Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 1

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Kodi muli mwana munafunsapo makolo anu kuti: “Kodi ana amachokera kuti?” Ngati munawafunsapo, kodi anakuyankhani kuti chiyani? N’kutheka kuti iwo sanakuyankheni kapena anayankha mwamanyazi chifukwa cha msinkhu wanu. Mwinanso anangokuuzani zinazake zomwe pambuyo pake, munazindikira kuti zinali zabodza. Komabe, kuti makolo athandize mwana wawo kudziwa zimene zimachitikira munthu akamakula komanso akakhala pabanja, ayenera kumuuza zoona pa nkhaniyi.

Makolo ambiri amachita manyazi kukambirana ndi ana awo zokhudza kumene ana amachokera. Mofanana ndi zimenezi, asayansi ena samafunanso kuyankha funso lofunika kwambiri lakuti, Kodi moyo unayamba bwanji? Koma kupeza yankho lolondola la funso limeneli kungathandize kwambiri munthu kusintha mmene amaonera moyo. Ndiye kodi moyo unayamba bwanji?

Selo la dzira la munthu lomwe lakulitsidwa maulendo 800

Kodi asayansi ambiri amanena zotani? Anthu ambiri amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, amanena kuti moyo unayambira m’mbali mwa dziwe linalake lakale kwambiri kapena pansi pa nyanja. Iwo amakhulupirira kuti m’malo amenewa tinthu tosiyanasiyana tinasakanikirana n’kukhala tinthu tokhala ngati thovu, n’kupanga mamolekyu omwe kenako anayamba kugawikana. Asayansiwa amaona kuti zamoyo zonse zapadzikoli zinangokhalako mwangozi kuchokera ku mamolekyu amenewa.

Koma asayansi ena odziwika bwino omwe amakhulupiriranso kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, sagwirizana ndi zimenezi. Iwo amanena kuti maselo oyambirira kapena mbali zake zikuluzikulu zinafika padziko lapansi kuchokera kuthambo. N’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa ngakhale kuti asayansi ayesetsa kuchita kafukufuku, sanapeze umboni wosonyeza kuti zamoyo zingachokere ku zinthu zopanda moyo. Mu 2008, pulofesa wa zinthu zamoyo dzina lake Alexandre Meinesz ananena kuti pa zaka 50 zapitazi, “sipanapezeke umboni weniweni wosonyeza kuti zamoyo zapadzikoli zinakhalako kuchokera ku zinthu zopanda moyo ndipo kupita patsogolo kwa sayansi sikunathandize kutsimikizira zimenezi.”1

Kodi umboni umasonyeza chiyani? Yankho la funso lakuti, ‘Kodi ana amachokera kuti?’ ndi lodziwika bwino ndipo umboni wake ulipo. Mfundo yoti zamoyo zonse zimachokera ku zamoyo zinzake ndi yodziwika bwino. Koma kodi n’zotheka kuti kalekalelo zinthu zamoyo zinayamba kuchokera ku zinthu zopanda moyo? Kodi n’chiyani chimafunika kuchitika kuti moyo ukhalepo?

Ochita kafukufuku apeza kuti pali zinthu zitatu zimene zimagwirira ntchito limodzi kuti selo likhale lamoyo. Zinthu zake ndi DNA, RNA ndi mapulotini. Masiku ano pali asayansi ochepa chabe amene anganene kuti selo lathunthu linangopangika lokha mwadzidzidzi kuchokera ku zinthu zopanda moyo. Koma kodi n’zotheka kuti RNA kapena mapulotini angoyambika mwangozi? *

Stanley Miller, 1953

Asayansi ambiri amakhulupirira kuti umboni wakuti zamoyo zinayambira ku zinthu zopanda moyo unapezeka kuchokera pa zimene wasayansi wina dzina lake Stanley L. Miller anachita mu 1953. Iye anayesera kupanga ma amino asidi omwe amathandiza kuti mapulotini apangike. Anachita zimenezi posakaniza mitundu yosiyanasiyana ya mpweya, zomwe ankati zikuimira mmene mlengalenga munalili kalekalelo, kenako n’kudutsitsa mphamvu za magetsi mumpweyawo. Pa nthawi inanso, asayansi anapeza ma amino asidi m’mwala womwe unagwa padzikoli kuchokera mlengalenga. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti zinthu zonse zomwe zimafunika kuti zamoyo zikhalepo zingathe kukhalako mwangozi?

