Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndikhululuke

Ndikhululuke

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Chakukhosi ndachisungadi.

    Chikulemera, ndafooka.

    Ndikuyenera kusintha.

    Ndifunika kukhululuka.

    N’zovuta ngati wolakwa si ‘ne.

    N’ngavutike kukhululuka.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndipempheretu ndipo n’sachedwe.

    Yehova akudziwa chilichonse.

    Wandipatsadi mphamvu

    (KOLASI)

    Kuti mpirire.

    Sin’ngakwanitse pandekha.

    Chonde M’lungu thandizeni

    Kuti n’khululuke.

    Nditsanzire M’lungu

    Pokhululuka, ndi kuiwala.

    Chonde M’lungu thandizeni

    Kuti n’khululuke.

    N’khululuke.

  2. 2. Ndayesetsa kuziiwala,

    Pena mmakumbukila.

    N’kanakonda kungoziiwala.

    Ndiiwale n’kakhululuka.

    Ukutu ndiye kukhululukadi.

    Moyo upitirirebe.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndipempheretu ndipo n’sachedwe.

    Yehova akudziwa chilichonse.

    Wandipatsadi mphamvu

    (KOLASI)

    Kuti mpirire.

    Sin’ngakwanitse pandekha.

    Chonde M’lungu thandizeni

    Kuti n’khululuke.

    Nditsanzire M’lungu

    Pokhululuka, ndi kuiwala.

    Chonde M’lungu thandizeni

    Kuti n’khululuke.

    N’khululuke.

    N’khululuke.

    N’khululuke.

    N’khululuke.