Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Nyama Zotchedwa Madainaso?

Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Nyama Zotchedwa Madainaso?

Yankho la m’Baibulo

 M’Baibulo, palibe pamene pamafotokoza mwachindunji za madainaso. Komabe Baibulo limanena kuti Mulungu ndi amene ‘analenga zinthu zonse.’ Choncho n’zodziwikiratu kuti nyamazi zinalengedwanso ndi iye. a (Chivumbulutso 4:11) Ngakhale kuti Baibulo silitchula mwachindunji za madainaso, limatchula mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zamoyo ndipo madainaso ayenera kukhala m’gulu la zamoyo zimenezi. Limatchula zamoyo ngati:

Kodi madainaso anachita kusintha kuchoka ku nyama zina?

 Umboni wa zinthu zakale, umasonyeza kuti nyamazi zinapezekapo pa nthawi imodzi ndipo palibe umboni wosonyeza kuti pakapita nthawi zinkasintha. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Baibulo limanena kuti Mulungu analenga zamoyo zonse. Mwachitsanzo pa Salimo 146:6 pamanena za Mulungu kuti ndi “Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mmenemo.”

Kodi nyamazi zinakhalako liti?

 Baibulo limanena kuti zamoyo za m’madzi ndi pamtunda zinalengedwa pa tsiku la 5 ndi la 6 m’nyengo ya kulenga zinthu. b (Genesis 1:20-25, 31) Choncho Baibulo limasonyeza kuti nyama zotchedwa madainaso zinakhalako kwa zaka zambiri.

Kodi Mvuu ndi Ng’ona ndi madainaso?

 Ayi. Ngakhale kuti mvuu (Behemoti m’Chiheberi) ndi ng’ona (Leviyatani m’Chiheberi) zinatchulidwa m’buku la Yobu, sitinganene motsimikiza kuti nyamazi ndi madainaso. Koma timadziwa kuti nyamazi zomwe zinatchulidwa m’buku la Yobu, ndi mvuu komanso ng’ona tikaona zomwe mavesiwa amanena pofotokoza zomwe nyamazi zimachita. (Yobu 40:15-23; 41:1, 14-17, 31) Yehova anauza Yobu kuti ayang’anitsitse zochita za nyamazo. Ndipo Yobu anakhalapo padzikoli madainaso atatha kale. Choncho sitinganene kuti “Mvuu” ndi “Ng’ona” ndi madainaso.​—Yobu 40:16; 41:8.

Kodi madainaso anapita kuti?

B aibulo silifotokoza kuti nyamazi zinatha bwanji. Komabe limanena kuti zinthu zonse zinalengedwa ‘mwa kufuna kwake [kwa Mulungu].’ Choncho n’zosakayikitsa kuti Mulungu analenga madainaso ndi cholinga. (Chivumbulutso 4:11) Ndipo cholingacho chitakwaniritsidwa, Mulungu analola kuti nyamazo zithe.

a Umboni wa zinthu zakale zokwiririka pansi, umasonyeza kuti kalelo kunali madainaso. Mafupa ndi zinthu zina zomwe akatswiri anafukula zimasonyeza kuti nyamazi zinalipo zambiri komanso zinali za misinkhu ndi maonekedwe osiyanasiyana.

b M’Baibulo mawu akuti “tsiku” akhozanso kutanthauza nthawi yaitali mwinanso kufika zaka masauzande.​—Genesis 1:31; 2:1-4; Aheberi 4:4, 11.