Nyimbo za Broadcasting
Nyimbo zosangalatsa zosonyeza kuyamikira chuma chathu chauzimu.
Mawu Onenedwa pa Nthawi Yoyenera
Mawu abwino angakhale olimbikitsa kwambiri.
Ukhale Mnzanga Mpaka Kalekale
Tingapirire mavuto aliwonse amene tingakumane nawo ngati tingakhale ogwirizana.
Mumatambasula Dzanja Lanu
Kodi kupatsa kwa Yehova kukuthandiza bwanji mlongo wachitsikana kukhala wosangalala akagawira ena zinthu?
Tikusangalala Chifukwa Maso Athu Amaona (Nyimbo ya Msonkhano wa 2026)
Imvani mmene mawu a Yesu amabweretsera chimwemwe chomwe chimatithandiza kuchepetsa nkhawa ndi kulimbitsa chiyembekezo chathu.
Ndidzayembekezera Yehova
Tiziyembekezera Yehova pomaganizira kwambiri za zinthu zina osati za mavuto omwe tikukumana nawo m’ndende, komanso pomalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu.
Mumamva Pemphero
Tikamauza Yehova nkhawa zathu momasuka, Iye adzatipatsa mtendere wosatha.
Zosowa Zanga Zauzimu
Kuchita zinthu zolimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova kumatithandiza kuti tizisangalala
Ndidzayembekezera Yehova
Tiziyembekezera Yehova pomaganizira kwambiri za zinthu zina osati za mavuto omwe tikukumana nawo m’ndende, komanso pomalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu.
Muziwauza Kuti Mumawakonda
Onani mmene anthu omwe akukumana ndi zinthu zosiyanasiyana akusonyezera ena chikondi mwa mawu ndi zochita.
Timakuona
Timanyadira alongo athu achikhristu kuzungulira dziko lonse lapansi.
Njira Yakumoyo Wosatha
Kuchita zambiri potumikira Yehova kuyambira tili achinyamata kumatithandiza kukhalabe pa njira yokapeza moyo wosatha.
Ndizigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi
Kuganizira za mphatso ya moyo kumatithandiza kuti tizigwiritsira ntchito bwino nthawi pocheza ndi anthu omwe timawakonda.
Ndi Chikondi cha Yehova
M’Baibulo muli mawu ambiri osangalatsa ofotokoza za chikondi. Onani mmene chikondichi chakhala chikulimbitsira komanso kuthandiza atumiki a Mulungu kuyambira kalekale.
Chikondi Chapamwamba
Ndi madalitso otani omwe akukudikirirani mukawonjezera utumiki wanu kwa Yehova?
“Ndimasangalala Kuchita Zimene Mumafuna” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2025)
Potsanzira chitsanzo cha Yesu chomvera Mulungu mwachimwemwe, nafenso timasangalala pochita zimene Mulungu amafuna.
Ndi Pompano
Tisangalala ndi madalitso m’dziko latsopano posachedwa.
Ndili M’manja Mwanu
Kulola kuumbidwa ndi Yehova kungathandize kusintha moyo wathu.
Kukhala Mwamtendere M’dziko Lopanda Mtendere
Kukhala mwamtendere kumalemekezetsa Yehova.
“M’patseni Yehova Ulemerero”
Timathokoza komanso kupereka ulemerero kwa Yehova chifukwa choti timamukonda.
Mphamvu Yoposa Yanga
Onani mmene Yehova amathandizira ”anthu amene alibe wowathandiza.”
Tizikhutira
Tidzakhaladi osangalala tikamakhutira ndi zimene Yehova amatipatsa.
Ima Uone
Kodi kuganizira za chilengedwe kungatithandize bwanji kuthana ndi mavuto amene atimakumana nawo pamoyo wathu?
“M’dziko Labwino”
Kuganizira kwambiri za chiyembekezo chathu kumatithandiza kupirira ngakhale mavuto aakulu.
