Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ganizira Nthawiyo

Ganizira Nthawiyo

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Pano moyo ndi wovuta.

    Chakudya n’choperewera.

    N’katseka maso ndimaona

    Ndili m’dziko latsopano.

    (KOLASI)

    Taganizira nthawi imene,

    Moyo udzakhaladi wabwino.

    Taganizira pomwe tidzati,

    “Zikomo moyo wabwino zonse zabwino.”

  2. 2. Ndinabadwatu wogontha,

    Masowa sakuonanso.

    Makutu adzayamba kumva.

    Maso anga adzaona.

    (KOLASI)

    Taganizira nthawi imene,

    Moyo udzakhaladi wabwino.

    Taganizira pomwe tidzati,

    “Zikomo moyo wabwino zonse zabwino.”

    (VESI LOKOMETSERA)

    Sin’ngayende koma ndikudziwa.

    Tsiku lina ndidzathamanga!

    (KOLASI)

    Taganizira nthawi imene,

    Moyo udzakhaladi wabwino.

    Ganizira chisangalalo chake

    Tsiku lililonse n’labwino.

    (KOLASI)

    Taganizira nthawi imene,

    Moyo udzakhaladi wabwino.

    Taganizira pomwe tidzati,

    “Zikomo moyo wabwinowu.”