Robert Shapiro, yemwe anali pulofesa pa yunivesite ya New York, anati: “Olemba mabuku ena amaganiza kuti zinthu zonse zofunika kuti moyo ukhalepo, zikhoza kupangidwa mosavuta ngati mmene Miller anapangira ma amino asidi komanso zimapezeka m’miyala yomwe imagwa padzikoli. Komatu zimenezi si zoona.”2 *

Taganizirani mmene molekyu ya RNA ilili. Imapangidwa ndi timamolekyu ting’onoting’ono totchedwa manyukiliyotaidi. Manyukiliyotaidi ndi mamolekyu osiyana ndi ma amino asidi ndipo ndi ogometsa kuposa ma amino asidi. Shapiro ananena kuti “palibe umboni wosonyeza kuti anthu anakwanitsapo kupanga manyukiliyotaidi pogwiritsa ntchito mphamvu zamagetsi kapena kuwapeza m’miyala imene inagwa kuchokera mlengalenga.”3 Iye anakayikiranso zoti molekyu ya RNA ikhoza kupangika mwangozi chifukwa cha kusakanikirana kwa tinthu tosiyanasiyana ndipo anati “ngati zingachitike kwinakwake m’chilengedwechi ungangokhala mwayi womwe sungapezekenso.”4

RNA (1) amafunika kuti mapulotini (2) apangike, ndipo mapulotini amafunikanso popanga RNA. Ndiye zingatheke bwanji kuti chimodzi kapena zonse zikhaleko mwangozi? Tidzakambirana za Maribosomu (3) mu gawo 2.

Nanga mamolekyu a pulotini amapangidwa bwanji? Amatha kupangidwa kuchokera ku ma amino asidi okwana 50 okha kapena okwana masauzande koma motsatira kwambiri ndondomeko. Nthawi zambiri pulotini yemwe amapezeka muselo amakhala ndi ma amino asidi 200. Koma maselowa amakhalanso ndi mapulotini ambirimbiri amitundu yosiyanasiyana. N’zokayikitsa kwambiri mwinanso zosatheka n’komwe kuti pulotini imodzi yokhala ndi ma amino asidi okwana 100 okha ipangike payokha.

Ngati mamolekyu opangidwa ndi asayansi amafunika luso lozama, kodi mamolekyu odabwitsa kwambiri omwe amapezeka muselo angangokhalako mwangozi?

Wasayansi wina dzina lake Hubert P. Yockey, yemwe amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, ananenanso kuti: “N’zosatheka kuti pa chiyambi zamoyo zinachokera ku mapulotini basi.”5 Kuti mapulotini apangike pamafunika ma RNA, koma kuti ma RNA apangike pamafunikanso mapulotini. Koma tiyerekeze kuti mamolekyu a pulotini ndi a RNA anapezeka mwangozi pamalo amodzi komanso pa nthawi yofanana, kodi zikanathekadi kuti asakanikirane bwinobwino, n’kupanga zinthu zamoyo zoti zingapitirize kukhala moyo n’kumachulukana? Dr Carol Cleland * yemwe ndi membala wa bungwe lina (National Aeronautics and Space Administration’s Astrobiology Institute) ananena kuti: “Zikuoneka kuti mwayi woti zimenezi zichitike mwangozi (zitakhala kuti mapulotini ndi ma RNA angosakanikirana) ndi wochepa kwambiri.” Iye ananenanso kuti: “Ngakhale zili choncho, asayansi ambiri amaganiza kuti ngati angamvetse zimene zinachitika kuti mapulotini komanso ma RNA apangike paokha ndiye kuti sizingavutenso kudziwa zimene zinachitika kuti asakanikirane n’kupanga zinthu zamoyo.” Pofotokoza zimene asayansi ena amanena pa nkhani yoti moyo unangoyamba mwangozi, Dr Carol Cleland ananenanso kuti: “Palibe wasayansi ngakhale mmodzi amene amafotokoza momveka bwino mmene moyowo unayambira.”6