“Uthenga Wabwino” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2024)
Kuyambira kale mpaka pano, anthu akhala akulalikira za uthenga wabwino mosangalala. Ntchitoyi ndi yaikulu kwambiri. Yesu ndi amene amaitsogolera ndipo angelo amathandiza nawo pa ntchitoyi.
Ndilimbitse Chikhulupiriro Changa
Limbitsani chikhulupiriro chanu kuti muthane ndi kukaikira.
Tisafooke
Muzidalira Yehova ndi kupitirizabe kulalikira ngakhale pomwe mukuchita mantha.
Amatidziwa Bwino
Yehova amadziwa bwino aliyense payekha ndipo amamvetsa zomwe zili mumtima mwathu.
“Timakobidi Tiwiri”
Yehova amayamikira zopereka zanu. Zambiri kaya zochepa.
Tidzamuimbira
Timasangalala ndi mtendere chifukwa chotumikira Yehova.
Ndimuyandikire
Yehova amachita chidwi ndi anthu amene akufunitsitsa kumuyandikira ndipo satengera zimene anthuwo ankachita m’mbuyomu.
“Sadzachedwa” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2023)
Muzitsanzira anthu okhulupirika pamene mukuyembekezera Yehova.
Moyo Wosatha
Tingakhale ndi moyo wosangalala ndi watanthauzo panopa komanso mtsogolo.
Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa
Ukaphunzirapo kanthu pa zimene walakwitsa, udzakhala wolimba kuposa kale.
Tigwirizanenso
Siyani kuganizira zimene ena akulakwirani ndipo muyambirenso kugwirizana
Yehova Ali Nane
Ndi thandizo la Yehova sitingaope chilichonse.
Ndingapite Kwa Ndani?
Tsanzirani mtumiki wa Yehova wokhulupirika amene akuyesetsa kumvera mawu a Yesu kwa moyo wake wonse.
Kudzakhala Mtendere (Nyimbo ya Msonkhano ya 2022)
M’malo momangoganizira za mavuto omwe tikukumana nawo, tiziganiziranso za mtendere umene M’lungu watilonjeza.
Pamodzi, Timalimba Mtima
Ndi thandizo la Yehova komanso ubale wathu wapadziko lonse tikhoza kupilira mayesero aliwonse.
Tili M’banja la Yehova
Padakali anthu ena m’dzikoli amene akusakasakabe choonadi. Vidiyoyi ikuthandizani kuona zimene mungachite kuti mupitirize kuthandiza anthu amene ali ngati nkhosawa.
Muzipeza Mpata Wolambira
Kuchita zambiri potumikira Yehova n’kofunika kwambiri pamoyo wathu.
Muone
Muzisangalala ndi chiyembekezo chokhudza dziko latsopano.
Gwiritsani Ntchito Mphamvu Zanu Potumikira Yehova
Gwiritsani ntchito mphamvu zanu potumikira Yehova. Simudzanong’oneza bondo!
“Kondwerani Nthawi Zonse”
Nyimbo yachisangalalo ikhoza kutikumbutsa zifukwa zambiri zokhalira osangalala.
Ndi Maso a Chikhulupiriro
Ganizirani tsogolo losangalatsa limene Mulungu wakonzera anthu.
Ndife Gulu Logwirizana
Timakhalabe gulu limodzi logwirizana, ngakhale pomwe tikukumana ndi zinthu zoyesa chikhulupiriro chathu komanso mavuto.
Muziteteza Maganizo Anu
Yehova angakuthandizeni kuti muwine nkhondo yolimbana ndi maganizo ofooketsa.
Ndiwe Wekha
Muzisangalala ndi mphatso ya banja imene Yehova anapereka.
Sitisiya
Kumanga chikhulupiriro cholimba kumadalira zipangizo zomangira zabwino.
Thamanga
Muzisankha zochita mwanzeru kuti mupambane pampikisano wokalandira moyo.
Ndikhululuke
Kodi wina wakukhumudwitsani? Kodi mukuvutika kuziiwala? Onani zimene mungachite kuti mukhululuke.
Chimwemwe Chosatha
Yehova ndi amene amatipatsa chimwemwe ndipo sadzasiya.
Tsimikizani
Tikhoza kutsimikiza mtima kuti Yehova amatikonda, ngakhale pomwe tikukumana ndi mayesero.
Ngati Mwana
Kodi tingakhale bwanji ngati mwana posonyeza chikondi?
Mutulire Yehova
Mukakhala ndi nkhawa, pitirizani kudalira Yehova kuti akupatseni mphamvu komanso akutonthozeni.
Ndadzipereka Kwa Inu
Chifukwa cha chikondi cha Yehova, timadzipereka mpaka kubatizidwa.
Chikondi Sichitha
Chikondi cha Yehova sichitha. Chimatipatsa chimwemwe ndi kutitonthoza.
Dziko Latsopano Lomwe Likubwera
Zimene timayerekezera kuona m’maganizo mwathu zikhoza kutichititsa kuona kuti zimene tikuyembekezera ndi zenizeni. Nyimboyi ikutithandiza kuti tiziika maganizo athu onse pa dziko latsopano.
Yehova Amatithandiza Nthawi Zonse
Yehova amafunitsitsa kutithandiza.
“Menya Nkhondo Yabwino Yosunga Chikhulupiriro”
Tikhoza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale pomwe tikukumana ndi mavuto.
Ndife Banja Limodzi
Kuli konse komwe tili, ndife a m’banja la Yehova.
Tiziyamikira Chilengedwe cha Mulungu
Muzipeza nthawi yoganizira mozama zinthu zimene Yehova analenga ndipo muzimuthokoza m’pemphero.
Ukhale Wolimba Mtima Ndipo Uchite Zinthu Mwamphamvu
Nyimbo yabwino kwambiri yotithandiza kupirira.
Tsiku Lililonse Lili N’zodetsa Nkhawa Zake
Tikhoza kupeza mtendere ndi chimwemwe ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto.
Ndidzakupatsani Zonse Zomwe Ndingathe
Yehova ndi woyeneradi kumutumikira ndi mtima wathu wonse.
Yehova Watithandiza Kukhala Amodzi
Ngakhale kuti tili mu dziko loipali, koma tili ndi abale athu okonda mtendere komanso ogwirizana.
Undidalire
Pamavuto ndi pamtendere, tingadalire mabwenzi enieni.
Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima
Yehova angatithandize kuti tipirire molimba mtima mayesero alionse amene tingakumane nawo.
Mabwenzi Enieni
Kodi tingapeze kuti mabwenzi enieni?
Kufufuza
Omwe akufunitsitsa kudziwa Mulungu angafunike kuchita khama pomwe akufufuza za iye.
Tisaope
Pamene zinthu zikuvuta pamoyo wathu, tizikumbukira kuti sitili tokha.
Kukonda Abale
Palibe gulu lina lililonse padzikoli limene lingafanane ndi Mboni za Yehova pa nkhani yothandizana.
Sangandisiye
Yehova Mulungu wathu sangatisiye!
Ndikusintha
Kodi mukufunitsitsa kusintha mmene mumachitira zinthu pa utumiki wanu?
Wokondedwa Wanga
Kudalira Yehova Mulungu kudzathandiza kuti banja lanu likhale lolimba!
Ndikukhulupirireni
Kuphunzira mawu a Mulungu ndi kuganizira zimene tikuphunzirazo kungatithandize kupirira mavuto amene tikukumana nawo pa moyo.
Zinthu Zofunika
Tiyenera kumapeza nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri—kupemphera, kuphunzira, ndi kudzipereka kwa Mulungu.
Chilengedwe Chanu Chimandidabwitsa
Ntchito za manja a Yehova zimatidabwitsa ndipo zimatichititsa kumuimbira.
