Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 2

Kodi Pali Chamoyo Chimene Si Chodabwitsa?

Kodi Pali Chamoyo Chimene Si Chodabwitsa?

Kodi n’zotheka kuti maselo a mitundu yoposa 200 amene ali m’thupi lanu anangokhalako mwangozi?

Thupi la munthu linapangidwa modabwitsa kwambiri kuposa zinthu zambiri m’chilengedwechi. Tikutero chifukwa m’thupi la munthu muli maselo pafupifupi 100 thiriliyoni ndipo alipo mitundu yoposa 200.8 Mwachitsanzo, maselo ena ndi a mafupa, ena a magazi ndipo ena ndi a ubongo.7

Maselo onsewa amagwira ntchito mogwirizana ngakhale kuti amaoneka mosiyana ndipo ntchito zawo n’zosiyananso. Anthu amalumikizana pa intaneti pogwiritsa ntchito makompyuta ndiponso nthambo zambirimbiri koma zimenezi sizigwira ntchito bwino ngati mmene zilili ndi maselo a m’thupi. Palibe munthu amene angapange chinthu chogwira ntchito modabwitsa ngati mmene selo limachitira. Ndiye kodi maselo a m’thupi la munthu anachokera kuti?

Kodi asayansi ambiri amanena zotani? Pali magulu awiri a maselo. Gulu lina lili ndi chinthu chamkati mwenimweni chotchedwa nyukiliyasi, pomwe gulu linalo lilibe. Maselo a anthu, zinyama ndiponso zomera amakhala ndi nyukiliyasi, koma maselo a mabakiteriya alibe. Choncho popeza maselo a mabakiteriya alibe nyukiliyasi, anthu ambiri amaganiza kuti maselo a zinyama ndiponso a zomera anachita kusintha kuchokera ku maselo a mabakiteriyawa.

Asayansi ena amanena kuti kwa zaka mamiliyoni ambiri, maselo enaake opanda nyukiliyasi anameza maselo ena koma sanawagaye. Ndiyeno maselo amene anamezedwawo anayamba kusintha mmene ankagwirira ntchito ndipo anakhalabe m’maselowo pa nthawi imene maselo amene anawamezawo anagawikana.9 *

Kodi Baibulo limanena zotani? Baibulo limasonyeza kuti zamoyo zapadzikoli zinachita kulengedwa ndi winawake wanzeru. Limafotokoza mosavuta kumva kuti: “N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheb. 3:4) Limanenanso kuti: “Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova! Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu. Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga. . . . [Pali] zinthu zoyenda zosawerengeka, [pali] zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.”​—Sal. 104:24, 25.

Kodi zingakhale zoona kuti selo linapangika lokha kuchokera ku zinthu zopanda moyo?

Kodi umboni umasonyeza chiyani? Kupita patsogolo kwa sayansi kwathandiza kuti akatswiri aone mkati mwa maselo opanda nyukiliyasi omwe ndi osadabwitsa kwambiri ngati maselo ena. Asayansi amene amakhulupirira kuti zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina amanena kuti maselo amoyo oyambirira ayenera kuti anali ngati maselo osadabwitsa kwambiri amenewa.10

Ngati ndi zoona kuti zinthu zinasintha kuchokera ku zinthu zina, ndiye kuti payenera kukhala umboni wosonyeza mmene maselo oyambirira anapangikira mwangozi. Koma ngati zamoyo zinachita kulengedwa, ndiye kuti payeneranso kukhala umboni, ngakhale m’zamoyo zing’onozing’ono, wosonyeza kuti zinapangidwa ndi winawake. Tiyeni tsopano tione mmene selo lopanda nyukiliyasi limakhalira. Tikamakambirana zimenezi, muzidzifunsa kuti, Kodi n’zothekadi kuti seloli linangopangika mwangozi?

MPANDA WOTETEZA SELO

Kuti mulowe mkati mwa selo lopanda nyukiliyasi muyenera kukhala wamng’ono ngati fulusitopu koma atagawidwa kambirimbiri. Koma ngakhale mutakhala wamng’ono chonchi, simungalowe museloli chifukwa limatetezedwa ndi khungu lamphamvu lomwe limakhala ngati mpanda wanjerwa. Kuti khunguli likhale lokhuthala ngati pepala limodzi, payenera kusanjikizidwa makungu pafupifupi 10,000. Koma khungu la selo ndi lodabwitsa kwambiri kuposa mpanda wanjerwa. N’chifukwa chiyani tikutero?

