Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi pali chifukwa chilichonse chimene Mulungu analengera dziko lapansili?

Mulungu analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mosangalala

Dziko lapansili linalengedwa m’njira yoti pazikhala zinthu zamoyo. Lili ndi madzi ambiri amene amathandiza kuti zamoyo zisamafe. Komanso mmene dzikoli limayendera, zimathandiza kuti madzi a m’nyanja zonse asamaundane chifukwa cha kuzizira kapena kuwira chifukwa cha kutentha. M’mlengalenga mwa dzikoli mulinso mpweya wosiyanasiyana umene umaliteteza. Palinso mphamvu inayake imene imachokera pansi pa nthaka yomwe imateteza dzikoli. Chinthu chinanso chogometsa kwambiri ndi kudalirana kumene kulipo pakati pa zomera, nyama komanso anthu padzikoli. Poganizira zinthu zonsezi, anthu ambiri amaona kuti Mulungu analenga dzikoli ndi cholinga.—Werengani Yesaya 45:18.

Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndiye kuti zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitika komanso mavuto ena onse, ndi mbali ya cholinga cha Mulungucho?’—Werengani Deuteronomo 32:4, 5.

Kodi Mulungu adzakwaniritsa cholinga chakechi?

Mulungu analenga dzikoli kuti anthu azikhalamo mosangalala, azikondana komanso azikonda Mlengi wawo. Choncho anthu ndi osiyana kwambiri ndi nyama komanso zomera. Anthufe tingathe kuphunzira zokhudza Mlengi wathu ndipo tingathe kutsanzira makhalidwe ake monga chikondi ndi chilungamo.—Werengani Mlaliki 12:13; Mika 6:8.

Mlengi wathu angathe kukwaniritsa zolinga zake zonse. Choncho tingakhale ndi chikhulupiriro choti adzathetsa mavuto onse padzikoli, ndipo anthu adzakhala angwiro ndiponso osangalala.—Werengani Salimo 37:11, 29; Yesaya 55:11.