumalo osungirako zachilengedwe, madera a kumidzi, kumapiri kapenanso kunyanja. Ana ambiri amakonda kuthamanga komanso kusewera m’mapaki, kuona nyama komanso kusambira m’mitsinje kapena m’nyanja. Tilitu ndi mipata yambiri yosangalala ndi zimene Yehova analenga.

17. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuthandiza ana awo kuti azisangalala ndi chilengedwe cha Mulungu?

17 M’dziko latsopano la Mulungu, makolo ndi ana adzasangalala ndi chilengedwe cha Yehova kuposa kale lonse. Mosiyana ndi masiku ano, sitizidzaopa nyama ndipo nyamazo sizidzaopa anthu. (Yes. 11:6-9) Tidzasangalala ndi zimene Yehova analenga mpaka kalekale. (Sal. 22:26) Koma makolo, musachite kudikira mpaka nthawi imeneyo kuti mudzathandize ana anu kuyamba kusangalala ndi chilengedwe. Mukamagwiritsa ntchito chilengedwe pophunzitsa ana anu zokhudza Yehova, mosakayikira iwo adzavomereza zimene Mfumu Davide inanena, kuti: “Inu Yehova, . . . palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.”​—Sal. 86:8.

NYIMBO NA. 134 Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Yehova

a Abale ndi alongo ambiri amakumbukirabe nthawi imene anasangalala kuona zinthu zachilengedwe limodzi ndi makolo awo. Amakumbukiranso mmene makolo awo anagwiritsira ntchito nthawi imeneyo powaphunzitsa zokhudza makhalidwe a Yehova. Ngati muli ndi ana, kodi mungagwiritse ntchito bwanji chilengedwe powaphunzitsa zokhudza makhalidwe a Mulungu? Nkhaniyi iyankha funso limeneli.