Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufufuza

Kufufuza

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. ‘M’funefune, mudzapeza’

    Izi ndi zomwe tinamva.

    Mayankho anzeru sankapezeka

    Zinatithetsa nzeru.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Tinafufuza, sitinaleke.

    Tinkadziwa kuti choonadi chilipo.

    (KOLASI)

    Kufufuza cho’nadi

    Kutitu chiyankhe,

    Mafunso othetsa nzeru:

    Chiyambi cha moyo, ndi kufunika kwa Ufumu wa M’lungu.

    Sizophwekadi.

  2. 2. Dzina la M’lungu talidziwa.

    Yehova ndi M’lungu wamoyo.

    Tinapezadi mtendere

    Titadziwa zoona.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Tinayesetsa, sitinasiye,

    Kufufuza cho’nadi chokhudzatu tsogolo.

    (CHORUS)

    Kufufuza cho’nadi

    Chimene chayankha,

    Mafunso othetsa nzeru:

    Chiyambi cha moyo, ndi paradaiso akubwera posachedwayu.

    Ndi zothekadi.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Pano takonzekatu kuthandiza ena

    N’cho’nadi chaulere.

    Kukayankha mafunso awo

    Mowagwiradi mtima.

    Adziwe zomwe tapeza.

    (KOLASI)

    Kufufuza cho’nadi

    Kutitu chiyankhe,

    Mafunso othetsa nzeru:

    Chiyambi cha moyo: moyo wosatha mu Ufumu wa M’lungu.

    Ndi zothekadi.