Yang’ane
Gwiritsani ntchito bwino nthawi yocheza ndi abale ndi alongo.
Malo Amene Adzachititsa Kuti Mulemekezedwe
Ndife osangalala kupereka kwa Yehova malo amene adzachititsa kuti dzina lake lalikulu lilemekezedwe.
Tisachedwe
Monga atumiki a Yehova, kuwonjezera zochita mu utumiki wathu m’njira iliyonse kungatibweretsere chimwemwe chochuluka.
Mwana Wanga Wamkazi Wapadera
Pamene zaka zikudutsa, bambo akuona mwana wake wamkazi akukula ndi kuyamba kuona choonadi kuti ndichakechake.
Ntchito Zanu N’zodabwitsa
Kusangalala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Yehova!
Ndidzadzukanso
Tsanzirani munthu yemwe poyamba anali wakhama potumikira Yehova ndipo akupezanso mphamvu n’kubwerera atakumbukira chikondi chimene mpingo unkamusonyeza.
Ndimasunga Malamulo Anu
Zolankhula ndi zochita zathu zizisonyeza kuti timakonda Yehova.
Yehova Amandithandiza Kukonza Tsogolo Langa
Tsiku ndi tsiku tizisankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova.
Zidzatiyendera Tikamapemphera
Kodi tingatani tikakumana ndi mavuto?
Mawu Anu Adzakhala Mpaka Kalekale
Tiyenera kutamanda Yehova chifukwa choti wasunga Mawu ake kuti anthu aziwagwiritsa ntchito
Muziphunzira Kuti Mukhale Olimba
Achinyamata akhoza kukhala olimba mwauzimu ngati atamaphunzira Mawu a Mulungu paokha.
Zimene Timasankha
Ndi nzeru kumaganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire utumiki wathu komanso anthu ena.
Dziko Latsopano Lili Pafupi
Kuyembekezera mwachidwi Paradaiso amene akubwerayu kungatithandize kuti tipirire.
Tizikhululukirana
Tiziyesetsa kutsanzira Yehova n’kumakhululukira ena.
Anzanga Apamtima
Kodi mungasankhe bwanji anzanu apamtima?
Tikuthokoza
Yehova amatithandiza ndi mzimu wake woyera, kupirira mavuto ochuluka amene timakumana nawo. Zimenezi zimatichititsa kumuimbira nyimbo zomuthokoza.
“Khalani Ochereza”
Kodi mungasonyeze kuchereza m’njira ziti?
Musathamange
Utumiki wathu komanso zinthu zina pamoyo wathu kawirikawiri zimayenda bwino tikamachita zinthu mosapupuluma.
Madalitso Ophunzira Chinenero China
Kodi mungapeze madalitso otani chifukwa chophunzira chilankhulo china?
Tiyendebe
Tipitirizebe kuyenda ndi gulu la Yehova lomwe likupita patsogolo
Ganizira Nthawiyo
Tikuyembekezera nthawi imene zinthu zonse zidzakhale zabwino.
Kusangalala ndi Misonkhano
Tikapita ku msonkhano, timasangalala ndi mgwirizano komanso chikondi chomwe abale padziko lonse ali nacho.
Yehova Wakulandira
Mzimu woyera wa Mulungu ungakuthandizeni kuti mubwerere kwa iye.
Kungomwetulira
Kumwetulira kungatithandize muutumiki komanso pa moyo wathu.
Ndasangalala Kuti Sindinagonje
N’chiyani chingathandize achinyamata kuti asatengere zochita za anzawo kusukulu?
Sindidzasiya
Muzidalira Yehova ndipo musasiye kumutumikira.
Moyo wabwino kwambiri
Timasangalala kwambiri tikamathandiza komanso kulimbikitsa ena.
Pepani, palibe mawu ofanana ndi omwe mwasankha.