Pamafunika anthu anzeru kuti apange maloboti komanso mapulogalamu othandiza kuti azichita zinthu ngati chinthu chamoyo. Ndiye kodi sipangafunikenso winawake wanzeru kuti apange selo kapenanso munthu weniweniyo?

N’chifukwa chiyani kudziwa mfundo zimenezi n’kofunika? Taganizirani mavuto omwe asayansi amene amati zamoyo zinangokhalako mwangozi amakumana nawo. Iwo anapezapo m’miyala ija ma amino asidi omwe amapezekanso m’maselo a zinthu zamoyo. Akhalanso akuchita khama kwambiri ndipo apanga mamolekyu ena. Ndipo amaganiza kuti angathe kupanga tinthu tonse tomwe timapezeka muselo. Zimene akuchitazi n’zofanana ndi zimene asayansi ena amachita. Iwo amatenga zinthu zam’chilengedwe n’kupanga zinthu monga mapulasitiki, mawaya, zitsulo ndi zinthu zina n’kupangira loboti. Kenako lobotiyo amaipanga kuti izitha kupanganso maloboti ena ofanana nalo. Kodi zimenezi zimasonyeza chiyani? Zimasonyeza kuti munthu wanzeru akhoza kupanga mashini ogometsa.

Mofanana ndi zimenezi, asayansi akanakwanitsa kupanga selo ndiye kuti angapange chinthu chodabwitsa kwambiri. Koma kodi zimenezi zingasonyeze kuti selo likhoza kupangika palokha? Ayi. Koma m’malomwake ungakhale umboni wakuti pali winawake wanzeru amene analipanga.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Maumboni onse a sayansi amene alipo panopa akusonyeza kuti zamoyo zimachokera ku zamoyo zinzake basi. Choncho n’zovuta kwambiri kukhulupirira kuti selo linapangika mwangozi kuchokera ku zinthu zopanda moyo.

Malinga ndi zimene takambiranazi, kodi mungakhulupiriredi zoti selo linapangika lokha? Musanayankhe funso limeneli, choyamba muyenera kudziwa bwino mmene selo limapangidwira. Kuchita zimenezi kukuthandizani kudziwa ngati zimene asayansi ena amanena zokhudza mmene moyo unayambira zili zoona, kapena ndi zongopeka ngati nkhani zabodza zimene makolo ena amanena zokhudza kumene ana amachokera.

^ ndime 8 Mu gawo 3 tidzakambirana mutu wakuti “Kodi Malangizo Anachokera Kuti?” ndipo mutuwu udzatithandiza kuona ngati DNA inangokhalako mwangozi.

^ ndime 10 Pulofesa Shapiro sakhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa. Amakhulupirira kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi m’njira inayake yomwe panopa sitikuidziwa bwinobwino. Mu 2009, asayansi a pa yunivesite ya Manchester ku England ananena kuti anakwanitsa kupanga mamolekyu enaake otchedwa manyukiliyotaidi. Komabe, Shapiro ananena kuti zinthu zimene anagwiritsa ntchito popanga mamolekyu amenewa sizikugwirizana ndi zinthu zimene iyeyo akudziwa kuti zimapanga RNA.

^ ndime 13 Dr. Cleland sakhulupirira zimene Baibulo limanena zoti zinthu zinachita kulengedwa. Iye amakhulupirira kuti zamoyo zinangokhalako mwangozi koma mwanjira inayake yomwe panopa sikudziwika bwinobwino.