Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwana Wasukulu Amvere Ziti?

Kodi Mwana Wasukulu Amvere Ziti?

Peter wayamba kuda nkhawa ndi nkhani imene aphunzitsi ake akuphunzitsa. Pa nkhani yophunzitsa, iye amawatayira kamtengo aphunzitsi akewo. Koma angomaliza kufotokoza zimene Charles Darwin ananena zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina ndiponso kuti mfundo imeneyi yathandiza asayansi kumvetsa mmene moyo unayambira. Kenako apempha ana a sukulu kuti afotokoze maganizo awo pankhaniyi.

Zimenezi zamuimitsa mutu Peter. Makolo ake anamuphunzitsa kuti Mulungu ndi amene analenga dziko komanso zamoyo zonse. Iwo anamuuza kuti zimene Baibulo limanena zokhudza chilengedwe ndi zolondola ndiponso kuti mfundo yoti zamoyo zinachita kusintha, ndi maganizo a anthu chabe ndipo zilibe umboni. Aphunzitsi a Peter komanso makolo ake amamufunira zabwino. Kodi pamenepa, Peter amve ziti?

Zimene zinachitikira Peter zimachitika m’masukulu ambiri padziko lonse. Ndiyeno kodi Peter ndi ana a sukulu ena angatani? Apa zikuonekeratu kuti akufunika kufufuza mokwanira kuti adziwe zoona zake pa nkhaniyi. Ndiyeno ayenera kusankha okha zoyenera kukhulupirira.

Baibulo limatichenjeza kuti si bwino kumangokhulupirira m’chimbulimbuli zimene ena akunena. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anati: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza” komanso kuti azitsimikizira ngati zimene akuphunzitsidwa ndi zoona.​—Aroma 12:1, 2.

Cholinga cha kabukuka si kuthandiza anthu azipembedzo amene amafuna kuti nkhani yokhudza kulengedwa kwa zinthu iziphunzitsidwa m’masukulu. Cholinga chake ndi kuunika zimene anthu amanena zoti zamoyo zinangokhalako zokha, komanso kuti nkhani ya m’Baibulo yoti zamoyo zinachita kulengedwa ndi yongopeka.

Tifotokoza kwambiri zokhudza selo chifukwa ndi pamene moyo umayambira. Muwerenga zinthu zosangalatsa zokhudza mmene maselo amapangidwira. Mukhalanso ndi mwayi wounika zifukwa zimene zimachititsa anthu ena kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina.

Tonsefe tikufunika kudziwa yankho la funso lakuti, kodi zamoyo zinachita kulengedwa kapena zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina? Muyenera kuti nkhaniyi munaiganizirapo mozama. Koma kabukuka kafotokoza maumboni ena omwe anathandiza anthu ambiri kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa.