Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 15

Kodi Ndinu “Chitsanzo . . . M’kalankhulidwe”?

Kodi Ndinu “Chitsanzo . . . M’kalankhulidwe”?

“Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe.”—1 TIM. 4:12.

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi luso lathu lotha kulankhula linachokera kuti?

 KULANKHULA ndi mphatso imene Mulungu wathu wachikondi anatipatsa. Munthu woyamba Adamu atangolengedwa, ankatha kulankhulana ndi Atate wake wakumwamba. Kuwonjezera pa mawu amene ankawadziwa kale, iye ankathanso kupanga mawu ena atsopano. Adamu anagwiritsa ntchito luso lotha kulankhula potchula mayina nyama zonse. (Gen. 2:19) Ndipotu iye ayenera kuti anasangalala kwambiri pamene kwa nthawi yoyamba analankhulana ndi mkazi wake wokongola, Hava.​—Gen. 2:22, 23.

2. Kodi mphatso yakulankhula inagwiritsidwa ntchito bwanji molakwika m’mbuyomu komanso panopa?

2 Patangopita nthawi, mphatso yakulankhula inagwiritsidwa ntchito molakwika. Satana Mdyerekezi ananamiza Hava ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthu achimwe komanso asakhale angwiro. (Gen. 3:1-4) Atalakwitsa zinthu, Adamu anagwiritsa ntchito molakwika lilime lake pamene anaimba mlandu Hava komanso Yehova. (Gen. 3:12) Kaini anauza Yehova zabodza atapha m’bale wake Abele. (Gen. 4:9) Pambuyo pake, Lameki yemwe anali mbadwa ya Kaini, ananena ndakatulo yosonyeza zachiwawa zomwe zinkachitika mu nthawi yake. (Gen. 4:23, 24) Kodi zinthu zili bwanji masiku ano? Timaona atsogoleri a ndale, mopanda manyazi akugwiritsa ntchito mawu oipa. Ndipo masiku ano n’zovuta kupeza mafilimu amene alibe mawu oipa. Ana amamva mawuwa akakhala kusukulu ndipo akuluakulu amawamva akakhala kuntchito. Mfundo yakuti kulankhula mawu oipa kuli paliponse, ikungosonyezeratu kuti dzikoli laipa kwambiri.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kusamala nazo, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Ngati sitingasamale tingayambe kuzolowera kumva mawu oipa mpaka nafenso kuyamba kuwagwiritsa ntchito. N’zoona kuti monga Akhristu, timafuna kusangalatsa Yehova ndipo zimenezi zimaphatikizapo kupewa mawu alionse oipa. Timafuna kugwiritsa ntchito mphatso yamtengo wapatali yakulankhula m’njira yabwino kwambiri polemekeza Mulungu. Munkhaniyi tikambirana mmene tingachitire zimenezi (1) mu utumiki, (2) pamisonkhano komanso (3) pocheza ndi ena. Koma choyamba tiyeni tikambirane chifukwa chake zimene timalankhula zimakhala zofunika kwa Yehova.

YEHOVA AMAKHUDZIDWA NDI ZIMENE TIMALANKHULA

Kodi zimene mumalankhula zimasonyeza kuti mtima wanu ndi wotani? (Onani ndime 4-5) *

4. Mogwirizana ndi Malaki 3:16, n’chifukwa chiyani zimene timalankhula zimamukhudza Yehova?

4 Werengani Malaki 3:16. Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yehova analemba ‘m’buku lake la chikumbutso’ mayina a anthu, omwe zolankhula zawo zinkasonyeza kuti ankamuopa komanso kuganizira za dzina lake? Zolankhula zathu zimasonyeza zomwe zili mumtima mwathu. Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Zimene timasankha kulankhula zimasonyeza mmene timakondera Yehova. Ndipo iye amafuna kuti anthu amene amamukonda adzasangalale ndi moyo mpaka kalekale m’dziko latsopano.

5. (a) Kodi zolankhula zathu zimagwirizana bwanji ndi kulambira kwathu? (b) Mogwirizana ndi chithunzichi, n’chifukwa chiyani tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula?

5 Zolankhula zathu zingachititse kuti Yehova avomereze kulambira kwathu kapena ayi. (Yak. 1:26) Anthu ena omwe sakonda Mulungu, amalankhula mwaukali, mwamwano komanso modzikuza. (2 Tim. 3:1-5) Ifeyo sitingakonde kukhala ngati anthu amenewa. Timafunitsitsa kuti Yehova azisangalala ndi zomwe timalankhula. Koma kodi Yehova angamasangalale nafe ngati timalankhula mokoma mtima kumisonkhano komanso mu utumiki, koma n’kumalankhula mwamwano komanso mopanda chikondi kwa anthu a m’banja lathu tikakhala kwatokha?​—1 Pet. 3:7.

6. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zomwe zinachitika chifukwa chakuti Kimberly ankalankhula mawu abwino?

6 Tikamagwiritsa ntchito bwino mphatso yakulankhula timasonyeza kuti ndife atumiki a Yehova. Timathandiza ena kuona kusiyana kumene kulipo “pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.” (Mal. 3:18) Zimenezi ndi zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Kimberly. * Iye anapatsidwa zoti achite limodzi ndi mnzake wa m’kalasi. Atamaliza, mnzakeyo anaona kuti Kimberly anali wosiyana kwambiri ndi ana ena pasukulupo. Iye sankanenera anzake zoipa koma ankalankhula mokoma mtima ndipo sankagwiritsa ntchito mawu oipa. Mnzake wa Kimberly anachita chidwi ndi zimenezi ndipo anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Yehovatu amasangalala kwambiri tikamalankhula m’njira imene ingachititse kuti anthu ena aphunzire choonadi.

7. Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani ndi mphatso yakulankhula yomwe Mulungu anakupatsani?

7 Tonsefe tikufuna kuti tizilankhula m’njira imene imalemekeza Yehova komanso kuchititsa kuti tizigwirizana ndi abale athu. Tsopano tiyeni tikambirane njira zina zimene zingatithandize kupitirizabe kukhala “chitsanzo . . . m’kalankhulidwe.”

MUZIKHALA CHITSANZO MU UTUMIKI

Kulankhula ndi anthu mokoma mtima mu utumiki kumasangalatsa Yehova (Onani ndime 8-9)

8. Kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani ya mmene ankalankhulira mu utumiki?

8 Muzilankhula mokoma mtima komanso mwaulemu ngakhale ena akukwiyitseni. Pa utumiki wake, Yesu ankanamiziridwa kuti anali munthu wokonda kwambiri vinyo, wosusuka, mtumiki wa Mdyerekezi, wosasunga Sabata ngakhalenso wonyoza Mulungu. (Mat. 11:19; 26:65; Luka 11:15; Yoh. 9:16) Komabe Yesu sankayankha ndi mawu aukali. Mofanana ndi Yesu, ifenso sitiyenera kubwezera ngakhale anthu atatilankhula mwamwano. (1 Pet. 2:21-23) Komatu kudziletsa mwa njira imeneyi sikophweka. (Yak. 3:2) Ndiye n’chiyani chingatithandize?

9. N’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula bwino tikakhala mu utumiki?

9 Muziyesa kuganizira zimene zachititsa mwininyumba kulankhula mawu osayenera. M’bale wina dzina lake Sam ananena kuti: “Ndimayesa kuganizira mfundo yakuti munthuyo ayenera kumva choonadi komanso kuti angathe kusintha.” Nthawi zina mwininyumba angakwiye chifukwa choti tamupeza pa nthawi yolakwika. Tikakumana ndi munthu yemwe wakwiya, tingachite zimene amachita mlongo wina dzina lake Lucia. Tikhoza kupemphera mwachidule, kum’pempha Yehova kuti atithandize kukhala wodekha komanso kuti tisalankhule mawu oipa kapena opanda ulemu.

10. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 4:13, kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chotani?

10 Muziwonjezera luso lanu lophunzitsa. Timoteyo anali Mkhristu waluso, komabe iye ankafunika kuwonjezera luso lake. (Werengani 1 Timoteyo 4:13.) Kodi tingatani kuti tiziphunzitsa bwino mu utumiki? Tizikonzekera bwino. N’zosangalatsa kuti tili ndi zinthu zosiyanasiyana zophunzitsira zomwe zingatithandize kukhala aphunzitsi aluso. Mukhoza kupeza mfundo zothandiza m’kabuku kakuti, Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso komanso mbali yakuti, “Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki” mu Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Kodi mumagwiritsa ntchito zinthu zimenezi? Tikakonzekera bwino sitichita mantha kwambiri ndipo timalankhula ndi mtima wonse.

11. Kodi n’chiyani chathandiza Akhristu ena kuti akhale aphunzitsi abwino?

11 Tingathenso kukhala aphunzitsi abwino poona komanso kuphunzira pa zimene ena mumpingo amachita. Sam, yemwe tamutchula kale uja, amadzifunsa chimene chimachititsa Akhristu ena kuti akhale aphunzitsi abwino. Amaona njira zimene amagwiritsa ntchito pophunzitsa kenako n’kumayesetsa kuwatsanzira. Mlongo wina dzina lake Talia amachita chidwi ndi mmene abale aluso amakambira nkhani za onse Chifukwa cha zimenezi iye anaphunzira mmene angafotokozere momveka bwino nkhani zimene anthu amafunsa kawirikawiri mu utumiki.

