Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Mwana

Ngati Mwana

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Yesutu anati

    Tikhale ngati ana,

    M’dzikolitu anthu ndi onyada,

    Tikhaletu ngati mwana.

    Kuona ena mmene Yehova amawaonera.

    (KOLASI)

    Ngati mwana, tizikondana kwambiri,

    Tione zabwinotu mwa ‘bale athu.

    Ngati mwana, tikhale okoma mtima,

    Tisamaone mavuto mwa anzathu.

  2. 2. Pamene tikukula

    M’dziko limene n’loipa,

    Tingamakaikiretu ena,

    Zolinga, n’zonena zawo.

    Sizophweka kuona ena kukhala otiposa.

    (KOLASI)

    Ngati mwana, tizikondana kwambiri,

    Tione zabwinotu mwa ‘bale athu.

    Ngati mwana, tikhale okoma mtima,

    Tisamaone mavuto mwa anzathu.

    Ngatitu mwana.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Potumikira,

    Yehova M’lungu,

    Timapezadi

    Chisangalalo,

    Tikumbukire

    M’dziko lonyadali,

    Tizikhalatu ngati mwana.

    (KOLASI)

    Ngati mwana, tizikondana kwambiri,

    Tione zabwinotu mwa ‘bale athu.

    Ngati mwana, tikhale okoma mtima,

    Tisamaone mavuto mwa anzathu.

    Ngatitu mwana.