Undidalire
Pangani Dawunilodi:
1. Timavutika
N’zotigwera mwadzidzidzi.
Moyo ukanakhala wabwino
Popandatu mavutowa.
M’lungu amaona;
Amatidziwanso bwino.
Amadziwa tingachite zambiri.
Ngati tingasankhe bwino.
(KUKONZEKERA KOLASI)
Amatikondadi,
Sayang’ana luso ndi mphatso zathu.
Amafuna kuti
Nafe tizithandizana.
(KOLASI)
Ndiwe mnzanga wokhala nane
Pamavuto ndi pamtenderenso
Ndilipo
Pomwe ukufuna wokuthandiza
Inetu ndilipo
Undidalire.
2. Omwe akulira
Nafe timalira nawo.
Pena misozi imafotokoza,
Mmenetu zatikhudzira.
(KUKONZEKERA KOLASI)
Tikafookatu,
Yehova angatilimbikitsedi.
Nafe tim’tsanzire,
Pomwe tikuthandizana.
(KOLASI)
Ndiwe mnzanga wokhala nane
Pamavuto ndi pamtenderenso.
Ndilipo
Pomwe ukufuna wokuthandiza
Inetu ndilipo.
Undidalire.
(KOLASI)
Ndiwe mnzanga wokhala nane
Pamavuto ndi pamtenderenso.
Ndilipo
Pomwe ukufuna wokuthandiza.
Inetu ndilipo.
Undidalire.