MUZIKHALA CHITSANZO PAMISONKHANO

Tikamaimba ndi mtima wonse pamisonkhano timatamanda Yehova (Onani ndime 12-13)

12. Kodi ena zimawavuta kuchita chiyani?

12 Tonsefe tingathandize kuti misonkhano iziyenda bwino poimba nawo nyimbo mokweza komanso kupereka ndemanga zimene tazikonzekera bwino. (Sal. 22:22) Ena zimawavuta kuimba nyimbo kapena kupereka ndemanga pamisonkhano. Kodi inunso zimakuvutani? Ngati ndi choncho, mungakonde kudziwa zimene zathandiza ena kuti asamaope kuimba nyimbo komanso kupereka ndemanga.

13. N’chiyani chingatithandize kuti tiziimba ndi mtima wonse pamisonkhano?

13 Muziimba ndi mtima wonse. Tikamaimba nyimbo za Ufumu, cholinga chathu chachikulu chizikhala kutamanda Yehova. Mlongo wina dzina lake Sara amaona kuti saimba bwino kwenikweni. Komabe amafuna kutamanda Yehova poimba nyimbo. Choncho amaona kuti n’zothandiza kukonzekera nyimbo ngati mmene amachitira ndi mbali zina zapamisonkhano. Iye amayeserera nyimbozo n’kuona mmene mawu ake akugwirizanira ndi zimene akaphunzire pamisonkhano. Anati: “Zimenezi zimandithandiza kuti ndiziganizira kwambiri mawu a munyimboyo, osati luso langa loimba.”

14. Ngati mumachita mantha, kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muziyankha pamisonkhano?

14 Muzipereka ndemanga pafupipafupi. Kunena zoona, ena zimawavuta kuchita zimenezi. Talia, yemwe tamutchula kale uja, ananena kuti: “Ndimachita mantha ndikafuna kulankhula pagulu ngakhale kuti ena sazindikira zimenezi chifukwa mawu anga amamveka bwinobwino. Choncho kupereka ndemanga pamisonkhano kumandivuta.” Komabe zimenezi sizimamulepheretsa Talia kuti azipereka ndemanga. Akamakonzekera misonkhano, amakumbukira kuti yankho loyamba liyenera kukhala lalifupi komanso lachindunji. Iye anati: “Zimenezi zikutanthauza kuti palibe vuto kupereka ndemanga yaifupi, yosavuta komanso yachindunji chifukwa ndi zimenenso wochititsayo amafuna.”

15. Kodi tizikumbukira chiyani pa nkhani yopereka ndemanga?

15 Nthawi zinanso ngakhale Akhristu omwe si amanyazi kapena amantha zimawavuta kuyankha pamisonkhano. Chifukwa chiyani? Mlongo wina dzina lake Juliet anafotokoza kuti: “Nthawi zina ndimaopa kupereka ndemanga chifukwa choganiza kuti ndemanga yanga ndi yaifupi kwambiri kapena si yabwino kwenikweni.” Komabe tizikumbukira kuti Yehova amafuna kuti tizipereka ndemanga zabwino mmene tingathere. * Iye amayamikira tikayesetsa kumutamanda pamisonkhano ya mpingo ngakhale kuti nthawi zina timachita mantha.

MUZIKHALA CHITSANZO MUKAMACHEZA NDI ENA

16. Kodi ndi mawu enanso ati amene tiyenera kupewa?

16 Muzipewa kulankhula “mawu achipongwe.” (Aef. 4:31) Monga tanenera kale, mawu alionse oipa sayenera kutuluka pakamwa pa Mkhristu. Koma pali mawu ena amene sangaonekeretu kuti ndi oipa omwe tiyenera kusamala nawo. Mwachitsanzo, tiyenera kukhala osamala kuti tisamalankhule zoipa zokhudza anthu ena omwe timasiyana nawo chikhalidwe, mtundu kapena mayiko. Kuwonjezera pamenepo, sitiyenera kukhumudwitsa ena powalankhula mawu achipongwe. M’bale wina anavomereza kuti: “Nthawi zina ndinalankhulapo mawu amene ndi achipongwe poganiza kuti ndi nthabwala chabe kapena zongocheza, koma omwe anakhumudwitsa ena. Kwa zaka zambiri mkazi wanga wakhala akundithandiza kwambiri pondiuza pandekha zimene sindinalankhule bwino zomwe zinamukhumudwitsa iyeyo komanso anthu ena.”

