Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Anu Adzakhala Mpaka Kalekale

Mawu Anu Adzakhala Mpaka Kalekale

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Anaona m’mwamba

    Ankaopa Yehova.

    Ankathokoza M’lungu

    Powasonyeza chikondi.

    M’nawapatsa dzina,

    Ntchito yolalikira.

    Mawu othandiza.

    Kukhala n’chikhulupiriro.

    Ankakukondanidi,

    Ankachita zomwe angathe

    Munalola alembe Mawu,

    Anthu adziwe za inu.

    (KOLASI)

    Mawu anu ndamyaya,

    Mfundo zanu n’zozama.

    Uthenga wake umatitsitsimula,

    Tidzasunga Mawu anu.

  2. 2. O adani anayetsetsa,

    Kuletsa Mawuwa.

    Anthu anu analimba

    Ndi chikhulupirirodi.

    Anateteza Mawu anu,

    Ndi kulolera kuphedwa.

    Umboni wamphamvu anausonyeza,

    N’kuteteza Baibulo.

    (KOLASI)

    Mawu anu ndi a muyaya,

    Mfundo zanu n’zozama.

    Uthenga wake umatitsitsimula,

    Tidzasunga Mawu anu.

  3. 3. Tadziwa dzina lanu Yehova.

    Dzinali lilipobe.

    Mawu anu onse,

    Adzachitikadi,

    Tidzakutamandanibe.

    (KOLASI)

    Mawu anu ndamuyaya,

    Mfundo zanu n’zozama.

    Uthenga wake umatitsitsimula,

    Tidzasunga mawu anu,

    Nthawi zonse.