Mofanana ndi mpanda umene umazungulira fakitale, khungu lomwe limateteza selo limachititsa kuti zinthu zoopsa zisalowe muselolo. Khungulo limalola kuti mamolekyu ang’onoang’ono monga a okosijeni azidutsa. Koma limaletsa kuti mamolekyu omwe angawononge zinthu azidutsa popanda chilolezo. Khunguli limathandizanso kuti mamolekyu ofunika asachoke muselomo. Kodi khunguli limatha bwanji kuchita zonsezi?

Pafakitale pamakhala alonda amene amaona zinthu zimene zimalowa ndi kutuluka pageti la fakitaleyo. Mofanana ndi zimenezi, m’khungu la selo mumakhala mamolekyu apadera a pulotini omwe amakhala ngati mageti komanso alonda.

Khungu la selo limakhala ndi alonda amene amaona zinthu zolowa ndi zotuluka muselo

Ena mwa mapulotiniwa (1) amakhala ndi kampata pakati kamene kamalola mamolekyu amitundu inayake kuti azilowa kapena kutuluka muselo. Mapulotini ena ndi otseguka mbali imodzi (2) koma otsekeka mbali ina. Amakhala ndi malo ofikira (3) zinthu zinazake zapadera ndipo zimakwanirapo ndendende. Zinthuzo zikafika, mapulotiniwo amatseguka kuti zidutse (4). Zonsezi zimachitika pakhungu la selo lililonse, ngakhale limene si lodabwitsa kwambiri.

MKATI MWA SELO

Tiyerekeze kuti alonda amuselo alola kuti mudutse ndipo muli mkati mwa selolo. Muselo muli timadzi tokhala ndi michere yambiri komanso zinthu zina. Selo limagwiritsa ntchito zinthuzi kuti lipange zinthu zina zofunika. Koma zimenezi sizimangochitika mwachisawawa. Mofanana ndi pafakitale pamene ntchito imayenda mwadongosolo kwambiri, selo limachititsa kuti zinthu zambirimbiri zimene zimachitika mkati mwake ziziyenda mwadongosolo kwambiri komanso pa nthawi yake.

Selo limathera nthawi yambiri popanga mapulotini. Kodi limapanga bwanji zimenezi? Choyamba, limapanga ma amino asidi a mitundu yosiyana yokwana 20. Ma amino asidiwa amatumizidwa ku maribosomu (5), omwe ali ngati mashini amene amalumikiza ma amino asidi munjira zosiyanasiyana kuti apange mapulotini osiyanasiyana. Nthawi zina mafakitale amakhala ndi pulogalamu yapakompyuta imene imathandiza kuti chilichonse chiziyenda bwino. Nawonso maselo amakhala ndi malangizo mu DNA amene amathandiza kuti ntchito zambiri za muselomo ziziyenda bwino (6). Malangizo a mu DNA amauza maribosomu mtundu wa mapulotini amene ayenera kupangidwa komanso mmene angawapangire (7).

Zimene zimachitika kuti mapulotiniwa apangike ndi zodabwitsa kwambiri. Mapulotini amapindika mosiyanasiyana n’kukhala ndi mbali zitatu (8). Kapindikidwe ka pulotini ndi kamene kamasonyeza ntchito imene pulotiniyo izigwira. * Zimakhala ngati fakitale imene imapanga mbali zosiyanasiyana za injini. Kuti injiniyo igwire ntchito, mbali iliyonse iyenera kupangidwa mosalakwitsa kalikonse. N’chimodzimodzi ndi mapulotini. Ngati sanapangidwe bwino kapena kupindidwa moyenera, sangagwire bwino ntchito ndipo mwina akhoza kuwononga selo.

Selo lili ngati fakitale yokhala ndi mashini opanga zinthu n’kumakaziika pamalo oyenera

Ndiye kodi mapulotini akapangidwa, amadziwa bwanji koyenera kupita? Pulotini iliyonse ikapangidwa imakhala ndi malangizo amene amakhala ngati adiresi yosonyeza koyenera kupita. Pa miniti iliyonse, mapulotini masauzande ambiri amapangidwa koma iliyonse imafika bwinobwino pamalo ake.