17. Mogwirizana ndi Aefeso 4:29, kodi tingalimbikitse bwanji ena?

17 Muzilankhula zimene zingalimbikitse ena. Muziyamikira ena m’malo mofulumira kuwadzudzula kapena kudandaula. (Werengani Aefeso 4:29.) Aisiraeli anali ndi zinthu zambiri zomwe zikanawachititsa kukhala oyamikira, koma nthawi zambiri iwo ankangodandaula. Tisamaiwale kuti ngati timakonda kudandaula zingachititse kuti enanso azidandaula. Mwina mungakumbukire kuti zinthu zosalimbikitsa zimene azondi 10 ananena zinachititsa kuti ‘ana onse a Isiraeli ayambe kudandaula za Mose.’ (Num. 13:31–14:4) Koma kuyamikira ena, kungathandize kuti aliyense azisangalala. Sitikukayikira kuti mwana wamkazi wa Yefita analimbikitsidwa kwambiri kuti apitirize utumiki wake chifukwa choti atsikana anzake ankamuyamikira. (Ower. 11:40) Sara, yemwe tamutchula kale uja anati: “Tikamayamikira ena timawathandiza kuona kuti Yehova amawakonda komanso kuti ndi ofunika kwambiri m’gulu lake.” Choncho muziyesetsa kuyamikira ena mochokera pansi pa mtima.

18. Mogwirizana ndi Salimo 15:1, 2, n’chifukwa chiyani tiyenera kumalankhula zoona, nanga zimenezi zimaphatikizapo chiyani?

18 Muzilankhula zoona. Yehova sangasangalale nafe ngati sitilankhula zoona. Iye amadana ndi kunama kwa mtundu uliwonse. (Miy. 6:16, 17) Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amaona kuti palibe vuto kunama, ife timayesetsa kuti tiziona nkhaniyi mmene Yehova amaionera. (Werengani Salimo 15:1, 2.) N’zoona kuti timapewa kulankhula mabodza ochita kuonekeratu, koma timapewanso kuchititsa anthu mwadala kuti aziona zinthu molakwika.

Kusiya miseche n’kuyamba kulankhula zinthu zabwino, kumachititsa kuti Yehova azitikonda (Onani ndime 19)

19. Kodi ndi chinthu china chiti chimene tiyeneranso kusamala nacho?

19 Muzipewa miseche. (Miy. 25:23; 2 Ates. 3:11) Juliet, yemwe tamutchula kale uja, anafotokoza mmene amamvera pa nkhani ya miseche. Iye anati: “Kumvetsera miseche sikumalimbikitsa ndipo kumandichititsa kuti ndisamakhulupirirenso munthu amene akundiuza misecheyo. Komanso ndingadziwe bwanji ngati munthuyo sanganenenso miseche yokhudza ineyo kwa munthu wina?” Mukaona kuti munthu wina wayamba kulankhula miseche, muziyesetsa kusintha nkhaniyo.​—Akol. 4:6.

20. Kodi mwatsimikiza mtima kuchita chiyani pa nkhani ya zomwe mumalankhula?

20 Popeza kuti tikukhala m’dziko limene anthu ambiri amalankhula mawu oipa, tiyenera kuyesetsa kuti zolankhula zathu zizisangalatsa Yehova. Tizikumbukira kuti kulankhula ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo amakhudzidwa ndi mmene timaigwiritsira ntchito. Iye adzatidalitsa tikamayesetsa kugwiritsa ntchito bwino luso lolankhula mu utumiki, pamisonkhano komanso pocheza ndi ena. Yehova akadzawononga dziko loipali, zidzakhala zosavuta kumamulemekeza ndi zolankhula zathu. (Yuda 15) Koma panopa tiyeni tikhale otsimikiza kuti tizisangalatsa Yehova ndi “mawu a pakamwa” pathu.​—Sal. 19:14.

NYIMBO NA. 121 Timafunika Kukhala Odziletsa

^ Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali yakulankhula. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sagwiritsa ntchito mphatsoyi ngati mmene Yehova ankafunira. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tizilankhula zoyenera komanso zolimbikitsa m’dziko loipali? Kodi tingatani kuti zolankhula zathu zizisangalatsa Yehova tikakhala mu utumiki, pamisonkhano komanso tikamacheza ndi anthu ena? Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso amenewa.

^ Mayina ena asinthidwa.

^ Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yopereka ndemanga, onani nkhani yakuti, “Tizitamanda Yehova Mumpingo” mu Nsanja ya Olonda ya January 2019.

^ MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: M’bale akulankhula mwaukali kwa mwininyumba yemwe wakwiya; m’bale akuchita manyazi kuimba pamisonkhano; ndipo mlongo akulankhula miseche.