Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri

Onani zimene umboni umanena kenako musankhe nokha kukhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa kapena zinakhalako zokha.

Kodi Mwana Wasukulu Amvere Ziti?

Mwana wasukulu yemwe wakhala akuphunzitsidwa kuti zamoyo zinachita kulengedwa nthawi zambiri sadziwa zoti amvere.

FUNSO 1

Kodi Moyo Unayamba Bwanji?

Yankho la funsoli lingasinthiretu mmene munthu amaonera moyo.

FUNSO 2

Kodi Pali Chamoyo Chimene Si Chodabwitsa?

Ngati ndi zoona kuti zinthu zinasintha kuchokera ku zinthu zina, ndiye kuti payenera kukhala umboni wosonyeza mmene maselo oyambirira anapangikira mwangozi.

FUNSO 3

Kodi Malangizo Anachokera Kuti?

Asayansi akhala akuphunzira za majini a anthu komanso malangizo amene amakhala mu DNA.

FUNSO 4

Kodi Zamoyo Zonse Zinachokera ku Chinthu Chimodzi?

Charles Darwin ndi anzake ananena kuti zamoyo zonse zinachokera ku chinthu chamoyo chimodzi. Kodi zimenezi n’zimene zinachitikadi?

FUNSO 5

Kodi Ndi Nzeru Kukhulupirira Baibulo?

Anthu ambiri amafotokoza Baibulo m’njira yoti lizioneka kuti ndi losamveka, lotsutsana ndi sayansi komanso si lolondola. Kodi zimenezi ndi zoona?

Bibliography

Chigawochi chili ndi mndandanda wa mabuku amene munatengedwa mfundo zina za m’kabukuka.