N’chifukwa chiyani kudziwa mfundo zimenezi n’kofunika? Mamolekyu amuselo sangagawikane paokha. Akangochoka muselo amayamba kuwonongeka. Mkati mwa selolo amathandizidwa ndi mamolekyu ena kuti agawikane. Mwachitsanzo, pamafunika maenzayimu kuti mamolekyu apadera opatsa mphamvu apangike, koma pamafunikanso mphamvu zochokera ku mamolekyuwo kuti maenzayimu apangike. Ndi mmene zililinso ndi DNA. Pamafunika DNA (tikambirana bwinobwino za DNA m’chigawo chachitatu) kuti maenzayimu apangike koma pamafunikanso maenzayimuwo kuti DNA ipangike. Mapulotini ena amapangidwa ndi maselo okha basi koma maselowo amapangidwanso ndi mapulotini. *

Wasayansi wina dzina lake Radu Popa sagwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo yoti zinthu zinachita kulengedwa. Koma mu 2004, iye anafunsa kuti: “Kodi zingatheke bwanji kuti zamoyo zipangike zokha pamene ifeyo tayesetsa kukonza zinthu kuti tipange zamoyozo, koma zatikanika?”13 Iye ananenanso kuti: “Zinthu zonse zimene zimafunika kuti selo lizigwira bwinobwino ntchito yake n’zodabwitsa kwambiri moti n’zokayikitsa kuti zonsezi zinangokhalapo mwangozi pa nthawi imodzi.”14

Nyumba yansanjikayi ikugwa chifukwa choti ilibe maziko olimba. Izitu zikufanana ndi zimene asayansi amaphunzitsa zoti zinthu zinasintha kuchokera ku zinthu zina chifukwa nawonso sangatsimikizire mmene zamoyo zinayambira.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Anthu amene amakhulupirira kuti zinthu zinasintha kuchokera ku zinthu zina, amanena kuti zamoyo padzikoli sizinachite kulengedwa ndi Mulungu. Koma akamaphunzira zambiri zokhudza zamoyozo m’pamene amavutikanso kutsimikizira kuti zinakhalako zokha. Asayansi ena akasowa chonena pa nkhaniyi amanena kuti vutoli silikukhudzana ndi zomwe amaphunzitsa zoti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Koma kodi zimenezi ndi zomveka?

Zimene amaphunzitsazi zimachokera pa mfundo yakuti zinthu zinkangochitika mwangozi mpaka kufika poti zamoyo zapangika. Ndiyeno mfundo ina ndi yakuti zinthu zinkachitikanso mwangozi kuti zamoyozo zizisintha mpaka kukhala zamoyo zosiyanasiyana zimene zili padzikoli. Koma ngati mfundo yoyambayo yomwe ili ngati maziko ndi yosatsimikizirika, kodi zingakhale zomveka kukhulupirira mfundo zinazo? Apatu zimene amaphunzitsazo zili ngati nyumba yansanjika yopanda maziko olimba yomwe ikhoza kugwa nthawi ina iliyonse.

Malinga ndi mfundo zimene takambirana pa nkhani ya maseloyi, kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika mwangozi, kapena pali winawake wanzeru amene anazipanga? Ngati mpaka pano mukukayikirabe, tikukupemphani kuti muone malangizo amene amathandiza kuti zinthu zonse zochitika muselo ziziyenda bwino.

^ ndime 6 Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti zimenezi zingatheke.

^ ndime 18 Mapulotini ena amene maselo amapanga amakhala maenzayimu. Enzayimu iliyonse imapindidwa munjira yapadera kuti izifulumizitsa zinthu zosiyanasiyana zimene zimachitika muselo. Maenzayimu ambirimbiri amagwira ntchito limodzi pothandiza kuti ntchito za muselo ziziyenda bwino.

^ ndime 20 Maselo ena m’thupi la munthu amapangidwa ndi mamolekyu a pulotini pafupifupi 10 biliyoni11 ndipo amakhala amitundu yosiyanasiyana yokwana masauzande ambiri.12